Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO

N’cifukwa Ciani Yesu Anavutika Ndi Kufa?

N’cifukwa Ciani Yesu Anavutika Ndi Kufa?

‘Ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzela mwa ucimo.’—Aroma 5:12

Mungayankhe bwanji mutafunsidwa kuti, “Kodi mungakonde kukhala ndi moyo kwamuyaya?” Anthu ambili angakambe kuti inde, koma amaona kuti zimenezo sizingacitike. Iwo amakamba kuti anthufe tinalengedwa kuti tizifa.

Koma bwanji ngati akufunsani kuti, “Kodi mwakonzekela kufa?” Anthu ambili angakambe kuti iyai. Izi zionetsa kuti mwacibadwa anthufe timafuna kukhalabe ndi moyo, ngakhale kuti timakumana ndi mavuto ambili. Baibulo limakamba kuti Mulungu analenga anthu ndi cifuno cokhala ndi moyo kwamuyaya. Limakamba kuti “[iye] anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”—Mlaliki 3:11.

Koma zoona zake n’zakuti anthu sakhala ndi moyo kwamuyaya. Nanga n’ciani cinalakwika? Kodi Mulungu anacitapo ciliconse kuti akonze zinthu? Mayankho a m’Baibulo ndi okhazika mtima pansi, ndipo amaonetsa cifukwa cake Yesu anavutika ndi kufa.

N’CIANI CINALAKWIKA?

Macaputala atatu oyambilila a buku la Genesis m’Baibulo, amatiuza kuti Mulungu anapatsa anthu oyambilila Adamu ndi Hava mwai wakuti akhale ndi moyo kwamuyaya. Iye anawauza zimene anayenela kucita kuti akhale kwamuyaya. Macaputala amenewa afotokoza kuti iwo sanamvele Mulungu ndipo anataya mwai umenewo. Anthu ambili amaona kuti nkhani imeneyo ndi nthano cabe. Koma mofanana ndi mabuku a Uthenga Wabwino, zimene zinalembedwa m’buku la Genesis ponena za mbili yakale n’zoona. *

Kodi n’ciani cinacitika pambuyo pakuti Adamu sanamvele Mulungu? Baibulo limayankha kuti: “Monga mmene ucimo unaloŵela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi [Adamu] ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.” (Aroma 5:12) Mwakusamvela Mulungu, Adamu anacimwa. Zimenezi zinacititsa kuti ataye mwai wokhala ndi moyo kwamuyaya. Patapita nthawi, iye anafa. Popeza ndife mbadwa zake, tinatengela ucimo kwa iye. Ndiye cifukwa cake timadwala, timakalamba, ndi kufa. Izi n’zofanana ndi mmene mwana amatengela zocita za makolo ake. Kodi Mulungu anacitapo ciliconse kuti akonze zinthu?

ZIMENE MULUNGU ANACITA

Mulungu anapanga makonzedwe akuti abwezeletse mwai wokhala ndi moyo kwamuyaya umene Adamu anataya kwa mbadwa zake. Kodi Mulungu anacita bwanji zimenezo?

M’Baibulo, pa Aroma 6:23 pamati: “Malipilo a ucimo ndi imfa.” Zimenezi zitanthauza kuti ucimo umabweletsa imfa. Adamu anacimwa, ndiye cifukwa cake anafa. Mofananamo, ifenso ndife ocimwa ndipo timalandila malipilo a ucimo amene ndi imfa. Conco, timabadwa ndi ucimo ngakhale kuti si mwakufuna kwathu. Mwacikondi, Mulungu anatuma Mwana wake, Yesu, kudzatilipilila “malipilo a ucimo.” Kodi zimenezi zinatheka bwanji?

Imfa ya Yesu inatsegula njila yodzakhala ndi moyo wacimwemwe komanso wamuyaya

Popeza munthu mmodzi wangwilo, Adamu, anabweletsa ucimo ndi imfa mwa kusamvela Mulungu, panafunikanso munthu wangwilo womvela mpaka imfa n’colinga cakuti atimasule ku ucimo. Baibulo limafotokoza kuti: “Monga mwa kusamvela kwa munthu mmodziyo, ambili anakhala ocimwa, momwemonso kudzela mwa kumvela kwa munthu mmodziyu, ambili adzakhala olungama.” (Aroma 5:19) “Munthu mmodziyu,” ndi Yesu. Iye anacoka kumwamba, ndi kukhala munthu wangwilo *, kenako anatifela. Pa cifukwa cimeneci, zinakhala zotheka kwa ife kuyesedwa olungama ndi kuima pamaso pa Mulungu, komanso kukhala ndi mwai wodzakhala ndi moyo kwamuyaya.

