Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi anthu a Mulungu analowa liti mu ukapolo wa m’Babulo Wamkulu?

Ukapolo umenewu unayamba m’zaka za m’ma 100 C.E. ndipo unatha mu 1919. Koma kodi n’chifukwa chiyani tasintha zimene tinkakhulupirira poyamba?

Umboni ukusonyeza kuti ukapolo umenewu unatha mu 1919, pamene Akhristu odzozedwa anasonkhanitsidwa n’kupanganso mpingo wachikhristu. Ufumu wa Mulungu utangokhazikitsidwa mu 1914, * anthu a Mulungu anayesedwa komanso kuyeretsedwa. (Mal. 3:1-4) Kenako mu 1919, Yesu anaika “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azipereka “chakudya pa nthawi yoyenera” kwa anthu amene anali atangoyeretsedwawo. (Mat. 24:45-47) Chakachi ndi chimenenso anthu a Mulungu anamasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu. (Chiv. 18:4) Koma kodi ukapolowo unayamba liti?

Poyamba tinkafotokoza kuti anthu a Mulungu anakhala mu ukapolo wa Babulo Wamkulu kwa nthawi yochepa kuyambira mu 1918. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya March 15, 1992 inanena kuti: “Monga momwedi anthu akale a Mulungu analowera mu ukapolo ku Babulo kwakanthawi, choteronso atumiki a Yehova analowa mu ukapolo winawake kwa Babulo Wamkulu mu 1918.” Koma umboni ukusonyeza kuti anthu a Mulungu analowa mu ukapolowu kale kwambiri chaka cha 1918 chisanafike.

Mwachitsanzo, tiyeni tikambirane ulosi wina umene umanena za ukapolo wa anthu a Mulungu komanso kumasulidwa kwawo. Ulosiwu umapezeka pa Ezekieli 37:1-14. M’masomphenya, Ezekieli anaona chigwa chomwe munali mafupa ambiri. Yehova anauza Ezekieli kuti mafupawo ankaimira “nyumba yonse ya Isiraeli.” Koma kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosiwu kunali kokhudza “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16; Mac. 3:21) Ndiyeno Ezekieli anaona kuti mafupa aja ayamba kukhala amoyo ndipo kenako anakhala gulu lalikulu lankhondo. Izitu zikufotokoza bwino zimene zinachitika kuti anthu a Mulungu amasulidwe mu ukapolo wa Babulo Wamkulu mu 1919. Koma kodi masomphenyawa akutiuza chiyani za kutalika kwa nthawi imene anthuwa anakhala mu ukapolo?

Choyamba, mafupawo anali “ouma kwambiri.” (Ezek. 37:2, 11) Izi zikusonyeza kuti eniake a mafupawo anali oti anamwalira kalekale. Chachiwiri, Ezekieli anaona kuti akufawo sanauke kamodzin’kamodzi koma ankauka mwapang’onopang’ono. Poyamba panamveka phokoso la mafupa kuti gobedegobede ndipo ‘mafupawo anayamba kubwera pamodzi n’kumalumikizana.’ Ndiyeno ‘mitsempha ndi mnofu zinakuta mafupawo ndipo khungu linabwera pamwamba pake.’ Kenako ‘mpweya unalowa mwa anthuwo ndipo anakhala amoyo.’ Anthuwa atakhalanso ndi moyo Yehova anawabwezera kudziko lawo. Zonsezi zinatenga nthawi yaitali kuti zichitike.—Ezek. 37:7-10, 14.

Aisiraeli anakhala akapolo kwa nthawi yaitali. Ukapolo wawo unayamba mu 740 B.C.E. pamene mafuko 10, omwe ankapanga ufumu wakumpoto, anachotsedwa m’dziko lawo. Kenako mu 607 B.C.E. Yerusalemu anawonongedwa ndipo mafuko awiri, omwe ankapanga ufumu wakum’mwera wa Yuda, anatengedwa n’kupita ku ukapolo. Ukapolowu unatha mu 537 B.C.E. pamene Ayuda otsala anabwerera ku Yerusalemu kukamanganso kachisi n’kuyambiranso kulambira Yehova.

Tikaganizira mfundo za m’Malemba zimenezi, zikuonekeratu kuti anthu a Mulungu anakhala mu ukapolo wa Babulo Wamkulu kwa nthawi yaitali, osati kungoyambira mu 1918 kufika mu 1919. Nthawi ya ukapoloyi imafanananso ndi nthawi imene namsongole anakulira limodzi ndi tirigu yemwe akuimira “ana a ufumu.” (Mat. 13:36-43) Pa nthawiyi, Akhristu oona anali ochepa poyerekeza ndi ampatuko. Choncho tingati analowa mu ukapolo wa Babulo Wamkulu. Ukapolowu unayamba m’zaka za m’ma 100 C.E. ndipo unapitirira mpaka pamene kachisi wauzimu anayeretsedwa pa nthawi yamapeto.—Mac. 20:29, 30; 2 Ates. 2:3, 6; 1 Yoh. 2:18, 19.

