Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

N’cifukwa Ciani Kudzicepetsa N’kofunikabe?

N’cifukwa Ciani Kudzicepetsa N’kofunikabe?

“Koma nzelu zimakhala ndi anthu odzicepetsa.”—MIY. 11:2.

NYIMBO: 38, 69

1, 2. N’cifukwa ciani munthu amene anali wodzicepetsa anakaniwa na Mulungu? (onani pikica pamwambapa)

PAMENE SAULI, mfumu ya Aisiraeli, anayamba ulamulilo wake, anali munthu wodzicepetsa ndi wopatsiwa ulemu. (1 Sam. 9:1, 2, 21; 10:20-24) Koma posapita nthawi, anayamba kucita zinthu modzitama. Pamene mneneli Samueli anacedwa kufika ku Giligala, Sauli anataya mtima. Apa n’kuti afilisiti akukonzekela kuwathila nkhondo, ndipo Aisiraeli ena anali atayamba kucoka kwa Sauli. N’kutheka kuti m’maganizo mwake anati, ‘N’cedwa pano, nifunika kucitapo kanthu mwamsanga.’ Basi iye n’kupeleka nsembe kwa Mulungu, cinthu cimene sanali kuloledwa kucita. Zimenezi zinakwiitsa Yehova kwambili.—1 Sam. 13:5-9.

2 Samueli atafika ku Giligala, anadzudzula Sauli. Koma m’malo molandila uphungu, Sauli anapeleka zifukwa zodzikhululukila, kukankhila ena mlanduwo, ndi kucepetsa colakwa cake. (1 Sam. 13:10-14) Ici ndiye cinali ciyambi ca masoka amene pothela pake anam’tayitsa ufumu wake. Koma coipilatu n’cakuti anakaniwa na Yehova. (1 Sam. 15:22, 23) Conco, ngakhale kuti ciyambi ca Sauli cinali cabwino, mapeto ake anali tsoka lomvetsa cisoni.—(1 Sam. 31:1-6.)

3. (a) Kodi anthu ambili amakuona bwanji kudzicepetsa? (b) Kodi tidzapeza mayankho pa mafunso ati?

3 Cifukwa ca mzimu wa mpikisano masiku ano, anthu ambili amacita zinthu n’colinga cakuti adziŵike. Mwa ici, sakhala odzicepetsa. Mwacitsanzo, munthu wina wochuka m’mafilimu atakhala wandale anati: “Kudzicepetsa si mbali yanga, ndipo nipemphela kuti kusakakhaleko mbali yanga.” Koma n’cifukwa ciani kudzicepetsa kuli kofunikabe? Ndipo kudzicepetsa n’ciani maka-maka? Nanga tingakhale bwanji odzicepetsa pamene zinthu n’zovuta, kapena pamene athu ena atisoŵetsa mtendele? Nkhani ino idzayankha mafunso aŵili oyamba. Funso yacitatu idzayankhiwa mu nkhani yotsatila.

N’CIFUKWA CIANI KUDZICEPETSA N’KOFUNIKA?

4. Kodi kucita zinthu modzikweza n’kucita bwanji?

4 Baibo imasiyanitsa kudzicepetsa ndi kudzikweza. (Ŵelengani Miyambo 11:2.) Mwanzelu, Davide anapempha Yehova kuti “mundiletse kucita modzikuza.” (Sal. 19:13) Kodi “kucita modzikuza” kumatanthauza ciani? Ngati munthu alephela kuyembekezela kapena kuleza mtima, koma acita zinthu zimene alibe nazo cilolezo, kumeneko ndiye kudzikuza, kapena kuti kudzimvela. Cifukwa ndife opanda ungwilo, nthawi zina tonse timacita zinthu modzikuza. Koma monga taonela m’citsanzo ca Mfumu, ngati tayamba kudzikudza, tidzadzipeza m’mavuto aakulu ndi Mulungu. Salimo 119:21 imakamba za Yehova kuti: ‘Mumadzudzula odzikuza.’ Koma cifukwa ciani?

