Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingathandize Bwanji Kulimbitsa Mgwirizano Wathu?

Kodi Tingathandize Bwanji Kulimbitsa Mgwirizano Wathu?

“Kuchokera kwa iye, thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwachikondi, pokhala lolumikizika bwino ndi logwirizana.”—AEF. 4:16.

NYIMBO: 53, 107

1. Perekani umboni wosonyeza kuti kugwirizana kunayamba kalekale.

YEHOVA ndi Yesu anayamba kugwirizana kalekale zinthu zina zonse zisanalengedwe. Yehova anayamba kulenga Yesu asanalenge chilichonse. Kenako Yesu anagwira ntchito ndi Mulungu ndipo anali “pambali pake monga mmisiri waluso.” (Miy. 8:30) Chifukwa chakuti Yehova ndi Yesu ankagwirizana kwambiri, anakwanitsa kulenga zamoyo zonse zomwe timaonazi. Nawonso atumiki a Yehova akale ankachita zinthu mogwirizana. Mwachitsanzo, Nowa ndi banja lake anamanga chingalawa. Patapita nthawi, Aisiraeli anagwira ntchito yomanga chihema. Akamasamuka, ankachiphwasula n’kukachimanga pamalo ena. Komanso Aisiraeli ankaimba nyimbo zotamanda Mulungu pakachisi. Anthu a Mulunguwa anatha kuchita zonsezi chifukwa chakuti anali ogwirizana.—Gen. 6:14-16, 22; Num. 4:4-32; 1 Mbiri 25:1-8.

2. (a) Kodi zinthu zinali bwanji mumpingo wa Akhristu oyambirira? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

2 Nawonso Akhristu oyambirira ankagwirizana. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti ngakhale kuti Akhristu odzozedwawa anali ndi luso komanso ntchito zosiyanasiyana, ankachita zinthu mogwirizana. Iwo ankatsatira Yesu Khristu, yemwe ndi Mtsogoleri wawo. Paulo anati Akhristuwa anali ngati thupi limene limakhala ndi ziwalo zosiyanasiyana koma zonse zimagwira ntchito limodzi. (Werengani 1 Akorinto 12:4-6, 12.) Nanga bwanji masiku ano? Kodi ifeyo tingatani kuti tizigwira ntchito yolalikira mogwirizana? Nanga tingatani kuti tizigwirizana mumpingo komanso m’banja?

TIZIGWIRA NTCHITO YOLALIKIRA MOGWIRIZANA

3. Kodi mtumwi Yohane anaona masomphenya otani?

3 Chakumapeto kwa nthawi ya atumwi, mtumwi Yohane anaona masomphenya a angelo 7 ndipo mngelo aliyense analiza lipenga. Pamene mngelo wa 5 analiza lipenga lake, Yohane anaona “nyenyezi” itagwa kuchokera kumwamba. Nyenyeziyo inali ndi kiyi ndipo inatsegula dzenje lolowera kuphompho. Ndiyeno utsi unatuluka kuchokera m’phomphomo ndipo mu utsiwo munatulukanso dzombe. Komabe dzombelo silinadye zomera koma linavulaza ‘anthu amene analibe chidindo cha Mulungu pamphumi pawo.’ (Chiv. 9:1-4) M’nthawi ya Mose, dzombe linawononga kwambiri zomera ku Iguputo. (Eks. 10:12-15) Choncho Yohane ayenera kuti ankadziwa kuti dzombe ndi loopsa. Dzombe limene Yohane anaona linkaimira Akhristu odzozedwa amene akhala akulalikira uthenga woti zipembedzo zonyenga zidzawonongedwa. Panopa pali Akhristu ambiri omwe adzakhale padziko lapansi amene akugwira ntchitoyi mogwirizana ndi odzozedwa. Uthenga womwe amalalikira wathandiza anthu ambiri kuti atuluke m’zipembedzo zonyenga komanso asiye kutsogoleredwa ndi Satana.

4. Kodi Akhristufe tili ndi ntchito iti, ndipo tingatani kuti tikwanitse kuigwira?

4 Akhristufe tili ndi ntchito yaikulu yolalikira “uthenga wabwino” padziko lonse mapeto asanafike. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Tiyenera kuitana anthu onse kuti adzamwe “madzi a moyo kwaulere.” (Chiv. 22:17) Koma kuti zimenezi zitheke, tiyenera kugwira ntchitoyi mogwirizana.—Aef. 4:16.

5, 6. Kodi ndi zinthu ziti zimene timachita zomwe zimathandiza kuti tizigwira ntchito yolalikira mogwirizana?

5 Kuti tithe kulalikira anthu ambiri, tiyenera kugwira ntchito yathuyi mwadongosolo. N’chifukwa chake gulu limatipatsa malangizo kudzera kumpingo. Malangizowa amathandiza kuti anthu a Mulungu padziko lonse azigwira ntchitoyi mogwirizana. Msonkhano wokonzekera utumiki ukatha, timapita kukalalikira uthenga wa Ufumu kwa anthu a mitundu yonse. Timathandiza anthu kuti amve uthengawu polankhula nawo komanso powapatsa mabuku athu. Kodi inuyo mumagwira nawo ntchito yapadera yoitanira anthu kumsonkhano, ku Chikumbutso kapena yowauza anthu uthenga winawake? Mukamachita zimenezi, mumakhala kuti mukugwirizana ndi abale ndi alongo padziko lonse pogwira ntchito yolalikira uthenga umenenso angelo amalengeza.—Chiv. 14:6.

6 Timasangalala kwambiri tikamawerenga Buku Lapachaka n’kuona lipoti lofotokoza mmene ntchito yathu ikuyendera padziko lonse. Komanso timagwira ntchito mogwirizana tikamaitanira anthu kumsonkhano. Pamisonkhanoyi timamvetsera nkhani zolimbikitsa za m’Baibulo komanso kuonera masewero ndi zitsanzo. Zonsezi zimatithandiza kuti tizitumikira Yehova ndi mtima wathu wonse. Timakhalanso ogwirizana ndi abale ndi alongo athu padziko lonse tikapezeka pa Chikumbutso. (1 Akor. 11:23-26) Timachita mwambowu pa Nisani 14, dzuwa litalowa. Tikamachita mwambowu timasonyeza kuti timayamikira zimene Yehova anatichitira komanso timamvera lamulo la Yesu. Anthu oyenera kupezeka pamwambowu si a Mboni okha. Choncho kutatsala milungu ingapo kuti Chikumbutso chichitike, timaitanira anthu kumwambo wofunikawu.

7. Kodi timakwanitsa kuchita chiyani tikamagwira limodzi ntchito yolalikira?

7 Dzombe limodzi palokha silingawononge kwambiri zomera. Ifenso patokha sitingathe kulalikira anthu onse. Koma tikamalalikira mogwirizana, timathandiza anthu mamiliyoni ambiri kuti ayambe kutumikira Yehova. Koma palinso zinthu zina zimene tingachite kuti tizigwirizana.

TIZIGWIRIZANA MUMPINGO

8, 9. (a) Kodi Paulo anafotokoza fanizo liti pophunzitsa za kufunika koti Akhristu azigwirizana? (b) Kodi tingatani kuti tizigwirizana mumpingo?

8 Mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Efeso zinthu zimene zimathandiza kuti mpingo uziyenda bwino. Anawauzanso kuti onse mumpingo ayenera ‘kukula m’zinthu zonse.’ (Werengani Aefeso 4:15, 16.) Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha thupi la munthu pofotokoza kuti Mkhristu aliyense angathandize kuti mpingo ukhale wogwirizana komanso kuti uzitsatira Yesu yemwe ndi Mutu wa mpingo. Mtumwiyu ananena kuti malo amene mafupa amalumikizana ndi amene amathandiza kuti thupi likhale logwirizana. Ndiye kodi tingatani kuti mpingo wathu uzigwirizana komanso uziyenda bwino?

9 Tiyenera kulemekeza akulu amene Yesu wawaika mumpingo komanso kutsatira malangizo awo. (Aheb. 13:7, 17) Nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Komabe tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake kuti uzitithandiza kumvera akulu ndi mtima wonse. Tizidziwa kuti tikamamvera modzichepetsa malangizo a akulu, zimathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana komanso kuti tizikondana kwambiri ndi Akhristu anzathu.

10. Kodi atumiki othandiza amathandiza bwanji kuti mpingo uzigwirizana? (Onani chithunzi patsamba 13.)

10 Atumiki othandiza nawonso amathandiza kwambiri kuti mpingo ukhale wogwirizana. Abalewa amagwira ntchito zofunika kwambiri mumpingo ndipo timawayamikira. Mwachitsanzo, amathandiza akulu poonetsetsa kuti pampingo pali mabuku okwanira ogwiritsa ntchito mu utumiki. Amathandizanso pa ntchito yoyeretsa ndi kukonza Nyumba ya Ufumu komanso amalandira anthu obwera kumisonkhano. Tikamatsatira malangizo a abalewa, zinthu zimayenda bwino pampingo.—Yerekezerani ndi Machitidwe 6:3-6.

11. Kodi achinyamata angathandize bwanji kuti mpingo ukhale wogwirizana?

11 Akulu ena akhala akugwira ntchito za mpingo mwakhama kwa zaka zambiri. Koma mwina chifukwa cha ukalamba, panopa sangathenso kuchita zinthu ngati kale. Choncho abale achinyamata angathandize kwambiri. Ngakhale kuti sakudziwa zambiri, ataphunzitsidwa bwino angathe kukhala ndi maudindo osiyanasiyana mumpingo. Choncho atumiki othandiza ayenera kuyesetsa kuti ayenerere kukhala akulu. (1 Tim. 3:1, 10) Akulu ena omwe ndi achinyamata ayesetsa mpaka kuyenerera kukhala oyang’anira madera n’kumatumikira abale ndi alongo m’mipingo. Timayamikira kwambiri tikaona achinyamata akudzipereka chonchi.—Werengani Salimo 110:3; Mlaliki 12:1.

TIZIGWIRIZANA M’BANJA

12, 13. Kodi mabanja angatani kuti azigwirizana kwambiri?

12 Nanga kodi tingatani kuti banja lathu likhale logwirizana? Ambiri amaona kuti kuchita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse kumawathandiza. Makolo ndi ana akamaphunzira limodzi za Yehova, amayamba kukondana kwambiri ndipo izi zimapangitsanso kuti azigwirizana. Pa nthawiyi, angakonzekere zoti akanene mu utumiki ndipo izi zingawathandize kuti azilalikira mogwira mtima. Aliyense akamafotokoza mfundo za m’Mawu a Mulungu n’kumasonyeza kuti amakonda Yehova ndipo akufuna kumutumikira, banja lonse limakhala logwirizana.

Kulambira kwa pabanja kumathandiza kuti makolo ndi ana azigwirizana (Onani ndime 12 ndi 15)

13 Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi wake azigwirizana kwambiri. Iwo akamakonda kwambiri Yehova n’kumamutumikira, amakhala osangalala komanso ogwirizana. Abulahamu ndi Sara, Isaki ndi Rabeka komanso Elikana ndi Hana ankakondana kwabasi. (Gen. 26:8; 1 Sam. 1:5, 8; 1 Pet. 3:5, 6) Inunso yesetsani kuti muzikondana kwambiri ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Mukamachita zimenezi, mumakhala ogwirizana komanso ubwenzi wanu ndi Yehova umalimba.—Werengani Mlaliki 4:12.

14. Ngati mwamuna kapena mkazi wanu satumikira Yehova, kodi mungatani kuti banja lanu likhalebe lolimba?

14 Baibulo limanena kuti sitiyenera kukwatirana ndi munthu amene satumikira Yehova. (2 Akor. 6:14) Komabe pali abale ndi alongo ena amene anakwatirana ndi munthu woti si Mboni. Palinso ena omwe anakhala a Mboni atakwatirana kale ndi munthu wosatumikira Yehova ndipo mnzawoyo sanakhalebe wa Mboni. Ndiye pali abale ndi alongo enanso amene anakwatirana ndi wa Mboni koma mnzawoyo anasiya kutumikira Yehova. Anthu onsewa ayenera kuyesetsa kuti banja lawo likhale lolimba. Kuti izi zitheke ayenera kutsatira mfundo za m’Baibulo nthawi zonse. Koma kuchita zimenezi sikophweka. Mwachitsanzo, poyamba a Mary ankatumikira Yehova limodzi ndi amuna awo a David. Koma kenako amuna awowo anasiya kusonkhana. A Mary ankapitabe kumisonkhano yampingo komanso ikuluikulu. Ankayesetsanso kutsatira mfundo za m’Baibulo ndipo ankaphunzitsa ana awo 6. Anawo atakula n’kuchoka pakhomo, a Mary anapitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika ngakhale kuti zinali zovuta kuchita zimenezi okha. Kenako a Mary ankasiya magazini penapake n’cholinga choti amuna awo aja aziwerenga ndipo ankawerengadi. Komanso mdzukulu wawo wazaka 6 akapita ku Nyumba ya Ufumu ankasungira malo a David ndipo akabwerera kunyumba ankawauza kuti: “Agogo, ndadandaula kuti simunapite kuholo lero. Ndinakusungirani malo.” Patatha zaka 25 a David anayambiranso kusonkhana. Panopa iwo ndi akazi awo akutumikira Yehova mogwirizana ndipo akazi awowa akusangalala kwambiri ndi zimenezi.

15. Kodi achikulire amene akhala m’banja zaka zambiri angathandize bwanji mabanja a achinyamata?

15 Masiku ano Satana akulimbana kwambiri ndi mabanja. Choncho atumiki a Mulungu ayenera kuyesetsa kuti akhale ndi banja logwirizana. Kaya mwakhala m’banja zaka zingati, muziganizira zimene mungachite kapena kulankhula kuti mulimbitse banja lanu. Komanso achikulire amene akhala m’banja zaka zambiri angathandize mabanja a achinyamata. Angathe kuwaitana kuti adzakhale nawo pa kulambira kwawo kwa pabanja. Ndiyeno iwo akaona mmene achikulirewo amachitira zinthu, angazindikire kuti kaya anthu akhala m’banja kwa zaka zambiri bwanji, ayenera kusonyezana chikondi komanso kuchita zinthu mogwirizana.—Tito 2:3-7.

“TIYENI TIPITE KUKAKWERA PHIRI LA YEHOVA”

16, 17. Kodi anthu a Mulungu akuyembekezera chiyani?

16 Aisiraeli akapita kuzikondwerero ku Yerusalemu, ankachita zinthu mogwirizana. Ankakonzekera zonse zofunika pa ulendowo, ankathandizana m’njira komanso akafika ku Yerusalemuko ankalambira Yehova mogwirizana. (Luka 2:41-44) Ifenso pamene tikuyembekezera kulowa m’dziko latsopano, tiziyesetsa kuchita zinthu mogwirizana. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

17 Anthu ambiri m’dzikoli sagwirizana ndipo amakangana pa zinthu zambiri. Koma timayamikira kwambiri kuti Yehova watiphunzitsa Mawu ake ndipo amatithandiza kuti tizikhala mwamtendere. Panopa tikuona kuti zimene mneneri Yesaya ndi Mika analemba zikukwaniritsidwa. Iwo analemba kuti anthu a Mulungu adzapita kukakwera “phiri la Yehova” mogwirizana. (Yes. 2:2-4; werengani Mika 4:2-4.) “M’masiku otsiriza” ano, tikuonadi kuti anthu a Mulungu padziko lonse akumulambira m’njira imene iye amafuna. Koma tidzasangalala kwambiri m’tsogolo pamene anthu onse padziko lapansi azidzalambira Mulungu mogwirizana.