Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudzatengelapo Phunzilo pa Zimene Zinalembedwa?

Kodi Mudzatengelapo Phunzilo pa Zimene Zinalembedwa?

“Zinthu zimenezi . . . zinalembedwa kuti ziticenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikila.”—1 AKOR. 10:11.

NYIMBO 11, 61

1, 2. N’cifukwa ciani tidzakambilana zitsanzo za mafumu anayi aciyuda?

MUKAONA munthu wateleleka n’kugwa, kodi inu simungasamale poyenda pa njilayo? Kuganizila zolakwa zimene anthu ena anacita, kungatithandize kupewa kucita zolakwa zofananazo. Ni mmenenso zilili pa umoyo wathu wauzimu. Tingaphunzile mfundo zothandiza pa zolakwa za ena, kuphatikizapo za anthu amene anachulidwa m’Baibo.

2 Mafumu anayi aciyuda amene tinakambilana m’nkhani yapita, anatumikila Yehova ndi mtima wathunthu. Koma anacitapo zolakwa zina zazikulu. Kodi tingaphunzile ciani pa zimene zinawacitikila? Nanga tingapewe bwanji kucita zolakwa ngati zimene iwo anacita? Kuganizila zitsanzo zimenezi, kungatithandize kupindula na zinthu zimene zinalembedwa kale-kale kuti zitilangize.—Ŵelengani Aroma 15:4.

KUDALILA NZELU ZA ANTHU KUMABWELETSA MAVUTO

3-5. (a) Kodi Asa anakumana ndi vuto lanji ngakhale kuti anali ndi mtima wathunthu kwa Yehova? (b) N’ciani mwina cimene cinapangitsa Asa kudalila anthu pamene Basa anaukila dziko la Yuda?

3 Coyamba, tiyeni tikambilane za Asa, ndi kuona mmene Mau a Mulungu angatithandizile pa umoyo wathu. Asa anadalila Yehova pamene asilikali a ku Itiyopiya 1,000,000 anabwela kudzamenyana ndi dziko la Yuda. Koma iye analephela kudalila Mulungu pamene Basa anayamba kumanga mpanda wolimba kuzungulila mzinda wa Rama, umene unali m’malile mwa dziko la Yuda. (2 Mbiri 16:1-3) Pamene Basa anaukila Yuda, Asa anadalila nzelu zake ndipo anatumiza cuma kwa Mfumu Beni-hadadi ya Siriya kuti ikalimbane ndi Basa. Kodi zimene Asa anacita zinathandiza? Baibo imati: “Basa atangomva zimenezi, nthawi yomweyo anasiya kumanga Rama n’kuimitsa nchito yake.” (2 Mbiri 16:5) Conco, zimene Asa anacita, zinaoneka monga zathandiza.

4 Koma kodi Yehova anamvela bwanji na zimene Asa anacita? Mulungu anatuma Haneni kuti akam’dzudzule cifukwa cosadalila Yehova. (Ŵelengani 2 Mbiri 16:7-9.) Haneni anakamba kuti, “kuyambila tsopano anthu azicita nanu nkhondo.” N’zoona kuti Basa analeka kulimbana ndi Asa. Koma anthu ena sanaleke kucita nkhondo ndi Asa pamodzi ndi anthu ake, mu ulamulila wake wonse.

5 Malinga n’zimene tinakambilana m’nkhani yapita, Mulungu anasanthula mtima wa Asa ndi kuona kuti unali wathunthu. (1 Maf. 15:14) Mulungu anaona kuti, mbali yaikulu, Asa anam’tumikila mokhulupilika mogwilizana ndi zimene iye amafuna. Komabe, Asa anakumana ndi mavuto cifukwa cocita zinthu mosaganiza bwino. Polimbana ndi Basa, n’ciani cinacititsa Asa kudzidalila komanso kudalila anthu ena monga Beni-hadadi m’malo modalila Yehova? Kodi iye anaganiza kuti kucita mgwilizano ndi maufumu ena kapena kukhala na luso pa nkhondo n’kumene kukanam’teteza kuposa kudalila Mulungu? Kodi anakhala na maganizo amenewa cifukwa ca malangizo oipa amene anthu ena anam’patsa?

