Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Anamasuka Kucoka ku Cipembedzo Conama

Anamasuka Kucoka ku Cipembedzo Conama

“Tulukani mwa iye anthu anga.”—CHIV. 18:4.

NYIMBO: 72, 82

1. N’cifukwa ciani anthu a Mulungu anali na ciyembekezo cakuti adzamasuka mu ukapolo kwa Babulo? Nanga tikambilana mafunso ati?

M’NKHANI yapita, tinaphunzila mmene Akhiristu okhulupilika analoŵela mu ukapolo wa m’Babulo. Koma cokondweletsa n’cakuti sanakhalemo mpaka kale-kale. Kukanakhala kuti panalibe munthu amene akanatha kucoka mu ukapolo wa zipembedzo zonama, lamulo la Mulungu lakuti, “tulukani mwa iye anthu anga” likanakhala lopanda tanthauzo. (Ŵelengani Chivumbulutso 18:4.) Tifunitsitsa kudziŵa kuti ni liti pamene anthu a Mulungu anamasukilatu mu ukapolo wa m’Babulo. Koma coyamba, tifunika kuyankha mafunso aya: Kodi Ophunzila Baibo anatenga kaimidwe kabwanji kulinga ku Babulo Wamkulu cikalibe kufika caka ca 1914? Kodi abale athu anali okangalika mu nchito yolalikila m’nthawi ya nkhondo yoyamba ya pa dziko lonse? Kodi kutengedwa kwawo ukapolo ndi Babulo Wamkulu kunali njila yowawongolela ndi kuwalanga?

“KUGWA KWA BABULO”

2. Kodi Ophunzila Baibo oyambilila anatenga kaimidwe kanji kulinga ku zipembedzo zonama?

2 M’zaka zokafikitsa ku nkhondo yoyamba ya dziko lonse, Charles Taze Russell na anzake anazindikila kuti Machechi Acikhiristu sanali kuphunzitsa coonadi ca m’Baibo. Conco, iwo sanafune kugwilizana ngakhale pang’ono na zipembedzo zonama. Mu November 1879, magazini ya Zion’s Watch Tower inafotokoza mosapita m’mbali kaimidwe kawo kogwilizana ndi malemba. Magaziniyo inati: “Chechi iliyonse imene imakamba kuti ni namwali woyela wa Khiristu koma m’ceni-ceni imagwilizana ndi kucilikiza maboma (cilombo), mwa kunena kwa malemba chechi imeneyo ni hule,” kutanthauza Babulo Wamkulu.—Ŵelengani Chivumbulutso 17:1, 2.

3. Kodi Ophunzila Baibo anacita ciani molimba mtima, poonetsa kuti anaona kufunika kolekana ndi cipembedzo conama? (Onani pikica kuciyambi kwa nkhani ino.)

3 Amuna na akazi oopa Mulungu anali kudziŵa coyenela kucita. Anadziŵa kuti ngati apitiliza kucilikiza zipembedzo zonama, sangalandile madalitso a Mulungu. Conco, Ophunzila Baibo ambili analemba makalata olaila machechi awo. Ena anali kuŵelenga poyela makalata awo m’machechi. Kumene sanawavomeleze kuŵelenga poyela, ophunzilawo anatumiza makope a makalata kwa mamemba onse a chechi yawo. Sanafunenso kugwilizana na cipembedzo conama m’njila iliyonse. Kumadela ena, kucita zimenezo kunali kuika moyo wa munthu pa ciopsezo. Koma pofika kumapeto kwa ma 1800, maboma ambili sanali kucilikizanso machechi. M’maiko amenewo anthu lomba anali omasuka kukambilana nkhani za cipembedzo, ngakhale kutsutsa poyela ziphunzitso za machechi.

4. Pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya dziko lonse, kodi cinali kucitika n’ciani pakati pa Ophunzila Baibo na Babulo Wamkulu?

4 Ophunzila Baibo anazindikila kuti sizinali zokwanila kungodziŵitsa cabe abululu ŵawo, anzawo, na mamemba a chechi yawo zakuti acoka m’cipembedzo conama. Dziko lonse linafunikila kudziŵa za cigololo ca Babulo Wamkulu. Conco, kuyambila mu December 1917 mpaka kuciyambi kwa 1918, Ophunzila Baibo okwana masauzande angapo anagaŵila mwakhama mathirakiti 10,000,000 akuti, “Kugwa kwa Babulo.” Unali uthenga wolasa kumtima Machechi Acikhiristu. Ngakhale kuti azibusa awo anakwiya kwambili, Ophunzila Baibo sanabwelele m’mbuyo pa nchito yofunika imeneyo. Anatsimikiza mtima kumvela “Mulungu monga wolamulila, osati anthu.” (Mac. 5:29) Kodi tikuona mfundo yanji pamenepa? Mfundo yakuti pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya dziko lonse imeneyi, Akhiristu amenewa sanali kuloŵa mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu ayi. M’malomwake, iwo anali kumasuka kucoka m’cipembedzo conama, na kuthandizanso ena kucokamo.

