Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Khulupirira Yehova Ndipo Chita Zabwino”

“Khulupirira Yehova Ndipo Chita Zabwino”

“Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino . . . khala wokhulupirika m’zochita zako zonse.”—SAL. 37:3.

NYIMBO: 133, 63

1. Kodi Yehova anatipatsa luso liti?

YEHOVA anatipatsa luso lapadera kwambiri. Luso lake ndi lotha kuganiza. Izi zimatithandiza kuti tizithana ndi mavuto komanso kukonzekera zam’tsogolo. (Miy. 2:11) Iye anatipatsanso luso loti tizitha kukhala ndi mapulani komanso zolinga n’kumazikwaniritsa. (Afil. 2:13) Yehova anatipatsanso chikumbumtima chimene chimatithandiza kudziwa zinthu zoyenera ndi zosayenera. Izi zimatithandiza kuti tizipewa kuchita zoipa komanso kuti tizikonza zimene talakwitsa.—Aroma 2:15.

2. Kodi Yehova amafuna kuti tizigwiritsa ntchito bwanji luso lathu?

2 Yehova amafuna kuti tizigwiritsa ntchito bwino luso limene anatipatsali. Zili choncho chifukwa iye amatikonda komanso amadziwa kuti tikagwiritsa ntchito bwino luso limeneli timasangalala. M’Mawu ake timapezamo malangizo komanso mfundo zambiri zotilimbikitsa kuti tizigwiritsa ntchito bwino luso limene iye watipatsa. Mwachitsanzo, m’Malemba Achiheberi timapezamo mfundo yakuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.” Komanso muli malangizo akuti: “Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse.” (Miy. 21:5; Mlal. 9:10) M’Malemba Achigiriki timapezanso mawu oti: “Ngati tingathe, tiyeni tichitire onse zabwino.” Komanso akuti: “Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana.” (Agal. 6:10; 1 Pet. 4:10) Izi zikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti tizichita zinthu zimene zingathandize ifeyo komanso anthu ena.

3. Kodi anthufe patokha sitingathe kuchita zinthu ziti?

3 Koma Yehova amadziwanso kuti pali zinthu zina zimene sitingathe kuchita. Mwachitsanzo, patokha sitingakhale angwiro, sitingachotse uchimo ndipo sitingathetse imfa. Sitingaletsenso anthu ena kuchita zinthu zina chifukwa nawonso ali ndi ufulu wosankha. (1 Maf. 8:46) Ndipo ngakhale titadziwa zinthu zambiri bwanji, timakhalabe ngati ana pamaso pa Yehova.—Yes. 55:9.

Tikakumana ndi mavuto, ‘tizikhulupirira Yehova ndipo tizichita zabwino’

4. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

4 Choncho tiyenera kudalira Yehova n’kumamulola kuti azititsogolera chifukwa akhoza kutichitira zinthu zimene sitingakwanitse. Komabe tiyenera kuchita zimene tingathe kuti tithane ndi mavuto athu komanso tithandize anzathu. (Werengani Salimo 37:3.) Mwachidule tingati tiyenera ‘kukhulupirira Yehova, ndi kuchita zabwino.’ Komanso tiyenera ‘kukhala okhulupirika m’zochita zathu zonse.’ Tiyeni tikambirane zimene tingaphunzire kwa Nowa, Davide komanso atumiki ena okhulupirika amene anadalira Yehova. Tiona kuti panali zimene akanatha kuchita komanso zimene sakanatha. Koma iwo ankangoyesetsa kuchita zimene akanathazo.

ANTHU AMBIRI AKAMACHITA ZOIPA

5. Kodi zinthu zinali bwanji pa nthawi ya Nowa?

5 Nowa ankakhala m’dziko limene “linadzaza ndi chiwawa” komanso chiwerewere. (Gen. 6:4, 9-13) Iye ankadziwa kuti Yehova adzawononga dziko loipalo. Ngakhale zinali choncho zimene zinkachitikazo ziyenera kuti zinkamunyasa. Koma iye ankadziwa kuti panali zinthu zina zimene akanatha kuchita ndi zimene sakanatha kuchita.