5. N’cifukwa ciani tifunika kupewelatu kucita zinthu modzikweza?

5 Kucita cinthu modzikweza kumasiyana ndi kuphonyetsa cabe zinthu. Tikacita zinthu modzikweza, coyamba timalephela kulemekeza Yehova monga Mfumu yathu. Caciŵili, ngati tikonda kucita zinthu m’mphamvu zathu, posapita nthawi, kapena m’kupita kwa nthawi, tidzayamba kukwesana ndi anzathu. (Miy. 13:10) Ndipo cacitatu, zikadziŵika poyela kuti tinacita zinthu modzigangila (m’mphamvu zathu), tikhoza kucititsidwa manyazi kapena kudzitonzetsa. (Luka 14: 8, 9) Mulimonse, kudzikweza kulibe cotulukapo cabwino. Monga mwa kunena kwa Malemba, kudzicepetsa ndiko njila yanzelu nthawi zonse.

KODI TINGAONETSE BWANJI KUDZICEPETSA?

6, 7. Kodi kudzicepetsa n’ciani, ndipo kuli na ubwino wanji?

6 M’Baibo, kudzicepetsa kumatanthauza kupewa mzimu wonyada ndi mwano. (Afil. 2:3) Munthu wodzicepetsa amazindikila maluso ake ndi zinthu zimene amakwanitsa kucita bwino. Komanso, amazindikilanso zolakwa zake na kuzivomeleza. Savutikanso kulandila maganizo a ena ndi atsopano. Inde, Yehova amakondwela ngako na munthu wodzicepetsa.

7 M’Baibo, kudzicepetsa kumatanthauzanso kusadziika pamene suli, komanso kudziŵa bwino zimene sungakwanitse. Inde, kudzidziŵa bwino kumeneko kudzatithandiza kudziŵa mocitila zinthu, kapena mokhalila ndi anthu ena.

8. Kodi zizindikilo za mzimu wa kudzikuza n’ciani?

8 Nanga tingadziŵe bwanji kuti tayamba kudzikuza? Tiyeni tione zizindikilo zingapo. Tingayambe kudziona ife eni, kapena utumiki wathu monga ndiye wofunika kwambili. (Aroma 12:16) Tingamacitenso zinthu mofuna kukopela cidwi ca anthu pa ife. (1 Tim. 2:9, 10) Mwinanso tingafune kumalimbikitsa njila zina zake, cabe cifukwa ca udindo wathu, maganizo athu, kapena pofuna kulimbikitsa maganizo a anthu amene timamvana nawo. (1 Akor. 4:6) Kambili, tikayamba kucita zinthu mwanjila imeneyi, ndiye kuti mzimu wa kudzikuza wayamba kutiloŵelela.

9. N’ciani cinapangitsa anthu ena kuyamba kudzikweza? Pelekani citsanzo ca m’Baibo.

9 Munthu aliyense angayambe kuonetsa mzimu wodzikweza ngati agonja ku zilakolako za thupi. Mwacitsanso, kukhala na zolinga zapamwamba zakuthupi, kaduka, ndi kusalamulila mkwiyo, zapangitsa ambili kukhala odzikweza. Anthu ochulidwa m’Baibo monga Abisalomo, Uziya, ndi Nebukadinezara, anakhala odzikuza cifukwa cogonja ku “nchito za thupi.” Ndipo Yehova anawatsitsa mocititsa manyazi.—2 Sam. 15:1-6; 18:9-17; 2 Mbiri 26:16-21; Dan. 5:18-21.

10. N’cifukwa ciani tiyenela kupewa kuganizila molakwa zolinga za ena? Pelekani citsanzo ca m’Baibo.

10 Palinso zifukwa zina zingapangitse munthu kucita zinthu modzikuza. Mwacitsanso, ganizilani nkhani za m’Baibo za pa Genesis 20:2-7 ndi Mateyu 26:31-35. Kodi tingati Abimeleki ndi Petulo anacita zinthu cifukwa ca mzimu wodzikweza? Kapena kodi n’cifukwa cakuti analibe cithunzi bwino-bwino, mwina anangolephela kuzindikila bwino? Popeza sitikhoza kudziŵa za mumtima wa munthu, tiyenela kupewa kuganizila molakwa zolinga za anthu ena.—Ŵelengani Yakobo 4:12.