Pa nthawi ya ukapoloyi, atsogoleri achipembedzo komanso andale ankalepheretsa anthu kudziwa Mawu a Mulungu. Iwo ankachita izi chifukwa chofuna kukhalabe pa maudindo awo. Moti nthawi ina kuwerenga Baibulo m’zilankhulo zina unali mlandu. Anthu ena amene anapezeka akuchita zimenezi ankawapachika pamtengo n’kuwawotcha. Komanso aliyense amene ankatsutsa zimene atsogoleri achipembedzowo ankaphunzitsa ankapatsidwa chilango chowawa. Choncho zinali zovuta kwambiri kuphunzira choonadi kapena kuphunzitsa ena.

Masomphenya a Ezekieli aja akusonyezanso kuti anthu a Mulungu anakhalanso ndi moyo ndipo pang’ono ndi pang’ono anamasulidwa ku ukapolo wachipembedzo chonyenga. Kodi izi zinayamba liti kuchitika ndipo zinachitika bwanji? Paja masomphenyawa ananena kuti panamveka ‘phokoso la mafupa.’ Izi zinayamba kunakwaniritsidwa kutatsala zaka mahandiredi angapo kuti nthawi yamapeto ifike. Pa zaka zimenezi panali anthu okhulupirika amene ankafuna kudziwa choonadi komanso kutumikira Mulungu ngakhale kuti kuchita izi kunali kovuta. Anthuwa anayamba kuphunzira Baibulo ndipo ankayesetsa kuuza ena zimene aphunzirazo. Ena analimba mtima n’kumasulira Baibulo m’zilankhulo zina.

Kenako chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800 Charles Taze Russell ndi anzake anayesetsa kuti choonadi cha m’Baibulo chidziwikenso. Izi zinali ngati minofu ndi khungu zayamba kukuta mafupa. Charles Russel ndi anzakewo anathandiza anthu kuti adziwe choonadi pogwiritsa ntchito magazini ya Zion’s Watch Tower komanso zinthu zina. Ndiyeno mu 1914, panatuluka “Sewero la Pakanema la Chilengedwe,” ndipo mu 1917 panatuluka buku lakuti, The Finished Mystery. Izi zinathandizanso kwambiri anthu a Mulungu. Pofika mu 1919 tingati anthu a Mulungu anakhalanso amoyo, anayamba kulankhula ndipo anabwezeretsedwa kudziko lawo. Anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo padzikoli anayamba kugwirizana ndi Akhristu odzozedwawa. Magulu awiri onsewa akulambira Yehova mogwirizana ndipo ali ngati “khamu lalikulu la gulu lankhondo.”—Ezek. 37:10; Zek. 8:20-23. *

Choncho n’zoonekeratu kuti anthu a Mulungu analowa mu ukapolo wa Babulo Wamkulu m’zaka za m’ma 100 C.E. pamene anthu ampatuko anachuluka kwambiri. Iyi inali nthawi yovuta ngati mmene zinalili pamene Aisiraeli anali ku ukapolo. Koma panopa uthenga wa m’Baibulo ukulalikidwa kwa anthu onse. Tikusangalala kwambiri kuti tikukhala m’nthawi imene ‘anthu ozindikira akuwala’ ndipo anthu ‘akudziyeretsa’ komanso ‘akuyengedwa.’—Dan. 12:3, 10.

Kodi Satana anapitadi ndi Yesu kukachisi kapena anangomuonetsa masomphenya?

Sitikudziwa ngati Yesu anaimadi pakachisi kapena ngati anangoona masomphenya. M’mabuku athu takhala tikufotokoza ziwiri zonsezi.

Mtumwi Mateyu analemba kuti: “Kenako Mdyerekezi anamutenga [Yesu] ndi kupita naye mumzinda woyera, ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi.” (Mat. 4:5) Pomwe Luka analemba kuti: “Kenako anamutengera ku Yerusalemu, ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi.”—Luka 4:9.

Poyamba mabuku athu ankanena kuti mwina Satana sanachite kupitadi ndi Yesu kukachisi. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya March 1, 1961 inayerekezera izi ndi zimene Satana anachita poonetsa Yesu maufumu onse a dziko lapansi atakwera pamwamba pa phiri. Inafotokoza kuti popeza palibe phiri limene munthu angaimepo n’kuona maufumu onse, ndiye kuti Satana sanapitedi ndi Yesu paphiri. Ndiyeno magaziniyi inanena kuti, ndiye kuti apanso Satana sanapitedi ndi Yesu kukachisi. Komabe nkhani zotsatira za m’magazini yomweyi zinafotokoza kuti zikanakhala kuti Yesu wadumphadi pamwamba pa kachisiyo, akanafa.

