Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Muzikwanilitsa Zimene Mwalonjeza”

“Muzikwanilitsa Zimene Mwalonjeza”

“Uzikwanilitsa malonjezo ako kwa Yehova.”—MAT. 5:33

NYIMBO: 63, 59

1. (a) Kodi Woweluza Yefita na Hana anali kulingana m’mbali ziti? (Onani mapikica pamwambapa.) (b) Ni mafunso ati amene adzayankhidwa m’nkhani ino?

WOWELUZA Yefita anali mtsogoleli wolimba mtima, ndipo Hana anali mkazi wogonjela. Yefita analinso msilikali wolimba mtima, pamene Hana anali mzimayi wodzicepetsa. Yefita, ndi Hana mkazi wa Elikana, onse anali kulambila Mulungu mmodzi. Nanga n’ciani cina cimene cinali colingana pa anthu aŵiliwa? Onse analonjeza Mulungu zinazake, ndipo anakwanilitsa zimene analonjezazo. Iwo n’zitsanzo zabwino ngako kwa amuna ndi akazi amakono, amene amacita malonjezo kwa Yehova. Komabe, tingafunse kuti: Kodi lonjezo n’ciani? N’cifukwa ciani malonjezo amene timapanga kwa Mulungu ni nkhani yaikulu? Nanga tingaphunzile ciani kwa Yefita ndi Hana pa nkhaniyi?

2, 3. (a) Kodi lonjezo n’ciani? (b) Kodi Malemba amati ciani pa nkhani yopanga malonjezo kwa Mulungu?

2 M’Baibo, liwu lakuti lonjezo limatanthauza cowinda cimene munthu amapanga kwa Mulungu. Munthu angalonjeze kucita zinthu, kupeleka mphatso, kuyamba utumiki, kapena kupewa kucita zinazake. Munthu amapanga lonjezo mwa kufuna kwake. Komabe, Mulungu amaona kuti malonjezo amene timapanga ni opatulika, ndipo ni osasinthika cifukwa amalowetsamo lumbilo lakuti munthu adzacita zinthu zina kapena sadzacita. (Gen. 14:22, 23; Aheb. 6:16, 17) Kodi Malemba amaonetsa bwanji kuti kupanga malonjezo kwa Mulungu ni nkhani yaikulu?

3 Cilamulo ca Mose cinati: “Munthu akalonjeza kwa Yehova, kapena akacita lumbilo . . . , asalephele kukwanilitsa mau ake. Acite malinga ndi mau onse otuluka pakamwa pake.” (Num. 30:2) Pambuyo pake, Solomo anauzilidwa kulemba kuti: “Ukalonjeza kwa Mulungu usamacedwe kukwanilitsa lonjezo lako, cifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa. Uzikwanilitsa zinthu zimene walonjeza.” (Mlal. 5:4) Yesu nayenso anaonetsa kuti kupanga malonjezo ni nkhani yaikulu. Iye anati: “Munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbile koma osacita, m’malomwake uzikwanilitsa malonjezo ako kwa Yehova.’”—Mat. 5:33.

4. (a) Kodi kupanga lonjezo kwa Mulungu ni nkhani yaikulu bwanji? (b) Tidzaphunzila zotani zokhudza Yefita ndi Hana?

4 Apa n’zoonekelatu kuti kupanga malonjezo kwa Mulungu si nkhani yofunika kuitenga mopepuka. Zimene timacita pa malonjezo amene tinapanga zimakhudza ubale wathu na Yehova. Davide anati: “Ndani angakwele m’phili la Yehova? Ndipo ndani anganyamuke kukaloŵa m’malo ake opatulika? Aliyense . . . amene sanaone Moyo wanga ngati wopanda pake, kapena kulumbila mwacinyengo.” (Sal. 24:3, 4) Kodi Hana ndi Yefita analonjeza ciani? Nanga kodi cinali copepuka kwa iwo kukwanilitsa malonjezo awo?

