Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumasankha Bwanji Zochita?

Kodi Mumasankha Bwanji Zochita?

“Pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.”—AEF. 5:17.

NYIMBO: 69, 57

1. Kodi malamulo ena opezeka m’Baibulo ndi ati, nanga kumvera malamulowa n’kothandiza bwanji?

M’BAIBULO muli malamulo osiyanasiyana amene Yehova watipatsa. Mwachitsanzo, Yehova amaletsa chiwerewere, kulambira mafano, kuba komanso kuledzera. (1 Akor. 6:9, 10) Komanso Mwana wake, Yesu Khristu anatipatsa lamulo lakuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:19, 20) Tikamatsatira malamulo amenewa zinthu zimatiyendera bwino. Mwachitsanzo, timakhala ndi moyo wabwino, timakhala ndi banja losangalala komanso anthu amatilemekeza. Koma chofunika kwambiri n’choti Yehova amasangalala nafe ndiponso amatidalitsa.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani pali nkhani zina zimene m’Baibulo mulibe malamulo ake? (b) Kodi m’nkhaniyi tikambirana mafunso ati? (Onani chithunzi pamwambapa.)

2 Komabe pali nkhani zambiri zimene m’Baibulo mulibe malamulo ake. Mwachitsanzo, palibe malamulo onena za zovala zoyenera kwa Akhristu. Zimenezi zimasonyeza kuti Yehova ndi wanzeru. Tikutero chifukwa zikhalidwe zimasiyana, komanso masitayelo a zovala amasintha mogwirizana ndi nthawi. Choncho m’Baibulo mukanakhala mndandanda wa masitayelo oyenera kwa Akhristu, anthu akanasiya kukonda masitayelo amenewo pasanapite nthawi yaitali. N’chifukwa chakenso m’Baibulo mulibe malamulo onena za ntchito zimene tingagwire, thandizo lamankhwala lomwe tingalandire komanso zosangalatsa zimene tiyenera kuchita. Choncho mitu ya mabanja komanso munthu aliyense ali ndi udindo wosankha zochita pa nkhani zimenezi.

3 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tikhoza kusankha zilizonse pa nkhanizi osaganizira zimene Yehova amafuna? Kodi Atate wathu wakumwamba angagwirizane ndi zilizonse zimene tasankha malinga ngati sizikuphwanya lamulo la m’Baibulo? Nanga ngati m’Baibulo mulibe lamulo lokhudza nkhani inayake, kodi tingadziwe bwanji maganizo a Yehova pa nkhaniyo?

ZIMENE TIMASANKHA ZIMAKHUDZA IFEYO KOMANSO ANTHU ENA

4, 5. Kodi zosankha zathu zingakhudze bwanji ifeyo komanso anthu ena?

4 Anthu ena angaganize kuti palibe vuto ndi zimene amasankha kuchita. Koma kuti tikondweretse Yehova, tiyenera kuganizira malamulo komanso mfundo zopezeka m’Mawu ake n’kusankha mogwirizana ndi zimenezo. Mwachitsanzo, kuti Mulungu azisangalala nafe tiyenera kutsatira lamulo lake pa nkhani ya magazi. (Gen. 9:4; Mac. 15:28, 29) Tingamupemphe kuti atithandize kuti tizisankha zochita mogwirizana ndi malamulo komanso mfundo za m’Malemba.

5 Zimene timasankha pa nkhani zikuluzikulu zingalimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova kapena kuuwononga. Komanso zosankha zolakwika zingafooketse chikhulupiriro cha ena, kuwakhumudwitsa ndiponso zingasokoneze mtendere mumpingo. Choncho kusankha zochita mwanzeru n’kofunika kwambiri.—Werengani Aroma 14:19; Agalatiya 6:7.

