Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

BAIBULO IMASINTHA ANTHU

Zinanitengela Nthawi Yaitali Kuti Nisinthe

Zinanitengela Nthawi Yaitali Kuti Nisinthe
  • CAKA COBADWA: 1953

  • DZIKO: AUSTRALIA

  • MBILI YANGA: N’NALI N’CIZOLOŴEZI COTAMBA ZAMALISECE

KUKULA KWANGA:

Atate anasamukila ku Australia kucoka ku Germany mu 1949. Iwo anapita kukafuna nchito ku makampani okonza za magetsi ndi a migodi ndipo anakhala ku midzi ya ku Victoria. Ali kumeneko, anakwatila amayi, ndiyeno mu 1953 ine n’nabadwa.

Patangopita zaka zocepa, amayi anayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova. Nikaganizila zakale, nimakumbukila zimene n’nali kuphunzila m’Baibulo. Koma atate anali kudana ndi cipembedzo ciliconse. Iwo anayamba kucita nkhanza, ndipo amayi anali kuwaopa kwambili. Amayi anapitiliza kuphunzila Baibulo mwakabisila, ndipo anayamba kukonda zimene anali kuphunzila. Atate akacokapo, amayi anali kuuza ine ndi mlongosi wanga zimene aphunzila. Iwo anali kutiuza za ciyembekezo codzakhala ndi moyo m’paradaiso pa dziko lapansi. Anali kutiuzanso kuti tingakhale osangalala ngati titsatila mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo.—Salimo 37:10, 29; Yesaya 48:17.

N’takwanitsa zaka 18, n’naganiza zocoka panyumba cifukwa ca nkhanza ya Atate. Ngakhale n’nali kukhulupilila zimene Amayi anali kutiphunzitsa, sin’nali kuziona kuti n’zofunika. Conco, n’naleka kuzitsatila. N’nayamba kugwila nchito ya zamagetsi m’migodi. N’tafika zaka 20, n’nakwatila. Mwana wathu woyamba anabadwa patapita zaka zitatu. Ndiyeno n’nayambanso kuganizila cinthu cofunika kwambili paumoyo wanga. N’naona kuti Baibulo ingathandize banja lathu, conco n’nayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova. Koma mkazi wanga sanali kufuna Mboni za Yehova. N’tapezeka pa msonkhano wa Mboni za Yehova, mkazi wanga ananiuza kuti nisankhepo pali kuleka kuphunzila Baibulo kapena kuthetsa cikwati. N’tasoŵa cocita, n’namvela zimene iye ananiuza ndipo n’naleka kuphunzila na Mboni. Patapita nthawi, n’nayamba kudziimba mlandu cifukwa colephela kucita zimene n’naona kuti n’zoyenela.

Tsiku lina, anzanga a ku nchito anayamba kunionetsa zamalisece. Zinali zokopa koma zinali zoipa, ndipo zinanicititsa kuti nizidziimba mlandu. N’takumbukila zimene n’naphunzila m’Baibulo, n’nayamba kuona kuti Mulungu adzanilanga. Popeza n’nali kuona zithunzi zambili zamalisece, n’nayamba kuzikonda. M’kupita kwa nthawi, n’nazoloŵela kutamba zamalisece.

Patapita zaka zoposa 20, n’nalekelatu kutsatila mfundo zimene amayi ananiphunzitsa. Khalidwe langa linaonetselatu zimene zinali m’maganizo mwanga. Kakambidwe kanga sikanali kabwino, ndipo n’nali kukonda nthabwala zotukwana. N’nayamba kuiona molakwika nkhani ya kugonana. Ngakhale kuti n’nali na mkazi, n’nalinso na akazi ena akumbali. N’nayamba kudziona kuti ndine wacabecabe ndiponso wonyansa.

Cikwati cinatha ndi mkazi wanga ndipo n’nayamba kukumana ndi mavuto ambili. Ndiyeno, n’napemphela kwa Yehova ndi mtima wanga wonse. N’nayambanso kuphunzila Baibulo ngakhale kuti panali patapita zaka 20. Pamene izi zinali kucitika, atate anali atamwalila kale, ndipo amayi anali atabatizika n’kukhala Mboni ya Yehova.

