Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Tinaona Cisomo ca Mulungu m’Njila Zambili

Tinaona Cisomo ca Mulungu m’Njila Zambili

POKHALA mnyamata woopa Mulungu, atate, a Arthur, anali n’colinga codzakhala m’busa wa chechi ca Methodist. Komabe, colinga cawo cinasintha pamene anayamba kuŵelenga zofalitsa za Ophunzila Baibo ndi kugwilizana nawo. Iwo anabatizika mu 1914, apo n’kuti ali ndi zaka 17. Panthawiyo, nkhondo yoyamba ya dziko lonse inali itafika poipa. Motelo, anaitanidwa kuti aloŵe usilikali. Cifukwa cokana kunyamula zida za nkhondo, analamulidwa kukapika jele kwa miyezi 10 m’ndende yochedwa Kingston Penitentiary ku Ontario, ku Canada. Atamasulidwa, Atate anayamba utumiki wa nthawi zonse monga kopotala (mpainiya).

Mu 1926, Arthur Guest anamanga banja ndi Hazel Wilkinson, amene amayi awo anaphunzila coonadi mu 1908. N’nabadwa pa 24 April, 1931, ndipo ndine mwana waciŵili pa ana awo anayi. Banja lathu linali kukonda kwambili kulambila Yehova. Atate anali kulemekeza kwambili Baibo, ndipo izi zinacititsa kuti ifenso tiziyamikila Mau a Mulungu. Nthawi zonse tinali kulalikila kunyumba ndi nyumba pamodzi monga banja.—Mac. 20:20.

KUSATENGABE MBALI M’NKHONDO NDI KUYAMBA UPAINIYA MONGA ATATE

Mu 1939, nkhondo yaciŵili ya dziko lonse inayamba. Caka cotsatila, nchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa m’dziko la Canada. M’masukulu a boma munali kucitika miyambo yosonyeza kukonda dziko, monga kucitila sawacha mbendela ndi kuimba nyimbo ya fuko. Ine na mlongosi wanga wamkulu, Dorothy, tinali kucotsedwa m’kilasi panthawi ya miyambo imeneyi. Codabwitsa n’cakuti tsiku lina, aphunzitsi anga ananicititsa manyazi mwa kukamba kuti n’nali wamantha. N’takomboka kusukulu, anzanga angapo a m’kilasi ananimenya n’kunigwetsela pansi. Koma nkhanza zimenezo zinangolimbitsa cosankha canga ‘comvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.’—Mac. 5:29.

Mu July 1942, pa msinkhu wa zaka 11, n’nabatizika m’tanki yamadzi pa famu. Caka ciliconse nikatsekela sukulu, n’nali kukonda kucitako upainiya wapachuthi (tsopano timati upainiya wothandiza). Kwa caka cimodzi, n’nagwilizana ndi abale atatu kulalikila anthu odula mitengo omwe anali kukhala m’gawo losalalikidwa, kumpoto kwa Ontario.

Pa 1 May, 1949, n’nakhala mpainiya wa nthawi zonse. Panthawiyo, pa nthambi panali nchito yomanga. Conco, ananiitana kukathandiza, ndipo n’nakhala ciwalo ca banja la Beteli ku Canada pa December 1. N’nali kuseŵenzela kopulintila mabuku, ndipo n’naphunzila kugwilitsila nchito makina opulintila. Kwa mawiki angapo, n’nali kuseŵenza usiku. Tinali kupulinta kapepa kauthenga kokamba za cizunzo cimene anthu a Yehova anali kukumana naco ku Canada.