6. Kodi tingasankhe bwanji zochita pa nkhani zimene m’Baibulo mulibe malamulo ake?

6 Ndiye kodi tingasankhe bwanji zochita pa nkhani zimene m’Baibulo mulibe malamulo ake? Zikatere, sitiyenera kungosankha zimene tikufuna. M’malomwake tiyenera kufufuza mfundo zonse zokhudza nkhaniyo kenako n’kusankha zimene Yehova angasangalale nazo.—Werengani Salimo 37:5.

TIZIZINDIKIRA CHIFUNIRO CHA YEHOVA

7. Ngati palibe lamulo lililonse la m’Baibulo pa nkhani inayake, kodi tingadziwe bwanji zimene Yehova angasangalale nazo?

7 Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingadziwe bwanji zimene Yehova angasangalale nazo ngati palibe lamulo lililonse la m’Baibulo pa nkhaniyo?’ Lemba la Aefeso 5:17, limati: “Pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.” Ndiye kodi tingazindikire bwanji chifuniro cha Yehovacho? Tiyenera kupemphera kwa iye komanso kulola kuti mzimu wake uzititsogolera.

8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankazindikira zimene Yehova ankafuna kuti iye achite?

8 Yesu ankazindikira zimene Atate wake ankafuna kuti iye azichita. Mwachitsanzo, kawiri konse iye anapemphera kwa Yehova ndipo anachulukitsa chakudya n’kukwanira anthu ambirimbiri. (Mat. 14:17-20; 15:34-37) Koma pamene Mdyerekezi anamuyesa m’chipululu anakana kusandutsa miyala kuti ikhale mikate ngakhale kuti anali ndi njala. (Werengani Mateyu 4:2-4.) Chifukwa chakuti amadziwa maganizo a Atate wake, sanalole kusandutsa miyala kuti ikhale mikate. Yesu anazindikira kuti Yehova sangasangalale ngati iyeyo atagwiritsa ntchito mphamvu zake kuti apeze zimene akufuna. Choncho pokana kusandutsa miyala kukhala mikate, anasonyeza kuti ankadalira Yehova kuti azimutsogolera komanso kum’patsa zofunika pa moyo.

9, 10. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru? Perekani chitsanzo.

9 Ngati tikufuna kusankha zochita mwanzeru, ifenso tiyenera kudalira Yehova kuti azititsogolera. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kutsatira mawu anzeru awa: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako. Usamadzione kuti ndiwe wanzeru. Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.” (Miy. 3:5-7) Choncho tikamaphunzira Baibulo n’kudziwa mmene Yehova amaonera zinthu, zimakhala zosavuta kuzindikira zimene tiyenera kuchita pa nkhani zosiyanasiyana. Izi zingathandize kuti tikhale ndi mtima womvera.—Ezek. 11:19.

10 Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mzimayi wapita kogula zinthu. Ndipo waona nsapato zimene wazikonda koma ndi zodula kwambiri. Kenako akuganizira kuti, ‘Kodi mwamuna wanga angamve bwanji akaona kuti ndawononga ndalama zambiri chonchi?’ Yankho la funsoli akhoza kulipeza ngakhale kuti mwamuna wakeyo kulibe. Zili choncho chifukwa chakuti wakhala naye nthawi yaitali ndipo amadziwa maganizo ake pa nkhani ya ndalama. Nafenso tikamadziwa maganizo a Yehova, sitingavutike kudziwa zimene akufuna kuti tichite pa nkhani inayake.

KODI TINGADZIWE BWANJI MAGANIZO A YEHOVA?

11. Kodi ndi mafunso ati amene tingadzifunse powerenga kapena pophunzira Baibulo? (Onani bokosi lakuti, “ Mafunso Oti Tizidzifunsa Tikamaphunzira Mawu a Mulungu.”)

