Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muzifuna-funa Ufumu, Osati Zinthu Zakuthupi

Muzifuna-funa Ufumu, Osati Zinthu Zakuthupi

“Pitilizani kufunafuna ufumu [wa Mulungu], ndipo zinthu zimenezi zidzawonjezedwa kwa inu.”—LUKA 12:31.

NYIMBO: 40, 98

1. Kodi zimene timafunikila mu umoyo zimasiyana bwanji ndi zimene timalakalaka?

PALI zinthu zocepa zimene timafunikila kuti tikhale na moyo. Koma zinthu zimene timalakalaka n’zambili. Anthu ambili sadziŵa kuti zinthu zimene timafunikila zisiyana ndi zimene timalakalaka. Kodi zisiyana bwanji? “Zinthu zimene timafunikila” ni zinthu zimene munthu afunika kukhala nazo kuti akhale ndi moyo. Mwacitsanzo, timafunikila cakudya, zovala, na malo okhala. Koma “zinthu zimene timalakalaka” ni zinthu zimene timafuna kukhala nazo, koma n’zosafunika kwenikweni kuti munthu akhale na moyo.

2. Ni zinthu zina ziti zimene anthu amafuna?

2 Zimene anthu amafuna zimasiyana kwambili malinga ndi dela limene amakhala. M’maiko osauka, anthu ambili amafuna cabe kukhala ndi ndalama kuti agule foni, honda, kapena malo ocepa okhalapo. M’maiko olemela, anthu amalakalaka kukhala na zovala zambili zapamwamba, nyumba ikulu, kapena galimoto yodula. Mosasamala kanthu za kumene timakhala kapena ndalama zimene tili nazo, tonse tingagwidwe mu msampha wokonda cuma ndi kumangolakalaka kukhala ndi zinthu zambili zakuthupi kaya zinthuzo n’zofunika kwambili kwa ife kapena ayi, kaya n’zochipa kapena ayi.

PEWANI KUKONDA ZINTHU ZAKUTHUPI

3. Kodi kukonda zinthu zakuthupi kumatanthauza ciani?

3 Kodi kukonda zinthu zakuthupi kumatanthauza ciani? Kumatanthauza kukondesetsa zinthu zakuthupi kuposa zinthu za kuuzimu. Munthu wokonda cuma amadziŵika mwa kuona zimene amalakalaka, zimene amafuna kucita, ndi zimene amaika patsogolo mu umoyo wake. Iye amafuna kukhala ndi zinthu zambili zakuthupi. Nthawi zina, munthu wokonda zinthu zakuthupi sakhala cabe munthu wandalama zambili kapena katundu wodula. Ngakhale anthu osauka angakhale ndi mzimu wokonda cuma cakuti angaleke kufuna-funa Ufumu coyamba.—Aheb. 13:5.

4. Kodi Satana amaseŵenzetsa bwanji “cilakolako ca maso”?

4 Satana amaseŵenzetsa dzikoli kuti atipangitse kuganiza kuti tingakhale acimwemwe pokhapo ngati tili ndi zinthu zambili. Iye ni waluso pokopa anthu ndi “cilakolako ca maso.” (1 Yoh. 2:15-17; Gen. 3:6; Miy. 27:20) M’dzikoli muli zinthu zakuthupi zosiyanasiyana, zapamwamba ndi zacabe-cabe. Zina mwa zinthu zimenezo zimakhala zokopa. Kodi munagulapo zinthu zimene simunali kufunikila cabe cifukwa cakuti zinali kuoneka zokongola kapena cifukwa cokopeka ndi zokamba za otsatsa malonda? Kodi pambuyo pake munazindikila kuti zinthu zimenezo zinali zosafunikila kwenikweni? Ngati timagula zinthu zosafunikila, tikhoza kusokoneza umoyo wathu, ndipo tingayambe kukhala ndi nkhawa kwambili. Zinthu zimenezo zingakhale msampha, ndipo zingatilepheletse kucita zinthu zakuuzimu monga kuphunzila Baibulo, kukonzekela ndi kupezeka pa misonkhano, ndi kupita mu ulaliki nthawi zonse. Musaiŵale kuti mtumwi Yohane anapeleka cenjezo lakuti: “Dziko likupita limodzi ndi cilakolako cake.”