ANAKWANILITSA MALONJEZO AWO KWA MULUNGU MOKHULUPILIKA

5. Kodi Yefita analonjeza ciani? Nanga panakhala zotulukapo zanji?

5 Yefita anasunga lonjezo limene anauza Yehova pamene anali kupita kukacita nkhondo ndi Aamoni, amene anali kuwopseza anthu a Mulungu. (Ower. 10:7-9) Pofuna kuti akapambane pa nkhondoyo, Yefita analonjeza kuti: “Ngati mudzapelekadi ana a Amoni m’manja mwanga, ine ndidzapeleka kwa Yehova aliyense amene adzatuluka m’nyumba yanga kudzandicingamila pamene ndikubwela mwamtendele kucokela kwa ana a Amoni.” Kodi zotulukapo zake zinali zotani? Aamoni anagonjetsedwa, ndipo amene anatuluka m’nyumba ya Yefita kudzam’cingamila pocokela kunkhondo atapambana, anali mwana wake wokondedwa. Mwanayo ndiye anafunika ‘kupelekedwa kwa Yehova.’ (Ower. 11:30-34) Kodi zimenezi zinatanthauza ciani kwa mwanayo?

6. (a) Kodi cinali copepuka kwa Yefita na mwana wake kukwanilitsa zimene analonjeza kwa Mulungu? (b) Pankhani yopanga malonjezo kwa Mulungu, kodi tiphunzilapo ciani pa lemba la Deuteronomo 23:21, 23 ndi la Masalimo 15:4?

6 Kuti mwana wa Yefita akwanilitse lonjezo la atate ake, anafunika kutumikila Yehova nthawi zonse pa cihema. Kodi Yefita anacita lonjezo limeneli mopupuluma? Iyayi. Iye ayenela kuti anali kudziŵa kuti amene adzatuluke m’nyumba n’kubwela kudzakumana naye angakhale mwana wake. Ngakhale n’conco, sicinali copepuka kwa Yefita ndi mwanayo kukwanilitsa zimene analonjeza. Onse anafunikadi kudzimana zinazake. Conco, Yefita ataona mwana wake, “anayamba kung’amba zovala zake” ndi kukamba kuti mtima wake wasweka. Mwana wake ‘analilila unamwali wake.’ Cifukwa ciani? Yefita analibe mwana aliyense wamwamuna. Ndipo cifukwa ca lonjezo limeneli, mwana wake wamkazi mmodzi yekhayu sakanakwatiwa kuti amubelekele adzukulu. Panalibenso amene akanatenga dzina la banja ndi kulandila coloŵa. Olo kuti zinali conco, nkhawa yaikulu ya Yefita siinali pa zimene tachulazi. Iye anati: “Ndatsegula pakamwa panga pamaso pa Yehova, ndipo sindingathe kubweza mau anga.” Ndipo mwana wake anati: “Ndicitileni mogwilizana ndi zimene zatuluka pakamwa panu.” (Ower. 11:35-39) Yefita ndi mwana wake anali okhulupilika, ndipo sanaganizilepo zophwanya lonjezo limene anacita kwa Mulungu Wam’mwambamwamba, ngakhale kuti anafunika kudzimana zambili kuti akwanilitse lonjezolo.—Ŵelengani Deuteronomo 23:21, 23; Masalimo 15:4.

7. (a) Kodi Hana analonjeza ciani, ndipo n’cifukwa ciani? Nanga zinamuyendela bwanji? (b) Kodi lonjezo la Hana linatanthauza ciani kwa Samueli? (Onani mau a munsi.)

7 Hana nayenso anasunga mokhulupilika lonjezo limene anapanga kwa Yehova. Iye anacita lonjezo limeneli pamene anali kusautsika ndi nkhawa mumtima mwake cifukwa ca kusabeleka ndiponso cifukwa cotonzedwa nthawi zonse ndi mkazi mnzake. (1 Sam. 1:4-7, 10, 16) Hana anakhutulila Mulungu nkhawa zake zonse na kum’lonjeza kuti: “Inu Yehova wa makamu, mukaona nsautso yanga, ine kapolo wanu wamkazi, ndi kundikumbukila, ndiponso ngati simudzaiŵala kapolo wanu wamkazi ndi kum’patsa mwana wamwamuna, ndidzam’peleka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo lezala silidzadutsa m’mutu mwake.” * (1 Sam. 1:11) Mulungu anayankha pemphelo la Hana, ndipo iye anabeleka mwana woyamba wamwamuna. Hana anakondwela kwambili. Koma sanaiŵale zimene analonjeza Mulungu. Atabeleka mwana wamwamunayo, iye anati: “Ndinam’pempha kwa Yehova.”—1 Sam. 1:20.

