Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Khulupilila Yehova Ndipo Cita Zabwino”

“Khulupilila Yehova Ndipo Cita Zabwino”

“Khulupilila Yehova ndipo cita zabwino . . . khala wokhulupilika m’zocita zako zonse.” —Sal. 37:3.

NYIMBO: 133, 63

1. Kodi Yehova anatilenga ndi maluso anji apadela?

YEHOVA anatilenga ndi maluso apadela. Anatipatsa luso loganiza pothetsa mavuto, na luso lokonzekela za m’tsogolo. (Miy. 2:13) Anatipatsa nzelu zopanga mapulani, na kudziŵa mowakwanilitsila mapulaniwo. (Afil. 2: 3) Anatilenga na cikumbumtima, cimene ni luso lobadwa nalo, lotithandiza kudziŵa cabwino ndi coipa. Limatithandizanso kuwongolela zolakwa zathu.—Aroma 2: 15.

2. Kodi Yehova amafuna kuti tiziseŵenzetsa bwanji maluso athu?

2 Yehova amafuna kuti tiziseŵenzetsa bwino maluso athu. Cifukwa cake n’cakuti amatikonda. Amadziŵanso kuti tikaseŵenzetsa mphatso zimenezi timapindula. Kupitila m’Mau ake, Yehova amatilangiza mobweleza-bweleza kuti tiziseŵenzetsa bwino maluso athu. Mwacitsanzo, m’Malemba Aciheberi, timapezamo mau akuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulila,” ndi akuti: “Ciliconse cimene dzanja lako lapeza kuti licite, ucicite ndi mphamvu zako zonse.” (Miy. 21:5; Mlal. 9:10) M’Malemba Acigiriki Acikhiristu, timauzidwa kuti: “Ngati tingathe, tiyeni ticitile onse zabwino.” Ndi kutinso: “Molingana ndi mphatso imene aliyense walandila, igwilitseni nchito potumikilana monga oyang’anila abwino.” (Agal. 6:10; 1 Pet. 4:10) N’zoonekelatu kuti Yehova amafuna tizicita zinthu zopindulitsa ife ndi anthu ena.

3. N’zinthu ziti zimene anthu sangakwanitse kucita?

3 Koma Yehova amadziŵanso zinthu zina zimene sitingazikwanitse. Pa ise tekha sitingacotsepo kupanda ungwilo, ucimo, na imfa. Komanso, sitingalamulile anthu pa zocita zawo, aliyense ali na ufulu wake. (1 Maf. 8:46) Ndiponso, kaya tikhale na nzelu kapena luso labwanji, tidzakhalabe monga ana kwa Yehova.—Yes. 55:9

Polimbana ndi mavuto, dalilani Yehova, ndipo citani zabwino

4. Kodi tidzaphunzila ciani m’nkhani ino?

4 Pa zocitika zonse, tifunika kudalila Yehova kuti atitsogolele. Tizikhulupilila kuti adzaticilikiza pa zimene tiyenela kucita, ndipo adzaticitila zimene sitingakwanitse. Koma nafenso tifunika kucitapo kathu kuti tithetse mavuto amene tingathe, ndi kuthandiza ena. (Ŵelengani Salimo 37:3.) Mwacidule, tifunika kucita zonse ziŵili, kudalila Yehova ndi kucita zabwino, kapena kuti kucitapo kanthu mokhulupilika. Conco, tiyeni tione zimene tingaphunzile pa zitsanzo za Nowa, Davide, ndi atumiki ena okhulupilika a Yehova amene anam’dalila na kucitapo kanthu. Yesani kuzindikila zimene sakanakwanitsa kucita, ndi zimene anakwanitsa kucita.

PAMENE TAZINGIDWA NDI ANTHU OIPA

5. Fotokozani zimene Nowa anayang’anizana nazo.

5 Nowa anali kukhala m’dziko ‘lodzala ndi ciwawa’ ndi zaciwelewele. (Gen. 6:4, 9-13) Ngakhale kuti anadziŵa kuti Yehova adzawononga anthu oipawo, iye anali wokhumudwa ndi makhalidwe awo osaopa mulungu. Koma Nowa anadziŵanso kuti zinthu zina sangazikwanitse kucita, koma zina angakwanitse.

