Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | ANGELO KODI ALIKO ZOONA? CIFUKWA CAKE TIFUNA KUDZIŴA

Zoona Zake Ponena za Angelo

Zoona Zake Ponena za Angelo

Kodi mungakonde kudziŵa zoona zake ponena za angelo? Kodi iwo ndani? Nanga anakhalako bwanji? Kodi amagwila nchito yabwanji? Kulibe kwina kumene tingapeze mayankho a zoona kuposa m’Mau ouzilidwa a Mulungu, Baibo. (2 Timoteyo 3:16) Kodi Baibo imatiuza ciani?

  • Molingana ndi Mulungu amene ni Mzimu, nawonso angelo ni mizimu yosaoneka imene ‘ilibe mnofu ndi mafupa.’ Angelo okhulupilika amakhala kumwamba, ndipo amatha kuona Mulungu mwacindunji.—Luka 24:39; Mateyu 18:10; Yohane 4:24.

  • Nthawi zina angelo anali kuonekela na matupi aumunthu kuti acite zimene Mulungu anawatuma padziko lapansi. Akatsiliza, anali kuvula matupi aumunthu na kubwelela kumwamba.—Oweruza 6:11-23; 13:15-20.

  • Ngakhale kuti Baibo pokamba za angelo imawachula monga amuna, ndipo poonekela kwa anthu akhala akuonekela monga aamuna, kweni-kweni kulibe angelo aamuna kapena aakazi. Iwo sakwatila, kukwatiwa kapena kubala ana. Komanso angelo sanayambe akhalapo anthu padziko monga makanda, ana, kapena acikulile. Angelo anacita kulengedwa na Yehova. Ndiye cifukwa cake m’Baibo amachulidwa kuti “ana a Mulungu woona.”—Yobu 1:6; Salimo 148:2, 5.

  • Pofuna kuonetsa kuti angelo ali ndi cinenelo ndipo amalankhula, Baibo imakamba za “malilime a anthu ndi a angelo.” Ngakhale kuti Mulungu anakambapo ndi anthu kupitila mwa angelo, iye satilola kuwalambila kapena kupemphela kwa iwo.—1 Akorinto 13:1; Chivumbulutso 22:8, 9.

  • Angelo alipo miyanda miyanda yoculuka, mwina amafika m’mabiliyoni ambili. *Danieli 7:10; Chivumbulutso 5:11.

  • Angelo ni “amphamvu” kwambili kuposa anthu, ndipo ali na nzelu zakuya kutipambana. Komanso iwo amauluka paliŵilo lalikulu kupambana liŵilo la cinthu ciliconse ca padziko lapansi kapena ca kuthambo.—Salimo 103:20; Danieli 9:20-23.

  • Olo kuti angelo ali na nzelu ndi mphamvu zapamwamba kwambili, pali zinthu zina zimene sadziŵa na zimene sangakwanitse kucita.—Mateyu 24:36; 1 Petulo 1:12.

  • Angelo analengedwa ndi maumunthu osiyana-siyana, makhalidwe aumulungu, na ufulu wosankha zocita. Conco, molingana ndi ife anthu iwo angathe kusankha kucita zabwino kapena zoipa. N’zacisoni kuti angelo ena anasankha kupandukila Mulungu.—Yuda 6.

^ par. 8 Mwanda umodzi ni 10,000. Ndipo mwanda umodzi kuculukitsa ndi mwanda umodzi timapeza 100 miliyoni. Komabe, lemba la Chivumbulutso limakamba za “miyanda kuculukitsa ndi miyanda” ya angelo. Izi zikutanthauza mamiliyoni mahandiledi ambili, ngakhalenso mabiliyoni, a zolengedwa zauzimu!