Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ‘Mumasunga Nzeru Zopindulitsa’?

Kodi ‘Mumasunga Nzeru Zopindulitsa’?

NTHANO ina imati m’mudzi wina munali mnyamata wosauka. Ambiri ankaona kuti mnyamatayo saganiza bwino ndipo ankamuseka. Kukabwera alendo, anthu ankasewera naye n’cholinga choti azimuseka. Ankamuonetsa makobili awiri, ina yaikulu yasiliva, ina yaing’ono yagolide. Ndiyeno ankamuuza kuti: “Tengapo imene ukufuna.” Mnyamatayo ankangotolapo yaikuluyo n’kuthawa.

Tsiku lina mlendo wina anamufunsa kuti: “Kodi iwe sudziwa kuti ndalama ya golideyo yangoona kuchepa koma ndi imene ungakagulire zinthu zambiri?” Mnyamatayo anangomwetulira n’kunena kuti: “Ndikudziwa.” Ndiye mlendoyo anafunsa kuti: “Nanga bwanji umakonda kutenga yasiliva? Mmesa ya golide imodziyo ikufanana ndi zasiliva ziwiri?” Mnyamatayo anati: “Kodi ndikatenga ya golideyo anthu apitiriza kundipatsa ndalama? Mukudziwa ndalama zimene ndapeza chifukwa cha zimene ndimachitazi?” Apatu tingati mnyamatayu anasonyeza nzeru zopindulitsa ndipo ife tikhoza kuphunzirapo kanthu.

Baibulo limati: “Usunge nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino. Ukatero udzayenda panjira yako popanda chokuopseza, ndipo ngakhale phazi lako silidzapunthwa ndi chilichonse.” (Miy. 3:21, 23) Lembali likusonyeza kuti munthu akakhala ndi nzeru zopindulitsa n’kumadzigwiritsa ntchito, amakhala wotetezeka. Tinganene kuti iye sangapunthwe mwauzimu.

KODI NZERU ZOPINDULITSA N’CHIYANI?

Nzeru zopindulitsa n’zosiyana kwambiri ndi kudziwa kapena kumvetsa zinthu. Tikutero chifukwa choti munthu amene ali ndi nzeru samangotolera mfundo n’kuona kugwirizana kwake ndi zinthu zina. Iye amazigwiritsa ntchito m’njira yothandiza kapena kuti yopindulitsa.

Mwachitsanzo, munthu akhoza kuwerenga buku la, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani n’kulimaliza ndiponso n’kumvetsa mfundo zake. Pophunzira naye, akhoza kumayankha bwinobwino. Mwinanso angayambe kufika pamisonkhano n’kumayankhanso pamisonkhanopo. Umenewu ungakhale umboni woti akupita patsogolo koma si umboni woti ali ndi nzeru zopindulitsa. Mwina wangokhala wogwira zinthu mwamsanga. Koma akamagwiritsa ntchito zimene waphunzirazo m’njira yoyenera amasonyeza kuti ndi wanzeru. Ndipo nzeruzo zingaonekere pamene akusankha zochita. Munthu wanzeru amayamba waganiza kaye ndipo zimene wasankhazo zimakhala zothandiza.

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi fanizo la Yesu lopezeka pa Mateyu 7:24-27. Mu fanizoli, “munthu wochenjera” anaganizira zimene zingachitike ndipo anamanga nyumba yake pathanthwe. Iye ankaona patali n’kudziwa zoyenera kuchita. Sanaganize kuti kumanga nyumba pamchenga n’kotchipa. Anazindikira mavuto amene angabwere ngati ataimanga pamchengapo. Choncho chimvula champhamvu chitafika, nyumba yakeyo sinagwe. Ndiyeno funso n’kumati, ‘Kodi ifeyo tingatani kuti tipeze nzeru zopindulitsa n’kuzisunga?’

KODI TINGAPEZE BWANJI NZERU ZOPINDULITSA?

Choyamba, lemba la Mika 6:9 limati: “Munthu wanzeru zopindulitsa adzaopa dzina [la Mulungu].” Munthu amene amaopa dzina la Mulungu amamulemekeza. Amazindikira tanthauzo la dzinalo ndipo amaona kuti mfundo zake ndi zapamwamba. Kuti tilemekeze munthu, timafunika kudziwa maganizo ake. Kenako timayamba kumukhulupirira komanso kumutsanzira. Choncho tingasonyeze kuti tili ndi nzeru zopindulitsa ngati timaganizira kaye mmene zochita zathu zingakhudzire ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndiyeno n’kusankha zinthu mogwirizana ndi mfundo zake.

Chachiwiri, lemba la Miyambo 18:1 limati: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” Tikapanda kusamala tikhoza kusiyana ndi Yehova komanso gulu lake. Choncho tiyenera kupeza nthawi yocheza ndi anthu amene amaopa Mulungu komanso amatsatira mfundo zake. Tiyeneranso kuyesetsa kuti tizisonkhana limodzi ndi abale ndi alongo athu. Tikakhala pamisonkhano, tizimvetsera mwatcheru kuti zimene tikuphunzirazo zizitifika pamtima.

Kupemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima n’kofunikanso chifukwa kumathandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. (Miy. 3:5, 6) Tiyeneranso kuphunzira mwakhama Baibulo komanso mabuku athu. Tikatero zidzatithandiza kudziwiratu zotsatira za chilichonse chimene tingachite ndipo tikhoza kumasankha zochita mwanzeru. Ndi bwinonso kutsatira malangizo amene abale ozindikira angatipatse. (Miy. 19:20) Tikamachita zonsezi, tidzapeza ndiponso kusunga nzeru zopindulitsa.

KODI NZERU ZOPINDULITSA ZINGATHANDIZE BWANJI M’BANJA?

Nzeru zopindulitsa zimathandizanso m’banja. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti akazi “azilemekeza kwambiri” amuna awo. (Aef. 5:33) Kodi mwamuna angatani kuti azilemekezedwa? Ngati atamachita zinthu mwankhanza akhoza kulemekezedwa kwa nthawi yochepa. Mwina mkaziyo angamusonyeze ulemu pa nthawi imene alipo n’cholinga choti asayambane. Koma akangochoka, ulemu wonse ukhoza kuthera pomwepo. Choncho ndi bwino kuganizira zimene zingathandize kuti azimulemekeza nthawi zonse. Mwachitsanzo, ngati atakhala ndi makhalidwe amene mzimu umatulutsa monga chikondi ndi kukoma mtima, mkaziyo akhoza kumamulemekeza nthawi zonse. Izi zili apo, mkazi wachikhristu ayenera kulemekeza mwamuna wake popanda kuganiza ngati ali woyenera kulemekezedwa kapena ayi.—Agal. 5:22, 23.

Baibulo limanenanso kuti mwamuna ayenera kukonda mkazi wake. (Aef. 5:28, 33) Akazi ena amaona kuti si bwino kunena zinthu zimene zingakhumudwitse mwamuna wawo. Amaganiza kuti akatero ndiye kuti aziwakonda kwambiri. Koma kodi ndi nzeru kuchita zimenezi? Kodi mwamunayo akazindikira kuti mkazi wake ankamubisira zinthu zina angamve bwanji? N’zodziwikiratu kuti sangapitirize kumukonda. Mwamuna angasangalale kwambiri ngati mkazi wake amapeza nthawi yoyenera n’kumufotokozera modekha zinthu zina ngakhale zitakhala zokhumudwitsa. Izi zingachititse kuti azimukonda kwambiri.

Zimene mumachita mwana akalakwitsa, zingakhudze ubwenzi wanu ndi iyeyo m’tsogolo

Baibulo limanenanso kuti makolo ayenera kulera ana awo m’malangizo a Yehova ndipo ana ayenera kumvera makolo awo. (Aef. 6:1, 4) Kodi izi zikutanthauza kuti makolo akhale ndi mndandanda wa malamulo ouza ana kuti izi muzichita, izi musamachite? Kuti zinthu ziziyenda bwino pamafunika zambiri osati kungopereka malamulo ndi chilango. Makolo anzeru amathandiza ana awo kuzindikira ubwino womvera.

Tiyerekeze kuti mwana walankhula mwamwano kwa makolo ake. Ndiyeno makolowo n’kumukalipira kapena kumulanga nthawi yomweyo. Mwanayo akhoza kukhala phee koma ali ndi mkwiyo mumtima mwake. Izi zingachititse kuti mwanayo asamamasuke ndi makolowo.

Makolo anzeru angaganize njira yabwino yomuthandizira komanso mmene njirayo ingadzamuthandizire m’tsogolo. Si bwino kulanga mwana nthawi imene wakukhumudwitsani. Ndi bwino kudikira kaye n’kukambirana naye mwachifatse. Mwina mungamufotokozere kuti Yehova amafuna kuti iye azikulemekezani ndipo akamachita zimenezo adzadalitsidwa kwamuyaya. Ndiyeno mwanayo angayambe kukulemekezani n’cholinga choti alemekezenso Yehova. (Aef. 6:2, 3) Izi zingathandize kuti mtima wa mwanayo usinthe. Atha kuona kuti mumamukonda ndipo angamakulemekezeni kwambiri. Zikatero, akhoza kumakudalirani komanso kukufunsani akakumana ndi vuto lililonse.

Makolo ena sadzudzula ana awo, ati poopa kuwakhumudwitsa. Koma kodi chingachitike n’chiyani mwanayo akakula? Kodi angamaope Yehova n’kumaona kuti mfundo zake n’zothandiza? Nanga angamadalire Yehova n’kumalola kuti azimuphunzitsa?—Miy. 13:1; 29:21.

Munthu wogwira ntchito zosemasema amadziwiratu chimene akufuna kupanga. Iye samangosema chisemeseme n’kumaganiza kuti apanga chinthu chabwino. Nawonso makolo anzeru amapeza nthawi yophunzira mfundo za Yehova n’kumazitsatira ndipo izi zimawathandiza kuti azimuopa. Iwo sadzipatula kwa Yehova kapena gulu lake ndipo amapeza nzeru zomangira banja lawo.

Tsiku lililonse timafunika kusankha zochita. Ndipo zimene tingasankhe lero zikhoza kutikhudza kwa moyo wathu wonse. Choncho tiziganiza kaye tisanasankhe zochita. Tiziona patali n’kudziwa zotsatira zake. Tizipempha Yehova kuti atitsogolere ndipo tiziyendera nzeru zake. Tikatero tidzasonyeza kuti timasunga nzeru zopindulitsa ndipo tidzapeza moyo.—Miy. 3:21, 22.