Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yehova Amatsogolela Anthu Ake

Yehova Amatsogolela Anthu Ake

“Yehova azidzakutsogolelani nthawi zonse.”—YES. 58:11.

NYIMBO: 152, 22

1, 2. (a) Kodi amene amatsogolela pakati pa Mboni za Yehova amasiyana bwanji ndi atsogoleli a m’machechi ena? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino ndi yotsatila?

“N’NDANI amakutsogolelani?” Nthawi zambili anthu amafunsa Mboni za Yehova funso limeneli. Mpake kuti amafunsa conco. M’machechi yambili mwamuna kapena mkazi amakhala mtsogoleli kapena m’busa. Mosiyanako, ise timanyadila kuuza anthu amene amatifunsa kuti mtsogoleli wathu si munthu wopanda ungwilo. Timatsatila citsogozo ca Khiristu woukitsidwa amene nayenso amatsatila citsogozo ca Atate ake, Yehova.—Mat. 23:10.

2 Komabe, pali gulu la amuna ooneka ndi maso, amene ndi “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Kapoloyu ndiye atsogolela anthu a Mulungu masiku ano. (Mat. 24:45) Koma tidziŵa bwanji kuti Yehova ndiye akutitsogolela kupitila mwa Mwana wake wosaoneka? M’nkhani ino ndi yotsatila, tidzaphunzila mmene Yehova kwa zaka zambili wagwilitsila nchito amuna ena kuti atsogolele. M’nkhani zonse ziŵili, tidzakambilana maumboni atatu oonetsa kuti zoona Yehova anali kucilikiza amunawo. Izi zionetsa kuti ndiye anali kuwatsogolela, ndi kuti akali Mtsogoleli wa anthu ake.—Yes. 58:11.

ANALIMBITSIDWA NDI MZIMU WOYELA

3. N’ciani cinathandiza Mose kutsogolela Aisiraeli?

3 Mzimu woyela unalimbitsa amuna oimilako Mulungu. Ganizilani Mose amene anaikidwa kukhala mtsogoleli wa Aisiraeli. N’ciani cinam’thandiza kusamalila udindo waukulu umenewo? Yehova “anaika mzimu wake woyela mwa iye.” (Ŵelengani Yesaya 63:11-14.) Mwa kuthandiza Mose ndi mzimu woyela, Yehova anapitiliza kutsogolela anthu Ake.

4. Kodi Aisiraeli anadziŵa bwanji kuti Mose anali na mzimu wa Mulungu? (Onani pikica kuciyambi kwa nkhani ino.)

4 Popeza mzimu woyela ni mphamvu yosaoneka, kodi Aisiraeli anadziŵa bwanji kuti unali kugwila nchito pa Mose? Mzimu woyela unathandiza Mose kucita zozizwitsa ndi kulengeza dzina la Mulungu kwa Farao. (Eks. 7:1-3) Mzimu woyela unathandizanso Mose kukhala ndi makhalidwe abwino monga cikondi, kufatsa, ndi kuleza mtima. Makhalidwe amenewa anam’thandiza kutsogolela Aisiraeli. Izi zinali zosiyana kwambili ndi atsogoleli ankhanza ndi odzikonda a mitundu ina. (Eks. 5:2, 6-9) Apa umboni unali woonekelatu kuti Yehova anali atasankha Mose kukhala mtsogoleli wa anthu Ake.

5. Fotokozani mmene Yehova anathandizila amuna ena aciisiraeli kutsogolela anthu ake.

5 M’kupita kwa nthawi, mzimu woyela wa Yehova unalimbitsa amuna ena amene anasankhidwa kutsogolela anthu ake. “Yoswa mwana wa Nuni anali wodzazidwa ndi mzimu wa nzelu.” (Deut. 34:9) “Gidiyoni anagwidwa ndi mzimu wa Yehova.” (Ower. 6:34) Ndipo “mzimu wa Yehova unayamba kugwila nchito pa Davide.” (1 Sam. 16:13) Amuna onsewa anadalila mzimu wa Mulungu kuwathandiza. Ndipo mzimuwo unawathandiza kucita zinthu zazikulu zimene sakanazikwanitsa mwa mphamvu zawo. (Yos. 11:16, 17; Ower. 7:7, 22; 1 Sam. 17:37, 50) Zotsatilapo n’zakuti Yehova ndiye analandila citamando cifukwa ca nchito zazikulu zimenezo.

