Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Khalanibe Auzimu Potumikila Mumpingo wa Cinenelo Cina

Khalanibe Auzimu Potumikila Mumpingo wa Cinenelo Cina

“Ndasunga mosamala mau anu mumtima mwanga.”—SAL. 119:11.

NYIMBO: 142, 92

1-3. (a) Olo kuti zinthu zikhale bwanji, n’ciani cimene tiyenela kuikako nzelu? (b) Ni mavuto abwanji amene anthu ophunzila cinenelo catsopano amakumana nawo? Nanga izi zibweletsa mafunso yanji? (Onani pikica pamwamba.)

A MBONI za Yehova ambili masiku ano akulalikila mwacangu. Iwo akukwanilitsa ulosi wakuti uthenga wabwino udzalalikidwa “kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 14:6) Kodi ndinu mmodzi wa anthu amene akuphunzila cinenelo cina? Kodi mutumikila kosoŵa kapena monga mmishonale kudziko lina? Kapena kodi mwayamba kusonkhana mumpingo wa cinenelo cina?

2 Ife atumiki a Mulungu, tiyenela kuikako nzelu ku umoyo wathu wauzimu na wa banja lathu. (Mat. 5:3) N’zoona kuti nthawi zina, cingativute kucita phunzilo la umwini lopindulitsa cifukwa cotangwanika na zinthu zina. Koma amene atumikila ku gawo la cinenelo cina amakumana na mavuto ena.

3 Kuwonjezela pa kudziŵa cinenelo catsopano, amene atumikila ku gawo la cinenelo cina, afunika kuonetsetsa kuti akudya cakudya cotafuna ca kuuzimu. (1 Akor. 2:10) Koma kodi angacite bwanji zimenezi ngati samvetsetsa cinenelo cimene cikambidwa mumpingo mwawo? N’cifukwa ciani makolo acikhiristu ayenela kuonetsetsa kuti Mau a Mulungu akufika pamtima pa ana awo?

CIMENE CINGAIKE UMOYO WAUZIMU PACISWE

4. N’ciani cingaike umoyo wathu wauzimu paciswe? Pelekani citsanzo.

4 Ngati sitimvetsetsa Mau a Mulungu m’cinenelo cacilendo, umoyo wathu wa kuuzimu ungakhale paciswe. Mu 500 B.C.E., Nehemiya anada nkhawa atadziŵa kuti ana ena pakati pa Ayuda amene anabwelela ku Babulo, anali kukangiwa kukamba Ciheberi. (Ŵelengani Nehemiya 13:23, 24.) Ana amenewo anayamba kufooka mwauzimu cifukwa cosamvetsetsa bwino tanthauzo la Mau a Mulungu.—Neh. 8:2, 8.

5, 6. Kodi makolo amene atumikila mumpingo wa cinenelo cina azindikila ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

5 Makolo ena amene atumikila mumpingo wa cinenelo cina, azindikila kuti ana awo sakonda kwambili coonadi. Cifukwa cosamvetsetsa cinenelo, anawo sapindula ndi misonkhano. Pedro,  [1] wa ku South America, amene anasamukila ku Australia pamodzi na banja lake anati: “Ngati munthu aphunzila zinthu zauzimu, amafunika kukhudzidwa mtima.”—Luka 24:32.

6 Zimene tingaŵelenge m’cinenelo cacilendo, sizingatifike pamtima ngati mmene zingakhalile tikaŵelenga m’cinenelo cathu. Kuwonjezela apo, kulephela kukamba na ena m’cinenelo cacilendo kungativutitse maganizo ndi kutifoketsa mwauzimu. Conco, potumikila Yehova mumpingo wa cinenelo cina, tingacite bwino kuteteza umoyo wathu wauzimu.—Mat. 4:4.

ANATETEZA UMOYO WAWO WAUZIMU

7. Kodi Ababulo anayesa bwanji kusintha Danieli kuti agwilizane na cikhalidwe ndi cipembedzo cawo?

7 Pamene Daniel ndi anzake anatengedwa ukapolo, Ababulo anayesa kuwasintha kuti agwilizane na cikhalidwe cawo mwa kuwaphunzitsa “cinenelo ca Akasidi.” N’cifukwa cake, mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu, amene anali kuwaphunzitsa anawapatsa maina a Cibabulo. (Dan. 1:3-7) Daniel anapatsidwa dzina lakuti Belitesazara. Ili linali dzina la mulungu wamkulu wa Ababulo. Mwina Mfumu Nebukadinezara anafuna kupangitsa Danieli kuganiza kuti Mulungu wake Yehova amalamulidwa na mulungu wa Ababulo.—Dan. 4:8.