KUKANGALIKA PA NCHITO MKATI MWA NKHONDO YOYAMBA YA DZIKO LONSE

5. Pali umboni wanji woonetsa kuti abale anali okangalika pa nchito yolalikila panthawi ya nkhondo yoyamba ya dziko lonse?

5 M’zaka za kumbuyoku, tinali kukhulupilila kuti Yehova anali wokhumudwa ndi anthu ake cifukwa, pa nthawi ya nkhondo ya dziko lonse, anali atabwelela m’mbuyo pa nchito yolalikila. Tinali kukhulupilila kuti pa cifukwa cimeneci, Yehova analola Babulo Wamkulu kutengela anthu Ake mu ukapolo kwa kanthawi. Komabe, abale na alongo okhulupilika amene anatumikila Mulungu kucokela mu 1914 mpaka 1918, pambuyo pake iwo anafotokoza momveka bwino kuti monga gulu, anthu a Ambuye anali okangalika pa nchito yolalikila kuti isalekeke. Ndipo pali maumboni amphamvu otsimikizila zimenezi. Kumvetsetsa mbili ya gulu lathu kwatithandiza kuzindikila bwino zocitika zina zolembedwa m’Baibo.

6, 7. (a) Ni mavuto anji amene Ophunzila Baibo anawagonjetsa panthawi ya nkhondo yoyamba ya dziko lonse? (b) Pelekani zitsanzo zoonetsa kuti Ophunzila Baibo anali okangalika.

6 Kukamba zoona, Ophunzila Baibo amene analiko panthawi ya nkhondo yoyamba ya dziko Lonse (1914-1918) anacitila umboni motamandika. Koma sicinali copepuka kwa iwo pa zifukwa zingapo. Tiyeni tikambilane ziŵili cabe. Coyamba, nchito ikulu panthawiyo inali kugaŵila mabuku ophunzilila Baibo. Pamene boma inawaletsa kugaŵila buku lakuti The Finished Mystery kuciyambi-yambi kwa 1918, ulaliki unakhala wovuta kwa abale ambili. Anali asanaphunzile kulalikila na Baibo cabe. Anali kudalila buku lakuti The Finished Mystery “kuwalankhulilako.” Cifukwa caciŵili cinali kubuka kwa mlili wa matenda a Fuluwenza mu 1918. Cifukwa ca kuopsa kwa matenda oyambukila amenewa, kunali kovuta kuti ofalitsa aziyenda-yenda na kulalikila kwa anthu. Koma ngakhale kuti panali zovuta zimenezi, Ophunzila Baibo anacitabe zonse zotheka kuti nchito yolalikila ipitilize.

Ophunzila Baibo anali okangalika pa ulaliki! (Onani palagilafu 6 na 7)

7 M’caka ca 1914 cabe, Ophunzila Baibo ocepawo anatambitsa “Seŵelo la Pakanema la Cilengedwe” kwa anthu oposa 9,000,000. Seŵelo imeneyi inaphatikiza kanema, mapikica, ndi mau ofotokoza mbili ya munthu kucokela pamene analengedwa mpaka kumapeto kwa zaka Cikwi. Cimeneci cinali cipambano cacikulu. Tangoganizani, anthu amene anatamba seŵelo imeneyi m’caka ca 1914 cokha, anali ambili kupambana alaliki a Ufumu onse amene alipo lelo. Malipoti aonetsanso kuti m’caka ca 1916, anthu okwana 809,393 anapezeka pa misonkhano ya anthu onse ku America. Ndipo mu 1918, ciŵelengelo cinakwela kufika pa 949,444. Kodi wonsewu si umboni wakuti Ophunzila Baibo analidi okangalika pa nchito yawo?