Anthu akamatsutsa uthenga wathu (Onani ndime 6 mpaka 9)

6, 7. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene Nowa sanakanatha kuchita? (b) Kodi ifeyo tikufanana bwanji ndi Nowa?

6 Zimene Nowa sakanatha kuchita: Ngakhale kuti Nowa ankauza anthu uthenga wochenjeza, sakanatha kukamiza anthu oipawo kuti amvetsere uthenga wakewo. Iye sakanathanso kupangitsa kuti Chigumula chibwere mwamsanga. Koma iye ankakhulupirira kuti Yehova adzakwaniritsa lonjezo lake ndipo adzabweretsa Chigumula pa nthawi yake.—Gen. 6:17.

7 Ifenso tikukhala m’dziko loipa ndipo tikudziwa kuti posachedwapa Yehova aliwononga. (1 Yoh. 2:17) Sitingakakamize anthu kuti azimvetsera ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ Palibenso zimene tingachite kuti “chisautso chachikulu” chibwere mwamsanga. (Mat. 24:14, 21) Koma mofanana ndi Nowa, tiyenera kukhulupirira kuti posachedwapa Mulungu awononga dziko loipali. (Sal. 37:10, 11) Tikudziwa kuti nthawi yowononga dzikoli ikadzafika, Yehova sadzalola kuti ipitirire ngakhale ndi tsiku limodzi.—Hab. 2:3.

8. M’malo motaya mtima, kodi Nowa ankangoyesetsa kuchita chiyani? (Onani chithunzi patsamba 7.)

8 Zimene Nowa akanatha kuchita: M’malo motaya mtima chifukwa cha zomwe sakanatha kuchita, Nowa ankangoyesetsa kuchita zimene akanatha. Iye anali “mlaliki wa chilungamo” ndipo ankagwira mokhulupirika ntchito yochenjeza anthu imene Mulungu anamupatsa. (2 Pet. 2:5) Izi ziyenera kuti zinamuthandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Kuwonjezera pa ntchito yolalikira, Nowa ankagwiranso ntchito yomanga chingalawa.—Werengani Aheberi 11:7.

9. Kodi tingatsanzire bwanji Nowa?

9 Nafenso timayesetsa kuti tizichita ‘zambiri mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Ntchito ina imene tingagwire ndi yomanga nawo Nyumba za Ufumu kapena Malo a Misonkhano. Tingathenso kugwira nawo mongodzipereka ntchito zina pamisonkhano ikuluikulu. Tikhozanso kukatumikira pa Beteli kapena kumaofesi a omasulira mabuku. Koma ntchito yofunika kwambiri imene timagwira ndi yolalikira ndipo imatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Mlongo wina anati: “Ukamauza ena madalitso amene Ufumu udzabweretse, umaoneratu kuti anthu alibe chiyembekezo ndipo amaona ngati mavutowa sadzatha.” Mwachidule tingati ntchito yolalikira imatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti zimene Mulungu walonjeza zidzakwaniritsidwa. Imatithandizanso kuti tipitirizebe pa mpikisano wokalandira moyo.—1 Akor. 9:24.

TIKALAKWITSA ZINAZAKE

10. Fotokozani zimene zinachitikira Davide.

10 Yehova ananena kuti Mfumu Davide anali ‘munthu wapamtima pake.’ (Mac. 13:22) N’zoona kuti Davide anali wokhulupirika kwa Yehova. Komabe nthawi ina anachita tchimo lalikulu. Iye anachita chigololo ndi Bati-seba. Pofuna kubisa tchimoli, anakonza zoti mwamuna wa Bati-sebayo aphedwe kunkhondo. Ndipotu Davide anapatsira Uriya yemweyo kalata yonena zoti akaphedwe. (2 Sam. 11:1-21) Koma patapita nthawi, machimo ake anadziwika. (Maliko 4:22) Ndiye kodi Davide anatani?