5. Kodi anthu amene amacita khama kuti akhale ndi zinthu zambili amakumana ndi mavuto ya bwanji?

5 Satana amafuna kuti tikhale akapolo a Cuma m’malo motumikila Yehova. (Mat. 6:24) Anthu amene amacita khama kuti akhale ndi zinthu zambili, amakhala ndi umoyo wopanda tanthauzo cifukwa amafuna cabe kukhutilitsa zilakolako zawo zadyela. Kuonjezela apo, umoyo wawo wa kuuzimu umasokonezeka ndipo sakhala okondwela. (1 Tim. 6:9, 10; Chiv. 3:17) Izi zigwilizana ndi zimene anakamba Yesu m’fanizo lake la wofesa mbewu. Iye anati uthenga wa Ufumu ‘ukafesedwa paminga, . . . zilakolako za zinthu zina, zimaloŵa ndi kulepheletsa mawuwo kukula, ndipo sabala zipatso.’—Maliko 4:14, 18, 19.

6. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Baruki?

6 Ganizilani za Baruki, mlembi wa mneneli Yeremiya. Yerusalemu atatsala pang’ono kuonongedwa, Baruki anayamba ‘kufunafuna zinthu zazikulu.’ Koma zinthu zimenezo zinali zosakhalitsa. Iye anafunika cabe kuyembekezela zimene Mulungu anamulonjeza. Yehova anamulonjeza kuti: “Ndidzakupatsa moyo wako monga cofunkha cako.” (Yer. 45:1-5) Yehova anakamba kuti adzawononga mzindawo ndipo sadzateteza katundu wa munthu aliyense. (Yer. 20:5) Lomba, tikukhala kumapeto kwenikweni kwa dziko la Satana. Conco, ino si nthawi yodziunjikila cuma. Ndipo tisaganize kuti pambuyo pa cisautso cacikulu, tidzakhalabe ndi zinthu zimene tili nazo masiku ano, ngakhale kuti timazikonda bwanji.—Miyambo 11:4; Mateyu 24:21, 22; Luka 12:15.

7. Kodi tikambilana ciani lomba? Nanga n’cifukwa ciani?

7 Yesu anatipatsa malangizo abwino kwambili amene angatithandize kupeza zinthu zofunika mu umoyo popanda kucenjenekwa, kukonda zinthu zakuthupi kapena kukhala ndi nkhawa kwambili. Anapeleka malangizo amenewa pa ulaliki wake wa pa Phiri. (Mat. 6:19-21) Lomba tiyeni tiŵelenge ndi kupenda lemba la Mateyu 6:25-34. Kucita zimenezi kudzatilimbikitsa kupitilizabe ‘kufunafuna Ufumu,’ osati zinthu zakuthupi.Luka 12:31.

YEHOVA AMATIPATSA ZIMENE TIMAFUNIKILA MU UMOYO

8, 9. (a) N’cifukwa ciani sitiyenela kudela nkhawa kwambili zinthu zofunikila mu umoyo? (b) N’ciani cimene Yesu anali kudziŵa ponena za anthu ndi zinthu zimene amafunikila?

8 Ŵelengani Mateyu 6:25. Pamene Yesu anauza ophunzila ake kuti “lekani kudela nkhawa moyo wanu,” anali kutanthauza kuti ayenela “kuleka kudandaula.” Iwo anali kudela nkhawa zinthu zimene sanafunike kuda nazo nkhawa. Yesu anali ndi zifukwa zomveka pamene anawauza kuti aleke kudela nkhawa. Kukonda kudela nkhawa kapena kudandaula pa zinthu zimene sitifunika kuda nazo nkhawa, ngakhale pa zinthu zomveka kungavutitse cabe maganizo a munthu ndi kumulepheletsa kuganizila zinthu za kuuzimu zimene ndiye zofunika kwambili. Yesu anali kukonda kwambili ophunzila ake cakuti pa ulaliki wake wa pa phili anacita kuwacenjeza ka 4 za kuopsa kodela nkhawa zinthu zosafunika.—Mat. 6:27, 28, 31, 34.

