Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amatsogolera Anthu Ake

Yehova Amatsogolera Anthu Ake

“Yehova azidzakutsogolerani nthawi zonse.”—YES. 58:11.

NYIMBO: 152, 22

1, 2. (a) Kodi a Mboni za Yehova amasiyana bwanji ndi zipembedzo zina? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi komanso yotsatira?

ANTHU ambiri amakonda kutifunsa kuti: “Kodi mtsogoleri wanu ndi ndani?” Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa choti m’zipembedzo zambiri mumakhala munthu mmodzi amene amatsogolera. Koma ife timasangalala kuuza anthu kuti Mtsogoleri wathu ndi wangwiro osati munthu wochimwa. Ife timatsatira Khristu ndipo Khristuyo amatsatira Atate wake Yehova.—Mat. 23:10.

2 Ngakhale zili choncho, pali kagulu ka anthu kotchedwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kamene kamatsogolera anthu a Mulungu masiku ano. (Mat. 24:45) Ndiye kodi timadziwa bwanji kuti Yehova akutitsogolera pogwiritsa ntchito Mwana wake yemwe sitingamuone? M’nkhaniyi komanso yotsatira, tikambirana mmene Yehova wakhala akugwiritsira ntchito anthu ena potsogolera anthu ake. Tionanso maumboni atatu otsimikizira kuti Yehova ndi amene akutsogolera anthu ake ndipo wakhala akugwiritsa ntchito anthu ena.—Yes. 58:11.

ANKATHANDIZIDWA NDI MZIMU WOYERA

3. N’chiyani chinathandiza Mose kuti azitsogolera Aisiraeli?

3 Mzimu woyera unkathandiza anthu amene Mulungu ankawagwiritsa ntchito. Taganizirani za Mose amene Mulungu anamusankha kuti atsogolere Aisiraeli. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti akwanitse kugwira ntchito yovutayi? Yehova “anaika mzimu wake woyera mwa iye.” (Werengani Yesaya 63:11-14.) Yehova ankatsogolera anthu ake pogwiritsa ntchito Mose ndipo ankamuthandiza ndi mzimu wake woyera.

4. Kodi n’chiyani chikanathandiza Aisiraeli kudziwa kuti Mose anali ndi mzimu wa Mulungu? (Onani chithunzi patsamba 18.)

4 Popeza mzimu woyera suoneka, kodi Aisiraeli akanadziwa bwanji kuti Mose ankatsogoleredwa ndi mzimu? Mzimu woyera unamuthandiza kuti achite zodabwitsa komanso kuti auze Farao za dzina la Yehova. (Eks. 7:1-3) Unamuthandizanso kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi, kufatsa komanso kuleza mtima. Makhalidwewa ndi amene anamuthandiza kuti azitsogolera bwino Aisiraeli. Izitu n’zosiyana kwambiri ndi mmene atsogoleri ena analili chifukwa anali ankhanza komanso odzikonda. (Eks. 5:2, 6-9) Panali umboni wokwanira woti Yehova anasankha Mose kuti azitsogolera anthu ake.

5. Fotokozani mmene Yehova anathandizira Aisiraeli ena amene ankatsogolera anthu ake.

5 Patapita nthawi, mzimu woyera unathandizanso anthu ena amene Mulungu anawasankha kuti azitsogolera anthu ake. Mwachitsanzo, “Yoswa mwana wa Nuni anali wodzazidwa ndi mzimu wa nzeru.” (Deut. 34:9) “Gidiyoni anagwidwa ndi mzimu wa Yehova.” (Ower. 6:34) Ndiponso “mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide.” (1 Sam. 16:13) Anthu onsewa ankadalira mzimu woyera ndipo unkawathandiza kuchita zinthu zimene sakanakwanitsa paokha. (Yos. 11:16, 17; Ower. 7:7, 22; 1 Sam. 17:37, 50) Ndipo Yehova ndi amene ankatamandidwa chifukwa cha zinthu zimene anthuwa ankachita.

6. Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu ankafuna kuti anthu ake azilemekeza atsogoleri awo?

6 Aisiraeli ankafunika kumvera anthu amene ankawatsogolera chifukwa panali umboni wosonyeza kuti anthuwo akuthandizidwa ndi mzimu woyera. Nthawi ina anthu akudandala za Mose, Yehova anafunsa kuti: “Kodi anthu awa apitiriza kundinyoza kufikira liti?” (Num. 14:2, 11) Yehova anasankha Mose, Yoswa, Gidiyoni ndi Davide kuti azitsogolera anthu m’malo mwake. Aisiraeli akamamvera anthu amenewa ankakhala kuti akumvera Yehova.

