Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse”

“Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse”

“Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza . . .  ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”—MAT. 28:19, 20.

NYIMBO: 141, 97

1, 2. Malinga ndi zimene Yesu ananena palemba la Mateyu 24:14, kodi tingafunse mafunso ati?

NGAKHALE kuti anthu ena amatsutsa uthenga wathu, ambiri amavomereza kuti a Mboni za Yehova amadziwika ndi ntchito yolalikira. Mwina mwakumanapo ndi anthu ena amene amati ngakhale kuti sagwirizana ndi uthenga womwe timalalikira, amaona kuti timachita bwino kulalikira. Yesu ananeneratu kuti uthenga wabwino wa Ufumu uyenera kulalikidwa padziko lonse. (Mat. 24:14) Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti ntchito yolalikira imene timagwira ikukwaniritsa ulosi wa Yesu? Kodi tikamanena kuti ifeyo ndi amene tikugwira ntchito imeneyi tikudzitamandira?

2 Anthu a zipembedzo zambiri amati amalalikira Uthenga wabwino. Koma nthawi zambiri amangolalikira m’tchalitchi, pawailesi, pa TV, pa Intaneti kapenanso kwa munthu mmodzi. Ena amati amalalikira pothandiza ovutika, pomanga zipatala kapena masukulu. Koma kodi izi n’zimene Yesu ankatanthauza pamene anati otsatira ake azilalikira?

3. Malinga ndi lemba la Mateyu 28:19, 20, kodi otsatira a Yesu ayenera kuchita zinthu 4 ziti?

3 Kodi otsatira a Yesu ankayenera kungokhala n’kumadikira kuti anthu abwere kwa iwo? Ayi. Ataukitsidwa anauza ophunzira ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza . . .  ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.” (Mat. 28:19, 20) Choncho ophunzira a Yesu ayenera kuchita zinthu 4. Ayenera kupita kwa anthu, kuwaphunzitsa, kuwathandiza kuti akhale ophunzira a Yesu komanso kuwabatiza. Katswiri wina wa Baibulo anafotokoza tanthauzo la mawu a Yesu akuti “pitani.” Anati Yesu ankatanthauza kuti: “Mkhristu aliyense akulamulidwa kuti ‘apite’ kukalalikira kulikonse, kaya awoloka msewu kapena nyanja.”—Mat. 10:7; Luka 10:3.

4. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani ponena kuti ophunzira ake akhale “asodzi a anthu”?

4 Kodi Yesu ankatanthauza kuti munthu aliyense azingolalikira payekha, kapena ankafuna kuti otsatira ake azilalikira monga gulu? Zikuoneka kuti ankafuna azilalikira monga gulu chifukwa munthu mmodzi sangalalikire kwa “anthu a mitundu yonse.” Umboni wa zimenezi ndi woti iye anauza ophunzira ake kuti akhale “asodzi a anthu.” (Werengani Mateyu 4:18-22.) Apa Yesu sankanena mmene msodzi mmodzi amaphera nsomba pogwiritsa ntchito nyambo ndi mbedza. Koma ankanena za kupha nsomba pogwiritsa ntchito khoka. Pamafunika asodzi ambiri kuti athandizane kukoka khokalo.—Luka 5:1-11.

5. Kodi ndi mafunso 4 ati amene tiyenera kudziwa mayankho ake, ndipo n’chifukwa chiyani?

5 Mayankho a mafunso 4 otsatirawa angatithandize kudziwa amene akulalikira uthenga wabwino masiku ano pokwaniritsa ulosi wa Yesu.

  • Kodi ndi uthenga uti umene tiyenera kulalikira?

  • Tikamalalikira, kodi cholinga chathu chiyenera kukhala chotani?

  • Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito njira ziti polalikira?

  • Kodi tiyenera kulalikira kuti, ndipo tiyenera kulalikira mpaka liti?

Mayankho a mafunsowa atithandizanso kuti tipitirize kulalikira komanso kuti tizigwira ntchitoyi mokhulupirika.—1 Tim. 4:16.

KODI UTHENGA WAKE UYENERA KUKHALA WOTANI?