8. N’ciani cinathandiza Danieli kukhalabe wolimba mwauzimu pamene anali kukhala kudziko lacilendo?

8 Ngakhale kuti Danieli anapatsiwa cakudya ca mfumu, “anatsimikiza mumtima mwake kuti sadzidetsa.” (Dan. 1:8) Cifukwa cakuti anali ‘kuŵelenga mau a Yehova’ m’cinenelo cakwawo, Danieli anakhalabe wolimba mwauzimu pamene anali ku dziko lacilendo. (Dan. 9:2.) Ngakhale patapita zaka 70 ali ku Babulo, anali kudziŵikabe na dzina la Ciheberi.—Dan. 5:13.

9. Monga mmene Salimo 119 ionetsela, kodi Mau a Mulungu anam’thandiza bwanji wolemba salimo?

9 Mau a Mulungu anathandiza wolemba Salimo 119 kukhala wosiyana ndi ena. Anapilila zinthu zoipa zimene atumiki ena a m’bwalo la mfumu anali kumucitila. (Sal. 119:23, 61) Iye analola kuti Mau a Mulungu amufike pamtima.—Ŵelengani Salimo 119:11, 46.

KHALANIBE MUNTHU WAUZIMU

10, 11. (a) Tizikhala na colinga canji pophunzila Mau a Mulungu? (b) Zimenezi zingatheke bwanji? Pelekani citsanzo.

10 Olo kuti titangwanike na zinthu zauzimu kapena nchito yakuthupi, tifunika kupeza nthawi yocita phunzilo laumwini ndi kulambila kwa pabanja. (Aef. 5:15, 16) Komabe, sitifunika kucita zimenezi na colinga cofuna cabe kutsiliza buku kapena kupeza mayankho oyankha pamisonkhano. Tifunika kuonetsetsa kuti Mau a Mulungu atifika pamtima ndi kulimbitsa cikhulupililo cathu.

11 Kuti zimenezi zitheke, pophunzila sitifunika cabe kuganizila mmene mfundozo zikhudzila anthu ena, koma tiyenela kuganizilanso mmene zikhudzila ifeyo patekha. (Afil. 1:9, 10) Kumbukilani kuti nthawi zambili pokonzekela ulaliki, misonkhano kapena nkhani, sitingaganizile mmene mfundozo zikhudzila umoyo wathu. Mwacitsanzo: Ngakhale kuti wophika cakudya amalaŵa pophika, iye sangadalile cabe cakudya colaŵa kuti akhale na moyo. Kuti akhale wathanzi, afunika kudya cakudya copatsa thanzi. Nafenso tiyenela kuyesetsa kudyetsa mtima wathu cakudya cauzimu cogwilizana ndi zosoŵa zathu.

12, 13. N’cifukwa ciani amene atumikila mumpingo wa cinenelo cina amapindula ngati aphunzila Baibo m’cinenelo ca kwawo?

12 Ambili amene atumikila mumpingo wa cinenelo cina aona kuti kuphunzila Baibo nthawi zonse m’cinenelo “cimene anabadwa naco,” kumawapindulitsa. (Mac. 2:8.) Ngakhale amishonale amene atumikila m’dziko lina, amadziŵa kuti sangadalile cabe mfundo zing’ono-zing’ono zimene amamvelako pamisonkhano.

13 Alain amene wakhala akuphunzila Ciperisiya kwa zaka 8 anati: “Ngati nikonzekela misonkhano m’Ciperisiya nimangoika maganizo pa cinenelo. Popeza nimaika maganizo pa kudziŵa cinenelo, zimene nimaŵelenga sizinifika pamtima. Ndiye cifukwa cake nimapatula nthawi yophunzila Baibo ndi zofalitsa zina m’cinenelo ca kwathu.”

AFIKENI PAMTIMA ANA ANU

14. Kodi makolo ayenela kuonetsetsa ciani? Nanga cifukwa ciani?

14 Makolo Acikhiristu amacita bwino kuonetsetsa kuti Mau a Mulungu akufika pamtima pa ana awo. Pambuyo potumikila mumpingo wa cinenelo cina kwa zaka zitatu, Serge, na mkazi wake Muriel, anazindikila kuti mwana wawo wa zaka 17 sanali kukondwela na zinthu zauzimu. “Sanali kukondwela kulalikila m’cinenelo cina, koma kale anali kukondwela kulalikila m’cinenelo cathu Cifulenci,” anatelo Muriel. “Titaona kuti zimenezi zikupangitsa mwana wathu kusapita patsogolo kuuzimu, tinaganiza zobwelela kumpingo wakale,” anafotokoza conco Serge.

Muzionetsetsa kuti coonadi cikufika pamtima pa ana anu (Onani ndime 14, 15)

15. (a) N’zocitika ziti zimene zingacititse makolo kubwelela ku mpingo wa cinenelo cimene ana awo amamvetsetsa? (b) Ni malangizo ati opita kwa makolo amene ali pa Deuteronomo 6:5-7?

