Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Usacite Mantha. Ndikuthandiza”

“Usacite Mantha. Ndikuthandiza”

YELEKEZELANI kuti muyenda pamsewu usiku. Mwadzidzidzi, muona kuti munthu akukulondolani kumbuyo kwanu. Mukaima, nayenso aima. Mukayenda mwamsanga, nayenso ayenda mwamsanga. Ndiyeno mwayamba kuthaŵila ku nyumba ya mnzanu imene ili pafupi. Mnzanuyo atsegula citseko ndi kukuzani kuti muloŵe, ndipo mtima wanu ukhala pansi podziŵa kuti mwatetezeka tsopano.

Mwina zinthu ngati zimenezi zikalibe kukucitikilamponi. Koma nkhawa zina zimene timakhala nazo mu umoyo zingakucititseni kukhala na mantha. Mwacitsanzo, kodi muli ndi cofooka cinacake cimene mukulimbana naco? Kodi mwakhala pa ulova kwa nthawi yaitali ngakhale kuti mumayesetsa kusakila nchito? Kodi mumada nkhawa cifukwa coopa kukalamba ndi kukumana ndi mavuto amene amabwela cifukwa ca ukalamba? Kapena pali zina zake zimene zikudetsani nkhawa?

Kaya mukumana ndi mavuto a bwanji, kodi simungakondwele kukhala ndi mnzanu amene mungamauzeko nkhawa zanu ndiponso amene angakuthandizeni? Kodi muli naye mnzanu wotelo? Inde, muli naye. Yehova ndiye mnzanu wa conco. Pa Yesaya 41:8-13, timaŵelenga kuti iye anali bwenzi la kholo loyamba Abulahamu. Pa vesi 10 ndi 13, Yehova analonjeza kuti: “Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwila mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lacilungamo. Pakuti ine, Yehova Mulungu wako, ndagwila dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usacite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”

“NDIKUGWILA MWAMPHAMVU”

Mawu a Yehova amenewa ndi olimbikitsa kwambili. Yelekezelani kuti Yehova akuuza inu mawu amenewa. Vesi imeneyi siikamba kuti mukuyenda pamodzi ndi Yehova ndipo iye wakugwilani dzanja, ngakhale kuti zimenezo zingakhale zosangalatsa. Ngati mungayende naye pamodzi, ndiye kuti dzanja lake lamanja lingagwile dzanja lanu lamanzele. Koma Yehova amaseŵenzetsa ‘dzanja lake lamanja lacilungamo’ ndi kugwila ‘dzanja lanu lamanja,’ ngati kuti akukudonsani kuti mucoke pa malo oipa. Amacita izi, uku akukulimbikitsani kuti: “Usacite mantha. Ineyo ndikuthandiza.”

Kodi mumaona Yehova monga Tate wacikondi ndi Bwenzi lapamtima? Kodi mumakhulupilila kuti adzakuthandizani pamene mwakumana ndi mavuto? Yehova amakukondani ndipo amafuna kukuthandizani. Mukakumana ndi mavuto, Yehova amafuna kuti muzidzimva otetezeka cifukwa amakukondani kwambili. Zoona, iye ndi “thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.”—Sal. 46:1.

KUDZIIMBA MLANDU CIFUKWA CA ZOLAKWA ZAKALE

Anthu ena amakumbukilabe macimo amene anacita kale ndipo amakaikila kuti Mulungu anawakhululukila. Ngati mumamvela conco, ganizilani za munthu wokhulupilika Yobu. Iye anavomeleza kuti anacita zolakwa pamene ‘anali mnyamata.’ (Yobu 13:26) Pa nthawi ina, nayenso wamasalimo Davide anamvela conco, ndipo anapempha Yehova kuti: “Musakumbukile macimo a pa unyamata wanga ndi zolakwa zanga.” (Sal. 25:7) Popeza ndife opanda ungwilo, tonse ndife ‘ocimwa ndiponso opelewela pa ulemelelo wa Mulungu.’—Aroma 3:23.