6. N’cifukwa ciani Mulungu anafuna kuti anthu ake azilemekeza atsogoleli mu Isiraeli?

6 N’ciani cimene Aisiraeli anayenela kucita ataona umboni woonekelatu wakuti amunawo anali kutsogoleledwa na mzimu woyela? Pamene Aisiraeli anadandaula za utsogoleli wa Mose, Yehova anafunsa kuti: “Kodi anthu awa apitiliza kundinyoza kufikila liti?” (Num. 14:2, 11) Zoonadi, Yehova ndiye anasankha Mose, Yoswa, Gidiyoni, ndi Davide kuti amuimile monga Mtsogoleli. Anthu akamvela amuna amenewa, m’ceni-ceni anali kutsatila Yehova monga Mtsogoleli wawo.

ANATHANDIZIDWA NDI ANGELO

7. Kodi angelo anam’thandiza bwanji Mose?

7 Angelo anathandiza amuna oimilako Mulungu. (Ŵelengani Aheberi 1:7, 14.) Yehova analamula angelo kuti azilangiza, kuthandiza, ndi kutsogolela Mose. Mulungu anatumiza Mose “monga wolamulila ndi mpulumutsi kudzela mwa mngelo amene anaonekela kwa iye pacitsamba caminga cija.” (Mac. 7:35) Yehova anapeleka Cilamulo kupitila mwa angelo. Cilamuloco n’cimene Mose anaseŵenzetsa kulangiza Aisiraeli. (Agal. 3:19) Ndipo Yehova anamuuza kuti: ‘Tsogolela anthuwa kumalo amene ndakuuza. Taona! Mngelo wanga akhala patsogolo panu.’ (Eks. 32:34) Baibo siikamba kuti Aisiraeli anamuona mwacindunji mngelo akucita zimenezo. Koma mmene Mose anali kulangizila ndi kutsogolela anthu, zinaonetselatu kuti anali kuthandizidwadi ndi angelo.

8. Kodi angelo anathandiza bwanji Yoswa ndi Hezekiya?

8 Mose atafa, Yoswa, amene anamuloŵa m’malo, analimbikitsidwa ndi “kalonga wa gulu lankhondo la Yehova” kuti atsogolele anthu a Mulungu kukamenyana ndi Akanani. Aisiraeli anapambana nkhondoyo. (Yos. 5:13-15; 6:2, 21) Panthawi ina, Mfumu Hezekiya anakumana ndi gulu la asilikali a Asuri amphamvu amene anaopseza kuti adzawononga Yerusalemu. Usiku umodzi cabe, “mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri n’kukapha asilikali 185,000.”—2 Maf. 19:35.

9. Kodi zifooko za amuna oimila Mulungu zinacititsa Aisiraeli kuti asatsatile citsogozo cawo? Fotokozani.

9 Angelo ni angwilo, koma anthu amene iwo anali kuthandiza sanali angwilo. Panthawi ina Mose analephela kulemekeza Yehova. (Num. 20:12) Yoswa ananyalanyaza kufunsila malangizo kwa Mulungu asanacite pangano ndi Agibeoni. (Yos. 9:14, 15) Kwa kanthawi kocepa, “mtima [wa Hezekiya] unayamba kudzikuza.” (2 Mbiri 32:25, 26) Ngakhale kuti amunawa anali ndi zifooko, Aisiraeli anafunikabe kutsatila citsogozo cawo. Yehova anali kuthandiza amuna amenewo poseŵenzetsa angelo. Ndithudi, Yehova anali kutsogolela anthu ake.

