Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mtumwi Paulo analemba kuti Yehova “sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire.” (1 Akor. 10:13) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova amayamba waganizira kaye zimene tingapirire ndiyeno n’kusankha mayesero oti tikumane nawo?

Yehova atati azichita zimenezi pangakhale mafunso ambiri. Taganizirani chitsanzo ichi: M’bale wina mwana wake atadzipha, anadzifunsa kuti: ‘Kodi Yehova anaganizira bwinobwino nkhaniyi n’kutsimikizira kuti ine ndi mkazi wanga tikhoza kupirira ngati mwana wathu atadzipha? Kodi izi zachitikadi chifukwa choti Yehova ankadziwa kuti tipirira?’ Kodi n’zoonadi kuti Yehova amakonzeratu zimene zidzachitike pa moyo wathu?

Titaganizira bwinobwino mawu a Paulo a pa 1 Akorinto 10:13, taona kuti si zoona kuti Yehova amayamba waganizira kaye zimene tingapirire ndiyeno n’kusankha mayesero oti tikumane nawo. Tikutero pa zifukwa 4.

Choyamba, Yehova anatipatsa ufulu wosankha zochita. Iye amafuna kuti tizisankha tokha zimene tikufuna kuchita pa moyo wathu. (Deut. 30:19, 20; Yos. 24:15) Ngati tasankha zoyenera, Yehova amatitsogolera. (Miy. 16:9) Koma tikasankha zolakwika zotsatira zake sizikhala zabwino. (Agal. 6:7) Choncho Yehova akanakhala kuti amasankha mayesero oti tikumane nawo, ndiye kuti akanatiphera ufulu wathu wosankhawo.

Chachiwiri, Yehova satiteteza ku ‘zinthu zosayembekezereka zimene zimagwera anthu onse.’ (Mlal. 9:11) Nthawi zina tikhoza kukumana ndi ngozi yoopsa chifukwa choti ngoziyo yachitika pa nthawi imene ifeyo tinali pamalowo. Yesu anafotokoza kuti Mulungu si amene anachititsa kuti nsanja igwere anthu 18 n’kuwapha. (Luka 13:1-5) Choncho n’zosamveka kunena kuti pa zinthu ngati zimenezi Mulungu amakonzeratu amene ayenera kufa ndi amene ayenera kupulumuka.

Chachitatu, munthu aliyense amafunika kusonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Yehova. Paja Satana amanena kuti anthufe sitingakhalebe okhulupirika ngati titakumana ndi mavuto. (Yobu 1:9-11; 2:4; Chiv. 12:10) Ndiyeno Yehova akanakhala kuti amatiteteza kuti tisakumane ndi mavuto ena poona kuti sitingapirire, kodi zimene Satana amanenazi sizikanakhala ngati zoona?

Chachinayi, Yehova sasankha kuoneratu chilichonse chimene chingachitike pa moyo wathu. Kuti Yehova asankhe mayesero amene tingakumane nawo angafunike kudziwa chilichonse chimene chingachitike pa moyo wathu. Koma Baibulo limasonyeza kuti Yehova sachita zimenezi. N’zoona kuti Yehova angathe kudziwa zam’tsogolo. (Yes. 46:10) Koma Malemba amasonyeza kuti iye amachita kusankha zoti adziwiretu. (Gen. 18:20, 21; 22:12) Choncho amagwiritsa ntchito bwino mphamvu zake zodziwiratu zinthu, popanda kusokoneza ufulu wathu wosankha zochita. Kunena zoona Yehova ndi wachikondi komanso wachilungamo ndipo amalemekeza ufulu wathu.—Deut. 32:4; 2 Akor. 3:17.

Ndiyeno kodi mawu a Paulo akuti Mulungu “sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire” amatanthauza chiyani? Palembali Paulo ankafotokoza zimene Yehova amachita tikakumana ndi mayesero osati tisanakumane nawo. Mawu akewa amatitsimikizira kuti kaya tikumane ndi mavuto otani, Yehova adzatithandiza ngati timamudalira. (Sal. 55:22) Tiyeni tikambirane zifukwa ziwiri zimene zinachititsa Paulo kunena mawuwa.

Choyamba, mayesero amene timakumana nawo ndi amenenso “amagwera anthu ena.” Amakhala oti tikhoza kuwapirira ndithu ngati titadalira Mulungu. (1 Pet. 5:8, 9) Ponena mawu a pa 1 Akorinto 10:13, Paulo ankafotokoza za mayesero amene Aisiraeli anakumana nawo m’chipululu. (1 Akor. 10:6-11) Mayesero onsewo anali oti Aisiraeli akanatha kuwapirira. Koma Paulo ananena ka 4 konse kuti “ena mwa iwo” sanamvere Mulungu. N’zomvetsa chisoni kuti Aisiraeli ena anagonja n’kuyamba kuchita zoipa chifukwa choti sankadalira Mulungu.

Chachiwiri, “Mulungu ndi wokhulupirika.” Tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi anthu ake, zimasonyeza kuti iye amathandiza mokhulupirika “anthu amene amam’konda ndi kusunga malamulo ake.” (Deut. 7:9) Baibulo limasonyezanso kuti nthawi zonse Mulungu amakwaniritsa malonjezo ake. (Yos. 23:14) Chifukwa cha zimenezi, anthu amene amamukonda komanso kumumvera angakhale ndi chikhulupiriro choti iye (1) sadzalola kuti mayesero amene akukumana nawo akule mpaka kufika poti sangathe kuwapirira komanso (2) “adzapereka njira yopulumukira.”

Yehova “amatitonthoza m’masautso athu onse”

Koma kodi Yehova amapereka bwanji njira yopulumukira, anthu amene amamudalira akakumana ndi mayesero? Nthawi zina amachotsa mayeserowo. Koma nthawi zambiri Yehova amangotithandiza kuti tithe kupirira vuto lathulo. Musaiwale mawu a Paulo akuti, “iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.” Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene amachita.

  • Iye “amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akor. 1:3, 4) Yehova angatithandize kuti mtima wathu ukhale m’malo komanso kuti maganizo athu asasokonezeke. Angachite zimenezi pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake komanso chakudya chauzimu chomwe timalandira kwa kapolo wokhulupirika.—Mat. 24:45; Yoh. 14:16; Aroma 15:4.

  • Angatitsogolere pogwiritsa ntchito mzimu woyera. (Yoh. 14:26) Tikakumana ndi mayesero, mzimu ungatithandize kuti tikumbukire mfundo komanso nkhani za m’Baibulo zomwe zingatithandize kuti tidziwe zoyenera kuchita.

  • Angatithandize pogwiritsa ntchito angelo ake.—Aheb. 1:14.

  • Angagwiritse ntchito Akhristu anzathu kuti atilimbikitse kapena kutithandiza.—Akol. 4:11.

Tikaganizira zimene takambiranazi, kodi tingati mawu a Paulo a pa 1 Akorinto 10:13 akutanthauza chiyani? Yehova sasankha mayesero oti tikumane nawo. Koma mayesero akafika tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti, tikamudalira ndi mtima wonse, sadzalola kuti mayeserowo akule mpaka kufika poti sitingathe kuwapirira. Tizikhulupiriranso kuti nthawi zonse iye amapereka njira yopulumukira kuti tithe kupirira. Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri.