Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?

Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?

“Citani zonse ku ulemelelo wa Mulungu.”—1 AKOR. 10:31.

NYIMBO: 34, 61

1, 2. N’cifukwa ciani Mboni za Yehova zimayesetsa kuvala moyenelela? (Onani cithunzi pamwambapa.)

POKAMBA za mmene azibusa a machalichi amavalila pa misonkhano yawo, nyuzipepa ina ya ku Netherlands inati: “Amavala motailila maka-maka kukakhala kotentha.” Koma inapitiliza kunena kuti, “Mboni za Yehova sizivala conco. . . . Amuna acikulile ndi acicepele amavala matayi ndi majekete. Azimayi ndi atsikana amavala masiketi aatali bwino . . . oyenelela koma amakono.” Kukamba zoona, anthu amayamikila a Mboni za Yehova cifukwa ‘amadzikongoletsa ndi zovala zoyenela, povala mwaulemu ndi mwanzelu . . . mogwilizana ndi mmene akazi amene amati amalemekeza Mulungu amayenela kudzikongoletsela.’ (1 Tim. 2:9, 10) Apa mtumwi Paulo anali kukamba za akazi. Koma mfundo yake imagwilanso nchito kwa amuna acikhiristu.

2 Atumiki a Yehova afunika kuvala moyenelela. Ndipo nkhani imeneyi, ni yofunika kwambili kwa Mulungu amene timam’lambila. (Gen. 3:21) Zimene Malemba amakamba pa nkhani ya mavalidwe ndi kudzikonza, zimatithandiza kudziŵa bwino kuti Wolamulila wa cilengedwe conse ali na mfundo zabwino zimene afuna kuti olambila ake oona azitsatila. Pa cifukwa cimeneci, kudzikonza kwathu ndi zovala zimene timasankha, siziyenela kukondweletsa ife cabe. Ziyenelanso kulemekeza Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova.

3. Tiphunzilapo ciani pa malamulo amene Mulungu anapatsa Aisiraeli pa nkhani ya mavalidwe?

3 Mwacitsanzo, m’Cilamulo cimene Mulungu anapatsa Aisiraeli munali malamulo amene anali kuwateteza ku makhalidwe otayilila a mitundu yowazungulila. Cilamulo cimeneco cinaonetsa mmene Yehova amaonela mavalidwe amene sasiyanitsa amuna ndi akazi. Mavalidwe amenewo afala kwambili masiku ano. (Ŵelengani Deuteronomo 22:5.) Malamulo a Mulungu pa nkhani ya mavalidwe amationetsa kuti iye amadana ndi masitayelo opangitsa amuna kuoneka monga akazi, akazi kuoneka monga amuna, kapena amene amasokoneza kuti ni mwamuna kapena mkazi.

4. N’ciani cimene cingathandize Akhiristu kusankha bwino zovala?

4 Mau a Mulungu ali na mfundo zimene zimathandiza Akhiristu kusankha bwino mavalidwe. Tonse tifunika kutsatila mfundozi mosasamala kanthu za nyengo, cikhalidwe, kapena dela limene tikhalako. Safunika kucita kutichulila kuti kavalidwe aka ndiye koyenela, aka n’kosayenela iyai. Mfundo za m’Baibulo n’zimene ziyenela kutithandiza kusankha bwino mavalidwe. Lomba tiyeni tikambilane mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kucita “cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo,” posankha zovala.—Aroma 12:1, 2.

“TIKUSONYEZA . . . KUTI NDIFE ATUMIKI A MULUNGU”

5, 6. Kodi timafuna kuti athu aziganiza ciani akaona mavalidwe athu?

5 Mulungu anauzila mtumwi Paulo kugogomeza mfundo yofunika kwambili imene ipezeka pa 2 Akorinto 6:4. (Ŵelengani.) Maonekedwe athu amakamba zambili za ife. Mmene anthu amatiganizila zimadalila zimene ‘aona ndi maso’ awo. (1 Sam. 16:7) Monga atumiki a Mulungu, sitifunika kungovala ciliconse cimene takonda. Mfundo za m’Mau a Mulungu zimatilimbikitsa kupewa kuvala zothina, zoonetsa thupi, kapena zoutsa cilakolako. Munthu safunika kucita kumangika kapena kuyang’ana kumbali cifukwa ca mmene tavalila.

6 Ngati tivala mwaudongo, mwaukhondo, mwaulemu, ndi kudzikonza bwino, anthu adzatilemekeza monga atumiki a Yehova. Tikatelo, anthu adzafuna kudziŵa zambili za Mulungu amene timalambila. Komanso, mavalidwe athu abwino adzapeleka cithunzi cabwino ca gulu lathu. Mwa ici, anthu angafune kumvetsela uthenga wopatsa moyo umene tili nawo.

7, 8. Ni pa nthawi iti maka-maka pamene tifunika kuvala moyenelela?