11 Kuti tidziwe maganizo a Yehova tiyenera kuona kuti kuphunzira Baibulo n’kofunika kwambiri. Ndiyeno tikamaphunzira tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi nkhaniyi ikundiuza chiyani za Yehova, njira zake zolungama komanso maganizo ake?’ Tiyenera kukhala ndi maganizo amene Davide anali nawo. Paja iye anaimba kuti: “Ndidziwitseni njira zanu, inu Yehova. Ndiphunzitseni kuyenda m’njira zanu. Ndiyendetseni m’choonadi chanu ndi kundiphunzitsa, pakuti inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa. Chiyembekezo changa chili mwa inu tsiku lonse.” (Sal. 25:4, 5) Poganizira zimene mwawerenga m’Baibulo mungadzifunse kuti: ‘Kodi mfundo zimenezi ndingazigwiritse ntchito m’banja langa, kuntchito, kusukulu kapena mu utumiki?’ Tikazindikira kumene tingagwiritse ntchito mfundozo, zimakhala zosavuta kudziwanso mmene tingazigwiritsire ntchito.

12. Kodi mabuku athu komanso misonkhano zingatithandize bwanji kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani inayake?

12 Kutsatira malangizo amene gulu limatipatsa kungatithandizenso kuti tizidziwa maganizo a Yehova. Mwachitsanzo, zinthu monga Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani ndiponso Watch Tower Publications Index zimatithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana. Chinthu china chimene chingatithandize n’kupezeka pamisonkhano komanso kuyankhapo. Tikamaganizira kwambiri zimene tikuphunzira pamisonkhanoyo timayamba kuona zinthu mmene Yehova amazionera. Kuphunzira mabuku athu komanso kupezeka pamisonkhano kungatithandize kuti tidziwe bwino njira za Yehova. Izi zingathandizenso kuti tizisankha bwino zochita komanso kuti Yehova azitidalitsa.

MUZILOLA KUTI YEHOVA AZIKUTSOGOLERANI

13. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kudziwa maganizo a Yehova kungatithandize kuti tisankhe bwino zochita?

13 Tiyeni tikambirane chitsanzo chosonyeza kuti kudziwa maganizo a Yehova kungatithandize kuti tisankhe bwino zochita. Tiyerekeze kuti wofalitsa akufuna kuyamba upainiya wokhazikika. Ndiyeno kuti akwanitse angayambe kukhala moyo wosalira zambiri. Pa nthawi imodzimodziyo angamakayikire ngati angasangalaledi akakhala ndi zinthu zochepa. N’zoona kuti m’Baibulo mulibe lamulo loti tizichita upainiya ndipo n’zotheka kungokhala wofalitsa wokhulupirika. Koma Yesu ananena kuti anthu amene amalolera kusiya zinthu zina chifukwa cha Ufumu adzadalitsidwa kwambiri. (Werengani Luka 18:29, 30.) Komanso Malemba amanena kuti Yehova amasangalala kwambiri tikamapereka “nsembe zaufulu” ndiponso tikamamutumikira mokondwera. (Sal. 119:108; 2 Akor. 9:7) Ndiyeno wofalitsa ataganizira mfundo za m’malembawa komanso kupemphera kuti Mulungu amutsogolere akhoza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhaniyi. Izi zingathandize kuti asankhe zinthu zimene angakwanitse ndipo Yehova angamudalitse kwambiri.

14. Kodi mungadziwe bwanji maganizo a Yehova pa nkhani ya zovala?

14 Tiyeni tionenso chitsanzo china. Tiyerekeze kuti chovala chinachake chakusangalatsani komabe mukudziwa kuti chingakhumudwitse anthu ena mumpingo. Mukudziwanso kuti m’Baibulo mulibe lamulo loletsa chovalacho. Kodi mungadziwe bwanji maganizo a Yehova pa nkhani ngati imeneyi? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu ndi mwanzeru, osati kudzikongoletsa ndi masitayilo omangira tsitsi, golide, ngale, kapena zovala zamtengo wapatali. Koma azidzikongoletsa mogwirizana ndi mmene akazi amene amati amalemekeza Mulungu amayenera kudzikongoletsera. Azidzikongoletsa ndi ntchito zabwino.” (1 Tim. 2:9, 10) Mfundo za palembali zikukhudzanso amuna. Atumiki a Yehovafe sitimangoganizira zimene tikufuna koma timaganiziranso mmene ena angaonere zovala zathu. Kudzichepetsa komanso kukonda Akhristu anzathu kungapangitse kuti tiziwaganizira n’kumapewa kuwakhumudwitsa. (1 Akor. 10:23, 24; Afil. 3:17) Kuganizira zimene Malemba amanena kungatithandize kuzindikira maganizo a Yehova pa nkhani inayake n’kusankha mogwirizana ndi chifuniro chake.

