Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kumvela Cenjezo Kumapulumutsa

Kumvela Cenjezo Kumapulumutsa

PA December 26, 2004, civomezi camphamvu kwambili cinagwedeza cilumba ca Simeulue. Cilumba cimeneci cili kumpoto koma cakumadzulo kwa mzinda wa Sumatra ku Indonesia. Anthu onse anali kuyang’ana ku nyanja. Madzi a m’nyanja imeneyi anayamba kuoneka monga akucepa. Mofulumila anthu onse anayamba kuthaŵila ku mapili, uku akukuwa kuti “Smong! Smong!” mau otanthauza tsunami m’cinenelo cao. Patangopita mphindi 30 cabe, mafunde amphamvu anaomba cilumbaco ndi kuononga midzi ndi nyumba zambili.

Cilumba ca Simeulue cinali coyamba kuonongedwa ndi tsunami wa pa Nyanja ya India. Pa anthu 78,000 okhala pa cilumbaci, ndi anthu 7 cabe amene anafa. N’cifukwa ciani ndi anthu ocepa cabe amene anafa? * Mwambi wa anthu a pa cilumba umati: ‘Civomezi camphamvu cikayamba pa nyanja ndipo madzi akayamba kuoneka monga akucepa, thaŵilani ku mapili cifukwa madzi akakhutukila kumtunda adzaloŵa m’nyumba.’ Kucokela pa zimene zinawacitikilazi, anthu a ku Simeulue akaona zimene zikucitika pa nyanja, amadziŵa kuti kubwela tsunami. Kumvela cenjezo kunawapulumutsa.

Baibulo limakamba za ngozi imene ikubwela. Limati: “Kudzakhala cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko mpaka tsopano, ndipo sicidzacitikanso.” (Mateyu 24:21) Koma kumeneku si kutha kwa Dziko cifukwa ca zocita za anthu kapena ngozi za cilengedwe. Colinga ca Mulungu n’cakuti dziko lapansi likhalepo mpaka kalekale. (Mlaliki 1:4) Komabe, cisautso cimene cikubwela ndi nkhondo ya Mulungu “yoononga amene akuononga dziko lapansi.” (Chivumbulutso 11:18; Miyambo 2:22) Limenelo lidzakhala dalitso lalikulu.

Mosiyana ndi tsunami, zivomezi kapena kuphulika kwa mapili, nkhondo imene ikubwela sidzapha anthu osalakwa. Baibulo limati “Mulungu ndi cikondi.” Ndipo Mulungu amene dzina lake ndi Yehova, walonjeza kuti “olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (1 Yohane 4:8; Salimo 37:29) Kodi inu mungacite ciani kuti mukapulumuke cisautso cimeneci ndi kulandila madalitso oculuka? Cofunika ndi kumvela cenjezo.

KHALANI MASO KU ZOCITIKA ZA PADZIKOLI

Sitingathe kudziŵa tsiku lenileni pamene zinthu zoipa ndi kuvutika zidzatha. Yesu anati: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziŵa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” Ngakhale n’telo, Yesu anatilimbikitsa ‘kukhalabe maso.’ (Mateyu 24:36; 25:13) N’cifukwa ciani tifunika kukhalabe maso? Baibulo limafotokoza zimene zidzayamba kucitika padziko lapansi Mulungu asanaononge anthu oipa. Monga mmene kusintha kwa mwadzidzidzi kwa pa nyanja kunacenjezela anthu okhala ku Simeulue za kubwela kwa tsunami, zocitika za padzikoli zikuticenjeza kuti mapeto ali pafupi. Bokosi limene lili m’nkhani ino lionetsa zocitika zosiyanasiyana zimene Baibulo limakamba.

Zina mwa zocitika zimene zili ka bokosi zinacitikapo ndipo zikucitikanso. Yesu anakamba kuti mukadzaona “zinthu zonsezi” mukadziŵe kuti mapeto ali pafupi. (Mateyu 24:33) Dzifunseni kuti, ‘Ndi liti pamene zinthu zonse zochulidwa m’Baibulo (1) zinacitika padziko lonse lapansi, (2) zinacitika panthawi imodzi, ndi (3) zinaipilaipilabe?’ Ndithudi tikukhala m’nthawi imeneyi.

MMENE MULUNGU WAONETSELA KUTI AMATIKONDA

Amene anali pulezidenti wa dziko la U.S. anati: “Kucenjeza anthu kukali nthawi . . . kumapulumutsa moyo.” Tsunami amene anacitika mu 2004 atatha, boma linaika njila zocenjezela anthu m’madela onse okhudzidwa kuti ateteze miyoyo ya anthu ku ngozi yofanana. Mofananamo, Mulungu akupeleka cenjezo cionongeko cisanafike. Baibulo linakambilatu kuti: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.

Caka catha, Mboni za Yehova zinathela maola oposa 1.9 biliyoni zikulalikila uthenga wabwino m’maiko 240, m’zinenelo zoposa 700. Kupita patsogolo kwa nchito imeneyi ndi umboni wakuti mapeto ali pafupi. Cifukwa cokonda anzao, Mboni za Yehova zimacenjeza anthu ena za tsiku la ciweluzo la Mulungu limene likubwela. (Mateyu 22:39) Ngati mumapindula ndi uthenga umenewu, ndi umboni wakuti Yehova amakukondani. Kumbukilani kuti iye “[Mulungu] safuna kuti wina aliyense adzaonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Petulo 3:9) Kodi mudzayamikila cikondi ca Mulungu ndi kumvela cenjezo lake?

THAŴILANI KUMALO ACITETEZO

Kumbukilani kuti anthu a m’midzi ya ku Simeulue, anathaŵila ku mapili mwamsanga atangoona zizindikilo pa nyanja. Kucitapo kanthu kwao mwamsanga kunawapulumutsa. Kuti mupulumuke cisautso cimene cikubwela, mufunika kucitapo kanthu mwamsanga. Tingacite bwanji zimenezo? Mneneli Yesaya anauzilidwa kulemba za ciitano cosangalatsa cimene cikupelekedwa “m’masiku otsiliza” ano. Ciitano cimeneci cikuti: “Bwelani anthu inu. Tiyeni tipite kukakwela phili la Yehova . . . Iye akatiphunzitsa njila zake, ndipo ife tidzayenda m’njila zakezo.”—Yesaya 2:2, 3.

Kukwela pamwamba pa phili kudzakuthandizani kuti mukhale pamalo otetezeka. Mofananamo, kudziŵa Mulungu kupitila m’Baibulo, kwathandiza anthu mamiliyoni ambili padziko lonse kusintha umoyo wao. (2 Timoteyo 3:16, 17) Tsopano, io ‘akuyenda m’njila [za Mulungu]’ ndipo iye amawakonda ndi kuwateteza.

Kodi mudzavomela ciitano cimeneci ndi kulola Mulungu kukutetezani m’masiku ovuta ano? Tikupemphani kuti muŵelenge maumboni a m’Malemba amene ali pa bokosi oonetsa kuti tikukhala ‘m’masiku otsiliza.’ Mboni za Yehova za m’dela lanu n’zokonzeka kukuthandizani kumvetsetsa Baibulo, ndi mmene mungaseŵenzetsele mfundo zake. Mungapeze mayankho a mafunso anu pa webusaiti yathu ya www.pr418.com. Pitani polemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO.

^ par. 3 Tsunami ameneyu anacitika mu 2004 ndipo anapha anthu oposa 220,000. M’mbili yonse ya anthu, tsunami ameneyu ndi amene anapha anthu ambili.