ANKATHANDIZIDWA NDI ANGELO

7. Kodi angelo anathandiza bwanji Mose?

7 Angelo ankathandiza anthu amene Mulungu ankawagwiritsa ntchito. (Werengani Aheberi 1:7, 14.) Yehova anatuma angelo kuti akauze Mose zochita, akamupatse mphamvu komanso akamutsogolere. Mulungu anasankha Mose kuti akhale “wolamulira ndi mpulumutsi kudzera mwa mngelo amene anaonekera kwa iye pachitsamba chaminga.” (Mac. 7:35) Iye anaperekanso Chilamulo “kudzera mwa angelo” kuti Mose azichigwiritsa ntchito polangiza Aisiraeli. (Agal. 3:19) Ndipo Yehova anauza Mose kuti: “Tsopano atsogolere anthuwa kumalo amene ndakuuza. Taona! Mngelo wanga akhala patsogolo panu.” (Eks. 32:34) Baibulo silinena kuti Aisiraeli ankamuona mngeloyo. Koma zimene Mose ankachita powalangiza komanso kuwatsogolera zinkasonyezeratu kuti ali ndi mphamvu yapadera.

8. Kodi angelo anathandiza bwanji Yoswa ndi Hezekiya?

8 Mose atafa, “kalonga wa gulu lankhondo la Yehova” anathandiza Yoswa kuti atsogolere Aisiraeli pogonjetsa Akanani. (Yos. 5:13-15; 6:2, 21) Pa nthawi ya Mfumu Hezekiya, gulu la asilikali a Asuri linaopseza kuti liwononga Yerusalemu. Koma usiku umodzi wokha, “mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri n’kukapha asilikali 185,000.”—2 Maf. 19:35.

9. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ankayenera kumvera atsogoleri awo ngakhale kuti ankalakwitsa zina ndi zina?

9 Angelo ndi angwiro koma anthu amene ankathandizidwa ndi angelowo ankalakwitsa zinthu zina. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Mose analephera kulemekeza Mulungu. (Num. 20:12) Nayenso Yoswa anaiwala kufunsa kaye Mulungu asanachite pangano ndi anthu a ku Gibeoni. (Yos. 9:14, 15) Ponena za Hezekiya, Baibulo limati pa nthawi ina “mtima wake unayamba kudzikuza.” (2 Mbiri 32:25, 26) Koma ngakhale kuti anthuwa ankalakwitsa zina ndi zina, Aisiraeli ankayenerabe kuwamvera. Tikutero chifukwa choti Yehova ankatuma angelo kuti aziwathandiza. Choncho mwachidule tingati Yehovayo ndi amene ankatsogolera anthu ake.

ANKATSOGOLEREDWA NDI MAWU A MULUNGU

10. N’chiyani chikusonyeza kuti nayenso Mose ankatsatira malamulo a Mulungu?

10 Anthu amene Mulungu ankawagwiritsa ntchito ankatsogoleredwa ndi Mawu ake. Baibulo limatchula Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli kuti ndi ‘Chilamulo cha Mose.’ (1 Maf. 2:3) Ngakhale zili choncho, Malemba amasonyeza kuti Yehova ndi amene anapereka malamulowo ndipo Mose nayenso ankafunika kutsatira Chilamulo. (2 Mbiri 34:14) Komanso Yehova atamupatsa malangizo okhudza mmene angapangire chihema, “Mose anachita zonse monga mmene Yehova anamulamulira. Anachitadi momwemo.”—Eks. 40:1-16.

11, 12. (a) Kodi Yoswa komanso mafumu amene ankalamulira anthu a Mulungu anafunika kuchita chiyani? (b) Kodi Mawu a Mulungu anathandiza bwanji anthu amene ankatsogolera Aisiraeli?

11 Yoswa atangoyamba kulamulira anali ndi buku la Mawu a Mulungu. Iye anauzidwa kuti: “Uziliwerenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatira zonse zolembedwamo.” (Yos. 1:8) Mafumu onse amene ankalamulira anthu a Mulungu ankafunikanso kuchita chimodzimodzi. Iwo ankafunika kukopera Chilamulo, kuchiwerenga tsiku lililonse komanso ‘kusunga mawu onse a chilamulocho, kutinso azitsatira malangizo ake.’—Werengani Deuteronomo 17:18-20.

