Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI NDI NDANI ANGATITHANDIZE TIKAKHALA PA MAVUTO?

Zimene Zingakuthandizeni Mukamakumana ndi Mavuto

Zimene Zingakuthandizeni Mukamakumana ndi Mavuto

Mavuto amakhala osiyanasiyana ndipo n’zosatheka kufotokoza mavuto onse m’nkhaniyi. Koma tiyeni tikambirane mavuto 4 amene tatchula kale aja ndiponso mmene anthu omwe ankakumana ndi mavutowo analimbikitsidwira ndi Mulungu.

NTCHITO IKATHA

“Ndinayamba kugwira ntchito iliyonse yomwe inkapezeka komanso tinasiya kumangogula zinthu zosafunika kwenikweni.”​—Jonathan

Mwamuna wina dzina lake Seth * ananena kuti: “Ine ndi mkazi wanga tinachotsedwa ntchito nthawi yofanana. Kwa zaka ziwiri, tinkangodalira zimene achibale ankatipatsa komanso timaganyu tina ndi tina timene tinkapeza. Chifukwa cha zimenezi mkazi wanga Priscilla anayamba kudwala matenda ankhawa, pamene ine ndinkangodziona ngati wachabechabe.

“Pali zinthu zingapo zimene zinkatithandiza kupirira mavutowa. Mwachitsanzo, Priscilla ankakonda kuganizira mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 6:34. Palembali Yesu ananena kuti tisamade nkhawa ndi zamawa chifukwa tsiku lililonse limakhala ndi zodetsa nkhawa zake. Mkazi wanga ankapempheranso mochokera pansi pa mtima ndipo zinkamuthandiza kuti asamangokhalira kudandaula. Ineyo ndinkalimbikitsidwa kwambiri ndi lemba la Salimo 55:22. Mofanana ndi wolemba salimoli, ndinkatulira Yehova nkhawa zanga ndipo iye ankandichirikiza. Panopa ndinapeza ntchito ina komabe timayesetsa kukhala ndi moyo wosalira zambiri mogwirizana ndi malangizo a Yesu a pa Mateyu 6:20-22. Koma chofunika kwambiri n’chakuti zimene tinkachita pa nthawiyi zinathandiza kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Mulungu komanso kuti ine ndi mkazi wanga tizigwirizana kwambiri.”

Mwamuna winanso dzina lake Jonathan ananena kuti: “Bizinezi yathu itatha ndinkada nkhawa kuti zitithera bwanji. Tinali titagwira ntchito mwakhama mu bizineziyi kwa zaka 20, koma inangotha mwadzidzidzi chifukwa cha mavuto azachuma omwe anali m’dziko lathu. Izi zinachititsa kuti ine ndi mkazi wanga tiyambe kumakangana pa nkhani ya ndalama. Tinkaopanso kugula zinthu ndi khadi lathu logulira zinthu pa ngongole poganiza kuti kampani imene inatipatsa khadilo siingalole.

“Komabe Mawu a Mulungu komanso mzimu wake zinatithandiza kuti tizisankha zinthu mwanzeru. Ndinayamba kugwira ntchito iliyonse yomwe inkapezeka komanso tinasiya kumangogula zinthu zosafunika kwenikweni. Popeza ndife a Mboni za Yehova, tinkathandizidwanso ndi a Mboni anzathu. Ankatilimbikitsa komanso kutipatsa zinthu pamene tavutika kwambiri.”

BANJA LIKATHA

Raquel amene tamutchula kale uja ananena kuti: “Mwamuna wanga atandithawa, zinandipweteka kwambiri komanso zinandikwiyitsa. Koma ndinkadalira Mulungu ndipo iye ankandilimbikitsa. Ndinkapemphera kwa iye tsiku ndi tsiku ndipo ankandithandiza kuti ndikhale ndi mtendere wamumtima. Zinali ngati wachiritsa mtima wanga.

“Baibulo linkandithandizanso kuti ndisamakwiye kapena kusunga chakukhosi. Ndinkayesetsa kutsatira mawu a mtumwi Paulo a pa Aroma 12:21 akuti: ‘Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.’

“Pali nthawi imene tiyenera kungovomereza kuti zachitika basi. . . . Panopa ndimaganizira zinthu zimene zingandithandize kukhala wosangalala m’malo momangoganizira za mavuto anga.”​—Raquel

“Mnzanga wina wanzeru anandithandiza kuzindikira kuti ndiyenera kusiya kumangoganizira zimene zandichitikira. Anandisonyeza lemba la Mlaliki 3:6, n’kundiuza kuti pali nthawi imene tiyenera kungovomereza kuti zachitika basi. Malangizowa anali ovuta kutsatira koma anandithandiza kwambiri. Panopa ndimaganizira zinthu zimene zingandithandize kukhala wosangalala m’malo momangoganizira za mavuto anga.”

Mayi wina dzina lake Elizabeth ananena kuti: “Banja likatha umafunika kuti ena azikulimbikitsa. Ineyo ndinali ndi mnzanga wina yemwe ankandithandiza tsiku ndi tsiku. Ankalira nane limodzi, kundilimbikitsa komanso kundithandiza kuti ndizidzimva kuti ndine wofunika. Sindimakayikira kuti Yehova anamugwiritsa ntchito kuti achiritse mabala amene ndinali nawo mumtima.”