9 Zakudya, zakumwa, ndi zovala n’zofunika kwambili mu umoyo. Nanga n’cifukwa ciani Yesu anakamba kuti sitiyenela kudela nkhawa zinthu zimenezi? Ngati tisoŵa njila yopezela zinthu zimenezi, mwacibadwa timada nkhawa, ndipo ngakhale Yesu anali kudziŵa zimenezi. Iye anali kudziŵa zinthu zimene anthu amafunikila tsiku ndi tsiku. Koposa zonse, anali kudziŵa mavuto amene ophunzila ake anali kukumana nawo panthawiyo. Anadziŵanso kuti pakapita zaka zambili, iwo adzakhala “m’masiku otsiliza,” amene ni “nthawi yapadela komanso yovuta.” (2 Tim. 3:1) Zoona, zinthu n’zovuta masiku ano cifukwa anthu ambili ali pa ulova, zinthu n’zodula, cakudya n’cocepa, ndipo anthu ambili ni osauka. Ngakhale n’telo, Yesu anali kudziŵa kuti moyo ndiye wofunika kwambili kuposa cakudya, ndipo thupi n’lofunika kwambili kuposa covala.

10. Pophunzitsa ophunzila ake kupemphela, kodi Yesu anakamba kuti n’ciani ciyenela kukhala cofunika kwambili?

10 Yesu akalibe kupeleka malangizo amenewa, anaphunzitsa ophunzila ake kuti popemphela, azipempha atate wawo wakumwamba kuti awapatse zinthu zakuthupi. Anawauza kuti azipemphela kuti: “Mutipatse ife lelo cakudya cathu calelo.” (Mat. 6:11) Kapena kuti: “Mutipatse cakudya cathu calelo malinga ndi cakudya cofunika pa tsikuli.” (Luka 11:3) Koma apa Yesu sanatanthauze kuti basi tizingoganizila kuti ‘Kaya lelo nizadya cani.’ M’pemphelo la citsanzo limeneli, Yesu anaonetsa kuti cinthu cofunika kwambili ni kupemphelela Ufumu wa Mulungu kuti ubwele. (Mat. 6:10; Luka 11:2) Kuti awakhazike mtima pansi, Yesu anafotokoza mmene Yehova amasamalila zolengedwa zake.

11, 12. Tiphunzila ciani tikaganizila mmene Yehova amasamalila mbalame? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

11 Ŵelengani Mateyu 6:26. ‘Tizionetsetsa mbalame zam’mlengalenga.’ Ngakhale kuti mbalame ni zocepa thupi, zimadya kwambili zipatso, mbewu, tudoyo kapena nyongolotsi. Zili na matupi ang’ono koma zimadya kambili patsiku kuposa munthu. Koma zilibe munda umene zimabyalapo mbewu ndi kukolola zakudya. Amazipatsa Yehova zilizonse zimene zifunikila. (Sal. 147:9) Sikuti amacita kutenga zakudya ndi kuziika mkamwa mwa mbalame iyayi. Cakudya cimakhalako cambili koma zimafunika kuyenda kukacisakila na kucipeza.

12 Yesu anali kudziŵa kuti ngati Atate wake amasamalila mbalame, sangakangiwe kusamalila anthu. (1 Pet. 5:6, 7) Sitiyenela kukhala aulesi, ndi kuyembekezela kuti Yehova adzabweletsa cakudya ndi kuciika pa thebulo. Zimene Iye adzacita ni kutidalitsa ndi kukulitsa cakudya cimene tabyala, kapena kutithandiza kuti tipeze ndalama zogulila zinthu zimene timafunikila tsiku lililonse. Ngati tasoŵelatu cocita, angacititse kuti ena atipatseko zimene ali nazo. Ngakhale kuti Yesu sanakambepo zakuti mbalame zimakhala ndi malo okhala, Yehova anazilenga ndi nzelu ndiponso luso ndipo amazipatsa zinthu zofunikila kuti zikwanitse kumanga zisa zokhalamo. Ngati Yehova amathandiza mbalame kumanga zisa, ndiye kuti adzatithandiza kupeza malo oti tikhalemo pamodzi ndi banja lathu.