Uthenga umene uli pa Yesaya 41, poyamba analembela anthu a Mulungu akale. Iwo anacimwa kwambili cakuti Yehova anawalanga mwa kulola kuti Ababulo awatenge ndi kupita nawo kwawo monga akapolo. (Yes. 39:6, 7) Komabe, Mulungu anali kuyembekezela nthawi imene adzaombola anthu ake amene adzalapa ndi kubwelela kwa iye. (Yes. 41:8, 9; 49:8) Masiku ano, Yehova amakomelanso mtima anthu amene amalapa moona mtima.—Sal. 51:1.

Ganizilani citsanzo ca Takuya, * amene anali kulimbana ndi cizolowezi cotamba zamalisece ndi kuseŵeletsa malisece. Nthawi zambili anali kukangiwa kudziletsa. Kodi iye anali kumvela bwanji? Iye anakamba kuti: “N’nali kudziona monga munthu wacabe-cabe, koma nikapempha Yehova kuti anikhululukile, anali kunithandiza.” Kodi Yehova anali kumuthandiza bwanji? Akulu a mumpingo wake anamuuza kuti aziwatumila foni ngati wabwelezanso kucita zimenezi. Takuya anakamba kuti: “N’nali kucita mantha ndi manyazi nikafuna kuwatumila foni, koma nikawatumila, n’nali kulimbikitsidwa.” Ndiyeno akulu anakonza zakuti woyang’anila dela akamuyendele. Woyang’anila delayo anamuuza kuti: “Sizinacitike mwangozi kuti nibwele kuno. Nabwela kuno cifukwa akulu akonza zimenezi. Iwo asankha iwe kuti nikuyendele.” Takuya anati: “Ndine n’nali wocimwa, koma Yehova kupitila mwa akulu, anacitapo kanthu kuti anithandize.” Takuya anapita patsogolo cakuti anakhala mpainiya wa nthawi zonse, ndipo tsopano akutumikila pa ofesi ya nthambi. Mofanana ndi m’bale ameneyu, nanunso Mulungu adzakulimbitsani mukafooka.

KUDELA NKHAWA ZA MMENE TINGAPEZELE ZINTHU ZOFUNIKILA MU UMOYO

Anthu ambili amakhala na nkhawa cifukwa cosoŵa nchito. Ena amacotsedwa nchito ndipo amasoŵa njila ina yopezela ndalama. Kodi mungamvele bwanji ngati anthu akana kukulembani nchito? Anthu ena akakumana ndi vuto lotelo amayamba kudziona ngati acabe-cabe. Kodi Yehova angakuthandizeni bwanji? Sikuti angakupatseni nchito ya ndalama zambili. Koma angakuthandizeni mwa kukukumbutsani mau a Mfumu Davide akuti: “Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha cakudya.” (Sal. 37:25) Dziŵani kuti Yehova amaona kuti ndinu wamtengo wapatali, ndipo ndi ‘dzanja lake lamanja lacilungamo,’ adzakuthandizani kupeza zonse zofunikila kuti mupitilize kum’tumikila.

Kodi Yehova angakuthandizeni bwanji ngati mwacotsedwa nchito?

Sara, amene amakhala ku Colombia, anaona mmene Yehova amathandizila. Iye anali kuseŵenza pa kampani inayake yapamwamba, ndipo anali kulandila ndalama zambili. Koma nchitoyo siinali kumupatsa mpata wocita zinthu zina. Popeza kuti anali kufuna kucita zambili potumikila Yehova, analeka nchitoyo ndi kuyamba upainiya. Komabe, sanakwanitse kupeza nchito ya maola ocepa imene anali kufuna. Cotelo anapanga shopu yogulitsa aisi kilimu, koma ndalama zitamuthela anangotseka shopuyo. Sara anakamba kuti: “Panapita zaka zitatu nikukhala movutika, koma cifukwa ca thandizo la Yehova, n’nakwanitsa kupilila.” Iye anaphunzila kusiyanitsa zinthu zofunika kwambili ndi zosafunika kwenikweni. Anaphunzilanso kuti sayenela kudela nkhawa kwambili za tsiku lotsatila. (Mat. 6:33, 34) Patapita nthawi, bwana wake wakale anamuitana ndi kumupempha kuti ayambenso kugwila nchito imene anali kugwila poyamba. Iye anakamba kuti angalole kuseŵenza ngati adzayamba kugwila nchito maola ocepa ndiponso ngati adzayamba kumupatsa mpata wocita zinthu za kuuzimu. Ngakhale kuti Sara sapeza ndalama zambili ngati mmene anali kucitila kale, iye tsopano akwanitsa kucita upainiya. Pa zonse zimene zinamucitikila, iye anakamba kuti, “N’naona dzanja lacikondi la Yehova.”