KUZINDIKILA MALO ANTHU

11. Kodi kuzindikila malo anthu m’makonzedwe a Mulungu kumaonetsa ciani?

11 Kudzicepetsa kumayamba ndi kuzindikila malo athu m’makonzedwe a Mulungu. Monga Mulungu wadongosolo, Yehova amapatsa aliyense wa ife malo ake, kapena mbali yake, m’banja la Mulungu. Ngakhale kuti tili na mbali zosiyana-siyana, tonse ndife ofunika. Mwa cisomo cake, Yehova anatipatsa mphatso ndi maluso osiyana-siyana. Tiyenela kuziseŵenzetsa pa kulemekeza Mulungu na kuthandiza anthu ena. (Aroma 12:4-8) Yehova watipatsa udindo, umenenso ni umboni wakuti amatidalila na kutilemekeza.—Ŵelengani 1 Petulo 4:10.

Tingaphunzilenji kwa Yesu utumiki wathu ukasintha? (Onani palagilafu 12-14)

12, 13. N’cifukwa ciani sitiyenela kudabwa ngati malo athu m’gulu akusintha nthawi ndi nthawi?

12 Komabe, ni bwino kuzindikila kuti malo athu m’makonzedwe a Mulungu si acikhalile. Akhoza kusintha nthawi iliyonse. Mwacitsanso, ganizilani citsanzo ca Yesu. Poyamba iye anali yekha na Yehova. (Miy. 8:22) Kenako, anathandizila kulenga angelo ena, zinthu zakuthambo, pothela pake anthu. (Akol. 1:16) Pambuyo pakenso, Yesu anapatsidwa mbali ina pano padziko lapansi. Coyamba anabadwa monga khanda, ndipo anakula. (Afil. 2:7) Pambuyo pa imfa yake yodzipeleka nsembe, Yesu anabwelela ku moyo wauzimu kumwamba ndipo anakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu mu 1914. (Aheb. 2:9) Kodi ndiye kunali kusintha kotsiliza? Ayi. Pambuyo pa ulamulilo wake wa zaka 1000, Yesu adzapeleka Ufumu wake m’manja mwa Yehova, kuti ‘Mulungu akakhale zinthu zonse kwa aliyense.’—1 Akor. 15:28.

13 Monga Yesu, ifenso tiyenela kuyembekezela kuti utumiki wathu ungasinthe nthawi ndi nthawi. Kambili, izi zimacitika cifukwa ca zigamulo zimene zimapangidwa. Mwacitsanzo, kodi munali mbeta, koma lomba muli pabanja? Kodi tsopano muli ndi ana? Kodi m’mbuyomu munasintha zinthu pa umoyo wanu kuti muyambe utumiki wa nthawi zonse? Cosankha ciliconse cinabweletsa mwayi kwa inu komanso maudindo. Ndipo kusintha kwa zinthu, kukhoza kuwonjezela kapena kucepetsa utumiki wanu. Kodi ndimwe wacicepele, kapena mukukalamba? Kodi muli ndi thanzi labwino kapena m’madwala-dwala? Yehova amaona mbali imene tingam’tumikile bwino kwambili. Iye amalandila zimene tingakwanitse, ndipo amayamikila kwambili.—Aheb. 6:10.

14. Kodi kudzicepetsa kungatithandize bwanji kukhala okhutila ndi acimwemwe pamalo alionse amene tilipo?

14 Yesu anakondwela na mbali iliyonse imene anapatsiwa, nafenso tingacite cimodzi-modzi. (Miy. 8:30, 31) Munthu wodzicepetsa amakhala wokhutila ndi udindo umene ali nawo mumpingo. Satagwanika m’maganizo ndi maudindo amene angapeze mtsogolo, kapena maudindo amene ena akupeza ayi. Maganizo ake amangosumika pa kuyendetsa bwino udindo umene ali nawo, ndi kusangalala nawo, cifukwa couona kuti ni wocokela kwa Yehova. Panthawi imodzi-modzi, amalemekeza na mtima wonse maudindo amene Yehova wapeleka kwa ena. Kudzicepetsa kumatithandiza kulemekeza ena ndi kuwacilikiza.—Aroma 12:10.

ZIMENE KUDZICEPETSA SIKUTANTHAUZA

15. Kodi tingaphunzile ciani pa kudzicepetsa kwa Gidiyoni?

15 Gidiyoni anali citsanzo cabwino ngako ca kudzicepetsa. Pamene mngelo wa Yehova anaonekela kwa Gidiyoni, iye modzicepetsa anati sanali woyenelela udindowo pokhalanso wocokela ku banja lotsika. (Ower. 6:15) Koma pamene analandila udindowo kwa Yehova, Gidiyoni anayesetsa kuumvetsa udindo wake na kuusamalila bwino lomwe. Anadalilanso Yehova kuti amutsogolele. (Ower. 6:36-40) Ngakhale kuti Gidiyoni anali munthu wolimba mtima, anacitabe zinthu mosamala ndi mwanzelu. (Ower. 6:11, 27) Iye sanaumilile nga-nga-nga paudindo pofuna kuchuka ayi. Atangotsiliza nchito imene anapatsidwa, anali wokondwa kubwelela pamalo ake akale.—Ower. 8:22, 23, 29.