13. N’ciani cionetsa kuti ndife ofunika kwambili kuposa mbalame?

13 Yesu anafunsa ophunzila ake kuti: “Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” N’zoonekelatu kuti apa Yesu anali kuganizila zoti posacedwa apeleka moyo wake cifukwa ca mtundu wa anthu. (Yelekezelani ndi Luka 12:6, 7.) Sikuti Khiristu anapeleka dipo cifukwa ca zolengedwa zonse. Iye sanafele mbalame, koma anafela ife anthu kuti tikasangalale na moyo wosatha.—Mat. 20:28.

14. Kodi munthu amene ali ndi nkhawa sangacite ciani?

14 Ŵelengani Mateyu 6:27. N’cifukwa ciani Yesu anakamba kuti sitingatalikitse moyo wathu pang’ono mwa kuda nkhawa? Cifukwa cakuti kudela nkhawa kwambili cifukwa ca zinthu zofunikila mu umoyo sikungacititse kuti tikhale moyo utali. M’malo mwake, kungacititse cabe munthu kumwalila msanga.

15, 16. (a) Tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene Yehova amasamalila maluwa? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Ni funso liti limene tingadzifunse? Cifukwa?

15 Ŵelengani Mateyu 6:28-30. Munthu aliyense amasangalala akavala zovala zabwino, makamaka ngati ayenda mu ulaliki, ku misonkhano ya mpingo, kapena ya cigawo. Kodi izi zitanthauza kuti tizingodela nkhawa “pa nkhani ya zovala”? Apanso, Yesu anatikumbutsa za cilengedwe ca Yehova. Tingaphunzilepo kanthu tikaona “maluwa akuchile.” Mwina Yesu anali kuganizila za “maluwa” okongola osiyanasiyana. Maluwa amenewa satunga nsalu kapena zovala ndi kuzivalika kuti aoneke okongola. Koma ni okongola kwambili cakuti “ngakhale Solomo mu ulemelelo wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.”

16 Mfundo imene Yesu anali kukamba apa ni yakuti: “Ngati Mulungu amaveka cotelo zomela zakuchile . . . , kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo, acikhulupililo cocepa inu?” N’zosacita kufunsa. Koma ophunzila a Yesu cinawavuta kukhulupilila zimenezi cifukwa anali ndi cikhulupililo cocepa. (Mat. 8:26; 14:31; 16:8; 17:20) Anafunika kukhala ndi cikhulupililo colimba ndi kudalila Yehova. Nanga ife bwanji? Kodi timakhulupililadi kuti Yehova adzatipatsa zinthu zimene timafunikila?

17. N’ciani cingawononge unansi wathu ndi Yehova?

17 Ŵelengani Mateyu 6:31, 32. Mulungu amasamalila anthu amene amaika zinthu za Ufumu patsogolo mu umoyo wawo. Conco, ife sitifunika kutengela anthu a “mitundu ina,” amene alibe cikhulupililo mwa Atate wathu wacikondi wa kumwamba. Kufuna-funa mwakwama zinthu zimene “anthu a mitundu ina akufunafuna” kungawononge cabe unansi wathu ndi Yehova. Koma ngati timacita zoyenela ndi kuika zinthu za Ufumu patsogolo mu umoyo wathu, tisakaikile kuti Yehova adzatipatsa ciliconse cimene tifuna. Ndipo ngati zoona ndife “odzipeleka kwa Mulungu,” tidzakhala okhutila ndi zimene tili nazo monga “cakudya, zovala ndi pogona.”—1 Tim. 6:6-8; ftn.

KODI MUMAFUNA-FUNA UFUMU WA MULUNGU COYAMBA MU UMOYO WANU?