7 Tifunika kuvala zovala zimene zingalemekeze Mulungu wathu woyela, komanso abale na alongo athu. Zovala zathu ziyenelanso kulemekeza uthenga umene timalalikila, ndi kupeleka ulemelelo kwa Yehova. (Aroma 13:8-10) Tizivala bwino maka-maka pamene ticita zinthu zauzimu monga kusonkhana ndi kulalikila. Mavalidwe athu azigwilizana ndi “mmene [anthu] amene amati amalemekeza Mulungu amayenela kudzikongoletsela.” (1 Tim. 2:10) Komabe, mavalidwe amene angakhale oyenela kwina angakhale osayenela kumalo ena. Conco, anthu a Yehova padziko lonse lapansi amavala mogwilizana ndi kumene amakhala kuti asakhumudwitse ena.

Kodi mavalidwe anu amalemekeza Mulungu amene timaimila? (Onani ndime 7, 8)

8 Ŵelengani 1 Akorinto 10:31. Panthawi ya misonkhano ya dela ndi ya cigawo, mavalidwe athu ayenela kukhala abwino ndi aulemu. Tisatengele mavalidwe otayilila ndi ofala a ku dziko, ngakhale pofika pa hotela kapena pocoka. Tizivalanso bwino pamaceza mapulogilamu a msonkhano wa cigawo akalibe kuyamba ndi pambuyo pake. Tikatelo, anthu adzatidziŵa msanga kuti ndife Mboni za Yehova. Inde, tidzakhalanso omasuka kulalikila tikapeza mpata.

9, 10. Kodi Afilipi 2:4 ingatithandize bwanji pankhani ya mavalidwe?

9 Ŵelengani Afilipi 2:4. N’cifukwa ciani Akhiristu ayenela kuganizila mmene mavalidwe awo angakhudzile olambila anzawo? Cifukwa cimodzi n’cakuti anthu a Mulungu amayesetsa kusunga lamulo la m’Baibulo lakuti: “Cititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, cilakolako ca kugonana.” (Akol. 3:2, 5) Tisapangitse kuti cikhale covuta kwa Akhiristu anzathu kutsatila uphungu umenewu, makamaka ena amene kale anali ndi khalidwe lacisembwele. (1 Akor. 6:9, 10) Tisawonjezele mayeselo kwa iwo.

10 Tikakhala pakati pa abale ndi alongo athu auzimu, mavalidwe athu afunika kuonetsa kuti mumpingo muli anthu a makhalidwe abwino. Tifunika kuvala bwino, kaya tili pa msonkhano kapena poceza cabe. N’zoona kuti tili na ufulu wosankha zimene tifuna kuvala. Komabe, tonse tifunika kuvala zovala zimene zingathandize ena kusunga ciyelo cathu ca m’maganizo, m’mau, ndi m’zocita zathu. (1 Pet. 1:15, 16) Cikondi ceni-ceni “sicicita zosayenela, sicisamala zofuna zake zokha.”—1 Akor. 13:4, 5.

KUVALA MOGWILIZANA NDI NTHAWI NDI MALO

11, 12. Tiyenela kuganizila ciani posankha zimene tifuna kuvala?

11 Posankha zovala, atumiki a Mulungu amazindikila mfundo yakuti pali “nthawi yocitila cinthu ciliconse ndiponso yokhudza nchito iliyonse.” (Mlal. 3:1, 17) N’zomveka kuti tiyenela kuvala mogwilizana ndi nyengo. Mmene zinthu zilili paumoyo wathu zikhoza kukhudzanso mavalidwe athu. Ngakhale n’conco, mfundo za Mulungu sizisintha.—Mal. 3:6.

12 N’zoona kuti m’nyengo yotentha kungakhale kovutilapo kuvala zovala zina zaulemu. Komabe, abale na alongo athu amayamikila ngati tipewa kuvala zovala zothina, zotayilila kapena zoonetsa thupi. (Yobu 31:1) Ngakhale pamene tikupumula kapena kusangalala kumbali kwa nyanja, kapena ponyaya mu swiming’ipuu, zovala zathu zonyaila ziyenela kukhala zaulemu. (Miy. 11:2, 20) Anthu ambili amavala zovala zosambila zoonetsa thupi, koma ife amene titumikila Yehova timaganizila zimene zingalemekeze Mulungu wathu woyela amene timakonda.

13. N’cifukwa ciani tiyenela kutsatila malangizo a pa 1 Akorinto 10:32, 33 pa nkhani ya mavalidwe?

13 Palinso mfundo ina yofunika kwambili imene ingatithandize kusankha zovala zoyenela—kuganizila cikumbumtima ca ena, kaya ca alambili anzathu kapena iyai. (Ŵelengani 1 Akorinto 10:32, 33.) Tifunika kupewelatu zovala zimene zingakhumudwitse ena. Paulo analemba kuti: “Aliyense wa ife azikondweletsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa.” Anatinso: “Pakuti ngakhale Khiristu sanadzikondweletse yekha.” (Aroma 15:2, 3) Yesu anaika zofuna za ena patsogolo, ndipo anali kukonda ngako kuthandiza anthu pocita cifunilo ca Mulungu. Conco, tizipewa zovala zimene zingatseke matu a anthu amene tifuna kuwalalikila.

14. Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kusankha zovala zolemekezanso Mulungu?