12 Kodi Mawu a Mulungu anathandiza bwanji anthu amene ankatsogolera Aisiraeli? Tiyeni tione chitsanzo cha Mfumu Yosiya. Buku la Chilamulo litapezeka, mlembi wake anayamba kumuwerengera. * Ndiye kodi iye anatani? “Mfumuyo itangomva mawu a m’buku la chilamulolo, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake.” Kuwonjezera pamenepa, Yosiya anayamba chintchito chothetsa kulambira mafano komanso anakonza zoti achite chikondwerero chachikulu cha Pasika. (2 Maf. 22:11; 23:1-23) Popeza kuti Yosiya ndi atsogoleri ena okhulupirika ankatsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu, anali ofunitsitsa kusintha malangizo amene ankapatsa anthu a Mulungu. Kusintha kumeneku kunathandiza kuti Aisiraeli azichita zinthu zimene Mulungu amafuna.

13. Kodi anthu amene ankatsogolera Aisiraeli ankasiyana bwanji ndi mafumu a mitundu ina?

13 Anthu okhulupirika amene ankatsogolera Aisiraeli anali osiyana ndi mafumu a mitundu ina. Tikutero chifukwa chakuti mafumu enawo ankayendera nzeru za anthu ndipo sankaona patali. Mu ulamuliro wa Akanani anthu ankachita zinthu zoipa monga kugonana pachibale, kugonana amuna kapena akazi okhaokha, kugonana ndi nyama, kupereka ana nsembe komanso kulambira kwambiri mafano. (Lev. 18:6, 21-25) Nawonso atsogoleri a ku Babulo ndi ku Iguputo sankatsatira malangizo aukhondo amene Mulungu anapatsa Aisiraeli. (Num. 19:13) Koma anthu amene ankatsogolera Aisiraeli ankalimbikitsa ukhondo, makhalidwe abwino ndiponso kulambira Yehova yekha. N’zoonekeratu kuti Yehova ndi amene ankawatsogolera.

14. N’chifukwa chiyani Yehova ankalanga mafumu ena amene ankatsogolera anthu ake?

14 Si mafumu onse a anthu a Mulungu amene ankatsatira malangizo a Mulunguyo. Ndipo mafumu amene sankamvera Yehova ankakana kutsogoleredwa ndi mzimu woyera, angelo komanso Mawu a Mulungu. Zikatero, Yehova ankawalanga kapena kuwachotsa pa udindo. (1 Sam. 13:13, 14) Pa nthawi yake, Yehova anasankha mtsogoleri wabwino kuposa wina aliyense.

YEHOVA ANASANKHA MTSOGOLERI WABWINO KWAMBIRI

15. (a) Kodi aneneri anasonyeza bwanji kuti kunkabwera mtsogoleri wabwino kwambiri? (b) Kodi mtsogoleri amene analoseredwayu ndi ndani?

15 Kwa zaka zambiri, Yehova analosera kuti adzasankha mtsogoleri wabwino kwambiri wa anthu ake. Mwachitsanzo, Mose anauza Aisiraeli kuti: “Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati panu, kuchokera pakati pa abale anu, ndipo inu mudzamvere mneneri ameneyo.” (Deut. 18:15) Yesaya ananena kuti wosankhidwayo adzakhala “mtsogoleri ndi wolamulira.” (Yes. 55:4) Pomwe Danieli anauziridwa kulemba zoti kudzabwera “Mesiya Mtsogoleri.” (Dan. 9:25) Ndiyeno Yesu mwiniwake ananena kuti iyeyo ndi “Mtsogoleri” wa anthu a Mulungu. (Werengani Mateyu 23:10.) Ophunzira ake ankamutsatira ndi mtima wonse ndipo sankakayikira zoti ndi wosankhidwa ndi Mulungu. (Yoh. 6:68, 69) Kodi n’chiyani chinkawatsimikizira kuti Yehova wasankha Yesu Khristu kuti azitsogolera anthu ake?

16. N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankathandizidwa ndi mzimu woyera?

16 Yesu ankathandizidwa ndi mzimu woyera. Pamene iye ankabatizidwa, Yohane anaona “kumwamba kukutseguka, ndiponso mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzamutera.” Kenako “mzimuwo unamulimbikitsa kupita kuchipululu.” (Maliko 1:10-12) Mzimu woyera unkathandiza Yesu pa nthawi yonse imene anali padzikoli moti ankachita zodabwitsa komanso kulankhula ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu. (Mac. 10:38) Mzimu woyera unathandizanso Yesu kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi, chimwemwe ndiponso chikhulupiriro cholimba. (Yoh. 15:9; Aheb. 12:2) Palibe mtsogoleri ngakhale mmodzi amene ankachita zinthu ngati Yesu. N’zosachita kufunsa kuti Yesu anasankhidwadi ndi Yehova.

