Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi ‘Mumasunga Nzelu Zopindulitsa’?

Kodi ‘Mumasunga Nzelu Zopindulitsa’?

PALI nthano ina yakale, imene imakamba za kamnyamata kosauka kamene kanali kukhala m’mudzi wakutali. Anthu a ku tauni anali kukaseka cifukwa coganiza kuti kanali mbuli. Alendo akabwela m’mudziwo, anthu anali kucita nako nthabwala pofuna kuseketsa anzawo. Iwo anali kukaonetsa koini ikulu yasiliva, ndi ingo’ono ya golide imene inali yamphamvu kuŵilikiza kaŵili ndi ndalama ya siliva. Ndiyeno, anali kuuza kamnyamatako kuti: “Ufuna ndalama iti apa?” Kamnyamatako kanali kusankha ndalama ya siliva na kuthaŵa.

Tsiku lina, mlendo wina anafunsa kamnyamatako kuti, “Kodi udziŵa kuti koini yagolide ndiye yamphamvu kuŵilikiza kaŵili ndi ya siliva?” Iko kanamwetulila ndi kuyankha kuti, “Inde, nidziŵa.” Ndiyeno, mlendoyo anakafunsa kuti, “Nanga n’cifukwa ciani umasankha koini ya siliva?” Kanayankha kuti, “N’zoona kuti nikasankha koini ya golide nizakhala na ndalama zambili kuŵilikiza kaŵili ndi yasiliva. Koma tsiku limene nidzakasankha ya golide, ndiye kuti basi anthu adzaleka kunipanga coseketsa. Simungakhulupilile kuculuka kwa makoini a siliva amene nakhala ni kutenga.” Kamnyamata ka m’nthano imeneyo kanaonetsa khalidwe limene likanapindulitsa akulu-akulu. Khalidwe limenelo ni nzelu zopindulitsa.

Baibo imati: “Usunge nzelu zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino. Ukatelo udzayenda panjila yako popanda cokuopseza, ndipo ngakhale phazi lako silizapunthwa ndi ciliconse.” (Miy. 3:21, 23) Conco, kudziŵa kuti “nzelu zopindulitsa” n’ciani ndi mmene tingaziseŵenzetsele, kudzatiteteza. Nzelu zimenezo zidzatithandiza kuti tisapunthwe mwauzimu.

KODI NZELU ZOPINDULITSA N’CIANI?

Nzelu zopindulitsa zimasiyana ndi cidziŵitso komanso kumvetsa zinthu. Munthu amene ali na cidziŵitso amadziŵa mfundo zambili. Ndipo munthu womvetsa zinthu amakwanitsa kudziŵa mmene mfundo imodzi imagwilizanilana ndi inzake. Koma munthu wanzelu amakwanitsa kuseŵenzetsa cidziŵitso ndi kumvetsa zinthu panthawi imodzi kuti apindule.

Mwacitsanzo, m’nthawi yocepa cabe munthu angaŵelenge ndi kumvetsetsa buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni. Pophunzila Baibo, iye angadziyankha molongosoka. Angayambe kupezeka pa misonkhano ya mpingo na kuyankhapo mogwila mtima. Izi zingaonetse kuti munthuyo akupita patsogolo mwauzimu. Koma kodi zitanthauza kuti iye wakhala na nzelu? Osati kweni-kweni. Zingangotanthauza kuti sacedwa kugwila zinthu. Komabe, ngati agwilitsila nchito zimene waphunzila, ndi kuseŵenzetsa cidziŵitso na kumvetsa zinthu m’njila yoyenela, ndiye kuti wayamba kukhala wanzelu. Ndipo ngati zosankha zake zamubweletsela mapindu cifukwa cosankha mwanzelu, amaonetsa kuti wapeza nzelu zopindulitsa.