Pamene n’nali kugwila nchito m’Dipatimenti ya Utumiki, n’nafunsa mafunso apainiya amene anabwela kudzaona ofesi ya nthambi. Iwo anali kupita kukatumikila m’tauni ya Quebec, imene inali cimake ca citsutso. Mmodzi wa alendowo anali Mary Zazula, wa ku Edmonton, ku Alberta. Iye ndi Joe, mlongosi wake wamkulu, anathamangitsidwa panyumba ndi makolo awo okangalika a chechi ca Orthodox cifukwa cokana kuleka kuphunzila Baibo. Mu June 1951, onse aŵili anabatizika, ndipo anayamba upainiya pambuyo pa miyezi 6. Pamene n’nali kufunsa Mary mafunso, n’nacita cidwi ndi mmene anali kuonela zinthu zauzimu. N’nadziuza kuti, ‘Zioneka kuti uyu ndiye mkazi amene ndidzamanga naye banja, pokhapo ngati cina cake calepheletsa.’ Patapita miyezi 9, tinamanga banja pa 30 January, 1954. Ndiyeno, patapita wiki imodzi, tinaitanidwa kuti tipite ku maphunzilo a nchito ya m’dela. Ndipo tinatumikila monga oyang’anila dela kumpoto kwa Ontario kwa zaka ziŵili zotsatila.

Nchito yolalikila ya padziko lonse itapita patsogolo, panafunika amishonali. Tinaganiza kuti ngati tinakwanitsa kupilila nyengo yozizila kwambili ndi udzudzu nthawi yotentha ku Canada, ndiye kuti tingakwanitsenso kupilila zovuta mu utumiki uliwonse. Mu July 1956, tinatsiliza Sukulu ya Giliyadi ya namba 27. Ndiyeno, mu November tinayamba utumiki wathu ku Brazil.

KUCITA UMISHONALI KU BRAZIL

Pamene tinafika pa nthambi ku Brazil, tinayamba kuphunzila Cipwitikizi. Titangophunzilako mau ocepa ndi kuloweza pamtima ulaliki wacidule wogaŵila magazini, tinayamba kuyenda mu ulaliki. Mwininyumba akaonetsa cidwi, tinauzidwa kuti tiziŵelenga malemba okamba za mmene umoyo udzakhalila mu Ufumu wa Mulungu. Tsiku loyamba pamene tinali mu ulaliki, mayi wina anamvetsela mwachelu. Conco, n’naŵelenga Chivumbulutso 21:3, 4. N’tangotsiliza kuŵelenga, n’nakomoka. N’nali n’sanajaile nyengo yotentha, ndipo n’nalimbana ndi vutoli kwa nthawi yaitali.

Tinali kucita utumiki wathu wa umishonali mu mzinda wa Campos, mmene tsopano muli mipingo 15. Titafika mu mzindawu, panali cabe kagulu kamodzi kutali ndi tauni. Panalinso nyumba ya amishonali mmene munali kukhala alongo anayi: Esther Tracy, Ramona Bauer, Luiza Schwarz, ndi Lorraine Brookes (tsopano amachedwa Lorraine Wallen). Nchito yanga panyumbapo inali kucapa zovala na kutola nkhuni. Tsiku lina pambuyo pa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda pa Mande, tinalandila mlendo amene sitinayembekezele. Mkazi wanga anali atagona pampando kuti apumuleko uku tikukambilana mmene tsiku layendela. Atautsa mutu wake pa pilo kuti adzuke, kunatuluka njoka imene inabweletsa mkosokonezo kufikila n’taipha.

N’taphunzila Cipwitikizi kwa caka cimodzi, n’naikidwa kukhala woyang’anila dela. Tinali kukhala umoyo wosalila zambili kumidzi. Kunalibe malaiti, tinali kugona pamphasa, ndipo pa maulendo tinali kuseŵenzetsa ngolo yokokedwa na hosi. Panthawi ya kampeni m’gawo losalalikidwa, tinakwela sitima kuyenda ku tauni ina m’mbali mwa mapili, ndipo tinacita lendi cipinda cina pa nyumba yogonamo alendo. Ofesi ya nthambi inatitumizila magazini ogaŵila mu ulaliki okwana 800. Tinayenda maulendo ambili kupita ku positi ofesi kukatenga mabokosi a magazini ndi kuwabweletsa kumene tinali kukhala.

