Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mdyelekezi Ndani?

Kodi Mdyelekezi Ndani?

Kodi Mdyelekezi ndani?

KODI MUMAONA KUTI Mdyelekezi ndi . . .

  • Munthu wauzimu?

  • Maganizo oipa a munthu?

  • Cinthu congoyelekezela?

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

Mdyelekezi anakamba ndi Yesu, ndi ‘kumuyesa.’ (Mateyu 4:1-4) Conco, Mdyelekezi si cinthu congoyelekezela kapena maganizo oipa a munthu. Iye ndi munthu woipa wauzimu.

ZINA ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

  • Poyamba, Satana anali mngelo wabwino, koma iye “sanakhazikike m’coonadi.” (Yohane 8:44) Iye anakhala wabodza ndipo anapandukila Mulungu.

  • Angelo enanso anapanduka ndi kugwilizana ndi Satana. —Chivumbulutso 12:9.

  • Mdyelekezi amacititsa anthu kuganiza kuti iye kulibe.​—2 Akorinto 4:4.

Kodi Mdyelekezi angalamulile anthu?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI zoti Mdyelekezi amalamulila anthu ndi nthano cabe, koma ena amaopa kugwidwa ndi ziŵanda. Nanga inu muganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mdyelekezi akusonkhezela anthu ambili kucita zoipa, koma sakulamulila anthu onse.

ZINA ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

  • Mdyelekezi amagwilitsila nchito cinyengo kuti asokoneze anthu ambili.​—2 Akorinto 11:14.

  • Nthawi zina ziŵanda zimavutitsa anthu.​—Mateyu 12:22.

  • Mothandizidwa ndi Yehova, mungathe ‘kutsutsa Mdyelekezi.’​—Yakobo 4:7.