15 N’zocitika ziti zimene zingapangitse makolo kubwelela ku mpingo wa cinenelo cimene ana awo amamvetsetsa? Coyamba, ayenela kuona ngati angakwanitse kuphunzitsa ana awo kukonda Yehova panthawi imodzi-modzi kuwaphunzitsa cinenelo cina. Caciŵili, ngati aona kuti ana awo ayamba kuleka kukonda zinthu zauzimu kapena kulalikila m’gawo la cinenelo ca mpingo umene atumikilamo. Pa zifukwa zimenezi, makolo Acikhiristu angaganize zobwelela ku mpingo wa cinenelo cimene ana awo amamvetsetsa mpaka pamene anawo adzakonda kwambili coonadi.—Ŵelengani Deuteronomo 6:5-7.

16, 17. Kodi makolo ena amakwanitsa bwanji kuphunzitsa ana awo zauzimu mumpingo wa cinenelo cina?

16 Komabe, makolo ena apeza njila yophunzitsila ana m’cinenelo cawo uku asonkhana mumpingo kapena kagulu ka cinenelo cina. Charles, tate wa ana atatu a zaka za pakati pa 9 mpaka 13, amasonkhana ku kagulu kokamba Cilingala. Iye anafotokoza kuti: “Tinakonza zakuti tizikonzekela misonkhano na kucita kulambila kwa pabanja ndi ana athu m’cinenelo cathu. Koma timakonzekela ulaliki ndi kucita maseŵela ena m’Cilingala kuti ana athu aziphunzila cinenelo uku akusangalala.”

Yesetsani kudziŵa cinenelo ca kumaloko ndi kuyankhapo pamisonkhano (Onani ndime 16, 17)

17 Kevin, tate wa ana aŵili, wina wa zaka 5 ndi wa zaka 8, anapeza njila zina zothandizila ana ake kuti azipindula ngakhale kuti sanali kumvetsetsa pamisonkhano. Iye anati: “Ine na mkazi wanga timacita kulambila kwa pabanja pamodzi ndi ana athu m’Cifulenci. Tinapanganso zoti tizipezeka pa misonkhano ya Cifulenci kamodzi pa mwezi. Tikakhala pa holide timapezelapo mwayi wopita kumisonkhano yacigawo ya m’cinenelo cathu.”

18. (a) Ni mfundo iti ya pa Aroma 15:1, 2 imene ingakuthandizeni kudziŵa zimene zingathandize ana anu? (b) Ni malingalilo abwanji amene makolo ena apelekapo? (Onani zakumapeto.)

18 Komabe, banja lililonse lili na ufulu wodzisankhila lokha njila imene ingathandize ana awo kukhala olimba kuuzimu. [2] (Agal. 6:5) Muriel, amene tamuchula kuciyambi kwa nkhani ino, anavomeleza kuti analolela kucita zimene mwana wawo anali kufuna n’colinga cakuti iye apindule mwauzimu. (Ŵelengani Aroma 15:1, 2.) Pokumbukila zimene anasankha, Serge aona kuti anasankha mwanzelu. Anati: “Pamene tinabwelela ku mpingo wa Cifulenci, mwana wathu anapita patsogolo kuuzimu ndipo anabatizika. Apa, ni mpainiya wanthawi zonse ndipo aganizilanso zobwelela ku kagulu ka cinenelo cina.”

LOLANI MAU A MULUNGU KUKUFIKANI PAMTIMA

19, 20. Tingaonetse bwanji kuti timakonda Mau a Mulungu?

19 Cifukwa cotikonda, Yehova wacititsa kuti Mau ake Baibo, amasulidwe m’zinenelo zambili kuti ‘anthu kaya akhale a mtundu wotani, adziŵe coonadi molondola.’ (1 Tim. 2:4) Iye adziŵa kuti anthu amapindula ngako ngati aŵelenga Mau ake m’cinenelo cawo.

20 Conco, mulimonse mmene zingakhalile paumoyo, tifunika kuyesetsa kudyetsa mtima wathu cakudya cotafuna cauzimu. Kuphunzila Malemba nthawi zonse m’cinenelo cathu, kudzatithandiza kukhalabe auzimu pamodzi na banja lathu. Ndipo zimenezi zidzaonetsa kuti tikusunga mosamala Mau a Mulungu.—Sal. 119:11.

^ [1] (ndime 5) Maina tawasintha.

^ [2] (ndime 18) Pokambilana mfundo za m’Baibo zimene zingathandize banja lanu, ŵelengani nkhani yakuti “Kulera Ana M’dziko Lachilendo—Mavuto ndi Mphoto Zake” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2002.