Mu 1962, Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ya abale ndi alongo amishonali inacitika m’dziko lonse la Brazil. Kwa miyezi 6, n’nauzidwa kuti nikacititse masukulu angapo, koma sin’napite ndi Mary. N’nali kuphunzitsa m’mizinda ya Manaus, Belém, Fortaleza, Recife, ndi Salvador. N’nakonzanso msonkhano wa cigawo m’bwalo ina yochuka ya maseŵela mumzinda wa Manaus. Pa msonkhanowo, panagwa cimvula camphamvu cimene cinaipitsa madzi ambili amene tinali kumwa. Cinacititsanso kuti tisoŵe malo abwino omangilapo kafiteliya pa msonkhano. (M’masiku amenewo, pa misonkhano ya cigawo anthu anali kupatsidwa cakudya.) N’nakambilana ndi asilikali, ndipo mkulu wa asilikali wokoma mtima anatipatsa madzi akumwa panthawi yonse ya msonkhano. Anatumanso asilikali kuti adzatimangile matenti aŵili aakulu. Ina inakhala kicheni ndipo ina kafiteliya.

Pamene n’nacokapo, Mary anali kulalikila m’gawo lamalonda la Cipwitikizi, mmene anthu anaika maganizo awo onse pa kufuna-funa ndalama basi. Iye sanakwanitse kukambilana ndi anthu nkhani za m’Baibo. Conco, anauza abale ena a pa Beteli kuti, “Ngati pali dziko limene sinifuna kukakhako mu umoyo wanga, ni Portugal.” Patangopita nthawi yocepa, tinadadwa kulandila kalata yotipempha kuti tikatumikile ku Portugal. Panthawiyo, nchito yathu yolalikila inali yoletsedwa kumeneko. Koma tinavomelabe utumikiwo ngakhale kuti mkazi wanga zinam’dabwitsa poyamba.

KUTUMIKILA KU PORTUGAL

Mu August 1964, tinafika mumzinda wa Lisbon, ku Portugal. Abale athu kumeneko anali kuzunzidwa koopsa ndi apolisi acipwitikizi (PIDE). Poganizila zimenezi, tinaona kuti ndi bwino kuti pasakhale anthu otilandila, komanso kuti tipewe kukambilana ndi Mboni za kumeneko. Tinali kukhala m’nyumba ina ya alendo poyembekeza kuti tipatsidwe cilolezo cokhala m’dzikolo. Titatenga maviza athu, tinayamba kucita lendi nyumba ina. Potsilizila, mu January 1965, tinakambilana ndi ofesi ya nthambi. Tinakondwela kwambili kupezeka pa msonkhano wathu woyamba pambuyo pa miyezi 5.

Tinazindikila kuti apolisi anali kufufuza m’nyumba za abale tsiku na tsiku. Popeza kuti Nyumba za Ufumu zinali zitatsekedwa, misonkhano ya mpingo inali kucitikila m’nyumba za abale. Mboni zambili zinatengedwela kupolisi kuti zikafunsidwe mafunso. Abale anali kumenyedwa pofuna kuti aulule maina a anthu amene anali kucititsa misonkhano. Pa cifukwa cimeneci, abale anayamba kuchulana maina awo eni-eni oyamba monga akuti José kapena Paulo, m’malo mwa ziwongo zawo. Ifenso tinacita cimodzi-modzi.

Maganizo athu onse anali pa kupeleka cakudya cauzimu kwa abale athu. Mary anali ndi nchito yotaipa nkhani zophunzila mu Nsanja ya Mlonda ndi zofalitsa zina poseŵenzetsa ziwiya zina zolembela zimene zinathandiza kuti azilemba makope ambili-mbili panthawi imodzi.

KUIKILA KUMBUYO UTHENGA WABWINO M’KHOTI

Mu June 1966, kunali mlandu wapadela m’khoti ya ku Lisbon. Ofalitsa onse 49 a mu Mpingo wa Feijó, anatengeledwa kukhoti cifukwa cocita msonkhano m’nyumba ya anthu popanda cilolezo. N’nawakonzekeletsa mlanduwo ndi kuwafunsa mafunso mwa kuyeselela kukhala loya. Tinadziŵa kuti tidzaluza mlanduwo, koma tinazindikila kuti udzakhala mwayi wathu wocitila umboni. Molimba mtima, loya wathu anatiteteza mwa kugwila mau a Gamaliyeli wa m’zaka 100 zoyambilila. (Mac. 5:33-39) Mlandu wathu unafalitsidwa m’nyuzipepa, ndipo abale ndi alongo 49 anaikidwa m’ndende. Anapatsidwa masiku osiyana-siyana okhala m’ndende kuyambila pa masiku 45 mpaka miyezi 5 ndi hafu. Ndife okondwa kuti loya wathu wolimba mtima anavomela kuphunzila Baibo. Analinso kupezeka pa misonkhano asanamwalile.