16, 17. Kodi munthu wodzicepetsa amaganizila ciani pofuna kupita patsogolo mwauzimu?

16 Koma kudzicepetsa sikutanthauza kuti sitingakalamile udindo kapena utumiki woonjezela iyai. Malemba amalimbikitsa tonse kupita patsogolo. (1 Tim. 4:13-15) Koma kodi kupita patsogolo nthawi zonse kumatanthauza kulandila udindo wina? Osati kweni-kweni. Ndi dalitso la Yehova, tikhoza kupita patsogolo mwauzimu pa udindo uliwonse umene tilipo. Tikhoza kunolela-nolela luso limene Mulungu anatipatsa ndi kupitiliza kucita nchito zabwino.

17 Munthu wodzicepetsa asanavomeleze udindo winawake, amayamba waona ngati angaukwanitse bwino-bwino. Moona mtima, amapenda mmene mikhalidwe yake ilili. Mwacitsanzo, kodi akalandila udindo wowonjezela umenewo, adzakwanitsabe kusamalila zinthu zina zofunika? Kodi ena a maudindo amene ali nawo pali pano, angafunikile kusiila abale ena kuti asamalile bwino udindo watsopano? Ngati yankho n’lakuti ayi pa funso imodzi kapena onse aŵiliwa, mwina zingakhale bwino kuti udindo watsopanowo upite kwa munthu wina amene angausamalile bwino. Ngati tidzipenda moona mtima ndi mwanzelu, tidzapewa kudziiunjikila maudindo ambili cifukwa codalila maluso athu. Ngati ndife odzicepetsa, tidzanena kuti ayi.

18. (a) Kodi kudzicepetsa kudzatithandiza kucita ciani tikalandila udindo watsopano? (b) Nanga Aroma 12:3 imati ciani za munthu wodzicepetsa?

18 Tikalandila udindo watsopano, citsanzo ca Gidiyoni ciyenela kutikumbutsa kuti sitingapambane popanda citsogozo ca Yehova ndi dalitso lake. Ndi iko komwe, timapemphedwa ‘kuyenda modzicepetsa ndi Mulungu wathu.’ (Mika 6:8) Conco, nthawi zonse tikalandila udindo watsopano, tifunika kuganizila mwa pemphelo zilizonse zimene Yehova akutiuza kupitila m’Mau ake na gulu lake. M’malo moyenda cozupila, titelo kukamba kwake, tifunika kuyenda moongoka potsatila citsogozo cowongoka ca Yehova. Tizikumbukila kuti cimene cidzatikweza si maluso athu, koma kudzicepetsa kwa Yehova. (Sal. 18:35) Conco, kuyenda modzicepetsa ndi Mulungu, kudzatithandiza kusadziganizila modzithuvula, kapena kudzitsitsa modzigwetselatu.—Ŵelengani Aroma 12:3.

19. Kukulitsa mzimu wa kudzicepetsa n’kofunika pa zifukwa ziti?

19 Munthu wodzicepetsa amalemekeza Yehova, cifukwa ni Mlengi wathu, komanso ni Mfumu ya Cilengwedwe Conse. (Chiv. 4:11) Kudzicepetsa kumatithandiza kukhutila ndi nchito imene Mulungu anatipatsa, ndi kuiyendetsa bwino. Kumatithandiza kupewa zinthu zimene zingatitayitse ulemu, ndipo timalimbikitsa mgwilizano pakati pa anthu a Yehova. Timaikanso zabwino za anzathu patsogolo pa zathu, timakhalanso osamala ndi kupeza zolakwa zikulu-zikulu. Pa zifukwa zimenezi, kudzicepetsa n’kofunikabe kwa anthu onse a Mulungu, ndipo Yehova amakonda ngako anthu odzicepetsa. Nanga bwanji pamene zinthu zili zotivuta? Nkhani yotsatila idzationetsa mmene tingakhalilebe odzicepetsa panthawi zovuta.