Tikamadziimba mlandu pa machimo akale (Onani ndime 11 mpaka 14)

11, 12. (a) Kodi Davide sakanatha kuchita zinthu ziti? (b) Ngati talakwitsa zinazake n’kulapa kuchokera mumtima, kodi Yehova angatithandize bwanji?

11 Zimene Davide sakanatha kuchita: Davide sakanatha kusintha zimene analakwitsa chifukwa paja madzi akatayika saoleka. Komanso sakanapewa zotsatira za machimo akewo. Ndipotu zotsatira zina zinakhudza moyo wake wonse. (2 Sam. 12:10-12, 14) Koma iye anafunika kukhulupirira kuti Yehova akhoza kumukhululukira ngati atalapa kuchokera mumtima. Anafunikanso kukhulupirira kuti Yehova angamuthandize kupirira mavuto amene angabwere chifukwa cha machimo akewo.

12 Popeza tonsefe si angwiro, timachimwa. Machimo ena amakhala aakulu ndipo ena amakhala aang’ono. Ifenso tikalakwitsa zinthu zina zimakhala ngati madzi atayika ndipo sangaoleke. Timangofunika kupirira zotsatira zake. (Agal. 6:7) Zoterezi zikachitika timafunika kukhulupirira zimene Mulungu ananena. Paja iye analonjeza kuti ngati talapa kuchokera mumtima, akhoza kutikhululukira komanso kutithandiza kupirira mavuto amene angabwere chifukwa cha zolakwa zathuzo.—Werengani Yesaya 1:18, 19; Machitidwe 3:19.

13. Kodi Davide anatani kuti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova?

13 Zimene Davide akanatha kuchita: Davide analola kuti Yehova amuthandize kukhalanso naye pa ubwenzi wolimba. Choyamba, anavomereza pamene mneneri wa Yehova dzina lake Natani anabwera kudzamudzudzula. (2 Sam. 12:13) Komanso iye anapemphera kwa Yehova, anavomereza machimo ake ndipo analapa. Anasonyezanso kuti ankafunitsitsa kuti Mulungu ayambirenso kumukonda. (Sal. 51:1-17) Davide sanalole kuti machimo ake amulepheretse kutumikira Mulungu, koma anangophunzirapo kanthu. Komanso anayesetsa kuti asadzabwerezenso machimowo. Patatha zaka zambiri anamwalira ali wokhulupirika ndipo Yehova akumukumbukirabe.—Aheb. 11:32-34.

14. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Davide anachita?

14 Kodi tikuphunzira chiyani kwa Davide? Tikachita tchimo lalikulu, tiyenera kuvomereza tchimo lathulo, kulapa kuchokera mumtima ndiponso kupempha Yehova kuti atikhululukire. (1 Yoh. 1:9) Tiyeneranso kufotokozera akulu kuti atithandize kukhalanso pa ubwenzi ndi Yehova. (Werengani Yakobo 5:14-16.) Tikachita zimenezi, timasonyeza kuti tikukhulupirira zoti Yehova angatikhululukire. Komabe, tiyenera kuphunzirapo kanthu n’kuyambiranso kutumikira Yehova mokhulupirika.—Aheb. 12:12, 13.

TIKAKUMANA NDI MAVUTO ENA

Tikadwala (Onani ndime 15)

15. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Hana?

15 Mwina mungaganizire za atumiki enanso akale omwe anasonyeza kuti ankakhulupirira Yehova ndipo anachita zonse zomwe angathe. Mwachitsanzo, Hana sakanathetsa yekha vuto lake losabereka. Koma ankakhulupirira kuti Yehova amuthandiza ndipo anapitiriza kumulambira pachihema. Iye ankapempheranso kuchokera pansi pa mtima. (1 Sam. 1:9-11) Hana ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe. Ngati tikudwala kapena tili ndi vuto linalake limene sitingalithetse patokha, tiyenera kutulira Yehova nkhawa zathu n’kumakhulupirira kuti atithandiza. (1 Pet. 5:6, 7) Ndiponso tiziyesetsa kuchita zomwe tingathe kuti tizipindula ndi misonkhano komanso zonse zimene Yehova amatipatsa.—Aheb. 10:24, 25.