18. N’ciani cimene Yehova amadziŵa cokhudza aliyense wa ife? Nanga adzaticitila ciani?

18 Ŵelengani Mateyu 6:33. Ophunzila a Khiristu afunika kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wawo nthawi zonse. Yesu anakamba kuti ngati ticita zimenezi “[zinthu] zina zonsezi zidzawonjezedwa” kwa ife. N’cifukwa ciani Yesu anakamba izi? Anafotokoza cifukwa cake pamene anati: “Atate wanu wakumwamba akudziŵa kuti inuyo mumafunikila zinthu zonsezi,” kutanthauza ciliconse cofunika mu umoyo wa munthu. Pankhani ya zakudya, zovala, ndi malo okhala, Yehova amadziŵa bwino-bwino kuti ‘uyu afunika izi, uje afunikila ici.’ Iye amadziŵa izi ife eni ake tikalibe kudziŵa. (Afil. 4:19) Ngati covala cinacake cimene timavala cili pafupi kusila, amadziŵa kuti tifunikila cina. Amadziŵanso mtundu wa zakudya zimene thupi limafunikila. Kuonjezela apo, amadziŵa kuti ife ndi banja lathu tifunika malo okhalapo. Zoona, Yehova adzaonetsetsa kuti tili ndi zinthu zofunikila mu umoyo.

19. N’cifukwa ciani sitiyenela kudela nkhawa za kutsogolo?

19 Ŵelengani Mateyu 6:34. Mwaona ka? Yesu anacita kukambanso kaciŵili kuti: “Musamade nkhawa.” Iye afuna kuti tisazidela nkhawa za maŵa koma tizidalila kwambili Yehova kuti adzatipatsa zimene tifunikila tsiku lililonse. Ngati munthu amakonda kudela nkhawa za kutsogolo, angayambe kudzidalila m’malo modalila Yehova. Ndipo kucita zimenezi kungasokoneze unansi wake ndi Yehova.—Miy. 3:5, 6; Afil. 4:6, 7.

MUZIFUNA-FUNA UFUMU COYAMBA NDIPO YEHOVA ADZAKUPATSANI ZOFUNIKILA

Mungacite ciani kuti mukhale na umoyo wosafuna zambili kuti muike patsogolo zinthu za Ufumu? (Onani ndime 20)

20. (a) Ni zolinga za bwanji zimene mungasankhe potumikila Yehova? (b) Mungacite ciani kuti mucepetseko zocita mu umoyo wanu?

20 Ni kusaganiza bwino kuleka kuika zinthu za Ufumu patsogolo cifukwa cofuna cabe kupeza zinthu zambili zakuthupi. Cofunika ni kuika zinthu za kuuzimu patsogolo mu umoyo wathu. Mwacitsanzo, ngati mufuna, mungasamukileko ku mpingo wosoŵa. Kapena mungayambe upainiya. Ngati munayamba kale upainiya, mwina mungafunsile kuti muloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Kapenanso mungapatule masiku angapo pa wiki kuti muziyenda kukathandizako nchito pa Beteli kapena pa ofesi ya omasulila mabuku. Cinanso, mungadzipeleke kuti muzitumikila m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga ndi kuseŵenzetsa nthawi yanu kumanga Nyumba za Ufumu. Ganizilankoni zimene mungacite kuti mukhale ndi umoyo wosafuna zinthu zambili kuti muzikhala ndi nthawi yambili yocita zinthu za kuuzimu. Mwa pemphelo pendani bokosi yakuti “ Zimene Mungacite Kuti Mukhale na Umoyo Wosafuna Zambili,” ndipo yambani kucitapo kanthu kuti mukwanilitse zimene mwasankha.

21. N’ciani cingatithandize kuti Yehova akhale bwenzi lathu?

21 Yesu amatifunila zabwino, ndiye cifukwa cake anatiphunzitsa kuti tiyenela kufuna-funa Ufumu coyamba osati zinthu zakuthupi. Tikacita zimenezo sitizayamba kudela nkhawa kwambili zinthu zimene timafunikila. Tikadalila Yehova ndi kupewa kufuna-funa zinthu zilibe phindu kapena kugula zinthu zilizonse zimene taona, Yehova adzakhala bwenzi lathu lapamtima. Kukamba zoona, kukhala moyo wosafuna zinthu zambili kudzatithandiza kuti ‘tigwile mwamphamvu moyo weniweniwo’ umene uli m’njila.—1 Tim. 6:19.

[1] (ndime 12) Nthawi zina, atumiki a Yehova sakhala na cakudya cokwanila. Kuti mudziŵe cifukwa cake Yehova amalolela kuti zimenezi zicitike, onani nkhani yakuti: “Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi” mu Nsanja ya Mlonda ya September 15, 2014, pa tsamba 22.