8. Kodi zosoŵa zauzimu za abale zinasamalidwa bwanji panthawi ya nkhondo yoyamba ya dziko lonse?

8 Mkati mwa nkhondo yoyamba ya dziko lonse, abale anayesetsa kupeleka cakudya cauzimu na cilimbikitso kwa Ophunzila Baibo amene anali m’malo osiyana-siyana. Izi zinalimbikitsa abale kupitiliza kugwila nchito yolalikila. M’bale Richard H. Barber amene anali wokangalika anakamba kuti: “Tinakwanitsa kulimbikitsa oyang’anila madela ocepa amene tinali nawo. Tinapitilizanso kufalitsa magazini ya Nsanja ya Mlonda mwezi uliwonse na kuitumiza m’dziko la Canada kumene inali yoletsedwa. N’nali na mwayi wotumiza makope a buku lakuti The Finished Mystery a saizi ya m’thumba kwa abale ambili amene anali atalandidwa mabuku awo. Ndiyeno, M’bale Rutherford anatipempha kulinganiza misonkhano m’mizinda ingapo ya kumadzulo kwa America ndi kutumiza alankhuli kuti akalimbikitse abale athu.

ANAFUNIKA KUYENGEDWA

9. (a) N’cifukwa ciani anthu a Mulungu anafunikila kuwongolelewa pakati pa 1914 ndi 1919? (b) Kodi kuwawongolela kumeneko sikunatanthauze ciani?

9 Sikuti zonse zimene Ophunzila Baibo anali kucita kuyambila mu 1914 kufika mu 1919 zinali zogwilizana na Malemba. Ngakhale kuti anali oona mtima, kamvedwe kawo ka mfundo ya kugonjela maboma sikanali kolongosoka kweni-kweni. (Aroma 13:1) Cifukwa ca ici, nthawi zina anali kupezeka kuti akucilikiza nkhondo m’njila zosiyana-ziyana. Mwacitsanzo, pamene pulezidenti wa ku America anagamula tsiku la 30 May 1918, kukhala lopemphelela mtendele, magazini ya Nsanja ya Mlonda inalimbikitsa Ophunzila Baibo kucita nawo mapemphelo amenewo. Abale ena anapeleka ndalama zocilikiza nkhondo, ndiponso analipo ena amene ananyamula mfuti na kuyenda ku nkhondo. Komabe, kungakhale kulakwa kuganiza kuti Ophunzila Baibo anatengedwa ukapolo ndi Babulo Wamkulu monga cilango cawo ndi kuwawongolela. Mosiyana ndi zimenezi, iwo anali ataimvetsetsa bwino-bwino mfundo yakuti afunika kulekana na cipembedzo conama. Ndipo podzafika nthawi ya nkhondo ya dziko lonse, anali atatsala pang’ono kucokelatu m’Babulo Wamkulu.—Ŵelengani Luka 12:47, 48.

10. Kodi Ophunzila Baibo analimba mtima na kutenga kaimidwe kotani cifukwa ca kupatulika kwa moyo?

10 Ngakhale kuti mbali zina Ophunzila Baibo sanali kuzimvetsetsa bwino-bwino, mofanana na ise masiku ano, mfundo yakuti Baibo imaletsa kupha munthu anali kuidziŵa bwino lomwe. Conco, ngakhale abale ocepawo amene ananyamula mfuti na kuyenda kunkhondo, pankhondo yoyamba ya dziko lonse, anakanilatu kwa mtu wagalu kuwombela mfuti munthu wina. Pa cifukwa cimeneci, ena anali kuikidwa kutsogolo kwa nkhondo kuti aphedwe.

11. Kodi akulu-akulu a boma anacita bwanji poona kaimidwe ka Ophunzila Baibo ka m’Malemba pankhani yomenya nkhondo?

11 Zinali zoonekelatu kuti Mdyelekezi anali wokwiya ngako cifukwa ca kaimidwe kamene abalewo anatenga pa nkhani ya nkhondo. Conco, anakonza ciwembu mwa ‘kupangitsa malamulo’ oyambitsa mavuto. (Sal. 94:20) Pokambilana na M’bale J. F. Rutherford ndi W. E. Van Amburgh, mkulu wa asilikali dzina lake James Franklin Bell wa ku America, anakamba kuti Dipatimenti Yoona za Cilungamo ku America inafuna kukhazikitsa lamulo lakuti munthu amene wakana kupita kunkhondo, aziphedwa. M’ceni-ceni anali kutanthauza Ophunzila Baibo. Mwaukali mkulu wa asilikaliyo anauza M’bale Rutherford kuti: “Pulezidenti Wilson [wa dziko la America] ni amene analetsa lamulo limenelo. Koma tidzapeza njila yokukhaulitsilani, mudzaciona!”

12, 13. (a) N’cifukwa ciani abale 8 audindo anaweluzidwa kukapika jele zaka zambili? (b) Kodi kumangiwa kwawo kunawatayitsa cikhulupililo mwa Yehova? Fotokozani.

