Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tizitani Tikalakwitsa Zinthu?

Kodi Tizitani Tikalakwitsa Zinthu?

A Don ndi a Margaret * anasangalala kwambiri mwana wawo wamkazi, mwamuna wake komanso ana awo awiri atapita kukawachezera kunyumba kwawo. Atatsala pang’ono kutsanzikana, a Margaret, omwe poyamba ankagwira ntchito yophika, anaganiza zophikira adzukulu awowo chakudya chomwe ankachikonda kwambiri. Chakudya chake chinali makaroni osakaniza ndi tchizi.

Nthawi yoti ayambe kudya itakwana, a Margaret anabweretsa poto n’kumuika pakati penipeni pa tebulo. Koma atavundukula potoyo, anaona kuti munali tchizi chokhachokha. A Margaret anali ataiwala kuthiramo makaroni. *

Tonsefe timalakwitsa zinthu ndipo zilibe kanthu kuti tili ndi zaka zingati kapenanso kuti timadziwa zinthu zochuluka bwanji. Mwachitsanzo, tingalankhule mawu osakhala bwino kapenanso kuchita zinthu pa nthawi yolakwika. Mwinanso tikhoza kuiwala kuchita zinazake. Koma kodi n’chifukwa chiyani timalakwitsa zinthu? Kodi tingatani ngati talakwitsa zinazake? Nanga n’chiyani chingatithandize kuti tisamalakwitse kwambiri zinthu? Kudziwa mayankho a mafunso amenewa kungatithandize kuti tizikhala ndi maganizo oyenera tikalakwitsa zinthu.

ANTHUFE TIMAONA ZOLAKWA MOSIYANA NDI MMENE MULUNGU AMAZIONERA

Tikachita zinthu zabwino, timasangalala ena akatiyamikira ndipo timavomereza kuti timayeneradi kuyamikiridwa. Ndiyetu tingachitenso bwino kumavomereza tikalakwitsa zinthu, ngakhale zomwe talakwitsa mwangozi kapenanso zimene ena sanazidziwe. Koma timafunika kukhala odzichepetsa kuti tichite zimenezi.

Ngati timadziona kuti ndife apamwamba, tikhoza kumadziikira kumbuyo, kumaloza ena chala kapenanso kukana kuti talakwitsa. Koma zimenezi zingabweretse mavuto ambiri. Mwachitsanzo, zingapangitse kuti tilephere kukonza zimene talakwitsazo. Zingachititsenso kuti ena aimbidwe mlandu pa zinthu zoti talakwitsa ndife. Koma tizikumbukira kuti, ngakhale titapanda kukumana ndi zotsatira za zolakwa zathu panopa, chifukwa choti tabisa kapena takankhizira ena, “aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.”​—Aroma 14:12.

Mulungu amaona moyenera zolakwa zimene anthufe timachita. Buku la Masalimo limafotokoza kuti Mulungu ndi “wachifundo ndi wachisomo.” Limanenanso kuti iye “sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse chifukwa cha zolakwa zathu, kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.” Mulungu amadziwa kuti anthufe si angwiro. Amadziwanso zimene timalakwitsa ndipo “amakumbukira kuti ndife fumbi.”​—Salimo 103:8, 9, 14.

Mofanana ndi bambo wachifundo, Mulungu amafuna kuti nafenso tiziona zolakwa moyenera. (Salimo 130:3) Iye amatipatsa malangizo othandiza kudzera m’Mawu ake n’cholinga choti tizidziwa zoyenera kuchita ngati talakwitsa zinthu kapena ngati ena alakwitsa zinazake.

KODI TIZITANI ZINTHU ZIKALAKWIKA?

Nthawi zambiri munthu akachita chinthu cholakwika, amataya nthawi n’kuimba mlandu anthu ena kapenanso kudziikira kumbuyo. Koma ngati mwalankhula zinthu zomwe zakhumudwitsa munthu wina, ndi bwino kungopepesa n’cholinga choti muzigwirizanabe ndi munthuyo. Kodi mwachita zinazake zolakwika zomwe zakubweretserani mavuto inuyo kapena anthu ena? M’malo modzikwiyira kapena kuloza chala munthu wina, mungachite bwino kuyesetsa kuti mukonze zinthu. Si bwinonso kukakamira kuti olakwa si inu chifukwa zimenezo zingangokulitsa vutolo. M’malomwake, ndi bwino kuphunzirapo kanthu pa zimene zachitikazo n’kuyesetsa kuchita zonse zofunika kuti muthetse vutolo.