Kuletsa nchito yathu (Onani palagilafu 6 mpaka 9)

6, 7. (a) N’ciani cimene Nowa sakanakwanitsa kucita? (b) Nanga n’zofanana bwanji kwa ifenso?

6 Zimene Nowa sakanakwanitsa kucita: Olo kuti Nowa analalikila za cenjezo la Yehova mokhulupilika, iye sakanatha kuumiliza anthu oipa kulandila uthengawo. Sakanathanso kufulumizitsa Cigumula. Nowa anafunika kukhulupilila Yehova kuti adzasunga lonjezo lake la kucotsa zoipa zonse, ndi kuti adzacita zimenezo panthawi yake.—Gen. 6:17.

7 Ifenso tikukhala m’dziko lodzala ndi zoipa, ndipo tidziŵa kuti Yehova adzaliwononga. (1 Yoh. 2:17) Sitingakakamize anthu kulandila “uthenga wabwino wa Ufumu.” Komanso, “cisautso cacikulu” sitingacifulumizitse ngakhale pang’ono. (Mat. 24:14, 21) Motengela Nowa, tiyeni tikhale na cikhulupililo colimba, podziŵa kuti Mulungu adzagwapo lomba apa. (Sal. 37:10, 11) Ndife otsimikiza kuti Yehova sadzacedwa ngakhale ndi tsiku limodzi, kuwononga dziko loipali.—Hab. 2:3.

8. Kodi Nowa anacita ciani na zimene akanakwanitsa kucita? (Onani pikica yakuciyambi.)

8 Zimene Nowa anakwanitsa kucita: M’malo molefuka ndi zimene sakanakwanitsa kucita, Nowa anasumika maganizo pa zimene anakwanitsa kucita. Monga “mlaliki wa cilungamo,” iye analalikila mokhulupilika uthenga wocenjeza umene anatumidwa. (2 Pet. 2:5) Zimenezi zinalimbitsa cikhulupililo ca Nowa. Anagwilitsilanso maluso ake na nzelu zake pa nchito imene Mulungu anam’patsa, yomanga cingalawa.—Ŵelengani Aheberi 11:7.

9. Tingatengele bwanji citsanzo ca Nowa?

9 Monga Nowa, tifunika kukhala na zocita ‘zambili mu nchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Nchito zimenezi zingaphatikizepo nchito yomanga, kukonzanso maholo kapena mabwalo olambilila, nchito zokhudza misonkhano ya dela ndi ya cigawo, kapena kutumikila pa ofesi ya nthambi kapena pa ofesi yomasulila mabuku. Koma yoposa zonse, n’kutangwanika m’nchito yolalikila, podziŵanso kuti imalimbitsanso ciyembekedzo cathu. Mlongo wina wokhulupilika anati: “Ukauzako anthu za madalitso a Ufumu wa Mulungu, umazindikila kuti anthuwo alibiletu ciyembekezo ciliconse. Ndipo amaona mavuto awo kuti sadzatha.” Inde, nchito yolalikila imatipatsa kapenyedwe kabwino ka zam’tsogolo, ndipo imatilimbikitsa kuti tisatope pa mpikisano wathu wa ku moyo.—1 Akor. 9:24.

TIKALAKWITSA ZINTHU

10. Fotokozani zinacitika ndi Davide.

10 Yehova anati Mfumu Davide anali “munthu wapamtima [pake].” (Mac. 13:22) Gawo lalikulu la moyo wake, Davide anali munthu wokhulupilika. Ngakhale n’conco, panthawi zina anacita macimo akulu-akulu. Anacita cigololo na Bati-seba. Kuipitsilatu zinthu, anayesa kubisa chimo lake pokonza ciwembu cakuti Uriya, mwamuna wa Bati-seba, akaphedwe kunkhondo. Davide anafika mpaka potuma Uliya kukapeleka kalata yokhala na malangizo amene anacititsa kuti Uliyayo aphedwe. (2 Sam. 11:1-21) Chimo la Davide silikanabisikabe. (Maliko 4:22) Koma pamene linaululika, kodi Davide anacita ciani?