6. Kodi tiphunzilapo ciani pa colakwa cimene Asa anacita? Pelekani zitsanzo.

6 Nkhani ya Asa iyenela kutilimbikitsa kudzifufuza pa zocita zathu. Tikakumana ndi mavuto aakulu, timazindikila kuti tifunika kudalila Yehova. Koma kodi timacita bwanji tikakumana ndi mavuto ena ooneka ngati ang’ono-ang’ono? Kodi timadalila nzelu zathu poyesa kuthetsa mavutowo? Kapena timafufuza mfundo za m’Baibo ndi kuyesetsa kuziseŵenzetsa, poonetsa kuti timadalila malangizo a Yehova pothetsa mavuto? Mwacitsanzo, nthawi zina anthu a m’banja lanu angakuletseni kupita ku misonkhano yampingo kapena yadela. Zikakhala conco, muyenela kupempha Yehova kuti akutsogoleleni ndi kukuthandizani kuti mudziŵe zimene mungacite. Nanga bwanji ngati nchito imene munali kugwila inatha ndipo simukupezanso ina? Pokamba na munthu amene afuna kukulembani nchito, kodi mudzamuuza kuti tsiku limodzi mkati mwa wiki iliyonse mumafunika kusonkhana? Conco, kaya vuto n’lalikulu kapena laling’ono, tifunika kumvela malangizo a wamasalimo akuti: “Lola kuti Yehova akutsogolele panjila yako, umudalile ndipo iye adzacitapo kanthu.”—Sal. 37:5.

N’CIANI CINGACITIKE NGATI TIGWILIZANA NDI ANTHU OIPA?

7, 8. N’zolakwa ziti zimene Yehosafati anacita? Ndipo panakhala zotsatilapo zotani? (Onani pikica kuciyambi.)

7 Nanga bwanji za Yehosafati mwana wa Asa? Iye anali na makhalidwe ambili abwino. Kudalila Mulungu kunamuthandiza kucita zinthu zambili zabwino. Koma nayenso nthawi ina anapanga zosankha mosaganiza bwino. Mwacitsanzo, Yehosafati anacita mgwilizano wacikwati ndi Ahabu, Mfumu yoipa ya ufumu wa kumpoto wa Isiraeli. Ndipo ngakhale kuti mneneli Mikaya anamucenjeza, iye anapitabe ndi Ahabu kukamenyana ndi Asiriya. Ku nkhondoko, Yehosafati anapulumuka ngakhale kuti anatsala pang’ono kuphedwa. Pambuyo pake, anabwelela ku Yerusalemu. (2 Mbiri 18:1-32) Zitatelo, mneneli Yehu anafunsa Yehosafati kuti: “Kodi cithandizo ciyenela kupelekedwa kwa oipa, ndipo kodi muyenela kukonda anthu odana ndi Yehova?”—Ŵelengani 2 Mbiri 19:1-3.

8 Kodi Yehosafati anaphunzilapo kanthu pa zimene zinacitikazo? Ngakhale kuti anayesetsabe kucita zinthu zokondweletsa Mulungu, zioneka kuti sanaphunzilepo kanthu pa zimene iye ndi Ahabu anakumana nazo, komanso pa mau ocenjeza amene Yehu anamuuza. Yehosafati anapanganso mgwilizano wina ndi anthu ena oipa. Anapanga mgwilizano ndi mdani wa Mulungu, Mfumu yoipa Ahaziya, mwana wa Ahabu. Yehosafati ndi Ahaziya anali kumangila pamodzi zombo. Koma zombozo zinasweka cakuti sanathenso kuzigwilitsila nchito.—2 Mbiri 20:35-37.

