Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumvera Chenjezo Kungapulumutse Moyo Wanu

Kumvera Chenjezo Kungapulumutse Moyo Wanu

PA 26 December 2004, pachilumba cha Simeulue panachitika chivomezi champhamvu kwambiri. Chilumbachi chili kumpoto chakumadzulo kwa chilumba cha Sumatra m’dziko la Indonesia. Chivomezichi chitangochitika, anthu onse amene anali m’mphepete mwanyanja ankangoyang’ana zomwe zikuchitika panyanjapo. Nyanjayo inaphwa mwamsanga kwambiri kuposa mmene imachitira nthawi zonse. Nthawi yomweyo aliyense anayamba kuthawira kumapiri ndipo ankakuwa kuti, “Smong! Smong!” mawu omwe amatanthauza tsunami. Kenako pasanathe maminitsi 30, madzi aja anabwerera mwamphamvu n’kuwononga midzi yambiri.

Chilumba cha Simeulue n’chimene chinali choyamba kuwonongedwa ndi tsunami wamphamvu kwambiri ameneyu. Pa nthawiyi pachilumbachi panali anthu okwana 78,000 koma anthu 7 okha ndi amene anamwalira chifukwa cha tsunamiyu. N’chifukwa chiyani panamwalira anthu ochepa chonchi? * Anthu a pachilumbachi amakonda kunena kuti: ‘Kukangochitika chivomezi champhamvu, madzi panyanja n’kuphwera, thawirani kumapiri chifukwa posakhalitsa madziwo abwerera mwamkokomo.’ Zimene zakhala zikuchitika panyanjayi zinathandiza kwambiri anthu a pachilumbachi kuzindikira kuti kuchitika tsunami. Ndipo ambiri anapulumuka chifukwa chomvera chenjezo.

Baibulo limanena kuti posachedwapa kuchitika “chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano, ndipo sichidzachitikanso.” (Mateyu 24:21) Tisamaganize kuti chisautsochi chidzakhala mapeto a dziko oyambika chifukwa cha zinthu zoipa zimene anthu akuchita kapenanso chifukwa cha ngozi zimene zikuchitika m’chilengedwe. Tikutero chifukwa Mulungu amafuna kuti dziko lapansili lidzakhalepo mpaka kalekale. (Mlaliki 1:4) Ndiponso Mulungu ndi amene adzayambitse chisautsochi pofuna ‘kuwononga amene akuwononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18; Miyambo 2:22) Zimenezitu zidzakhala zosangalatsa kwambiri.

Komanso chisautso chachikulu chidzawononga anthu oipa okhaokha mosiyana ndi mmene zimakhalira pakachitika tsunami, chivomezi kapenanso kuphulika kwa mapiri. Baibulo limati, “Mulungu ndiye chikondi.” Ndipo Mulungu amene dzina lake ndi Yehova, walonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (1 Yohane 4:8; Salimo 37:29) Ndiyeno mungatani kuti mudzapulumuke chisautso chachikuluchi ndi kudzasangalala ndi madalitso amene Mulungu walonjezawa? Chinsinsi chake chagona pa kumvera chenjezo.

MUZIKHALA TCHERU ZINTHU ZIKAMASINTHA

Anthufe sitinganeneretu tsiku lenileni limene Mulungu adzathetse mavuto ndi zinthu zoipa padzikoli, chifukwa Yesu ananena kuti: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” Komabe Yesu anatilimbikitsa kuti, “Khalanibe maso.” (Mateyu 24:36; 25:13) Kodi n’chifukwa chiyani ananena kuti tikhalebe maso? Baibulo limatifotokozera momveka bwino zinthu zomwe zichitike padzikoli, Mulungu asanabweretse mapeto. Anthu apachilumba cha Simeulue ataona kuti nyanja yaphwera mwadzidzidzi anadziwa kuti kuchitika tsunami. Mofanana ndi zimenezi, kusintha kwa zochitika zikuluzikulu zapadzikoli kukutithandizanso kuzindikira kuti mapeto ali pafupi kwambiri. Onani bokosi kuti mudziwe zochitika zikuluzikulu zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika.