NKHAWA CIFUKWA CA UKALAMBA

Cinthu cina cimene cimadetsa nkhawa anthu ambili ni ukalamba. Ambili amadela nkhawa kuti akadzafika pa zaka zopumula panchito sadzakwanitsa kupeza ndalama zokwanila zogulila zinthu zimene amafuna. Amadelanso nkhawa cifukwa ca mavuto amene amabwela ndi ukalamba. Davide anacondelela Yehova kuti: “Musanditaye nthawi ya ukalamba wanga. Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zikutha.”—Sal. 71:9, 18.

Nanga n’ciani cingathandize atumiki a Yehova kukhala opanda nkhawa pamene akukalamba? Afunika kupitiliza kulimbitsa cikhulupililo cawo mwa Mulungu ndi kumudalila kuti adzawasamalila. Acikulile ena anali ndi umoyo wa wofuwofu akalibe kukalamba, ndipo angafunike kusintha kuti akhale ndi umoyo wosalila zambili ndi kukhutila ndi zocepa zimene ali nazo. Iwo angamvetsetse mfundo yakuti kudya “zamasamba” kungakhale kosangalatsa ndiponso kopatsa thanzi kuposa kudya “nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino.” (Miy. 15:17) Ngati muika maganizo anu onse pa kucita cifunilo ca Yehova, iye adzakusamalilani panthawi ya ukalamba.

José na Rose ali pamodzi ndi Tony na Wendy

Ganizilani citsanzo ca José ndi Rose amene anatumikila Yehova mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 65. Zaka zambili zapitazo, iwo anali kusamalila atate ake Rose, amene anali kufunika kuwasamalila tsiku lonse. Kuwonjezela apo, José anali kuvutika ndi opaleshoni ya khansa ndiponso mankhwala a mphamvu amene anali kumwa. Koma Yehova anatambasula dzanja lake ndi kuthandiza banja lokhulupilika limeneli. Anacita zimenezi kupitila mwa Tony ndi mkazi wake Wendy, amene ali nawo mumpingo umodzi. Iwo anawapatsako nyumba yoti azikhalamo. Kuyambila kale, Tony ndi Wendy anali okonzeka kupeleka nyumbayi kwa apainiya aliwonse amene ali mu utumiki wa nthawi zonse. Zaka zambili m’mbuyomo, Tony akayang’ana pa windo ali ku sukulu, anali kuona José ndi Rose ayenda mu ulaliki. Iye anali kuyamikila khama lawo. Ndipo zimenezi zinamuthandiza kwambili cakuti anayamba kuwakonda. Ataganizila kuti banja lacikulile limeneli linatumikila Yehova mokhulupilika kwa umoyo wawo wonse, anadzipeleka kuti aziwasunga. Kwa zaka 15 tsopano, iwo akhala akuthandiza José ndi Rose amene ali ndi zaka za m’ma 80. Acikulile amenewa amaona kuti thandizo limene Tony ndi Wendy amapeleka ni mphatso yocokela kwa Yehova.

Mulungu amatambasula ‘dzanja lake lamanja lacilungamo’ kwa inu. Kodi inu mudzavomela mwa kutambasula dzanja lanu kwa Mulungu amene akulonjezani kuti: “Usachite mantha. Ndikuthandiza”?

^ par. 11 Maina ena asinthidwa.