9. Kodi kuceza ndi anthu oipa kungakhudze bwanji moyo wathu?

9 Kuŵelenga nkhani ya Yehosafati kuyenela kutilimbikitsa kudzifufuza. Tingacite bwanji zimenezo? Kumbukilani kuti Yehosafati anali mfumu yabwino ndithu. Iye anacita zoyenela ndipo “anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” (2 Mbiri 22:9) Komabe, sakanapewa zotulukapo za mayanjano oipa. Kumbukilani mwambi wouzilidwa uwu: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu, koma wocita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” (Miy. 13:20) Ife timayesetsa kuthandiza anthu acidwi kuphunzila coonadi. Koma tifunika kukumbukila zimene zinacitikila Yehosafati. Iye anatsala pang’ono kutaya moyo wake cifukwa coceza mosayenela ndi Ahabu. Nafenso ngati timakonda kuceza ndi anthu amene satumikila Yehova, tikhoza kukumana ndi mavuto.

10. (a) Ndi phunzilo lanji lokhudza kuloŵa m’banja limene tingatengepo pa nkhani ya Yehosafati? (b) Ni mfundo iti imene tiyenela kukumbukila ngati takopeka ndi anthu oipa?

10 Ndi phunzilo lanji limene tingatengepo pa zimene Yehosafati anakumana nazo? Mkhristu angayambe cibwenzi ndi munthu amene sakonda Yehova, cifukwa coganiza kuti pakati pa Akhristu palibe munthu womuyenelela. Kapena acibale osakhulupilila a Mkhristu angayambe kumukakamiza kuti akwatile kapena kukwatiwa kuti ‘angakalambile pamphala.’ Kuwonjezela apo, Akhristu ena angayambe kukhala na maganizo monga a mlongo wina, amene anati: “Mwacibadwa akazife timafuna kukondedwa ndi kukhala na mnzathu winawake pafupi.” Kodi Mkhristu ayenela kucita ciani zinthu zikakhala conco? Kuganizila zimene zinacitikila Yehosafati kungamuthandize. Nthawi zambili, iye anali kupempha Mulungu kuti amutsogolele. (2 Mbiri 18:4-6) Koma musaiŵale zimene zinamucitikila pamene anayamba kugwilizana ndi Ahabu, amene sanali kukonda Yehova. Yehosafati anafunika kukumbukila kuti maso a Yehova ali pa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye. Masiku anonso, maso a Mulungu “akuyendayenda padziko lonse lapansi,” ndipo iye ndi wokonzeka ‘kuonetsa mphamvu zake’ kwa ife. (2 Mbiri 16:9) Iye amatikonda ndipo amatimvetsetsa. Kodi inu mumakhulupilila kuti Mulungu adzakuthandizani kupeza mnzanu woyenelela amene angakukondeni? Musakayikile kuti panthawi ina yoyenelela, iye adzakuthandizani.

Khalani osamala kuti musamangidwe m’goli ndi osakhulupilila (Onani palagilafu 10)

PEWANI MTIMA WODZIKUZA

11, 12. (a) Kodi Hezekiya anaonetsa bwanji za mumtima mwake? (b) N’cifukwa ciani mkwiyo wa Mulungu sunamugwele Hezekiya?

11 Pa nkhani ya Hezekiya, tiphunzilapo mfundo yonena za mtima. Pa nthawi ina, Mulungu, amene amasanthula mitima analola Hezekiya kuonetsa zimene zinali mumtima mwake. (Ŵelengani 2 Mbiri 32:31.) Pamene Hezekiya anadwala kwambili, Mulungu anamupatsa cizindikilo cakuti adzacila. Cizindikilo cake cinali ca mthunzi umene unabwelela m’mbuyo. Pambuyo pake, mafumu a ku Babulo anatumiza amithenga kwa Hezekiya. Iwo ayenela kuti anawatuma kuti akamve za cizindikiloco. (2 Maf. 20:8-13; 2 Mbiri 32:24) Pa nthawiyo, Mulungu anamusiya Hezeziya, ndipo iye anaonetsa Ababulo “zonse za m’nyumba yake yosungilamo cuma.” Zinthu zopanda nzelu zimene Hezekiya anacita panthawiyo zinavumbula “zonse zimene zinali mumtima mwake.”