8. (a) Kodi cinali copepuka kwa Hana kukwanilitsa lonjezo lake? (b) Kodi mau a Davide a mu Salimo 61, amakukumbutsani bwanji citsanzo cabwino ca Hana?

8 Samueli atangoleka kuyamwa, mwina ali na zaka zitatu, Hana anacita ndendende zimene analonjeza Mulungu. Iye sanaganizeko kucita zosiyana ndi zimene analonjeza. Anatenga Samueli n’kupita naye kwa Mkulu wa Ansembe Eli, ku cihema ku Silo. Ndipo Hana anauza Eli kuti: “Ndinali kupemphela kuti Yehova andipatse mwana uyu, kuti andipatse cimene ndinam’pempha. Ndipo ine ndikum’peleka kwa Yehova. Ndam’peleka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.” (1 Sam. 1:24-28) Kumeneko “Mwanayo Samueli anapitiliza kukula, akukondedwa ndi Yehova.” (1 Sam. 2:21) Koma kodi zimenezo zinamukhudza bwanji Hana? Iye anali kum’konda kwambili mwana wake wam’ng’ono, koma apa sakanakwanitsa kukamba naye tsiku lililonse. Ganizilani mmene Hana anayewela kukumbatila mwana wake, kuseŵela naye, kum’phunzitsa, ndi kucita zinthu zina zosiyana-siyana zimene mayi wacikondi amacita ndi mwana wake wam’ng’ono akamakula. Ngakhale n’conco, Hana sanadandaule cifukwa cosunga lonjezo lake kwa Mulungu. Mtima wake unali kukondwela mwa Yehova.—1 Sam. 2:1, 2; ŵelengani Masalimo 61:1, 5, 8.

Kodi mukukwanilitsa malonjezo anu kwa Yehova?

9. Kodi tifunika kupeza mayankho pa mafunso ati?

9 Popeza lomba tadziŵa kuti kupanga lonjezo kwa Mulungu ni nkhani yaikulu, tiyeni tikambilane mafunso aya: Ndi malonjezo ati amene ise Akhristu tingapange? Nanga kuti tisunge malonjezowo, tifunika kuwaona bwanji?

LONJEZO LA KUDZIPELEKA KWANU KWA MULUNGU

Lonjezo la kudzipeleka (Onani palagilafu 10)

10. Ni lonjezo lofunika kwambili liti limene Mkhristu angapange? Nanga kucita zimenezi kuphatikizapo ciani?

10 Lonjezo lofunika kwambli limene Mkhristu angapange ni la kudzipeleka kwa Yehova. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa m’pemphelo lake la payekha, munthu ndi mtima wonse, amalonjeza Yehova kuti adzam’tumikila kwa moyo wake wonse zivute zitani. Mogwilizana ndi mau a Yesu, munthuyo ‘amadzikana yekha.’ Amasiya moyo wodzikondweletsa yekha, ndipo amalonjeza kuti adzaika patsogolo zofuna za Mulungu mu umoyo wake. (Mat. 16:24) Kuyambila tsiku limenelo kupita mtsogolo, munthuyo ‘amakhala wa Yehova.’ (Aroma. 14:8) Aliyense amene wacita lonjezo la kudzipeleka afunika kuiona kuti ni nkhani yaikulu monga mmene wamasalimo anacitila. Poneza za malonjezo amene anapanga kwa Mulungu, iye anati: “Yehova ndidzamubwezela ciani pa zabwino zonse zimene wandicitila? Ndidzakwanilitsa malonjezo anga kwa Yehova, pamaso pa anthu ake onse.”—Sal. 116:12, 14.

11. N’ciani cinacitika patsiku la ubatizo wanu?

11 Kodi munadzipeleka kwa Yehova ndi kuonetsa kudzipelekako mwa kubatizika m’madzi? Ngati n’conco, munacita bwino kwambili. Kumbukilani kuti patsiku la ubatizo wanu munafunsidwa mafunso pamaso pa mboni zambili. Munafunsidwa ngati munadzipeleka kwa Yehova ndi ‘kuzindikila kuti kudzipeleka kumene munacita, ndi kubatizidwa kwanu, zinakupangitsani kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, wogwilizana ndi gulu la Mulungu limene amalitsogolela ndi mzimu wake.’ Mayankho anu otsimikiza ndi omveka bwino, anaonetsa poyela kuti munadzipeleka na mtima wonse, ndi kuti munali oyenelela kubatizidwa monga mtumiki woikidwa wa Yehova. Yehova anakondwela ngako na zimene munacita patsikulo.