Kodi angelo anathandiza bwanji Yesu atangobatizidwa kumene? (Onani ndime 17)

17. Kodi angelo anathandiza bwanji Yesu?

17 Yesu ankathandizidwa ndi angelo. Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Yesu anabatizidwa, “kunabwera angelo ndi kuyamba kum’tumikira.” (Mat. 4:11) Kutatsala maola ochepa kuti aphedwe, “mngelo wochokera kumwamba anaonekera kwa iye ndi kumulimbikitsa.” (Luka 22:43) Yesu ankadziwa kuti Yehova azimutumizira angelo pa nthawi yoyenera kuti amuthandize kukwaniritsa chifuniro cha Mulungu.—Mat. 26:53.

18, 19. N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankatsatira Mawu a Mulungu pa moyo wake komanso pophunzitsa anthu?

18 Yesu ankatsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu. Yesu atangoyamba utumiki wake, ankalola kuti Mawu a Mulungu azimutsogolera. (Mat. 4:4) Iye ankamvera Mawu a Mulungu mpaka kufika pololera kuphedwa pamtengo wozunzikirapo. Ngakhale mawu amene ananena atatsala pang’ono kufa anali ochokera m’maulosi onena za Mesiya. (Mat. 27:46; Luka 23:46) Koma atsogoleri achipembedzo a nthawi imeneyo ankanyalanyaza Mawu a Mulungu akaona kuti akusemphana ndi miyambo yawo. Ndiyeno Yesu anawafotokoza pogwiritsa ntchito mawu amene Yesaya ananena akuti: “Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Amandipembedza pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.” (Mat. 15:7-9) Kodi Yehova akanasankha anthu ngati amenewa kuti azitsogolera anthu ake?

19 Yesu ankatsatira Mawu a Mulungu pa moyo wake komanso pophunzitsa anthu. Ena akamamutsutsa, iye sankawayankha pogwiritsa ntchito nzeru zake kapena zinthu zambirimbiri zimene akudziwa. M’malomwake ankagwiritsa ntchito Malemba. (Mat. 22:33-40) Pophunzitsa anthu, sankawauza zinthu zogometsa zokhudza kumwamba kapena zimene zinachitika polenga zinthu. M’malomwake ‘ankatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.’ (Luka 24:32, 45) Yesu ankakonda Mawu a Mulungu ndipo ankafunitsitsa kuphunzitsa ena Mawuwo.

20. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankagonjera Mulungu? (b) Kodi kusiyana pakati pa Yesu ndi Herode kukusonyeza bwanji kuti Yehova anasankha bwino mtsogoleri?

20 Anthu ankadabwa ndi “mawu ogwira mtima” amene Yesu ankalankhula. Koma iye ankapereka ulemerero wonse kwa Yehova chifukwa ndi amene anamuphunzitsa. (Luka 4:22) Mwachitsanzo, munthu wina wachuma atamutchula kuti “Mphunzitsi Wabwino,” Yesu anayankha modzichepetsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.” (Maliko 10:17, 18) Izi n’zosiyana kwambiri ndi zimene Herode Agiripa Woyamba anachita. Iye anakhala mfumu ya Yudeya patadutsa zaka 8 kuchokera pamene Yesu ananena mawuwa. Pa tsiku la msonkhano, Herode anavala “zovala zake zachifumu” n’kuyamba kulankhula. Anthu atamva mawu ake anayamba kufuula kuti: “Amenewa ndi mawu a mulungu, osati a munthu ayi!” Herode ayenera kuti anasangalala ndi mawu amenewa. Ndiye kodi chinachitika n’chiyani? “Nthawi yomweyo mngelo wa Yehova anamukantha, chifukwa sanapereke ulemerero kwa Mulungu. Ndipo anadyedwa ndi mphutsi n’kumwalira.” (Mac. 12:21-23) Kunena zoona, munthu wanzeru zake sangaganize kuti Herode anali mfumu yosankhidwa ndi Yehova. Koma nthawi zonse Yesu ankasonyeza kuti anasankhidwa ndi Mulungu ndipo ankatamanda Yehova chifukwa chakuti ndi Wolamulira Wamkulu wa anthu ake.

21. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

21 Ulamuliro wa Yesu si wa zaka zochepa ayi. Paja iye ataukitsidwa ananena kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Kenako anati: “Dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:18-20) Popeza Yesu ali kumwamba ndipo sitingamuone, kodi akutsogolera bwanji anthu a Mulungu padzikoli? Kodi Yehova anasankha ndani kuti azitsogolera anthu ake momvera Khristu? Nanga Akhristu angadziwe bwanji anthu amene Mulungu akuwagwiritsa ntchito kuti aziwatsogolera? M’nkhani yotsatira tidzapeza mayankho a mafunso amenewa.

^ ndime 12 Chilamulochi chiyenera kuti chinali chenicheni chimene Mose analemba.