12 Baibo siikamba cimene cinacititsa Hezekiya kukhala ndi mtima wodzikuza. Kodi mwina cingakhale cifukwa cakuti anagonjetsa Asuri kapena cifukwa Mulungu anamucilitsa mozizwitsa? Kapena n’cifukwa cakuti anali na “cuma cambili ndi ulemelelo woculuka zedi”? Mulimonsemo, cifukwa ca kudzikuza, Hezekiya “sanabwezele zabwino zimene anacitilidwa.” Zimenezi zinali zomvetsa cisoni kwambili. Ngakhale kuti Hezekiya anatumikila Mulungu ndi mtima wathunthu, iye nthawi ina anacita zinthu zokhumudwitsa Yehova. Koma pambuyo pake, “Hezekiya anadzicepetsa,” ndipo mkwiyo wa Mulungu sunamugwele iye pamodzi ndi anthu ake.—2 Mbiri 32:25-27; Sal. 138:6.

13, 14. (a) Ndi pa zocitika monga ziti pamene Yehova ‘angatisiye kuti atiyese’? (b) Tingacite ciani ngati anthu ena atitamanda pa zabwino zimene tacita?

13 Kodi kuŵelenga ndi kusinkhasinkha nkhani ya Hezekiya kungatipindulitse bwanji? Kumbukilani kuti kudzikuza kwa Hezekiya kunaonekela bwino pamene Yehova anagonjetsa Senakeribu, ndi kucilitsa Hezekiyayo pamene anadwala matenda aakulu. Nafenso tingacite zinthu zina-zake zabwino kwambili, ndipo Yehova ‘angatisiye kuti atiyese’ ndi kuona zonse zimene zili mumtima mwathu. Mwacitsanzo, m’bale angakonzekele bwino nkhani ndi kukaikamba bwino pa msonkhano waukulu. Ndipo abale ndi alongo ambili angayambe kumutamanda. Kodi iye afunika kucita ciani?

14 Anthu akatitamanda, tingacite bwino kutsatila mau a Yesu akuti: “Mukacita zonse zimene munapatsidwa ngati nchito yanu, muzinena kuti, ‘Ife ndife akapolo opanda pake. Tangocita zimene tinayenela kucita.’” (Luka 17:10) Palinso mfundo ina imene tingaphunzilepo pa nkhani ya Hezekiya. Iye anaonetsa kuti anali wodzikuza mwa ‘kusabwezela zabwino zimene anacitilidwa.’ Kuganizila zabwino zimene Yehova waticitila, kudzatithandiza kupewa makhalidwe amene iye amadana nawo. Tifunika kumakamba zinthu zoyamikila Yehova. Iye watipatsa Malemba Opatulika ndi mzimu woyela umene umathandiza anthu ake.

MUZISAMALA POPANGA ZOSANKHA

15, 16. N’cifukwa ciani Yosiya anaphedwa? Nanga n’cifukwa ciani Mulungu sanamuteteze?

15 Ndi cenjezo lanji limene tingatengepo pa zimene zinacitikila Mfumu yabwino Yosiya? Ganizilani zimene zinacititsa kuti iye agonjetsedwe ndi kuphedwa. (Ŵelengani 2 Mbiri 35:20-22.) Yosiya “anapita kukakumana” ndi Mfumu Neko ya Iguputo, ngakhale kuti mfumuyo inamuuza kuti siinali kufuna kumenyana ndi iye. Baibo imakamba kuti mau a Neko anali “ocokela pakamwa pa Mulungu.” Nanga n’cifukwa ciani Yosiya anapita kukamenyana naye? Baibo siikamba ciliconse.