MMENE BAIBULO INASINTHILA UMOYO WANGA:

Zimene n’nali kucita pa umoyo wanga zinali zosiyana kwambili ndi mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo. Koma panthawiyi, n’nali kufunitsitsa kukhala ndi mtendele wa m’maganizo umene Baibulo imakamba. Conco, n’naleka kukamba mau onyoza ndipo n’nayamba kulamulila mkwiyo wanga. N’nalekanso khalidwe laciwelewele, kuchova njuga, kumwa moŵa mwaucidakwa, ndi kubela abwana anga.

Koma anzanga a ku nchito sanamvetsetse cifukwa cake n’naleka zinthu zimenezi. Kwa zaka zitatu, iwo anali kunisonkhezela kuti niyambenso makhalidwe akale. Ndipo ngati nacita zinthu molakwitsako pang’ono, mwina nakwiya, kapena kukamba mau oipa, anali kufuula kuti: “Ahaa! Uyu ndiye Joe amene tidziŵa.” Kukamba zoona, mau amenewa anali kunikhumudwitsa kwambili. Ndipo n’nali kudzimva ngati wolephela.

Malo amene n’nali kugwilila nchito, anali odzaza ndi mapikica a zamalisece, kuphatikizapo a pa kompyuta. Monga mmene n’nali kucitila kale, anzanga ku nchito anali kutumizilana zithunzi-thunzi zimenezi. N’nali kuyesetsa kuti nisayambenso zizoloŵezi zanga, koma nthawi ndi nthawi anzanga amenewa anali kunisonkhezela kuti niyambenso. Koma zimenezi zikacitika, n’nali kupita kwa amene anali kuniphunzitsa Baibulo kuti anilimbikitse ndi kunithandiza. Iye anali kunimvetsela moleza mtima nikamamuuza mavuto anga. Mwa kuseŵezetsa mavesi a m’Baibulo, ananithandiza kudziŵa mmene ningathetsele zizoloŵezi zanga. Iye ananilimbikitsanso kuti nizipempha thandizo kwa Yehova nthawi zonse.—Salimo 119:37.

Tsiku lina n’naitana anzanga onse amene n’nali kugwila nawo nchito. Atabwela n’naŵauza kuti apatse moŵa anzanga ena aŵili amene anakamba kuti analeka kumwa mwaucidakwa. Koma anzangawo anafuula kuti “Iyai kucita zimenezo n’kulakwa! Anzathuwa akali kulimbana na cizolowezi cawo ca kumwa moŵa mwaucidakwa!” Ndiyeno n’nawauza kuti, “Mwakamba zoona. Inenso nikali kulimbana na cizolowezi cotamba zamalisece.” Kucokela pamenepo, anzangawo anazindikila kuti inenso nikali kulimbana na cizolowezi cimeneci ndipo analeka kunivutitsa.

Mwathandizo la Yehova, n’naleka kutamba za malisece m’kupita kwa nthawi. Mu 1999, n’nabatizika n’kukhala wa Mboni za Yehova. Ndine woyamikila kwambili kuti nilinso na mwayi wokhala ndi umoyo wabwino ndi wacimwemwe.

Tsopano nazindikila cifukwa cake Yehova amadana ndi zinthu zimene n’nali kukonda kwa nthawi yaitali. Monga Tate wacikondi, anali kufuna kuniteteza ku ngozi imene imabwela cifukwa cotamba zamalisece. Mau a pa Miyambo 3:5, 6, ni oona amene amati: “Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukila m’njila zako zonse, ndipo iye adzawongola njila zako.” Mfundo za m’Baibulo zaniteteza komanso zanicititsa kukhala na umoyo wabwino kwambili.—Salimo 1:1-3

MAPINDU AMENE NAPEZA:

Kale, n’nali kudziona ngati munthu wopanda pake, koma tsopano nimadzilemekeza ndipo nili na mtendele wa m’maganizo. Nili na umoyo wabwino ndipo nimadziŵa kuti Yehova ananikhululukila ndipo akunicilikiza. M’caka ca 2000, n’nakwatila Karolin, mlongo wokongola amene amakonda Yehova mmene ine nimam’kondela. Pa nyumba pathu pali mtendele. Timaona kuti ndi mwayi kukhala m’banja lacikhiristu la pa dziko lonse, limene muli anthu acikondi ndi amakhalidwe abwino.