Macimo akale (Onani palagilafu 11 mpaka 14)

11, 12. (a) Sakanakwanitsa kucita ciani Davide? (b) Ngati tinacita macimo aakulu koma talapa, tizikhulupilila kuti Yehova adzaticitila ciani?

11 Zimene Davide sakanakwanitsa kucita: Kwa Davide, inali nkhani ya madzi akatayika sayoleka, sakanatha kuzibwezela m’mbuyo. Sakanathanso kulewa zotulukapo za macimo ake. Ndipo zina anakhala nazo umoyo wake wonse. (2 Sam. 12:10-12, 14) Conco, anafunika kukhulupilila kuti ngati alapa, Yehova adzam’khululukila, ndi kum’thandiza kupilila zotulukapo zimenezo.

12 Pokhala opanda ungwilo, tonse timalakwa. Zolakwa zina zimakula msinkhu kuposa zina. Ndipo nthawi zina, n’zosatheka kusintha zimene tinalakwitsa. Timangofunikila kukhala ndi zotulukapo zake kwa umoyo wathu wonse. (Agal. 6:7) Koma tiyenela kukhulupilila kuti ngati tinalapa, Yehova adzaticilikiza m’mavuto athu, olo kuti mavutowo ni odzibweletsela tekha.—Ŵelengani Yesaya 1:18, 19; Machitidwe 3:19.

13. Kodi Davide anacila bwanji mwauzimu?

13 Zimene Davide anakwanitsa kucita: Davide analola Yehova kum’cilitsa mwauzimu. Njila imodzi imene anacitila zimenezi ni kulandila uphungu kwa woimila Yehova, mneneli Natani. (2 Sam. 12:13) Cina, Davide anapemphela kwa Yehova, kuulula macimo ake, kulapa mocokela pansi pa mtima, ndi kucondelela Yehova kuti am’khululukile. (Sal. 51:1-17) M’malo molola cikumbumtima cacisoni kum’khwethemulilatu, Davide anatengelapo phunzilo pa zolakwa zake. Sanawacitenso macimowo. M’kupita kwa zaka, Davide anamwalila ali wokhulupilika, ndipo mbili ya cikhulupililo cake inasindikizika m’cikumbukilo ca Yehova.—Aheb. 11:32-34.

14. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Davide?

14 Kodi tingaphunzile ciani pa citsanzo ca Davide? Tikagwela m’chimo lalikulu, tifunika kulapa moona mtima ndi kupempha cikhululukilo ca Yehova. Tifunika kuulula macimo athu kwa iye. (1 Yoh. 1:9) Tifunikanso kufikila akulu, kuti atipatse cithandizo cauzimu. (Ŵelengani Yakobo 5:14-16.) Ngati titsatila ndondomeko ya Yehova, timaonetsa kukhulupilila lonjelo lake lakuti adzaticilitsa na kutikhululukila. Pambuyo pake, tifunika kutengelapo phunzilo pa zolakwa zathu, kupitiliza kutumikila Yehova, ndi kuyang’ana kutsogolo mwacidalilo.—Aheb. 12:12, 13.

PA ZOCITIKA ZINA

Mavuto a kudwala (Onani palagilafu 15)

15. Tingaphunzile ciani pa citsanzo ca Hana?

15 Na imwe mungakumbukileko atumiki ena okhulupilika akale, amene anadalila Yehova ndi kucitapo kanthu moyenelela. Mwacitsanzo, palibe cimene Hana akanacita payekha kuti athetse vuto la kusabeleka. Koma anakhulupilila kuti Yehova adzam’tonthonza. Conco anapitiliza kulambila Mulungu pa kacisi, ndi kum’condelela m’pemphelo. (1 Sam. 1:9-11) Kodi si citsanzo cabwino kwa ife? Ngati tikuvutika ndi matenda kapena mavuto ena amene sitingawathetse, tiyenela kum’tulila Yehova nkhawa zathuzo, podziŵa kuti adzatisamalila. (1 Pet. 5:6, 7) Tiyenelanso kucita zimene tingakwanitse kuti tizipindula ndi misonkhano yathu na zinthu zina zauzimu.—Aheb. 10:24, 25

