Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kulimbana ndi Zimene Zingakulepheretseni Kupeza Madalitso

Pitirizani Kulimbana ndi Zimene Zingakulepheretseni Kupeza Madalitso

“Walimbana ndi Mulungu ndi anthu, ndipo potsirizira pake wapambana.”—GEN. 32:28.

NYIMBO: 60, 38

1, 2. Kodi atumiki a Yehova amalimbana ndi zinthu ziti?

KUNGOYAMBIRA nthawi ya Abele, atumiki okhulupirika a Mulungu akhala akulimbana ndi mavuto ambiri. Mtumwi Paulo analembera Akhristu achiheberi kuti iwo anapirira “mayesero aakulu ndi masautso” n’cholinga choti asangalatse Yehova komanso apeze madalitso. (Aheb. 10:32-34) Paulo anayerekezera moyo wa Akhristu ndi mipikisano imene Agiriki ankachita monga kuthamanga, masewera ogwetserana pansi komanso nkhonya. (Aheb. 12:1, 4) Pa mpikisano wathu wokapeza moyo wosatha, timakumana ndi adani amene angafune kutisokoneza, kutigwetsa, kutipitirira, kutikhumudwitsa komanso kutilepheretsa kukapeza mphoto.

2 Choyamba, timalimbana ndi Satana komanso dziko lake loipali. (Aef. 6:12) Tiyenera kuyesetsa kulimbana ndi “zinthu zozikika molimba” za m’dzikoli. Zinthu zake ndi monga ziphunzitso zabodza, nzeru za anthu, chiwerewere, kusuta, kuledzera ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza ubongo. Tiyeneranso kulimbana ndi zinthu zimene timalakwitsa ndiponso zimene zimatifooketsa.—2 Akor. 10:3-6; Akol. 3:5-9.

3. Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji kuti tizitha kulimbana ndi adani athu?

3 Koma kodi n’zotheka kulimbana ndi zinthu zonsezi n’kupambana? Inde, koma si zophweka. Pa nkhani imeneyi, Paulo anadziyerekezera ndi womenya nkhonya ndipo anati: “Mmene ndikuponyera nkhonya zanga, sikuti ndikungomenya mphepo ayi.” (1 Akor. 9:26) Mofanana ndi munthu wankhonya, tiyenera kudziteteza kuti adani athu asatipweteke. Yehova amatiphunzitsa komanso kutithandiza kuti timenye bwino nkhondoyi. Iye amagwiritsa ntchito Baibulo potipatsa malangizo othandiza kuti tidzapeze moyo. Malangizo ena timawapeza m’mabuku athu komanso kumisonkhano yampingo, yadera ndi yachigawo. Kodi inuyo mumayesetsa kutsatira zimene mumaphunzira? Ngati simutsatira ndiye kuti ‘mukungomenya mphepo’ ndipo simungathe kugonjetsa adani anu.

4. Kodi tingatani kuti tisagonjetsedwe ndi choipa?

4 Adani athu akhoza kutiukira pa nthawi imene sitikuyembekezera kapena pamene tafooka kwambiri. Choncho tiyenera kukhala maso nthawi zonse. Paja Baibulo limati: “Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:21) Mawu akuti “musalole kuti choipa chikugonjetseni” akusonyeza kuti tikhoza kugonjetsa zoipazo. Chongofunika ndi khama basi. Koma ngati sitili maso kapena tasiya kuchita khama, tikhoza kugonjetsedwa ndi Satana, dziko loipali komanso thupi lathu lochimwali. Tisalole kuti Satana atiopseze mpaka kufika posiya kumenya nkhondoyi.—1 Pet. 5:9.

5. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisagonje polimbana ndi zimene zingatilepheretse kupeza madalitso? (b) Kodi tikambirana za anthu ati?

