Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA ZAMBIRI ZOKHUDZA ANGELO?

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Angelo

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Angelo

Kodi mumafuna mutadziwa zoona zokhudza angelo? Mwachitsanzo, kodi angelo anachokera kuti, nanga amagwira ntchito yanji? Palibe kumene mungapeze mayankho olondola kuposa m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Ndiye kodi Baibulo limatiuza zotani zokhudza angelo?

  • Mofanana ndi mmene Mulungu alili, angelo ndi mizimu yosaoneka ndipo ‘alibe mnofu ndi mafupa.’ Angelo okhulupirika amakhala kumwamba ndipo amatha kuonekera pamaso pa Mulungu.​—Luka 24:39; Mateyu 18:10; Yohane 4:24.

  • Pa nthawi ina angelo anavala matupi a anthu kuti agwire ntchito imene Mulungu anawatuma padzikoli, ndipo atamaliza ntchitoyo anavula matupiwo n’kubwerera kumwamba.​—Oweruza 6:11-23; 13:15-20.

  • Ngakhale kuti Baibulo likamanena za angelo limawafotokoza ngati ndi aamuna, komanso akamaonekera kwa anthu amaoneka aamuna, sikuti pali angelo aamuna ndi aakazi. Angelo sakwatirana n’kubereka ana omwenso ndi angelo. Komanso sikuti angelo amayamba akhala kaye padzikoli ngati anthu kapena ana, kenako akamwalira n’kupita kumwamba. Angelo analengedwa ndi Yehova ndipo Baibulo limati ndi “ana a Mulungu woona.”​—Yobu 1:6; Salimo 148:2, 5.

  • Baibulo limati pali “malilime a anthu ndi a angelo,” kusonyeza kuti angelo amalankhula ndipo ali ndi chinenero chawo. Ngakhale kuti pa nthawi ina Mulungu ankagwiritsa ntchito angelo polankhula ndi anthu, iye safuna kuti tiziwalambira kapena kupemphera kwa iwo.​—1 Akorinto 13:1; Chivumbulutso 22:8, 9.

  • Pali miyandamiyanda ya angelo, mwinanso yokwana mabiliyoni ambiri. *​—Danieli 7:10; Chivumbulutso 5:11.

  • Angelo ndi “amphamvu” komanso anzeru kwambiri kuposa anthu. Iwo angathe kuyenda pa liwiro loposa chilichonse m’chilengedwechi.​—Salimo 103:20; Danieli 9:20-23.

  • Ngakhale kuti angelo ndi amphamvu komanso anzeru kwambiri, pali zinthu zina zimene sangathe kuchita komanso zimene sadziwa.​—Mateyu 24:36; 1 Petulo 1:12.

  • Angelo ndi osiyanasiyana ndipo ali ndi makhalidwe amene Mulungu ali nawo. Komanso Mulungu anawapatsa ufulu wosankha. Choncho mofanana ndi anthufe, nawonso angathe kusankha kuchita zabwino kapena zoipa. N’zomvetsa chisoni kuti angelo ena anasankha kusamvera Mulungu.​—Yuda 6.

^ ndime 8 Mwanda umodzi ndi 10,000. Choncho mwanda kuchulukitsa ndi mwanda ndi 100 miliyoni. Buku la Chivumbulutso limanena za angelo “miyanda kuchulukitsa ndi miyanda.” Izi zikusonyeza kuti pali mamiliyoni mwinanso mabiliyoni a angelo.