Ana opanduka (Onani palagilafu 16)

16. Kodi makolo angaphunzile ciani kwa Samueli?

16 Nanga bwanji kwa makolo okhulupilika amene ana awo anapanduka? Mneneli wacikulile Samueli sakanakwanitsa kuumiliza ana ake kuti akhalebe okhulupilika pa mfundo zolungama zimene anawaphunzitsa. (1 Sam. 8:1-3) Anafunikila kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Ngakhale n’conco, Samueli analimbitsa cikhulupililo cake-cake kwa Yehova, ndi kucita zinthu zokondweletsa Atate wake wakumwamba. (Miy. 27:11) Lelo linonso, makolo ambili acikhiristu, amadzipeza mu mkhalidwe umenewo. Iwo amakhulupilila kuti mofanana ndi tate wa mu fanizo la mwana woloŵelela, Yehova amayembekezela mwacidwi kulandila anthu olapa. (Luka 15:20) Komanso, makolo amenewo amakhalabe okhulupilika kwa Yehova, ndi kupemphelela kuti citsanzo cawo cabwino ciwatunthe anawo kubwelela.

Kusoŵa ndalama (Onani palagilafu 17)

17. N’cifukwa ciani citsanzo ca mkazi wamasiye n’colimbikitsa?

17 Ganizilaninso za Mkazi wamasiye wosauka wa m’nthawi ya Yesu. (Ŵelengani Luka 21:1-4.) Palibe cimene akanacitapo pa zacinyengo zimene zinali kucitika pa kacisi. (Mat. 21:12, 13) Mwinanso palibe kweni-kweni zimene akanacita kuti athetse umphawi wake. Koma iye anaponya ‘tumakhobili tuŵili twatung’ono’ na mtima wonse. Inde, ndalama “zonse zimene akanatha kucilikiza nazo moyo wake.” Mkaziyu anaonetsa kuika cidalilo conse mwa Yehova, podziŵa kuti akaika zinthu zauzimu patsogolo, Mulungu adzasamalila zosoŵa zake zakuthupi. Cifukwa ca cikhulupililo cake, mkaziyo anacilikiza makonzedwe a kulambila koona apanthawiyo. Ifenso timakhulupilila kuti tikafunafuna Ufumu coyamba, Yehova adzasamalila zosoŵa zathu zakuthupi.—Mat. 6:33.

18. Fotokozani citsanzo ca mtumiki wa Mulungu wamakono pa kaonedwe kabwino ka zinthu.

18 Atumiki a Mulungu ambili amakono, naonso aonetsa cikhulupililo mwa Yehova ndi kucita zinthu moyenelela. Citsanzo ni m’bale Malcolm, amene anakhalabe wokhulupilika mpaka imfa yake mu 2015. Pa zaka zoculuka zimene iye na mkazi wake anatumikila Yehova, anakumana na zothetsa nzelu zambili. Iye anati: “Nthawi zina zinthu zimangocitika mu umoyo, zovuta kucita nazo. Koma Yehova nthawi zonse amadalitsa amene amam’dalila.” Ndiyeno analangiza kuti: “Cofunika ni pemphelo kuti ukhalebe wokangalika potumikila Yehova. Sumika maganizo pa zimene ungakwanitse, osati zimene sungakwanitse.” *

19. (a) N’cifukwa ninji lemba la caka ca 2017 n’loyeneleladi? (b) Nanga imwe pa canu, lidzakuthandizani bwanji lembali mu umoyo wanu?

19 Pamene dzikoli ‘likuipila-ipila,’ tingayembekezele zinthu zovuta kwambili kutsogoloku. (2 Tim. 3:1, 13) Conco, tifunika kudzikonzekeletsa. Tisamakhwethemuke tikakumana ndi zovuta pali pano. Tikulitse cidalilo mwa Yehova pamene ticitapo kanthu moyenelela. Lemba la Salimo 37:3 limati: “Khulupilila Yehova ndipo cita zabwino.” Ha, likomelenji nanga monga lemba la caka ca 2017!

Lemba lathu la caka ca 2017: “Khulupilila Yehova ndipo cita zabwino.”

^ par. 18 Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 2013, mapeji 17-20.