5 Kuti munthu apambane pa mpikisano ayenera kudziwa cholinga chake. Kuti ifenso tisangalatse Yehova n’kudalitsidwa, tiyenera kukumbukira nthawi zonse mawu a pa Aheberi 11:6 akuti: “Aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “omufunafuna ndi mtima wonse” amasonyeza kuti pamafunika khama kwambiri. (Mac. 15:17) M’Baibulo muli zitsanzo za anthu amene anachita khama kuti adalitsidwe. Mwachitsanzo, Yakobo, Rakele, Yosefe ndi Paulo anakumana ndi mavuto aakulu koma anachitabe khama ndipo anadalitsidwa. Kodi ifeyo tingawatsanzire bwanji?

PAMAFUNIKA KHAMA KOMANSO KUPIRIRA KUTI MUNTHU ADALITSIDWE

6. Kodi n’chiyani chinathandiza Yakobo kuti asafooke, ndipo anapeza madalitso otani? (Onani chithunzi patsamba 8.)

6 Yakobo anachita khama komanso anapirira chifukwa ankakonda Yehova ndiponso zinthu zauzimu. Ankakhulupiriranso kwambiri lonjezo limene Mulungu anamupatsa loti adzadalitsa ana ake. (Gen. 28:3, 4) Iye ali ndi zaka pafupifupi 100 anachita zonse zimene akanatha kuti Mulungu amudalitse. Pa nthawi ina mpaka analimbana ndi mngelo. (Werengani Genesis 32:24-28.) N’zoona kuti Yakobo sanachite zimenezi ndi mphamvu zake zokha. Komabe iye anali wakhama ndipo sankafuna kuti chilichonse chimulepheretse kupeza madalitso ndipo anapezadi madalitsowo. Anapatsidwa dzina lomuyenerera lakuti Isiraeli, (kutanthauza “Mulungu Walimbana Naye,” kapena “Walimbana ndi Mulungu”). Zimene anachitazi zinachititsanso kuti Yehova azisangalala naye. Ifenso tizichita zonse zimene tingathe kuti Yehova asangalale nafe komanso atidalitse.

7. (a) Kodi Rakele anali ndi vuto lotani? (b) Kodi iye anatani ndi vuto lakeli?

7 Rakele yemwe anali mkazi wa Yakobo, ankafunitsitsa kuona mmene Yehova adzakwaniritsire zimene analonjeza kwa mwamuna wake. Koma panali vuto lina lalikulu. Iye analibe ana. Pa nthawiyo, kukhala opanda mwana kunali kowawa kwambiri. Ndipotu palibe chimene Rakele akanachita kuti athetse vuto lakeli. Kodi iye anapeza bwanji mphamvu kuti apitirize kupirira? Rakele sanataye mtima m’malomwake anapitirizabe kupemphera mochokera pansi pa mtima. Yehova anayankha mapemphero akewo ndipo anamudalitsa pomupatsa ana. Mpake kuti nthawi ina Rakele ananena mosangalala kuti: “Ndalimbana mwamphamvu . . . ndipo ndapambananso.”—Gen. 30:8, 20-24.

8. Kodi Yosefe anakumana ndi mavuto otani, nanga tingaphunzire chiyani pa zimene anachita?

8 Chitsanzo cha Yakobo ndi Rakele chinathandiza mwana wawo Yosefe kuti nayenso athe kupirira mayesero. Pamene Yosefe anali ndi zaka 17, anakumana ndi mavuto oposa msinkhu wake. Abale ake ankamuchitira nsanje mpaka anamugulitsa kuti akakhale kapolo ku Iguputo. Ali kumeneko, anaimbidwa mlandu wabodza ndipo anatsekeredwa m’ndende. (Gen. 37:23-28; 39:7-9, 20, 21) Koma iye sanataye mtima kapena kusungira chakukhosi abale akewo. M’malomwake ankaganizira kwambiri za ubwenzi wake ndi Yehova. (Lev. 19:18; Aroma 12:17-21) Chitsanzo cha Yosefe chingatithandizenso ifeyo. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti tinakula movutika kapena panopa tikukumana ndi mavuto enaake. Komabe tiyenera kupitiriza kulimbana ndi mavuto athuwo. Tizikhulupirira kuti tikachita zimenezi, Yehova adzatidalitsa.—Werengani Genesis 39:21-23.

9. Mofanana ndi Yakobo, Rakele ndi Yosefe, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzapeze madalitso amene Yehova walonjeza?

