Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti Ufumuwu umangoimira zimene zimachitika munthu akalola kuti Mulungu azilamulira mumtima mwake, pomwe ena amaganiza kuti ukuimira zimene anthu adzachite pokhazikitsa mtendere komanso mgwirizano padzikoli. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. . . . Udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo [a anthu].” (Danieli 2:44) Choncho Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Ufumu wa Mulungu umalamulira kuchokera kumwamba.—Mateyu 10:7; Luka 10:9.

  • Mulungu amagwiritsa ntchito Ufumu umenewu pokwaniritsa chifuniro chake chokhudza kumwamba ndi padziko lapansi.—Mateyu 6:10.

Kodi Ufumu wa Mulungu udzabwera liti?

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Palibe akudziwa

  • Posachedwapa

  • Sudzabwera

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Uthenga wabwino ukadzalalikidwa mokwanira padziko lonse, Ufumuwu udzabwera kuti udzachotse zinthu zonse zoipa padzikoli.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Padzikoli palibe amene akudziwa nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzabwere.—Mateyu 24:36.

  • Maulosi a m’Baibulo amasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kubwera.—Mateyu 24:3, 7, 12.

 

Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.pr418.com/ny