15, 16. (a) Kodi Yehova amamva bwanji tikamaganizira zachiwerewere? (b) Tikamasankha zosangalatsa, kodi tingadziwe bwanji zimene Yehova amasangalala nazo? (c) Kodi tingasankhe bwanji zochita pa nkhani zikuluzikulu?

15 Baibulo limasonyeza kuti Yehova amakhumudwa anthu akamachita zoipa komanso ‘malingaliro onse a m’mitima yawo akamakhala oipa okhaokha.’ (Werengani Genesis 6:5, 6.) Zimenezi zingatithandize kuzindikira kuti kuganizira zachiwerewere n’koipa chifukwa kungapangitse kuti munthu achite tchimo. Yehova amafuna kuti tiziganizira zinthu zabwino osati zoipa. Yakobo analemba kuti: “Nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, ndiponso yopanda chinyengo.” (Yak. 3:17) Kuzindikira mfundo imeneyi kungatithandize kuti tizipewa zosangalatsa zimene zingapangitse kuti tiziganizira kapena kuchita zoipa. Akhristu olimba mwauzimu sachita kufunsa ngati kuli koyenera kapena ayi kuwerenga buku, kuonera filimu kapena kuchita masewera amene Mulungu amadana nawo. Amadziwiratu maganizo a Yehova pa nkhaniyo.

16 Nthawi zina pamakhala njira zingapo zimene munthu angasankhe koma zonsezo zili zokondweretsa Yehova. Komabe pali nkhani zina zazikulu zimene tingafunike kupempha malangizo kwa akulu kapena Akhristu ena olimba mwauzimu. (Tito 2:3-5; Yak. 5:13-15) Koma sitiyenera kuwapempha kuti atisankhire zochita pa nkhaniyo. Mkhristu aliyense ayenera kuphunzira kugwiritsa ntchito mphamvu zake za kuzindikira. (Aheb. 5:14) Tizikumbukira zimene Paulo ananena. Paja iye anati: “Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.”—Agal. 6:5.

17. Kodi timapeza madalitso otani tikamasankha zochita mogwirizana ndi maganizo a Yehova?

17 Tikamayesetsa kusankha zinthu mogwirizana ndi maganizo a Yehova, ubwenzi wathu ndi iye umalimba. (Yak. 4:8) Komanso iye amasangalala nafe ndiponso amatidalitsa. Zimenezi zimapangitsa kuti tizikhulupirira kwambiri Atate wathu wakumwamba. Choncho tiyeni tiziyesetsa kutsatira malamulo ndi mfundo za m’Baibulo popeza zimatithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana. N’zoona kuti kuphunzira za Yehova sikudzatha. (Yobu 26:14) Komabe tikamachita khama kuphunzira za iye, tingakhale anzeru, odziwa zinthu komanso ozindikira ndipo tingasankhe zochita mwanzeru. (Miy. 2:1-5) Maganizo ndi zochita za anthu zimasintha pakapita nthawi. Koma Baibulo limati: “Zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale. Maganizo a mumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.” (Sal. 33:11) Izi zikusonyeza kuti tikamasankha zochita mogwirizana ndi maganizo a Yehova, yemwe ndi wanzeru, zosankha zathu zimakhalanso zanzeru.