9 Kodi nanunso mukukumana ndi vuto linalake? Mwina anthu ena akukuchitirani zinthu zopanda chilungamo, kukusalani kapena kukunyozani. Mwinanso munthu wina anakunamizirani zinazake chifukwa cha nsanje. M’malo mofooka, mungachite bwino kuganizira zimene zinathandiza Yakobo, Rakele ndi Yosefe kuti apitirizebe kutumikira Yehova mosangalala. Mulungu anawathandiza komanso kuwadalitsa chifukwa ankakonda zinthu zauzimu. Iwo sanafooke ndipo ankachita zinthu mogwirizana ndi mapemphero awo. Popeza tili kumapeto kwenikweni kwa dziko loipali, tiyenera kuyesetsa kuti tisafooke n’cholinga choti tidzapeze madalitso amene Mulungu walonjeza. Kodi inuyo mukuyesetsa kuti Mulungu azisangalala nanu? Nanga mukuyesetsa kulimbana ndi zinthu zimene zingakulepheretseni kudzapeza madalitso?

YESETSANI NDI MTIMA WONSE KUTI MUPEZE MADALITSO

10, 11. (a) Kodi tingafunike kulimbananso ndi zinthu ziti kuti Mulungu atidalitse? (b) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisankha bwino zinthu komanso tisafooke tikakumana ndi mavuto?

10 Kodi tingafunike kulimbananso ndi zinthu ziti kuti Mulungu atidalitse? Akhristu ambiri akuyesetsa kuti athane ndi zinthu zimene amalakwitsa. Ena akuyesetsa kuti azikondabe ntchito yolalikira. Ndiye palinso ena amene akuvutika chifukwa cha matenda kapena kusowa wocheza naye. Enanso zikuwavuta kukhululukira munthu amene anawakhumudwitsa kapena kuwalakwira. Kaya tinabatizidwa liti, tonsefe tiyenera kulimbana ndi zimene zingatilepheretse kutumikira bwino Yehova. Tisamaiwale kuti iye amadalitsa anthu okhulupirika.

Kodi Mukuyesetsa Kulimbana ndi Zinthu Zimene Zingakulepheretseni Kupeza Madalitso? (Onani tsamba 10 ndi 11)

11 Nthawi zina zimakhala zovuta kusankha bwino zinthu komanso kuchita zoyenera, makamaka ngati mtima wathu ukutinyenga kuti tichite zoipa. (Yer. 17:9) Ngati mwazindikira kuti pali mbali ina imene simukuchita bwino, pemphani Yehova kuti akupatseni mzimu woyera. Pemphero ndiponso mzimu woyera zingakuthandizeni kuti muchite zoyenera komanso kuti Yehova akudalitseni. Muyeneranso kuchita mogwirizana ndi mapemphero anu. Muziwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso muzipeza nthawi yophunzira panokha ndiponso kuchita Kulambira kwa Pabanja.—Werengani Salimo 119:32.

12, 13. Kodi Akhristu awiri anathandizidwa bwanji kuti asiye kulakalaka zoipa?

12 Pali abale ndi alongo ambiri amene athandizidwa ndi Mawu a Mulungu, mzimu woyera komanso mabuku athu kuti asinthe zinthu zimene ankalakwitsa. Mwachitsanzo, mnyamata wina wazaka 17 anawerenga nkhani yakuti, “Kodi Mungalimbane Bwanji ndi Zilakolako Zoipa?” mu Galamukani! ya December 8, 2003. Iye anati: “Panopa ndikulimbana ndi maganizo olakwika. Magaziniyi inanena kuti ‘kwa anthu ambiri, nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa ndi yaikulu.’ Zimenezi zinandilimbikitsa chifukwa ndinazindikira kuti sindili ndekha.” Nkhani ina imene inamuthandiza ndi yakuti, “Kodi Mulungu Amavomereza Makhalidwe a Kugonana Kwachilendo?” yomwe inatuluka mu Galamukani! ya October 8, 2003. Anawerenga kuti kwa anthu ena nkhondoyi ili ngati “munga m’thupi.” (2 Akor. 12:7) Ngakhale kuti si zapafupi kuti anthuwa akhalebe ndi makhalidwe abwino, mtima wawo umakhala m’malo akaganizira za m’tsogolo. Mnyamata uja anati: “Mfundo imeneyi imandilimbikitsa kuti ndiziyesetsa kukhala wokhulupirika tsiku lililonse. Ndimayamikira Yehova chifukwa choti amagwiritsa ntchito gulu lake potithandiza kuti tikhalebe okhulupirika m’dziko loipali.”