6. N’chiyani chikutsimikizira kuti a Mboni za Yehova amalalikira uthenga woyenera?

6 Werengani Luka 4:43. Yesu ankalalikira “uthenga wabwino wa Ufumu” ndipo amafuna kuti otsatira ake azichitanso chimodzimodzi. Ndiyeno kodi ndi gulu liti limene likulalikira uthengawu kwa “anthu a mitundu yonse”? Ndi a Mboni za Yehova okha basi. Ngakhale anthu amene amatitsutsa amadziwa zimenezi. Chitsanzo ndi zimene wansembe wina yemwe wakhala akuchita umishonale m’mayiko ambiri anauza m’bale wina. Iye anati ankafunsa a Mboni za Yehova m’dziko lililonse limene anapita kuti amuuze uthenga umene amalalikira. Wansembeyo anati: “Onse ndi opusa chifukwa ankandiyankha mofanana kuti: ‘Timalalikira uthenga wabwino wa Ufumu.’” Komatu zimenezi sizikusonyeza kuti a Mboni ndi opusa. Zikungosonyeza kuti amalankhula mogwirizana. (1 Akor. 1:10) Mpake kuti magazini yathu ya Nsanja ya Olonda imalengezanso Ufumu wa Yehova womwewu. Magaziniyi ikupezeka m’zilankhulo 254 ndipo magazini 59 miliyoni amasindikizidwa mwezi uliwonse. Palibenso magazini ena amene amasindikizidwa ochuluka chonchi.

7. Tikudziwa bwanji kuti atsogoleri a matchalitchi salalikira uthenga woyenera?

7 Atsogoleri a matchalitchi salalikira za Ufumu wa Mulungu. Akati anene za Ufumuwo, ambiri amangoti umakhala mumtima mwa Mkhristu aliyense. (Luka 17:21) Iwo sathandiza anthu kuzindikira kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba ndipo Mfumu yake ndi Yesu Khristu. Sanenanso zoti Ufumuwo ndi umene udzathetse mavuto ndi zoipa zonse padzikoli. (Chiv. 19:11-21) M’malomwake amalimbikitsa anthu kukumbukira Yesu pa Khirisimasi ndi pa Isitala. Sadziwa ngakhale pang’ono zimene Yesu adzachite akamadzalamulira padzikoli. Popeza sadziwa uthenga woyenera kulalikira, mpake kuti sadziwanso cholinga cholalikirira uthengawo.

KODI CHOLINGA CHATHU POLALIKIRA CHIYENERA KUKHALA CHOTANI?

8. Kodi anthu ena amalalikira ndi cholinga cholakwika chiti?

8 Kodi cholinga polalikira chiyenera kukhala chotani? Sichiyenera kukhala chongofuna kupeza ndalama komanso kumanga nyumba zogometsa. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mat. 10:8) Choncho sitiyenera kuchita malonda ndi Mawu a Mulungu. (2 Akor. 2:17) Anthu amene amalalikira uthenga wabwino sayenera kugwira ntchitoyi n’cholinga chofuna kupeza phindu linalake. (Werengani Machitidwe 20:33-35.) Ngakhale kuti pali malangizo omveka bwino pa nkhani yolalikira, matchalitchi ambiri amalalikira n’cholinga choti apeze ndalama zolipirira abusa awo komanso anthu ena ogwira ntchito. Ndipotu atsogoleri ambiri achipembedzo ndi olemera kwambiri kuposa Akhristu awo.—Chiv. 17:4, 5.

9. Kodi a Mboni za Yehova amasonyeza bwanji kuti salalikira n’cholinga chofuna kupeza ndalama?

9 Koma kodi a Mboni za Yehova amatolera zopereka pa Nyumba ya Ufumu kapena pamisonkhano ikuluikulu? Ayi, ndalama zoyendetsera ntchito yawo ndi zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo. (2 Akor. 9:7) Chaka chatha chokha, a Mboni za Yehova anathera maola pafupifupi 2 biliyoni akulalikira uthenga wabwino. Ankachititsanso kwaulere maphunziro a Baibulo oposa 9 miliyoni mwezi uliwonse. Chochititsa chidwi n’choti iwo salipidwa komanso amagwiritsa ntchito ndalama zawo akamagwira ntchitoyi. Pofotokoza ntchito imene a Mboni za Yehova amagwira, wochita kafukufuku wina ananena kuti: “Cholinga chachikulu cha a Mboni ndi kulalikira komanso kuphunzitsa. . . . Alibe abusa amene amalipidwa ndipo izi zimapangitsa kuti asamawononge ndalama zambiri.” Ndiyeno kodi cholinga chathu chimakhala chotani tikamalalikira? Mwachidule tingati timalalikira chifukwa timakonda Yehova komanso anzathu. Zimenezi zimakwaniritsa ulosi wa pa Salimo 110:3. (Werengani.)