ANATSOGOLELEDWA NDI MAU A MULUNGU

10. Kodi Mose anatsogoleledwa bwanji ndi Cilamulo ca Mulungu?

10 Mau a Mulungu anatsogolela amuna omuimilako. Baibo imachula Cilamulo cimene cinapatsidwa kwa Aisiraeli kuti “Cilamulo ca Mose.” (1 Maf. 2:3) Komabe, Malemba aonetsa kuti Yehova ndiye anapeleka Cilamulo, ndipo Mose anali pansi pa Cilamuloco. (2 Mbiri 34:14) Yehova atapatsa Mose malangizo a mmene angapangile cihema, “Mose anacita zonse monga mmene Yehova anamulamulila. Anacitadi momwemo.”—Eks. 40:1-16.

11, 12. (a) Kodi Yoswa ndi mafumu olamulila anthu a Mulungu anafunika kucita ciani? (b) Nanga Mau a Mulungu anakhudza bwanji atsogoleli a anthu a Mulungu?

11 Kucokela paciyambi pa utsogoleli wake, Yoswa anali ndi buku la Mau a Mulungu olembedwa. Iye anauzidwa kuti: “Uziliŵelenga ndi kusinkha-sinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatila zonse zolembedwamo.” (Yos. 1:8) Nawonso mafumu amene analamulila anthu a Mulungu anatsatila zimenezi. Iwo anafunika kuŵelenga Cilamulo tsiku na tsiku, kucikopela, ndi ‘kusunga mau onse a cilamuloco, kutinso azitsatila malangizo ake.’—Ŵelengani Deuteronomo 17:18-20.

12 Kodi Mau a Mulungu anawakhudza bwanji amuna amene anali kutsogolela? Ganizilani citsanzo ca Mfumu Yosiya. Atapeza mpukutu wa Cilamulo ca Mose, kalembela wa Yosiya anayamba kumuŵelengela. * Kodi mfumuyo inacita ciani? “Mfumuyo itangomva mau a m’buku la cilamulolo, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake.” Koma si zokhazo. Motsogoleledwa ndi Mau a Mulungu, Yosiya anayamba nchito yaikulu yocotsa mafano. Anakonzanso zakuti acite cikondwelelo ca Pasika cimene sicinacitikepo kumbuyoku. (2 Maf. 22:11; 23:1-23) Cifukwa cakuti Yosiya ndi atsogoleli ena okhulupilika anatsogoleledwa ndi Mau a Mulungu, iwo anali ofunitsitsa kusintha ndi kumveketsa bwino malangizo amene anali kupatsa anthu a Mulungu. Kusintha kumeneku kunathandiza anthu a Mulungu akale kucita zinthu mogwilizana ndi cifunilo cake.

13. N’kusiyana kwabwanji kumene kunalipo pakati pa atsogoleli a anthu a Mulungu ndi a mitundu ina?

13 Mafumu okhulupilika amenewo anali osiyana kwambili ndi atsogoleli a mitundu ina amene anali kutsogoleledwa ndi nzelu za anthu zosathandiza konse. Mwacitsanzo, pansi pa utsogoleli wacikanani, anthu anali kucita zinthu zonyansa, monga kugonana pa cibululu, kugonana amuna kapena akazi okha-okha, kugona nyama, kupeleka nsembe ana, ndi kulambila mafano. (Lev. 18:6, 21-25) Kuwonjezela apo, atsogoleli acibabulo ndi aciiguputo sanali kutsatila malamulo a zaukhondo ogwilizana ndi sayansi amene Mulungu anapatsa Aisiraeli. (Num. 19:13) Mosiyanako, anthu a Mulungu akale anaona mmene atsogoleli awo okhulupilika analimbitsila ciyelo cauzimu, cakuthupi ndi makhalidwe abwino. N’zoonekelatu kuti Yehova anali kuwatsogolela.