Munthu wina akachita zolakwika, zimakhala zosavuta kuchita zinthu zosonyeza kuti sitinasangalale nazo. Komatu ndi bwino kutsatira malangizo amene Yesu anapereka akuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” (Mateyu 7:12) N’zodziwikiratu kuti mukalakwitsa zinazake, ngakhale zochepa, mumafuna ena akuchitireni chifundo kapenanso angoziponyera kunkhongo. Ndiye bwanji nanunso osachitira ena zomwezo?​—Aefeso 4:32.

MFUNDO ZOTHANDIZA KUTI TISAMALAKWITSE KWAMBIRI ZINTHU

Buku lina lotanthauzira mawu linanena kuti anthufe timalakwitsa zinthu chifukwa choganiza molakwa, kusadziwa zonse zokhudza nkhani inayake, komanso chifukwa chosakhala ndi chidwi ndi zinthu. Tonsefe tingavomereze kuti zimenezi zimatichitikiradi nthawi zina. Komabe ngati titamatsatira mfundo za m’Baibulo sitingamalakwitse zinthu kwambiri.

Mfundo imodzi imene ingatithandize ndi ya palemba la Miyambo 18:13. Lembali limati: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.” Apa mfundo ndi yakuti, tisanalankhule kapena kuchita chilichonse, tizimvetsa kaye nkhani yonse kenako n’kuganizira zoyenera kuchita. Kumvetsa bwino nkhani yonse kungathandize kuti tisamaweruze ena molakwa.

Mfundo ina ya m’Baibulo imati: “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.” (Aroma 12:18) Muziyesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize kuti muzikhala mwamtendere komanso mogwirizana ndi anthu ena. Mukamagwira ntchito ndi ena, muzichita zinthu mowaganizira komanso mwaulemu ndipo muziwayamikira ndiponso kuwalimbikitsa. Mukamachita zimenezi, zimakhala zosavuta kuti muzikhululukirana komanso kuiwala zinthu zolakwika zimene wina walankhula kapena kuchita. Zimenezi zingathandizenso kuti mukalakwirana chachikulu, muzithetsa nkhaniyo mwamtendere.

Ngati mwalakwitsa zinthu, muziyesetsa kuona zimene mungaphunzirepo. M’malo modziikira kumbuyo, ganizirani zimene mungachite kuti musonyeze makhalidwe abwino. N’kutheka kuti mukufunika kumasonyeza makhalidwe monga kuleza mtima, kukoma mtima, kudziletsa, kufatsa, mtendere ndiponso chikondi. (Agalatiya 5:22, 23) Ndipotu zimenezi zingakuthandizeni kudziwa zoyenera kudzapewa nthawi ina. N’zoona kuti sitingafune kuti anthu ena atilankhule kapena kutichitira zinthu zosakhala bwino. Komabe zoterezi zikachitika, si bwino kumangoganizira mmene zatikhudzira. Kuchitako tinthabwala kumathandiza kuti vutolo lisakule kwambiri.

UBWINO WOONA ZOLAKWA MOYENERA

Tikakhala ndi maganizo oyenera pa zolakwa zathu komanso za ena, timapewa mavuto ambiri. Timakhala ndi mtendere wamumtima komanso timakhala mwamtendere ndi anthu ena. Tikamayesetsa kuphunzirapo kanthu pa zimene talakwitsa, timakhala anzeru komanso anthu amatikonda. Sitingakhumudwe kwambiri kapenanso kumadziona ngati achabechabe. Kuzindikira kuti anzathunso akuyesetsa kuti asamalakwitse zinthu kwambiri, kungatithandize kuti tizigwirizana nawo. Komanso zinthu zimatiyendera bwino kwambiri tikamatsanzira Mulungu poyesetsa kukonda ena komanso kuwakhululukira ndi mtima wonse.​—Akolose 3:13.

Zimene a Margaret, omwe tawatchula koyambirira kuja analakwitsa, sizinasokoneze kwambiri macheza awo. Aliyense, kuphatikizapo iwowo, anangoziona kuti zinali zoseketsa basi moti anadyabe tchizi chija chopanda makaroni. Patapita zaka, adzukulu awo awiri aja anafotokozera ana awo zinthu zoseketsa zomwe zinachitika tsiku limenelo ndiponso mmene anachezera bwino ndi agogo awo. Ankadziwa kuti sichinali chifukwa choti agogo awowo sankadziwa kuphika, koma anangolakwitsa basi.

^ ndime 2 Mayina asinthidwa.

^ ndime 3 Kuti munthu akonze chakudyachi, amaphika makaroni ndipo kenako amaika tchizi pamwamba pa makaroniwo.