13 Chitsanzo china ndi cha mtsikana wina wa ku United States. Iye analemba kuti: “Ndikukuthokozani kuti mumatipatsa chakudya choyenera, pa nthawi yoyeneranso. Ndikawerenga nkhani zina ndimangomva ngati alembera ineyo. Kwa zaka zambiri ndinkalimbana ndi mtima wolakalaka zinthu zimene Yehova amadana nazo. Ndinangotsala pang’ono kugonja. Ndinkadziwa kuti Yehova ndi wachifundo komanso amakhululuka. Koma ndinkaona kuti sangandithandize chifukwa choti pansi pa mtima wanga sindinkadana ndi zoipazo. Vuto limeneli linkandisowetsa mtendere kwambiri. . . . Koma nditawerenga nkhani yakuti, ‘Kodi Muli Ndi “Mtima Wodziwa” Yehova?’ mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2013, ndinazindikira kuti Yehova akufunitsitsa kundithandiza.”

14. (a) Kodi Paulo ankamva bwanji akaganizira zimene ankalakwitsa? (b) Kodi tingatani kuti tipambane pa nkhondo yolimbana ndi zimene timalakwitsa?

14 Werengani Aroma 7:21-25. Paulo ankadziwa bwino kuti kulimbana ndi zimene timalakwitsa si nkhani yamasewera chifukwa nayenso ankavutika. Koma iye ankakhulupirira kuti akhoza kupambana pa nkhondoyo ngati angadalire Yehova komanso kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. Ifenso tikhoza kupambana pa nkhondo imeneyi. Chofunika ndi kutsanzira Paulo basi. Tizidaliranso kwambiri Yehova osati mphamvu zathu ndipo tizikhulupirira kwambiri dipo.

15. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kukhalabe okhulupirika tikakumana ndi mavuto?

15 Koma nthawi zina Yehova amafuna kuti tisonyeze kuti timamudaliradi. Tiyerekeze kuti inuyo kapena munthu wina wa m’banja lanu akudwala kapenanso wachitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Kodi mungatani? Kodi mudzasonyeza kuti mumadalira Yehova popemphera mochonderera kuti akupatseni mphamvu n’cholinga choti mukhalebe okhulupirika, osangalala komanso olimba mwauzimu? (Afil. 4:13) Zitsanzo zakale komanso za masiku ano zikusonyeza kuti pemphero lingatithandize kupezanso mphamvu n’kumapirirabe mavuto athu.

PITIRIZANI KULIMBANA NDI ZIMENE ZINGAKULEPHERETSENI KUPEZA MADALITSO

16, 17. Kodi inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani pa nkhondo imene tili nayo?

16 Satana angasangalale kwambiri ngati mutagwa ulesi n’kusiya kulimbana ndi zinthu zimene zingakulepheretseni kupeza madalitso. Koma chitani zonse zimene mungathe kuti mugwire “mwamphamvu chimene chili chabwino.” (1 Ates. 5:21) Dziwani kuti mukhoza kupambana pa nkhondo yolimbana ndi Satana, dziko loipali komanso zimene mumalakwitsa. Chofunika ndi kudalira kwambiri Yehova kuti azitipatsa mphamvu.—2 Akor. 4:7-9; Agal. 6:9.

17 Choncho pitirizani kumenya nkhondo yolimbana ndi zinthu zimene zingakusokonezeni. Musagwe ulesi ndipo musafooke. Dziwani kuti mukamachita zimenezi, Yehova ‘adzakukhuthulirani madalitso oti mudzasowa powalandirira.’—Mal. 3:10.