PAMENE MUKUDWALA KAPENA MWAKALAMBA

“Ndikapemphera ndimamva kuti mzimu [wa Mulungu] ukundithandiza.”​—Luis

Luis yemwe tamutchula m’nkhani yoyambirira uja ali ndi vuto la mtima ndipo kwa maulendo awiri anatsala pang’ono kufa. Panopa amafunika kugwiritsa ntchito makina othandiza kupuma kwa maola 16, tsiku lililonse. Iye anati: “Ndimapemphera kwa Yehova nthawi zonse. Ndikapemphera ndimamva kuti mzimu wake ukundithandiza. Kupemphera kumandithandiza kuti ndipirire chifukwa ndimakhulupirira kuti Mulungu amandikonda ndipo andithandiza.”

Mayi wina wazaka za m’ma 80 dzina lake Petra ananena kuti: “Ndimafuna kuchita zinthu zambiri koma sindingakwanitse. Ndimadandaula ndikamaona kuti mphamvu zanga zikutha. Panopa ndimakhala wofooka ndipo ndimayenera kumwa mankhwala ambiri. Nthawi zambiri ndimaganizira zimene Yesu anachita popempha Atate wake kuti ngati n’zotheka asalole kuti akumane ndi vuto linalake. Yehova anapatsa Yesu mphamvu ndipo ndi zimenenso amandichitira ineyo. Ndimapemphera tsiku lililonse ndipo zimenezi zimandithandiza chifukwa ndikalankhula ndi Mulungu ndimamva bwino mumtima.”​—Mateyu 26:39.

Julian yemwe tamutchula kale uja wakhala akudwala matenda ofooketsa ziwalo kwa zaka pafupifupi 30. Iye anati: “Kale ndinali munthu wamphamvu zake ndiponso wolemekezeka koma panopa ndimayenda pa njinga ya anthu olumala. Komabe ndimaona kuti moyo wanga ndi wofunika chifukwa ndimadzipereka pothandiza anthu ena. Kuthandiza ena kungakuthandizeni kuti musamangoganizira za mavuto anu. Komanso Yehova amakwaniritsa lonjezo lake lakuti adzatipatsa mphamvu pa nthawi ya mavuto. Mofanana ndi mtumwi Paulo, inenso ndinganene kuti: ‘Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.’”​—Afilipi 4:13.

PAMENE WACHIBALE KAPENA MNZANU WAMWALIRA

Munthu wina dzina lake Antonio ananena kuti: “Bambo anga atamwalira pa ngozi yapamsewu, poyamba sindinakhulupirire chifukwa iwo ankangodziyendera mumsewu ndipo sanalakwitse chilichonse. Koma palibe chimene ndikanachita. Asanamwalire anakhala masiku 5 ali chikomokere. Sindinkalira ndikakhala ndi mayi anga, koma ndikakhala ndekha ndinkalira kwambiri. Ndinkangokhalira kudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani zimenezi zatichitikira?’

“Pa nthawi yovutayi, ndinkapempha Yehova kuti andithandize kuti ndisamadandaule kwambiri komanso kuti andipatse mtendere wamumtima. Izi zinandithandiza kuti mtima ukhale m’malo. Ndinakumbukira zimene Baibulo limanena zoti ‘zinthu zosayembekezereka’ zikhoza kugwera munthu aliyense. Popeza Mulungu sanganame, sindikukayikira kuti ndidzaonananso ndi bambo anga akadzaukitsidwa.”​—Mlaliki 9:11; Yohane 11:25; Tito 1:2.

‘Panopa timakumbukirabe zinthu zosangalatsa zimene tinkachitira limodzi ndi mwana wathu.’​—Robert

Nayenso Robert amene tamutchula m’nkhani yoyamba uja amaona kuti pemphero ndi lothandiza. Iye ananena kuti: “Ine ndi mkazi wanga tinakhala ndi mtendere wamumtima womwe umatchulidwa pa Afilipi 4:6, 7. Tinapeza mtenderewu chifukwa chopemphera kwa Yehova. Mtendere umenewu unkatithandiza kuti tizilankhula ndi atolankhani za chikhulupiriro chathu chakuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa. Panopa timakumbukirabe zinthu zosangalatsa zimene tinkachitira limodzi ndi mwanayo ndipo timayesetsa kuganizira kwambiri zinthuzo.

“A Mboni anzathu atatiuza kuti anationa pa TV tikufotokoza modekha zimene timakhulupirira, tinawauza kuti tinakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa anthu ambiri ankatipempherera. Ndimakhulupirira kuti Yehova ankatithandiza pogwiritsa ntchito mawu olimbikitsa omwe Akhristu anzathuwo ankatiuza.”

Monga mmene taonera m’zitsanzozi, Mulungu amatha kulimbikitsa anthu akakumana ndi vuto lililonse. Nanga kodi inuyo angakulimbikitseninso? Kaya mukukumana ndi mavuto otani, dziwani kuti Mulungu akhoza kukulimbikitsani. * Choncho mungachite bwino kupempha Yehova kuti akuthandizeni. Paja iye ndi Mulungu amene “amatitonthoza m’njira iliyonse.”​—2 Akorinto 1:3.

^ ndime 5 Mayina ena asinthidwa m’nkhaniyi.

^ ndime 23 Ngati mukufuna kuti mukhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu kuti azikulimbikitsani, lankhulani ndi a Mboni za Yehova am’dera lanu kapena lembani kalata yopita ku ofesi yawo yam’dziko lanu.