14. N’cifukwa ciani Yehova anali kulanga atsogoleli ena a anthu ake?

14 Si mafumu onse anali kutsatila malangizo a Mulungu polamulila anthu Ake akale. Amene sanamvele Yehova anali kukana kutsogoleledwa na mzimu woyela wa Mulungu, angelo ake, ndi Mau ake. Nthawi zina, Yehova anali kuwalanga kapena kusankha wina kuti atsogolele. (1 Sam. 13:13, 14) Panthawi yake, Mulungu anasankha wina wake amene anali kudzakhala wapamwamba kupambana amuna amene anagwilitsidwapo nchito.

YEHOVA ANASANKHA MTSOGOLELI WANGWILO

15. (a) Kodi aneneli anaonetsa bwanji kuti kudzabwela mtsogoleli wapadela? (b) N’ndani anali mtsogoleli wolonjezedwa?

15 Kwa zaka zambili, Yehova analosela kuti adzasankha mtsogoleli wapadela wa anthu ake. Mose anauza Aisiraeli kuti: “Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mneneli ngati ine, kucokela pakati panu, kucokela pakati pa abale anu, ndipo inu mudzamvele mneneli ameneyo.” (Deut. 18:15) Yesaya anakambilatu kuti ameneyo adzakhala “mtsogoleli ndi wolamulila.” (Yes. 55:4) Nayenso Danieli anauzilidwa kulemba za kubwela kwa “Mesiya Mtsogoleli.” (Dan. 9:25) Pomaliza, Yesu Khiristu anadziziŵikitsa kuti ndi “Mtsogoleli” wa anthu a Mulungu. (Ŵelengani Mateyu 23:10.) Ophunzila a Yesu anam’tsatila ndi mtima wonse, ndipo anatsimikiza kuti anasankhidwa ndi Yehova. (Yoh. 6:68, 69) N’ciani cinawathandiza kutsimikiza kuti Yehova anali kutsogolela anthu ake kupitila mwa Yesu Khiristu?

16. N’ciani cionetsa kuti mzimu woyela unalimbitsa Yesu?

16 Mzimu woyela unalimbitsa Yesu. Pa ubatizo wa Yesu, Yohane Mbatizi anaona “kumwamba kukutseguka, ndiponso mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzamutela.” Pambuyo pake, “mzimuwo unamulimbikitsa kupita kucipululu.” (Maliko 1:10-12) Pa utumiki wake wonse wa padziko lapansi, mzimu woyela wa Mulungu unathandiza Yesu kucita zozizwitsa ndi kulankhula ndi ulamulilo waukulu. (Mac. 10:38) Ndiponso, mzimu woyela unathandiza Yesu kukhala ndi makhalidwe abwino, monga cikondi, cimwemwe, ndi cikhulupililo colimba. (Yoh. 15:9; Aheb. 12:2) Panalibe mtsogoleli wina anaonetsapo umboni wotsimikiza umenewu. Yesu anasankhidwadi ndi Yehova.

Kodi angelo anam’thandiza bwanji Yesu atangobatizika? (Onani palagilafu 17)

17. Kodi angelo anathandiza bwanji Yesu?

17 Angelo anathandiza Yesu. Patangopita nthawi yocepa Yesu atabatizika, “kunabwela angelo ndi kuyamba kum’tumikila.” (Mat. 4:11) Kutatsala maola ocepa kuti Yesu aphedwe, “mngelo wocokela kumwamba anaonekela kwa iye ndi kumulimbikitsa.” (Luka 22:43) Yesu anali ndi cidalilo cakuti Yehova adzatumiza angelo kudzamuthandiza akafuna thandizo, kuti akwanilitse cifunilo ca Mulungu.—Mat. 26:53.

18, 19. Kodi Mau a Mulungu anatsogolela bwanji umoyo wa Yesu ndi ziphunzitso zake?