Lemba la Mateyu 7:24-27, limafotokoza fanizo la Yesu lokamba za amuna aŵili amene aliyense anamanga nyumba yake. Mwamuna mmodzi akuchulidwa kuti “wocenjela.” Iye anamanga nyumba yake pathanthwe cifukwa coganizila mavuto a mtsogolo. Anayang’ana za kutsogolo na kucita zinthu mwanzelu. Iye sanaganize kuti kumanga nyumbayo pamcenga kudzakhala kochipa ndipo sikudzatenga nthawi. Koma mwanzelu, anaganizila zotulukapo za zimene angasankhe kucita. Conco, cimphepo citawomba, nyumbayo siinagwe. Manje funso n’lakuti, Kodi tingapeze bwanji nzelu zopindulitsa na kuzisunga?

TINGAPEZE BWANJI NZELU ZOPINDULITSA?

Coyamba, onani zimene Mika 6:9 ikamba. Imati: “Munthu wanzelu zopindulitsa adzaopa dzina [la Mulungu].” Kuopa dzina la Yehova kumatanthauza kum’lemekeza, kulemekeza zimene dzina lake limaimila, ndi miyezo yake. Kuti munthu alemekeze wina, afunika kudziŵa mmene munthuyo amaonela zinthu. Ndiyeno, amayamba kum’khulupilila ndi kuphunzila kwa iye. Ngati timaganizila mmene zocita zathu zingakhudzile ubwenzi wathu ndi Yehova, komanso ngati timatsatila miyezo yake posankha zinthu, ndiye kuti tayamba kupeza nzelu zopindulitsa.

Caciŵili, lemba la Miyambo 18:1 limati: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amacita zosemphana ndi nzelu zonse zopindulitsa.” Ngati sitingasamale, tingadzipatule kwa Yehova ndi anthu ake. Conco, kuti tipewe kudzipatula, tifunika kugwilizana ndi anthu amene amaopa Mulungu ndi kulemekeza miyezo yake. Tifunikanso kupezeka pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse na kuyanjana ndi Akhiristu anzathu. Tikakhala pa misonkhano, tiyenela kumvetsela bwino-bwino ndi kulola zimene tiphunzila kukhudza mtima wathu.

Kuwonjezela apo, ngati timakhutulila Yehova zakukhosi m’pemphelo, timam’yandikila. (Miy. 3:5, 6) Pamene tiŵelenga Baibo ndi zofalitsa zimene gulu la Yehova limatipatsa, timadziŵa zimene zingatulukepo ngati sitinasankhe bwino. Izi zimatipangitsa kusankha mwanzelu. Cina, tifunika kumvela malangizo amene Akhiristu ofikapo kuuzimu angatipatse. (Miy. 19:20) Tikacita zimenezi, ndiye kuti ‘sitinakane nzelu zopindulitsa.’ M’malo mwake, tidzalimbikitsa khalidwe lofunika kwambili limeneli.

KODI ZINGATHANDIZE BWANJI MABANJA?

Nzelu zopindulitsa zingateteze kwambili mabanja. Mwacitsanzo, Baibo imalangiza mkazi kuti “azilemekeza kwambili” mwamuna wake. (Aef. 5:33) Kodi mwamuna angacite ciani kuti mkazi wake azim’lemekeza maningi? Ngati amacitila nkhanza mkazi wake ndi kum’kakamiza kuti azim’lemekeza, sangaphule kanthu. Pofuna cabe kupewa mikangano, mkazi angazilemekeza mwamuna wake ngati ali pafupi naye. Koma mwamunayo akacokapo, zingakhale zovuta kum’lemekeza. Conco, mwamuna afunika kuganizila zimene angacite kuti mkazi wake azim’lemekeza nthawi zonse. Ngati iye amaonetsa makhalidwe a mzimu wa Mulungu mwa kukonda mkazi wake na kum’komela mtima, mkaziyo adzam’lemekeza kwambili. Mkazi wacikhiristu afunikabe kulemekeza mwamuna wake, kaya mwamunayo akucita umutu wake mwacikondi kapena ayi.—Agal. 5:22, 23.