Anthu ena amati popeza Yesu sanali Mlevi, sakanaloledwa kuti akwere pamwamba pa kachisi. Choncho amati n’kutheka kuti Satana ‘anangotenga’ Yesu m’masomphenya n’kupita naye pamwamba pakachisipo. Amati nkhaniyi ikufanana ndi ya Ezekieli pamene nayenso anatengedwa m’masomphenya n’kupita kukachisi.—Ezek. 8:3, 7-10; 11:1, 24; 37:1, 2.

Koma ngati Yesu anangotengedwa m’masomphenya kupita pamwamba pa kachisi, tingafunse kuti:

  • Kodi mayeserowo analidi enieni kapena ongoyerekezera?

  • Ngati mayesero akuti Yesu asandutse miyala kukhala mikate komanso akuti achite zinazake zosonyeza kuti akulambira Satana anali enieni, kodi si ndiye kuti mayesero oti adumphe kuchokera pamwamba pa kachisi analinso enieni?

Komanso ngati Satana sanagwiritse ntchito masomphenya ndipo anatengadi Yesu n’kupita naye kukachisi, tingafunsenso kuti:

  • Kodi Yesu sanaswe lamulo poima pamwamba pa kachisiyo?

  • Kodi zinatheka bwanji kuti Yesu achoke kuchipululu n’kukapezeka kukachisi?

Tiyeni tikambirane mfundo zina zimene zingatithandize kuyankha mafunso awiri omalizawa.

Pulofesa wina dzina lake D. A. Carson ananena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kachisi” pamavesi awiri onse aja, amanena za “malo onse apakachisipo osati malo okha amene anthu omwe si alevi ankaletsedwa kufikako.” Ndipo kona ya kachisiyu yakum’mwera chakum’mawa inali ndi denga lafulati lomwe linali lalitali kwambiri. Choncho, mwina Yesu anaima padenga limenelo. Dengali linali lalitali mamita 137 kuchokera pansi pomwe panali chigwa cha Kidironi. Katswiri wina wolemba mbiri yakale dzina lake Josephus ananena kuti malowa anali aatali kwambiri moti munthu akayang’ana pansi “ankachita chizungulire.” Yesu sanali Mlevi koma akanatha kuima padengapo ndipo palibe akananena kuti waswa lamulo.

Koma kodi zinatheka bwanji kuti Yesu achoke kuchipululu n’kukapezeka kukachisi? Yankho ndi loti sitikudziwa. Baibulo limangofotokoza mwachidule za mayesero a Yesuwa. Silinena kuti panali mtunda wautali bwanji kukafika ku Yerusalemu komanso silinena kuti mayeserowo anatenga nthawi yaitali bwanji. Silifotokozanso ngati Yesu anakhalabe kuchipululuko pa nthawi yonse ya mayeserowo. Limangofotokoza kuti anatengedwa kupita ku Yerusalemu. Choncho, mwina Yesu anayenda kupita ku Yerusalemu ngakhale kuti zimenezi zinatenga nthawi yaitali.

Nanga bwanji zimene Baibulo limanena kuti Satana anaonetsa Yesu “maufumu onse a padziko”? N’zodziwikiratu kuti anamuonetsa m’masomphenya, chifukwa palibe phiri limene munthu angakwere n’kuona maufumu onse a padziko lapansi. Zimene Satana anachita ndi zofanana ndi kuonetsa munthu filimu yosonyeza zithunzi za maufumu a padziko lonse. Ngakhale zili chonchi, zoti Yesu ‘agwade n’kumuweramira’ zinali zenizeni osati zongoyerekezera. (Mat. 4:8, 9) Ndipo pamene Satana anatenga Yesu kupita naye kukachisi, ankafuna kuti Yesu adumphedi pakachisipo. Zikanakhala zongoyerekezera, ndiye kuti sakanakhala mayesero chifukwa Yesu sakanaika moyo wake pangozi.

Monga tanenera kale, sitikudziwa kuti zinatheka bwanji kuti Yesu achoke kuchipululu kupita ku Yerusalemu. Koma n’kutheka kuti iye anapitadi ku Yerusalemu n’kukaima pamwamba pakachisi. Chimene tikudziwa n’chakuti mayeserowa analidi enieni ndipo pamayesero onsewa Yesu anakana kuchita zofuna za Satana.

^ ndime 1 Lemba la Ezekieli 37:1-14 komanso la Chivumbulutso 11:7-12, limanena za kumasulidwa kwa anthu a Mulungu mu ukapolo komwe kunachitika mu 1919. Komabe ulosi wa pa Ezekieliwu ukunena za kumasulidwa kwa anthu onse a Mulungu amene anakhala mu ukapolo kwa nthawi yaitali. Pamene ulosi wa pa Chivumbulutso ukunena za kuyambiranso kwa kagulu ka abale odzozedwa komwe kanasankhidwa mu 1919 ndipo kakhala kakutsogolera anthu a Mulungu.