Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Anthu a m’zipembedzo zambili amakhulupilila kuti mzimu wa munthu sukufa

NKHANI YA PACIKUTO | KODI BAIBO IMATI CIANI PA NKHANI YA MOYO NA IMFA?

Funso Logometsa Mutu

Funso Logometsa Mutu

ANTHU ambili ali na maganizo osiyana-siyana pankhani ya moyo na imfa. Ena amaganiza kuti akafa, adzapitiliza kukhala na moyo, mwina m’cinthu cina kapena kumalo ena. Ena amaganiza kuti akafa adzabwadwanso na kukhala ndi moyo. Pali enanso amene amaganiza kuti imfa ndiye mapeto a zonse.

Na imwe muyenela kuti pali zimene mumakhulupilila pankhaniyi, malinga ndi kumene munakulila kapena cikhalidwe canu. N’ciani cimacitika munthu akafa? Ambili amapeleka mayankho osiyana-siyana pa funso limeneli. Koma kodi n’kuti kumene tingapeze yankho lodalilika ndi loona pa funso logometsa mutu limeneli?

Kwa zaka zambili, abusa a machechi akhala akuphunzitsa kuti munthu ali na mzimu umene sukufa. Anthu a m’zipembedzo pafupi-fupi zonse zikulu-zikulu—Akhristu, Ahindu, Ayuda, Asilamu, ndi ena—amakhulupilila kuti munthu ali na mzimu umene sukufa. Amakamba kuti munthu akafa, mzimuwo umacoka ndi kukakhala na moyo kumalo a mizimu. Komabe, Abuda amakhulupilila kuti munthu akabadwanso mobweleza-bweleza, mphamvu ya maganizo ake imafika pa mkhalidwe wochedwa kuti Nirvana. Akafika apo, munthuyo amapeza cimwemwe cacikulu.

Cifukwa ca ziphunzitso zimenezi, anthu ambili padziko lapansi amakhulupilila kuti imfa imatsegula nkhomo yoloŵela ku moyo wina. Conco kwa anthu ambili, imfa ni sitepi yofunika kwambili yoloŵela ku moyo winanso, ndipo amaiona kuti n’cifunilo ca Mulungu. Koma kodi Baibo imakamba ciani pankhani imeneyi? Ŵelengani nkhani yotsatila, ndipo mwina mudzadabwa ndi yankho lake.