Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI NDI NDANI ANGATITHANDIZE TIKAKHALA PA MAVUTO?

Tonse Timafunika Kulimbikitsidwa

Tonse Timafunika Kulimbikitsidwa

Kodi munayamba mwagwapo nthawi inayake muli mwana? N’kutheka kuti munavulala dzanja kapena bondo. Kodi mukukumbukira zimene mayi anu anachita pokuthandizani? Mwina anatsuka balalo n’kulimanga ndi kansalu. N’zosakayikitsa kuti munalira koma pasanapite nthawi munatonthola chifukwa mwina mayi anu anakukumbatirani ndiponso kukuuzani mawu olimbikitsa. N’zosachita kufunsa kuti pamene munali mwana simunkasowa anthu okulimbikitsani.

Koma munthu akakula mavuto ake amakhalanso aakulu ndipo zimavuta kuti apeze munthu amene angamulimbikitse. Mavuto amene akuluakulu amakumana nawo sangathetsedwe msanga ngati mmene zimakhalira ndi mavuto a ana. Tiyeni tione zitsanzo za mavuto ena amene timakumana nawo.

  • Kodi nthawi ina munachotsedwapo ntchito? Bambo wina dzina lake Julian ananena kuti atachotsedwa ntchito anasokonezeka maganizo kwambiri. Ankadzifunsa kuti, ‘Kodi ndikwanitsa bwanji kumasamalira banja langa? Ndakhala ndikugwira ntchito mwakhama kwa zaka zambiri pakampaniyi, ndiye n’chifukwa chiyani andichotsa ntchito ngati ndine wachabechabe?’

  • Mwinanso mukusowa mtengo wogwira chifukwa chakuti banja lanu linatha. Mayi wina dzina lake Raquel ananena kuti: “Mwamuna wanga anandithawa mwadzidzidzi ndipo panopa padutsa chaka ndi miyezi 6. Zinandipweteka kwambiri moti ngakhale m’thupi sindinkamva bwino. Ndinkachita mantha kuti zindiyambitsira mavuto ena.”

  • N’kutheka kuti mukudwala matenda enaake ndipo zikuoneka kuti simudzachira. Nthawi zina mungamve ngati mmene Yobu ankamvera. Iye anati: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Yobu 7:16) Mwinanso mumamva ngati mmene bambo wina wazaka za m’ma 80 dzina lake Luis amamvera. Iye anati: “Nthawi zina ndimaona ngati ndikungodikira imfa.”

  • Kapena mukhoza kumafuna kulimbikitsidwa chifukwa wachibale kapena mnzanu anamwalira. Bambo wina dzina lake Robert ananena kuti: “Mwana wanga atamwalira pa ngozi yandege sindinakhulupirire. Kenako ndinayamba kumva ululu waukulu kwambiri wofanana ndi ululu umene Baibulo limauyerekezera ndi umene munthu angamve atalasidwa ndi lupanga lalitali.”—Luka 2:35.

Robert, Luis, Raquel ndi Julian atakumana ndi mavutowa analimbikitsidwa ndi Mulungu wamphamvuyonse, ndipo palibe wina amene akanawalimbikitsa bwino kuposa iyeyo. Kodi Mulunguyo amalimbikitsa bwanji anthu? Nanga kodi inuyo angakulimbikitseni?