Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Usachite Mantha. Ineyo Ndikuthandiza”

“Usachite Mantha. Ineyo Ndikuthandiza”

TIYEREKEZE kuti mukuyenda nokhanokha usiku. Mwadzidzidzi mukuona munthu wina akubwera pambuyo panu. Mukuchita mantha n’kuima, koma nayenso akuima. Kenako mwayamba kuyenda mwandawala, ndipo nayenso akuyamba kuyenda mwandawala. Ndiyeno mukuyamba kuthamanga kuthawira kunyumba ya mnzanu amene amakhala chapafupi. Mutafika mnzanuyo akutsegula chitseko n’kukuuzani kuti mulowe. Apa mtima wanu ukukhala m’malo.

Mwina zoterezi sizinakuchitikirenipo. Koma n’kutheka kuti mukukumana ndi mavuto ena amene akukudetsani nkhawa. Mwachitsanzo, kodi mukuyesetsa kuti musiye zinthu zina zolakwika koma zikukuvutani? Kodi mwayesetsa kwa nthawi yaitali kuti mupeze ntchito koma simukuipeza? Nanga kodi mumadera nkhawa za mavuto amene mudzakumane nawo mukadzakalamba? Kapena pali mavuto ena amene amakudetsani nkhawa?

Kaya mukukumana ndi mavuto otani, kodi simungasangalale patakhala mnzanu amene mungathe kumuuza mavuto anuwo iyeyo n’kukuthandizani? Kodi inuyo muli ndi mnzanu woteroyo? Inde muli naye, ndipo ndi Yehova. Lemba la Yesaya 41:8-13 limasonyeza kuti iye anali mnzake wa Abulahamu, choncho angathenso kukhala mnzanu. Vesi 10 ndi 13 limasonyeza kuti Yehova anauza atumiki ake kuti: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo. Pakuti ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”

“NDIKUGWIRA MWAMPHAMVU”

Ngati mutawaganizira kwambiri mawu amenewa mutha kuona kuti ndi olimbikitsa kwambiri. Mawuwa sakusonyeza kuti mwagwirana manja ndi Yehova n’kumayenda naye limodzi, wina apa wina apa. Zikanakhala choncho ndiye kuti dzanja lake lamanja likanagwira dzanja lanu lamanzere. Koma lembali likusonyeza kuti Yehova akutambasula ‘dzanja lake lamanja lachilungamo’ n’kugwira ‘dzanja lanu lamanja.’ Zili ngati kuti akukukokani kuti akuchotseni pamalo ovuta kwambiri. Ndiyeno pochita zimenezi akukulimbikitsani ndi mawu oti: “Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.”

Kodi inuyo mumaona kuti Yehova ndi Atate wanu komanso Mnzanu amene angakuthandizeni mukapanikizika ndi mavuto? Iye amakuganizirani, amakufunirani zabwino komanso amafunitsitsa kukuthandizani. Yehova amakukondani kwambiri ndipo amafuna kuti musamade nkhawa mukakumana ndi mavuto. Mpake kuti Baibulo limati iye ndi “thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.”—Sal. 46:1.

NGATI TIMADZIIMBABE MLANDU

Anthu ena amadziimbabe mlandu kwambiri akaganizira zimene analakwitsa m’mbuyomu ndipo amakayikira zoti Mulungu anawakhululukira. Ngati inuyo mumadziimba mlandu mwina mungafanane ndi Yobu amene ankakumbukira ‘zolakwa zimene anachita ali mnyamata.’ (Yobu 13:26) Nayenso Davide ankadziimba mlandu ndipo anapempha Yehova kuti: “Musakumbukire machimo a pa unyamata wanga ndi zolakwa zanga.” (Sal. 25:7) Popeza tonsefe si angwiro, timachimwa ndipo ndife “operewera pa ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 3:23.

Mawu a mu Yesaya chaputala 41 ndi amene Yehova anauza anthu ake akale. Anthuwa anachimwa kwambiri moti Yehova anaganiza zowalanga polola kuti apite ku ukapolo ku Babulo. (Yes. 39:6, 7) Koma Yehova ankaganiziranso nthawi imene adzapulumutse amene adzalape n’kubwerera kwa iye. (Yes. 41:8, 9; 49:8) Masiku anonso, Yehova amakomera mtima anthu amene alapa ndipo akufunitsitsa kumusangalatsa.—Sal. 51:1.

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Takuya. * M’baleyu anali ndi vuto loonera zolaula komanso kuseweretsa maliseche. Iye ankafuna atasiya koma ankangopezeka kuti wachitanso zomwezo. Takuya anati: “Ndinkadziona kuti ndine wachabechabe. Komabe ndikapemphera kwa Yehova iye ankandigwira dzanja n’kundidzutsa.” Kodi Yehova ankachita bwanji zimenezi? Akulu a mumpingo wake anamuuza kuti aziwaimbira foni akagweranso mu vuto lakelo. Iye anati: “Kunena zoona sizinali zophweka kuwaimbira foni, koma ndikaimba ankandilimbikitsa kwambiri.” Kenako akuluwo anakonza zoti woyang’anira dera akamuone pa ulendo waubusa. Woyang’anira derayo atafika anamuuza kuti: “Sikuti ndangobwera kuno mwangozi. Akulu ndi amene andipempha kuti ndibwere. Anasankha iweyo kuti ndikuyendere.” Takuya anati: “Ngakhale kuti ndinkamuchimwira Yehova, iye anagwiritsa ntchito akulu kuti andithandize.” Takuya anakwanitsa kusiya zimene ankachitazo. Kenako anakhala mpainiya wokhazikika ndipo panopa akutumikira pa Beteli. Inunso Yehova angakuthandizeni kuti musiye zinthu zolakwika zimene zikukuvutani kusiya.