16 Koma kodi Yosiya akanadziŵa bwanji kuti mau a Neko anali ocokela kwa Yehova? Iye akanafunsa Yeremiya, mmodzi wa aneneli okhulupilika. (2 Mbiri 35:23, 25) Koma m’Baibo mulibe mau oonetsa kuti anacita zimenezo. Komanso Neko anali kupita kukacita nkhondo ku Karikemisi. Iye anali kupita kukamenyana “ndi mtundu wina,” osati Yerusalemu. Kuwonjezela apo, dzina la Mulungu silinali kukhudzidwa, cifukwa Neko sanali kutonza Yehova kapena anthu ake. Conco, sicinali cinthu canzelu Yosiya kukacita nkhondo ndi Neko. Kodi tiphunzilapo ciani pa nkhaniyi? Tikakumana ndi vuto, tifunika kuganizila zimene Yehova afuna kuti ticite.

17. Tikakumana ndi vuto, tingacite ciani kuti tipewe kucita colakwa ngati cimene Yosiya anacita?

17 Tikakumana ndi vuto linalake, tifunika kuganizila mfundo za m’Baibo zokhudzana ndi nkhaniyo ndi kuziseŵenzetsa m’njila yoyenela. Nthawi zina tingafunike kufunsa akulu. Tingafunikenso kuganizila mfundo zina zimene tikudziŵa kale pankhaniyo, ndiponso kufufuza m’zofalitsa zathu. Komanso pangakhale mfundo zina za m’Baibo zofunika kuziganizila zimene mkulu angatiuze. Mwacitsanzo, Mkhristu aliyense amadziŵa kuti ali ndi udindo wolalikila uthenga wabwino. (Mac. 4:20) Ndiyeno tiyelekezele kuti mlongo, amene mwamuna wake ndi wosakhulupilila, wakonza zakuti apite mu ulaliki. Koma mwamuna wakeyo afuna kuti mlongoyo akhale panyumba. Mwamunayo waona kuti iye ndi mkazi wake sakhala na nthawi yokwanila yoceza, ndipo afuna kuti iwo acitileko pamodzi zinthu zina monga banja. Mlongoyo angaganizile mfundo zofunika za m’Baibo monga mfundo yakuti tifunika kumvela Mulungu ndi yakuti tifunika kupanga ophunzila. (Mat. 28:19, 20; Mac. 5:29) Koma iye afunikanso kuganizila mfundo yakuti mkazi afunika kukhala wogonjela ndi wololela. (Aef. 5:22-24; Afil. 4:5) Angafunikenso kuganizila ngati mwamuna wakeyo nthawi zonse amamuletsa kupita muulaliki, kapena ndi tsiku limenelo cabe limene wam’pempha kuti asapite. Kukamba zoona, timafunika kukhala oganiza bwino pamene ticita cifunilo ca Mulungu ndiponso pamene tiyesetsa kukhala ndi cikumbumtima cabwino.

KHALANIBE NDI MTIMA WATHUNTHU KUTI MUKHALE ACIMWEMWE

18. Kodi kuganizila za mafumu anayi amene takambilana kungakupindulitseni bwanji?

18 Popeza ndife opanda ungwilo, nafenso tingacite zolakwa ngati zimene anacita mafumu anayi amene takambilana m’nkhani ino. Mwina tingayambe (1) kudalila nzelu za anthu mosadziŵa,  (2) kugwilizana ndi anthu oipa, (3) kudzikuza, kapena (4) kupanga zosankha tisanaganizile zimene Mulungu afuna. Yehova ni Mulungu wokoma mtima kwambili, ndipo amaona zabwino mwa ife monga mmene anacitila ndi mafumu anayi amene takambilana. Iye amaonanso kuti timamukonda kwambili, ndiponso timafuna kum’tumikila ndi mtima wonse. Conco, pofuna kutithandiza kuti tipewe kucita zolakwa zazikulu, Yehova watipatsa zitsanzo zoticenjeza. Tiyeni tipitilize kuganizila nkhani za m’Baibo zimenezi, ndipo tiziyamikila kuti Yehova watipatsa zitsanzo zimenezi kuti zitilangize.