KODI TIYENERA KUGWIRITSA NTCHITO NJIRA ZITI POLALIKIRA?

Timalalikira kulikonse kumene tingapeze anthu (Onani ndime 10)

10. Kodi Yesu ndi ophunzira ake ankagwiritsa ntchito njira ziti polalikira?

10 Kodi Yesu ndi ophunzira ake ankagwiritsa ntchito njira ziti akamalalikira uthenga wabwino? Iwo ankalalikira kulikonse kumene kunkapezeka anthu, kaya ndi m’misewu kapena m’misika. Ankapitanso kunyumba ndi nyumba n’kumafufuza anthu oyenera. (Mat. 10:11; Luka 8:1; Mac. 5:42; 20:20) Njira imeneyi inkathandiza kuti azilalikira kwa anthu onse.

11, 12. Pa nkhani yolalikira uthenga wabwino kodi Matchalitchi Achikhristu amasiyana bwanji ndi Mboni za Yehova?

11 Kodi anthu a m’Matchalitchi Achikhristu amatsatira zimene Yesu ankachita akamalalikira? Nthawi zambiri iwo amasiyira abusa awo kuti azigwira ntchitoyi. Koma m’malo moti atsogoleri a matchalitchiwa akhale “asodzi a anthu,” amangokhutira ndi nsomba zimene ali nazo kale kapena kuti anthu amene ali m’matchalitchi awo. N’zoona kuti nthawi zina atsogoleri a matchalitchi ena amalimbikitsa anthu kuti azilalikira. Mwachitsanzo, kumayambiriro kwa chaka cha 2001, Papa Yohane Paulo Wachiwiri ananena m’kalata yake kuti: “Kwa zaka zambiri, ndakhala ndi kulimbikitsa anthu kuti azilalikira ndipo panopo ndikubwerezanso . . . Tiyenera kumva ngati mmene Paulo ankamvera pamene anati: ‘Tsoka kwa ine ngati sindilalikira uthenga wabwino.’” Papayu anapitiriza kunena kuti anthu “sayenera kusiyira ntchito yolalikira ‘akatswiri’ okha chifukwa kulalikira ndi udindo wa anthu onse a Mulungu.” Koma ndi anthu ochepa chabe amene anatsatira malangizowa.

12 Nanga kodi a Mboni amachita bwanji pa nkhaniyi? Iwo amalalikira kuti Yesu wakhala akulamulira kuyambira mu 1914. Mogwirizana ndi malangizo a Yesu, iwo amaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. (Maliko 13:10) Buku lina linati: “A Mboni za Yehova amaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kuposa chilichonse. Akaona anthu akuvutika ndi zinthu monga njala komanso matenda amawathandiza. . . . Koma amadziwa kuti ntchito yawo yaikulu ndi kuuza anthu za mapeto a dzikoli komanso zimene angachite kuti adzapulumuke.” (Pillars of Faith—American Congregations and Their Partners) A Mboni za Yehova amalalikira potsatira njira zimene Yesu ndi ophunzira ake ankagwiritsa ntchito.

KODI TIYENERA KULALIKIRA KUTI, NANGA KWA NTHAWI YAITALI BWANJI?

13. N’chiyani chikusonyeza kuti ntchito yolalikira iyenera kugwiridwa padziko lonse?

13 Yesu ananena kuti uthenga wabwino wa Ufumu uyenera kulalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mat. 24:14) Ananenanso kuti tiyenera kuthandiza “anthu a mitundu yonse” kuti akhale ophunzira ake. (Mat. 28:19, 20) Zimenezi zikutanthauza kuti ntchitoyi iyenera kugwiridwa padziko lonse lapansi.

14, 15. N’chiyani chikutsimikizira kuti a Mboni za Yehova akukwaniritsa ulosi wa Yesu wakuti uthenga udzalalikidwa padziko lonse? (Onani zithunzi patsamba 8.)