18 Mau a Mulungu anatsogolela Yesu. Kucokela paciyambi pa utumiki wake, Yesu analola Malemba kum’tsogolela. (Mat. 4:4) Ndipo anakhalabe womvela Mau a Mulungu mpaka kufa pa mtengo wonzuzikilapo. M’mau ake otsiliza asanafe, iye anagwila mau a m’maulosi okhudza Mesiya. (Mat. 27:46; Luka 23:46) Mosiyanako, atsogoleli a zipembedzo a m’nthawi yake sanali kulemekeza Mau a Mulungu akaona kuti mauwo akutsutsa miyambo yawo. Pogwila Mau a Yehova kupitila mwa mneneli Yesaya, Yesu anati pokamba za iwo: “Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Amandipembedza pacabe, cifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.” (Mat. 15:7-9) Kodi Yehova akanasankhadi mmodzi wa amunawo kutsogolela anthu ake?

19 Yesu anali kulola Mau a Mulungu kum’tsogolela pa zocita zake ndi pophunzitsa. Potsutsa ziphunzitso zabodza zacipembedzo, iye sanaseŵenzetse nzelu zake zakuya kapena cidziŵitso cake. M’malomwake, anali kuseŵenzetsa Malemba. (Mat. 22:33-40) M’malo mosimbila omvela ake nkhani zokhudza umoyo wakumwamba, kapena mmene zinthu zinalengedwela, iye “anatsegulilatu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.” (Luka 24:32, 45) Yesu anali kukonda Mau a Mulungu, ndipo anali wofunitsitsa kuuzako ena.

20. (a) Kodi Yesu anazindikila bwanji kuti anafunika kugonjela Mulungu? (b) Kodi kusiyana kumene kulipo pakati pa Yesu na Herode Agiripa Woyamba kutiuza ciani ponena za mtsogoleli amene Yehova amasankha?

20 Ngakhale kuti Yesu anadabwitsa omvela ake ndi “mau ogwila mtima,” iye analemekeza Mphunzitsi wake, Yehova. (Luka 4:22) Pamene munthu wina wa cuma anafuna kulemekeza Yesu mwa kukamba kuti, “Mphunzitsi Wabwino,” modzicepetsa Yesu anamuyankha kuti: “N’cifukwa ciani ukundichula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.” (Maliko 10:17, 18) Izi n’zosiyana kwambili ndi zimene Herode Agiripa Woyamba anacita. Iye anakhala mfumu kapena mtsogoleli wa Yudeya patapita zaka pafupi-fupi 8. Pa msonkhano wina wapadela, Herode anavala “zovala zake zacifumu.” Gulu lake linafuula kuti: “Amenewa ndi mau a mulungu, osati a munthu ayi!” Herode anakondwela ndi citamando cimeneco. N’ciani cinatsatilapo? “Nthawi yomweyo mngelo wa Yehova anamukantha, cifukwa sanapeleke ulemelelo kwa Mulungu. Ndipo anadyedwa ndi mphutsi n’kumwalila.” (Mac. 12:21-23) Ndithudi, palibe aliyense akanakamba kuti Herode anasankhidwa ndi Yehova kukhala mtsogoleli. Komabe, Yesu anapeleka umboni wotsimikizika wakuti anasankhidwa ndi Mulungu. Nthawi zonse anali kulemekeza Yehova, Mtsogoleli Wamkulu wa anthu ake.

21. Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

21 Sikuti utsogoleli wa Yesu unali wa zaka zocepa cabe. Pambuyo poukitsidwa, iye anakamba kuti: “Ulamulilo wonse wapelekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi. . . . Ndipo dziŵani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:18-20) Popeza Yesu ni colengedwa cauzimu cosaoneka kumwamba, kodi akanatsogolela bwanji anthu a Mulungu padziko lapansi? N’ndani amene Yehova anali kudzagwilitsila nchito kutsogolela anthu Ake pansi pa utsogoleli wa Khiristu? Nanga Akhiristu akanawadziŵa bwanji anthu amene amamuimila? M’nkhani yotsatila tidzakambilana mayankho a mafunso amenewa.

^ par. 12 Umenewu uyenela kuti unali mpukutu woyambilila wolembedwa ndi Mose.