14 Makolo acikhiristu ali na udindo wophunzitsa ana awo kutsatila mfundo za m’Baibulo. Izi ziphatikizapo kuwaphunzitsa mavalidwe okondweletsa Mulungu. (Miy. 22:6; 27:11) Makolo angakhomeleze mfundo zabwino za Mulungu wathu woyela mwa ana awo. Angacite zimenezi mwa kukhala citsanzo cabwino kwa iwo ndi kuwalangiza mwacikondi. Ayenelanso kuthandiza ana awo kudziŵa kumene angakagule zabwino. N’zoona kuti ayenela kugula zovala zimene akonda, koma zikhalenso zoti akavala azimila bwino Yehova Mulungu.

MUZISANKHA MWANZELU

15. N’ciani cingatithandize kusankha bwino zovala?

15 Mau a Mulungu ali na malangizo otithandiza kupanga zosankha zolemekeza Mulungu. N’zoona kuti aliyense amafuna kugula zovala za kumtima kwake malinga ndi thumba lake. Komabe, zovala zathu ziyenela kukhala zooneka bwino, zoyela, zaulemu, zogwilizana ndi cocitikaco, ndi zovomelezeka kumaloko.

16. N’cifukwa ciani tifunika kuvala moyenelela?

16 Kukamba zoona, nthawi zina cimavuta kusankha zovala mogwilizana ndi mfundo za Mulungu. M’mashopu ambili amagulitsa zovala zamasitayelo amene afala. Conco, pangafunike nthawi ndi khama kufunafuna siketi yosathina, kapena dilesi, bulauzi, suti, kapena thilauzi. Tikapeza covala cabwino komanso coyenelela, Akhiristu anzathu adzayamikila kwambili, ndipo sitidzacita naco manyazi. Kuwonjezela apo, tidzakhala osangalala ndi okhutila kuti tikupeleka ulemelelo kwa Atate wathu wakumwamba.

17. N’ciani cingathandize m’bale kudziŵa ngati n’koyenela kuti azisunga ndevu kapena ayi?

17 Nanga bwanji za nkhani yosunga ndevu kwa abale? Cilamulo ca Mose cinalamula amuna kusunga ndevu. Ngakhale n’conco, Akhiristu sali pansi pa cilamulo ca Mose ndipo safunikila kucisunga. (Lev. 19:27; 21:5; Agal. 3:24, 25) M’zikhalidwe zina, kusunga ndevu zodulila bwino-bwino n’kololeka, ndipo kumapeleka ulemu. Komanso, sikulepheletsa anthu kumvela uthenga wa Ufumu. Ndipo abale ena a maudindo amasunga ndevu. Ngakhale n’conco, abale ena amasankhabe kucotselatu ndevu zonse. (1 Akor. 8:9, 13; 10:32) Kumaiko ena, kusunga ndevu si kofala ndipo si kololeka kwa Mkhiristu. Ndiponso kungakhale cifukwa comunenezela. Mwa ici, angalephele kupeleka ulemelelo kwa Mulungu.—Aroma 15:1-3; 1 Tim. 3:2, 7.

18, 19. Kodi lemba la Mika 6:8 lingatithandize bwanji kuti mavalidwe athu akhale olemekeza Mulungu?

18 Ndife oyamikila kuti Yehova sanatiikile malamulo ambili-mbili pa nkhani ya mavalidwe ndi kudzikonza. M’malomwake, amatilola kusakha tokha mwanzelu zovala zogwilizana ndi mfundo za m’Malemba. Timafuna kuonetsa kuti ‘tikuyenda modzicepetsa ndi Mulungu wathu,’ mwa mavalidwe athu ndi mmene timadzikonzela.—Mika 6:8.

19 Munthu wodzicepetsa amadzipenda, kapena kudzisanthula, kuti aone ngati amacita zinthu mogwilizana ndi ciyezo ca Yehova. Zili conco cifukwa timadalila malangizo a Mulungu opindulitsa. Munthu wodzicepetsa amaganizilanso mmene zocita zake zingakhudzile anthu ena. ‘Timayenda modzicepetsa ndi Mulungu wathu’ mwa kuyesetsa kutsatila mfundo za Mulungu mu umoyo wathu ndi kupewa kukhumudwitsa ena.

20. Kodi mavalidwe athu na mmene timadzikonzela afunika kupangitsa anthu kutiona bwanji?

20 Zovala zathu siziyenela kupangitsa anthu kukaikila ngati ndife Mboni za Yehova. Abale ndi alongo athu, ngakhalenso anthu ena onse, afunika kuona kuti ndife oyeneleladi kuimila Mulungu wathu wolungama. Iye ali na malamulo abwino ndipo timayesetsa kuwatsatila. Timayamikila kwambili abale na alongo amene amacita khama kuvala bwino ndi kusunga makhalidwe abwino. Iwo amathandizila kuti anthu oona mtima alandile uthenga wa m’Baibulo. Izi zimapeleka ulemelelo kwa Yehova ndi kum’sangalatsa. Ndithudi, kuvala bwino ndi kudzikonza moyenelela kumalemekeza Mulungu, amene ‘amadziveka ulemu ndi ulemelelo.’—Sal. 104:1, 2.