CIFUKWA CAKE YESU ANAVUTIKA NDI KUFA

Nanga n’cifukwa ciani Yesu anafunika kufa? Kodi Mulungu Wamphamvuyonse sakanangopeleka lamulo lakuti mbadwa za Adamu zikhale kwamuyaya? Iye anali ndi mphamvu yocita zimenezo. Koma kucita zimenezo kukanakhala kunyalanyaza lamulo lake lakuti malipilo a ucimo ndi imfa. Limenelo si lamulo wamba limene lingacotsedwe kapena kusinthidwa pofuna kusangalatsa ena. Lamulo limenelo limagwilizana kwambili ndi cilungamo cake.—Salimo 37:28.

Ngati kuti Mulungu sanaonetse cilungamo pankhaniyi, anthu akanaganiza kuti Mulungu sangacite zinthu mwacilungamo pankhani zinanso. Mwacitsanzo, kodi cikanakhala cilungamo ngati akanasankha mbadwa zina za Adamu kuti zikhale kwamuyaya? Kodi anthu akanam’khulupilila kuti amasunga malonjezo ake? Cilungamo cimene Mulungu anatsatila kuti atipulumutse, cimatitsimikizila kuti iye amacita zinthu mwacilungamo nthawi zonse.

Cifukwa ca nsembe ya Yesu, Mulungu anatsegula mwai wodzakhala ndi moyo wosatha m’Paladaiso padziko lapansi. Pa Yohane 3:16 Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asaonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” Imfa ya Yesu simangoonetsa cilungamo ca Mulungu, koma imaonetsanso cikondi cacikulu cimene Mulungu ali naco pa anthu.

Nanga n’cifukwa ciani Yesu anavutika ndi kufa imfa yoŵaŵa monga mmene zinalembedwela m’Mauthenga Abwino? Mwa kukhalabe wokhulupilika pokumana ndi mavuto aakulu, Yesu anaonetselatu kuti zimene Mdyelekezi anakamba zakuti anthu sangakhale okhulupilika kwa Mulungu akakumana ndi, n’zabodza. (Yobu 2:4, 5) Zimene Satana anakamba zinaoneka monga n’zoona cifukwa poyamba anacititsa Adamu munthu wangwilo kucimwa. Koma Yesu, amene anali wangwilo monga Adamu, anakhalabe womvela ngakhale kuti anavutika kwambili. (1 Akorinto 15:45) Motelo, iye anaonetsa kuti zinali zotheka kwa Adamu kusankha kumvela Mulungu. Mwa kupilila pamene anali kuvutitsidwa, Yesu anatisiila citsanzo cakuti titsatile.(1 Petulo 2:21) Mulungu anadalitsa Mwana wake cifukwa ca kumvela mwa kumuukitsila kumoyo wosafa, kumwamba.

MMENE MUNGAPINDULILE NDI IMFA YA YESU

Imfa ya Yesu inacitikadi, ndipo inatsegula njila yodzakhala ndi moyo kwamuyaya. Kodi mukufuna kudzakhala ndi moyo wosatha? Yesu anafotokoza zimene tifunika kucita pamene anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Kristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

Amene amafalitsa magazini ino akukupemphani kuti muphunzile zambili za Yehova, Mulungu woona, ndi za Mwana wake Yesu Kristu. A Mboni za Yehova amene ali m’dela lanu ndi okonzeka kukuthandizani. Mudzaphunzilanso zambili mukapita pa webusaiti yathu ya www.pr418.com.

^ par. 8 Onani nkhani yakuti “The Historical Character of Genesis,” m’buku lacingelezi la Insight on the Scriptures, pa tsamba 922, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ par. 13 Mulungu anasamutsa moyo wa mwana wake ndi kuuika m’mimba mwa Mariya, ndipo iye anakhala ndi pakati. Mzimu woyela wa Mulungu unateteza Yesu kuti asatengele kupanda ungwilo kwa Mariya.—Luka 1:31, 35.