14 Tiyeni tikambirane mfundo zotsimikizira kuti a Mboni za Yehova akukwaniritsa ulosi wa Yesu wakuti uthenga udzalalikidwa padziko lonse. Ku United States kuli atsogoleri pafupifupi 600,000 a zipembedzo zosiyanasiyana. Koma kuli a Mboni za Yehova pafupifupi 1,200,000. Komanso padziko lonse pali ansembe achikatolika ongopitirira pang’ono 400,000. Ndiye taganizirani chiwerengero cha a Mboni amene akulalikira za Ufumu wa Mulungu. Padziko lonse, pali a Mboni oposa 8 miliyoni ndipo akulalikira m’mayiko 240. Apa zikuonekeratu kuti a Mboni za Yehova akulalikira uthenga wabwino padziko lonse ndipo ntchito yawo ikuthandiza kuti Yehova atamandike.—Sal. 34:1; 51:15.

15 Cholinga chathu n’chakuti tilalikire kwa anthu ambirimbiri mapeto asanafike. Kuti zimenezi zitheke, timamasulira ndi kufalitsa mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Timapereka kwaulere zinthu monga mabuku, magazini ndi timapepala. Panopa mabuku athu akumasuliridwa m’zilankhulo zoposa 700. Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lafalitsidwa m’zilankhulo zoposa 130, ndipo Mabaibulo amene asindikizidwa ndi oposa 200 miliyoni. Chaka chatha chokha tinasindikiza mabuku ndi zinthu zina zokwana 4 biliyoni ndi hafu. Komanso zinthu za pawebusaiti yathu zimamasuliridwa m’zilankhulo zoposa 750. Kodi pali gulu linanso lachipembedzo limene lingafike pamenepa?

16. Kodi tikudziwa bwanji kuti a Mboni za Yehova ali ndi mzimu wa Mulungu?

16 Koma kodi ntchitoyi tiigwira mpaka liti? Yesu ananena kuti idzagwiridwa mpaka m’masiku otsiriza “kenako mapeto adzafika.” Kodi pali chipembedzo chinanso chimene chikugwirabe ntchito yolalikira uthenga wabwino m’masiku otsiriza ano? Anthu ena amanena kuti, “Inu mumagwira ntchito yolalikira koma ife tili ndi mzimu woyera.” Koma kodi kugwirabe ntchito yolalikira si umboni wakuti tili ndi mzimu wa Mulungu? (Mac. 1:8; 1 Pet. 4:14) Anthu a zipembedzo zina ayesapo kuchita zimene a Mboni za Yehova amachita koma alephera. Ena amachita umishonale kwakanthawi, kenako n’kusiya. Ndipo ena amalalikira kunyumba ndi nyumba koma uthenga umene amalalikira umakhala wosiyana ndi umene Yesu ankalalikira.

KODI NDANI AKULALIKIRADI UTHENGA WABWINO MASIKU ANO?

17, 18. (a) Kodi tingatsimikize bwanji kuti a Mboni za Yehova ndi amene akulalikira uthenga wa Ufumu masiku ano? (b) Kodi chimatithandiza n’chiyani kuti tipitirize kugwira ntchitoyi?

17 Ndiye kodi ndi ndani akulalikira uthenga wabwino masiku ano? Mosakayikira, tingayankhe kuti ndi “Mboni za Yehova.” Tikutero chifukwa chakuti timalalikira uthenga woyenera womwe ndi uthenga wabwino wa Ufumu. Komanso timagwiritsa ntchito njira yoyenera chifukwa timapita kwa anthuwo. Timagwira ntchito yolalikirayi chifukwa timakonda Yehova ndi anthu osati chifukwa chofuna kupeza ndalama. Ndipotu timalalikira padziko lonse ndiponso timayesetsa kulalikira anthu amitundu yonse komanso m’zilankhulo zonse. Tipitirizabe kugwira ntchito yolalikirayi mwakhama mpaka mapeto afike.

18 Timachita chidwi kwambiri tikaona zimene tikukwaniritsa kuchita pa ntchito yolalikira. Koma kodi n’chiyani chimatithandiza kukwaniritsa zonsezi? Zimene mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Filipi, zikuyankha funso limeneli. Iye anati: “Mulungu amachita zinthu m’njira imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.” (Afil. 2:13) Tiyeni tonsefe tipitirize kudalira Atate wathu wachikondi kuti azitithandiza pamene tikuyesetsa kukwaniritsa utumiki wathu.—2 Tim. 4:5.