NGATI TIKUDERA NKHAWA ZOFUNIKA PA MOYO

Vuto la ulova likudetsa nkhawa anthu ambiri. Ena amachotsedwa ntchito ndipo amasowa njira yopezera ndalama. Kodi mungamve bwanji mutakhala kuti mukuyesetsa kusaka ntchito koma osaipeza? Zoterezi zikachitika ena amayamba kudziona kuti ndi achabechabe. Ndiye kodi Yehova angakuthandize bwanji? Sikuti iye angakupatseni ntchito yabwino pompopompo ayi. Koma mwina angakuthandizeni kukumbukira mawu a Davide akuti: “Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya.” (Sal. 37:25) Yehova amaona kuti ndinu amtengo wapatali kwambiri ndipo ‘dzanja lake lamanja lachilungamo’ likhoza kukuthandizani kupeza zofunika, uku mukumutumikira.

Kodi Yehova angakuthandizeni bwanji ntchito itakutherani?

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Sara amene amakhala ku Colombia. Iye ankagwira ntchito pakampani yapamwamba ndipo ankalandira ndalama zambiri. Koma ntchito yakeyi sinkamupatsa mpata wochita zinthu zokhudza kulambira. Komabe iye ankafuna kuchita zambiri choncho anaisiya n’kuyamba upainiya. Ankafuna atapeza ntchito yoti azingogwira masiku ochepa koma sanaipeze. Choncho anangoyamba kabizinezi kogulitsa ayisikilimu. Koma bizinezi yakeyi inayamba kulowa pansi mpaka inatha. Sara anati: “Panadutsa zaka zitatu ndisakugwira ntchito kapena kuchita bizinezi koma Yehova anandithandiza kupirira.” Iye anaphunzira kusiyanitsa zinthu zofunika ndi zosafunika kwenikweni ndipo anasiya kudera nkhawa za mawa. (Mat. 6:33, 34) Kenako abwana ake aja anamuuza kuti akayambenso ntchito imene ankagwira ija. Iye ananena kuti akhoza kuyamba ngati atamulola kuti azigwira masiku ochepa komanso ngati azimupatsa mpata wosonkhana ndi kulalikira. Ngakhale kuti panopa Sara sapeza ndalama zambiri ngati zimene ankapeza poyamba, akukwanitsabe kuchita upainiya. Iye amanena kuti pa nthawi yonseyi wakhala akuona dzanja la Yehova likumuthandiza.

NGATI TIKUDERA NKHAWA ZA UKALAMBA

Nkhani ina imene imadetsa nkhawa anthu ambiri ndi ukalamba. Ena akamakalamba amada nkhawa kuti mwina azidzavutika kupeza zofunika pa moyo. Amaderanso nkhawa za matenda amene angabwere chifukwa cha ukalamba. Davide ayenera kuti ndi amene anachonderera Yehova kuti: “Musanditaye nthawi ya ukalamba wanga. Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zikutha.”—Sal. 71:9, 18.

Kodi n’chiyani chingathandize atumiki a Yehova kuti asamade nkhawa akakalamba? Chofunika n’kukhulupirira kwambiri Mulungu ndipo asamakayikire zoti aziwathandiza kupeza zofunika pa moyo. Mwina ngati anazolowera moyo wawofuwofu ayenera kuphunzira moyo wosalira zambiri. Angazindikirenso kuti kudya “zamasamba” kukhoza kukhala kosangalatsa komanso kothandiza kuposa kudya “nyama ya ng’ombe.” (Miy. 15:17) Ngati mumatumikira Yehova ndi moyo wanu wonse, iye adzaonetsetsa kuti mukupeza zofunika, ngakhale mutakalamba.

A José ndi a Rose ali limodzi ndi banja limene linawathandiza

Chitsanzo china ndi cha a José ndi akazi awo a Rose. Banjali lakhala likuchita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 65. Pa zaka zonsezi ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, bambo awo a Rose ankadwala ndipo ankafunika kuwasamalira usana ndi usiku. Nawonso a José anali ndi vuto la khansa ndipo anawachita opaleshoni komanso ankalandira chithandizo china. Koma Yehova anathandiza kwambiri banjali. Iye anagwiritsa ntchito banja la Tony ndi Wendy lomwe ankasonkhana nalo mumpingo umodzi. Kuyambira kale, Tony ankafuna kuti nyumba yake ina adzaipereke kwa apainiya. Iye ali pa sukulu ankaona banja la achikulirewa likupita kukalalikira. Izi n’zimene zinachititsa kuti patapita nthawi, iye ndi mkazi wake apereke nyumbayi kuti banjalo lizikhalamo kwaulere. Anachita izi poona kuti banjali linkadzipereka kwambiri potumikira Yehova. Panopa a José ndi akazi awo ali ndi zaka za m’ma 80 ndipo akhala m’nyumba imeneyi kwa zaka 15. Achikulirewa amaona kuti zimene banja lachinyamatali lachita ndi mphatso yochokera kwa Yehova.

Yehova akufuna kukuthandizaninso inuyo ndi ‘dzanja lake lamanja lachilungamo.’ Kodi mupereka dzanja lanu kuti akugwireni? Paja iye akukuuzani kuti: “Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.”

^ ndime 11 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.