Baibo imalangizanso mwamuna kuti azikonda mkazi wake. (Aef. 5:28, 33) Pofuna kuti mwamuna wake azim’konda, mkazi angaganize kuti ndi bwino kubisa nkhani zina zosakondweletsa zimene mwamuna wake afunika kudziŵa. Koma kodi kucita zimenezo ni nzelu zopindulitsa? Kodi pangakhale zotulukapo zabwanji ngati mwamunayo wadziŵa kuti mkazi wake anali kumubisa zinazake? Kodi adzapitiliza kum’konda? Kucita zimenezo kungakhale kovuta. Koma ngati mkazi apeza nthawi yabwino yofotokozela mwamuna wake zinthu zosakondweletsa mwaulemu, mwamunayo adzamuyamikila na kum’konda kwambili.

Mmene mumalangizila ana anu masiku ano, zidzakhudza mmene adzayamba kucitila akadzakula

Ana afunika kumvela makolo awo ndi kuleledwa m’malangizo a Yehova. (Aef. 6:1, 4) Kodi izi zitanthauza kuti makolo ayenela kuikila ana awo m’ndandanda wa malamulo? Pali zambili zimene ana afunika kudziŵa kuposa kungodziŵa cabe malamulo a panyumba, kapena cilango cimene angalandile akalakwitsa. Makolo amene ali ndi nzelu zopindulitsa amathandiza ana awo kumvetsetsa cifukwa cake afunika kuwamvela.

Mwacitsanzo, tiyelekeze kuti mwana wakamba mopanda ulemu kwa kholo lake. Kukamba mokhadzula kapena kumulanga msanga-msanga kungacititse manyazi mwanayo cakuti angaleke kumasukila makolo ake. Mwanayo akhoza kusunga mkwiyo mumtima mwake, ndipo zimenezi zingacititse kuti asakhale paubwenzi ndi makolo ake.

Makolo amene ali na nzelu zopindulitsa amaganizila mmene angalangile ana awo, komanso mmene cilangoco cingakhudzile anawo mtsogolo. Makolo sayenela kucitapo kanthu mwamsanga, cabe cifukwa cocititsidwa manyazi. Mwamseli, makolo angakambilane ndi mwanayo mofatsa ndi mwacikondi, na kumufotokozela kuti Yehova afuna kuti iye azilemekeza makolo ake kuti apindule pa umoyo wake. Ndiyeno, mwanayo akayamba kulemekeza makolo ake, adzazindikila kuti akulemekeza Yehova. (Aef. 6:2, 3) Kucita zinthu mwa njila imeneyi kudzam’fika pamtima mwana wanu. Iye adzaona kuti mumam’konda, ndipo adzakulemekezani kwambili. Izi zidzam’thandiza kuti azimasuka kupempha thandizo pankhani zofunika zimene zingabuke.

Makolo ena amalephela kulangiza ana awo cifukwa coopa kuwakhumudwitsa. Komabe, n’ciani cingacitike mwanayo akadzakula? Kodi adzaopa Yehova ndi kuzindikila ubwino wotsatila miyezo ya Mulungu? Kodi adzakhala wofunitsitsa kulandila malangizo a Yehova, kapena adzadzipatula mwauzimu?—Miy. 13:1; 29:21.

Katswili woumba mbiya amayamba waganizila ciwiya cimene afuna kuumba. Samangouka basi n’kuyamba kuumba, n’kuyembekezela kuti ciwiyaco cidzakhala bwino. N’cimodzi-modzi ndi makolo amene ali ndi nzelu zopindulitsa. Iwo amapatula nthawi yophunzila miyezo ya Yehova ndi kutsatila zimene amaphunzila. Akatelo, amaonetsa kuti amaopa dzina lake. Cifukwa copewa kudzipatula kwa Yehova na gulu lake, iwo amapeza nzelu zopindulitsa na kuzigwilitsila nchito kuthandiza banja lawo.

Tsiku ndi tsiku, timafunika kusankha zinthu zimene zingakhudze umoyo wathu wa kutsogolo. M’malo mocita zinthu mopupuluma, bwanji osayamba mwaganizilapo? Muziganizila mozama zotulukapo za zosankha zanu. Lolani Yehova kukutsogolelani, ndipo gwilitsilani nchito malangizo ake a nzelu. Mukacita zimenezi, mudzasunga nzelu zopindulitsa, ndipo mudzapeza moyo wosatha.—Miy. 3:21, 22.