Mu December 1966, n’naikidwa kukhala woyang’anila nthambi, ndipo nthawi zambili n’nali kusamalila nkhani zokhudza malamulo. Lamulo lamphamvu lolola Mboni za Yehova kuti zidzilambila mwaufulu linakhazikitsidwa. (Afil. 1:7) Pa 18 December, 1974, tinavomelezedwa mwalamulo kuti tizilambila mwaufulu. M’bale Nathan Knorr na Frederick Franz, ocokela ku likulu, anabwela ku Portugal kudzasangalala limodzi nafe pa msonkhano wosaiŵalika ku Oporto ndi ku Lisbon. Anthu 46,870 anapezekapo.

Yehova anali atatsegula khomo kuti pakhale ciwonjezeko pa zisumbu zingapo zimene anthu amakamba Cipwitikizi. Zisumbu zimenezo zinaphatikizapo Azores, Cape Verde, Madeira, ndi São Tomé na Príncipe. Pa cifukwa cimeneci, panafunika kukulitsa ofesi ya nthambi, ndipo n’zimene zinacitika mu 1988. Pa 23 April caka cimeneco, M’bale Milton Henschel anakamba nkhani yopatulila maofesi atsopano amenewo ku gulu la anthu acimwemwe okwana 45,522. Zinali zolimbikitsa kwambili kuonana ndi abale ndi alongo 20 amene anatumikilako monga amishonali m’dziko la Portugal. Iwo anali atabwela ku cocitika cosaiŵalika cimeneci.

TINAPINDULA NDI ZITSANZO ZA ANTHU OKHULUPILIKA

Kwa zaka zambili, tapindula kwambili cifukwa cogwilizana ndi abale okhulupilika. N’naphunzila mfundo yofunika pamene n’nali kuthandizila M’bale Theodore Jaracz paulendo wina wokacezela nthambi. Ofesi ya nthambi imene tinacezela inakumana ndi vuto lalikulu, ndipo abale a m’Komiti ya Nthambi anacita zimene akanakwanitsa kuti athetse vutolo. Powakhazika mtima pansi, M’bale Jaracz anati: “Tsopano tiyeni tipatse mpata mzimu woyela kuti ugwile nchito yake.” Paulendo wina tili ku Brooklyn zaka zambili zapitazo, ine na mkazi wanga, Mary, tinaceza ndi M’bale Franz na abale ena m’madzulo. Titam’pempha kukambako mau otsiliza okhudza zaka zambili zimene wakhala mu utumiki wa Yehova, M’bale Franz anati: “Cimene ningakuuzeni ni ici: Khalanibe m’gulu la Yehova looneka ndi maso zivute zitani. Ndilo gulu lokha limene likugwila nchito imene Yesu analamula ophunzila ake kucita—yolalikila uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu.”

Ine ndi mkazi wanga tapeza cimwemwe ceni-ceni cifukwa cogwila nchitoyi. Timakondwela kwambili tikaganizila maulendo athu ocezela nthambi zosiyana-siyana. Maulendo amenewa anatipatsa mwayi woyamikila zimene acicepele ndi acikulile amacita potumikila mokhulupilika, komanso kuwalimbikitsa kuti apilitize kutumikila Yehova mu utumiki wawo wa mtengo wapatali.

Zaka zambili zapitapo, ndipo tonse aŵili tili ndi zaka za m’ma 80. Mkazi wanga amadwala-dwala. (2 Akor. 12:9) Mayeselo amene takumana nawo alimbitsa cikhulupililo cathu ndi kutithandiza kukhalabe okhulupilika. Tikaganizila zimene tacita pa umoyo wathu, timavomeleza na mtima wonse kuti taonadi cisomo ca Yehova m’njila zambili-mbili. *

^ par. 29 Pamene nkhani ino inali kulembedwa kuti ifalitsidwe, m’bale Douglas Guest anamwalila pa 25 October, 2015 ali wokhulupilika kwa Yehova.