Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Nchitoyi Ndi Yaikulu”

“Nchitoyi Ndi Yaikulu”

NI NTHAWI ya msonkhano wofunika kwambili m’Yerusalemu. Mfumu Davide waitana akalonga ake onse, nduna za mfumu, ndi amuna olemekezeka. Onse ni okondwa ngako kumvela cilengezo capadela. Yehova wapatsa Solomo, mwana wa Davide, nchito yapadela yomanga kacisi kuti azilambililamo Mulungu woona. Mfumu ya Isiraeli yacikalambile inalandila mwa mzimu woyela mapulani akamangidwe ka kacisiyo. Ndipo iye lomba akupatsa mwana wake Solomo mapulaniwo. Ndiyeno, Davide akuuza anthuwo kuti: “Nchitoyi ndi yaikulu cifukwa cinyumba cacikuluci, si ca munthu ayi, koma ndi ca Yehova Mulungu.”—1 Mbiri 28:1, 2, 6, 11, 12; 29:1.

Ndiyeno Davide afunsa kuti: “Ndani lelo ali wokonzeka kupeleka mphatso kwa Yehova?” (1 Mbiri 29:5) Mukanakhalapo, kodi mukanayankha bwanji? Kodi mukanacilikiza nchito yaikulu imeneyo? Aisiraeli anagwapo pa nchito imeneyo. Ndithudi, “anasangalala cifukwa ca nsembe zaufulu zimene anapeleka, pakuti anapeleka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.”—1 Mbiri 29:9.

Patapita zaka zambili, Yehova anakhazikitsa cinthu cina capamwamba kupambana kacisi wakuthupi ameneyo. Iye anakhazikitsa kacisi wamkulu wauzimu, amene ni makonzedwe othandiza anthu kulambila Mulungu mwa nsembe ya Yesu. (Aheb. 9:11, 12) Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu kuyanjananso naye masiku ano? Amacita zimenezo kupitilila m’nchito yopanga ophunzila. (Mat. 28:19, 20) Cifukwa ca nchitoyi, caka ciliconse anthu mamiliyoni amaphunzila Baibo, enanso masauzande amabatizika, ndipo mipingo yatsopano mahandiledi imapangidwa.

Ciwonjezeko cimeneci cimafunanso kupulintha mabuku ambili ophunzilila Baibo, kumanga ndi kukonzanso Nyumba za Ufumu, ndi mabwalo a misonkhano ya dela ndi ya cigawo. Kodi simungavomeleze kuti nchito yathu yolalikila uthenga wabwino ni yaikulu komanso yopindulitsa?—Mat. 24:14.

Kukonda Mulungu ndi anthu, komanso pakuti nchito yolalikila Ufumu ifunika kucitika mwamsanga, anthu a Mulungu ‘akupeleka mphatso kwa Yehova’ mwa kucita zopeleka zaufulu. N’zokondweletsa cotani nanga, ‘kulemekeza Yehova ndi zinthu zathu zamtengo wapatali.’ N’coyamikilikanso kuona kuti zopelekazo amaziseŵenzetsa bwino pa nchito yaikulu imene siinacitikepo n’kale lonse.—Miy. 3:9.