N’zoona kuti zina mwa zinthu zimene zatchulidwa m’bokosili zinachitika m’mbuyomu pa nthawi zosiyanasiyana. Koma Yesu ananena kuti tikadzaona “zinthu zonsezi” tidzadziwe kuti mapeto ali pafupi. (Mateyu 24:33) Ndiyeno muzidzifunsa kuti, ‘M’mbiri yonse ya anthu, kodi ndi nthawi iti yomwe zinthu zoterezi (1) zinachitika pafupifupi dziko lonse, (2) zinachitika pa nthawi yofanana ndiponso (3) zafika poipa kwambiri?’ Apatu n’zoonekeratu kuti tikukhala m’nthawi imene mapeto ali pafupi kwambiri.

MULUNGU AMATICHENJEZA CHIFUKWA CHAKUTI AMATIKONDA

Pulezidenti wina wakale wa dziko la America ananena kuti, “Kuchenjeza anthu mwamsanga . . . kumathandiza kuti apulumuke.” Motero, pambuyo pa tsunami yemwe anachitika mu 2004, boma linaika maalamu m’dera limene munachitika tsunamiyo pofuna kuteteza anthu. Mulungu nayenso akuchenjezeratu anthu mapeto asanafike. Ndipotu Baibulo linaneneratu kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.

Chaka chatha, a Mboni za Yehova anathera maola oposa 1.9 biliyoni akulalikira uthenga wabwino m’mayiko 240, komanso m’zinenero zoposa 700. Umenewutu ndi umboni wosakaikitsa wosonyeza kuti mapeto ali pafupi. A Mboni za Yehova amagwira mwakhama ntchito yochenjeza anthu za tsiku la Mulungu lachiweruzo lomwe likubwera mwamsanga. Iwo amachita zimenezi chifukwa choti amakonda kwambiri anthu. (Mateyu 22:39) Zimene mwawerenga m’nkhaniyi zingakuthandizeni kuti mudzapulumuke ndipo umenewu ndi umboni wakuti Yehova amakukondani. Nthawi zonse muzikumbukira kuti “[Mulungu] safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Petulo 3:9) Kodi inuyo mumvera chenjezo limene Mulungu akukuuzani chifukwa chokukondani?

THAWIRANI KUMALO OMWE MUNGATETEZEKE

Anthu amene ankakhala m’mphepete mwa nyanja pachilumba cha Simeulue ataona kuti nyanja ikuphwera, anathawira kumapiri ndipo sanadikire kuti madzi ayambe abwerera kaye. Iwo anadziwa kuti akathawa mwamsanga apulumuka. Kuti nanunso mudzapulumuke chisautso chikubwerachi, muyenera kuthawira kumalo achitetezo omwe tingawayerekezere ndi mapiri ndipo muyenera kuchita zimenezi nthawi isanathe. Koma kodi mungachite bwanji zimenezi? Mulungu anauza mneneri Yesaya kuti alembe uthenga woitana anthu “m’masiku otsiriza” ano kuti: “Bwerani anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova . . . Iye akatiphunzitsa njira zake.”—Yesaya 2:2, 3.

Munthu amene wathawira paphiri amaona bwinobwino zimene zikuchitika pansi ndipo amakhala wotetezeka. Mofanana ndi zimenezi, anthu ambiri masiku ano akusintha moyo wawo chifukwa chodziwa bwino zimene Mulungu amafuna ndipo zimawathandiza kuti azisankha bwino zochita pamoyo wawo. (2 Timoteyo 3:16, 17) Komanso zimawathandiza kuti ayambe “kuyenda m’njira” za Mulungu ndipo Iye amawakonda ndi kuwateteza.

Kodi inuyo mumvera pamene Mulungu akukuitanani kuti muthawire kumalo achitetezo m’masiku otsiriza ano? Tikukulimbikitsani kuti muganizire mofatsa maumboni a m’Baibulo omwe ali m’bokosi patsamba 12 ndi 13, onena za ‘masiku otsiriza’. A Mboni za Yehova a m’dera lanu akhoza kukuthandizani kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo komanso mmene mungazigwiritsire ntchito pamoyo wanu. Mukhozanso kupeza mayankho a mafunso anu pawebusaiti yathu ya www.pr418.com. Fufuzani pa mawu akuti, ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO.

^ ndime 3 Anthu onse amene anaphedwa ndi tsunamiyu m’chaka cha 2004, anali opitirira 220,000. Palibenso tsunami wina amene anapha anthu ochuluka kuposa ameneyu.