Mwana akasiya kutumikira Yehova (Onani ndime 16)

16. Kodi makolo angaphunzire chiyani kwa Samueli?

16 Kodi makolo amene ana awo asiya kutumikira Yehova angaphunzire chiyani kwa Samueli? Iye sakanatha kuumiriza ana ake kuti azitsatira mfundo za Yehova zimene anawaphunzitsa. (1 Sam. 8:1-3) Choncho anangosiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Koma Samueli anayesetsa kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova ndipo ankachita zokondweretsa mtima wake. (Miy. 27:11) Masiku ano makolo ambiri achikhristu amakumananso ndi vuto ngati lomweli. Koma amakhulupirira kuti Yehova ndi wokonzeka kulandiranso olakwa omwe alapa mofanana ndi bambo wa mu fanizo la Yesu la mwana wolowerera. (Luka 15:20) Makolo amenewa amayesetsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ndipo amadziwa kuti chitsanzo chawo chingathandize ana awowo kuti abwerere.

Tikakhala ndi mavuto azachuma (Onani ndime 17)

17. Kodi chitsanzo cha mkazi wamasiye chingatilimbikitse bwanji?

17 Chitsanzo china ndi cha mkazi wamasiye wosauka wa m’nthawi ya Yesu. (Werengani Luka 21:1-4.) Palibe chimene mayiyu akanachita pa nkhani ya zoipa zimene zinkachitika pakachisi. (Mat. 21:12, 13) Ndiponso sakanatha kuchita chilichonse kuti athetse umphawi wake. Koma anapereka mofunitsitsa “timakobidi tiwiri tating’ono,” timene ‘akanatha kuchirikiza nato moyo wake.’ Mayiyu anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Ndipo ankadziwa kuti ngati angaike zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba, Yehova adzamupatsa zofunika pa moyo. Chikhulupiriro ndi chomwe chinathandiza mayi wamasiyeyu kuti apereke ndalama zothandiza pa kulambira koona. Ifenso tiyenera kukhulupirira kuti tikamafunafuna Ufumu choyamba, Yehova adzatipatsa zofunika pa moyo.—Mat. 6:33.

18. Perekani chitsanzo cha m’bale wina amene anali ndi maganizo oyenera.

18 Masiku anonso pali abale ndi alongo ambiri omwe asonyeza kuti amakhulupirira Yehova ndipo akakumana ndi mavuto amachita zomwe angathe. Chitsanzo ndi m’bale wina dzina lake Malcolm, yemwe anakhalabe wokhulupirika mpaka pamene anamwalira m’chaka cha 2015. Kwa zaka zambiri, iye ndi mkazi wake anakhala akutumikira Yehova ndipo anakumana ndi mavuto ambiri. Iye anati: “Nthawi zina zinthu zimasintha mosayembekezereka ndipo zimakhala zovuta kupirira. Koma Yehova amadalitsa anthu amene amamudalira.” M’bale Malcolm anapereka malangizo akuti: “Muzipemphera kuti Yehova akuthandizeni kuchita zonse zomwe mungathe pomutumikira. Ndipo muziganizira kwambiri zinthu zimene mungathe kuchita osati zomwe simungakwanitse.” *

19. (a) N’chifukwa chiyani lemba la chaka chino lili loyenera? (b) Kodi inuyo mungatsatire bwanji malangizo a m’lembali?

19 Pamene dzikoli ‘likuipiraipirabe’ tizikumana ndi mavuto ambirimbiri. (2 Tim. 3:1, 13) Koma tisamalole kuti mavuto amene tikukumana nawo atifooketse. M’malomwake tizikhulupirira kwambiri Yehova n’kumachita zimene tingathe. Mpake kuti lemba la chaka chino cha 2017 likuti: “Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino.”—Sal. 37:3.

Lemba la chaka cha 2017: “Khulupirira Yehova Ndipo Chita Zabwino”-Salimo 37:3.