12 Potsilizila, olamulila anapezadi njila yocitila ndi Ophunzila Baibo. Monga oimila Watch Tower Society, M’bale Rutherford, Van Amburgh, na abale ena 6 anamangidwa. Popeleka ciweluzo, jaji amene anali kuweluza mlandu wawo anati: “Cipembedzo cimene amuna awa alimo n’coopsa kwambili kupambana gulu la asilikali acijelemani . . . Iwo sanalakwile cabe akulu-akulu a Boma ndi gulu lankhondo la asilikali, komanso anyozela azibusa onse a machechi. Afunika cilango cowakhaulitsa mokwana!” (Malinga ndi buku yakuti Faith on the March yolembewa na A. H. Macmillan, tsa. 99) Ndipo cinali cokhaulitsadi. Ophunzila Baibo okwana 8 amenewo anawaweluza kuti aikidwe m’ndende kwa zaka zambili ku Atlanta, Georgia. Koma pamene nkhondo inatha, milandu yawo yonse inacoka washauti ndipo anawamasula onse.

13 Ngakhale pamene abale 8 amenewo anali m’ndende, sanagwedezeke pa cikhulupililo cawo ca m’Malemba. M’kalata imene analembela pulezidenti wa America yopempha kuti awacitile cifundo, iwo anati: “Lamulo la Ambuye linalembedwa m’Malemba kuti, ‘Usaphe munthu.’ Conco, memba aliyense wa Gulu [la Ophunzila Baibo la pa Dziko Lonse] amene anadzipeleka kwa Ambuye, koma mwadala aphwanya cipangano ca kudzipeleka kwake, ndiye kuti wataya ciyanjo ca Mulungu, moti akhoza kudzawonongedwa. Mwa ici, iwo sangatengeko mbali m’zocitika zilizonse zakupha anthu.” Ha, anali mau olimba mtima cotani nanga! Mwacionekele, abalewo analibiletu ganizo logonja pa cikhulupililo cawo.

AMASULIDWA POTHELA PAKE!

14. Fotokozani mwa Malemba zimene zinacitika kuyambila mu 1914 mpaka 1919.

14 Mau a pa Malaki 3:1-3 amafotokoza zocitika za pakati pa 1914 mpaka kuciyambi-yambi kwa 1919, pamene “ana a Levi” odzozedwa anali kudzayengedwa. (Ŵelengani.) Panthawiyo, Yehova Mulungu, “Ambuye woona” pamodzi na Yesu Khiristu, “mthenga wa pangano,” anabwela ku kacisi wauzimu kudzayendela otumikila m’kacisiyo. Pambuyo popatsidwa cilangizo cofunikila, anthu oyeletsedwa a Yehovawo anakhala okonzeka kulandilanso utumiki wina watsopano. Mu 1919, “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” anaikidwa kuti azipeleka cakudya cauzimu kwa a pa banja la cikhulupililo. (Mat. 24:45) Anthu a Mulungu lomba anali atamasukilatu kwa Babulo Wamkulu. Kucokela panthawiyo, mwa cisomo ca Yehova, anthu ake akhala akukula m’cidziŵitso pa cifunilo ca Mulungu, ndi m’cikondi cawo kwa Atate wawo wakumwamba. Ha, ndife okondwa cotani nanga pa madalitso onsewa! [1]

15. Kodi tiyenela kumvela bwanji poona kuti tinamasuka ku Babulo Wamkulu?

15 Ife kwathu n’kukondwela kuti tinamasulidwa mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu. Cam’kangilatu Satana kufafaniza Akhiristu oona pa dziko lapansi. Ngakhale n’conco, sitiyenela kuiŵala colinga cimene Yehova watipatsila ufulu umenewu. (2 Akor. 6:1) Anthu masauzande ambili akali mu ukapolo ku cipembedzo conama. Nawonso afunika kuwaonetsa njila yocokelamo, ndipo ise tingawalongoze njilayo. Conco, potengela citsanzo ca abale athu a m’zaka za m’ma 1900, tiyeni ticite ciliconse cotheka kuti tithandize anthu amenewo kumasuka.

^ [1] (palagilafu 14) Pali zolinganako zambili pakati pa ukapolo wa Ayuda wa zaka 70 ku Babulo, na zimene zinacitika kwa Akhiristu mpatuko utayamba. Komabe, sizikuoneka kuti ukapolo wa Ayuda kweni-kweni unacitila cithunzi zimene zinali kudzacitika kwa Akhiristu. Mwacitsanzo, utali wa zaka za ukopolo unali wosiyana. Conco, sitiyenela kuyesa kugwilizanitsa mbali zonse-zonse za ukapolo wa Ayuda ndi zimene zinacitika kwa Akhiristu odzozedwa m’zaka zokafikitsa ku 1919.