12. (a) Ni mafunso ati amene tifunika kudzifunsa? (b) Kodi Petulo anakamba kuti tifunika kukhala na makhalidwe ati?

12 Koma ubatizo ni ciyambi cabe. Tikabatizika, timafunika kucitabe zinthu mogwilizana ndi kudzipeleka kwathu mwa kutumikila Mulungu mokhulupilika. Conco, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi napita patsogolo mwauzimu kucokela pamene n’nabatizika? Kodi nipitiliza kutumikila Yehova na mtima wonse? (Akol. 3:23) Kodi nimapemphela, kuŵelenga Mau a Mulungu, kusonkhana, ndi kulalikila nthawi zonse? Kapena cangu canga cayamba kuzilala?’ Mtumwi Petulo anafotokoza zimene zingatithandize kuti tisakhale ozilala pa utumiki wathu. Iye anakamba kuti pa cikhulupililo cathu, tifunika kupitiliza kuwonjezelapo kudziŵa zinthu, kupilila, ndi kukhala odzipeleka kwa Mulungu.—Ŵelengani 2 Petulo 1:5-8.

13. Kodi Mkhristu wodzipeleka wobatizika afunika kuzindikila ciani?

13 Lonjezo la kudzipeleka kwathu kwa Mulungu n’losasinthika. Tikalonjeza, talonjeza. Ngati munthu walema na kutumikila Yehova kapena kutsatila mfundo zacikhristu, safunika kukamba kuti sanadzipeleke zeni-zeni kwa Mulungu, kapena kuti ubatizo wake unali wosayenelela. * Iye anadzipeleka ndithu kwa Mulungu. Conco, ngati munthuyo wacita chimo lalikulu, adzayankha mlandu kwa Yehova ndi ku mpingo. (Aroma 14:12) Tifunika kucita khama kuti ‘tisasiye cikondi cimene tinali naco poyamba.’ Tikatelo, Yesu adzatiuza kuti: “Ndikudziŵa nchito zako, cikondi cako, cikhulupililo cako, utumiki wako, ndi kupilila kwako. Ndikudziŵanso kuti nchito zako zapanopa n’zambili kuposa zoyamba zija.” (Chiv. 2:4, 19) Tiyeni tipitilize kucita khama kuti tizicita zinthu mogwilizana ndi lonjezo lathu la kudzipeleka. Tikacita conco, Yehova adzakondwela.

LONJEZO LANU LA CIKWATI

Lonjezo la cikwati (Onani palagilafu 14)

14. Ni lonjezo lina liti lofunika kwambili limene munthu angapange? Nanga n’cifukwa ciani n’lofunika kwambili?

14 Lonjezo lina lofunika kwambili limene munthu angapange, ni lonjezo la cikwati. Zili conco cifukwa cikwati n’copatulika. Mkwati ndi mkwatibwi amapanga malonjezo awo a cikwati pamaso pa Mulungu ndi pa anthu ambili. Iwo amalonjeza kuti adzakondana, kusamalilana, ndi kulemekezana ‘pa nthawi yonse imene aŵiliwo adzakhala ndi moyo padziko lapansi, mogwilizana ndi zimene Mulungu anakonza pa nkhani ya cikwati.’ Olo kuti ena sakamba mau amenewa ndendende, amakhalabe atalumbila pamaso pa Mulungu. Akatelo, amayamba kudziŵika kuti ndi banja, ndipo cikwati cawo cimafunika kukhala mgwilizano wa moyo wonse. (Gen. 2:24; 1 Akor. 7:39) “Conco,” mogwilizana ndi mau a Yesu, “cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.” Izi zitanthauza kuti mwamuna, mkazi kapena munthu wina aliyense safunika kuthetsa cikwati. Motelo, anthu amene akuloŵa m’banja safunika kukhala na maganizo akuti m’banja mukadzabuka mavuto, adzangothetsa cikwati.—Maliko 10:9.

15. N’cifukwa ciani Akhristu safunika kuona cikwati mopepuka monga mmene anthu a m’dzikoli amacitila?

15 Anthu onse amene amamanga banja ndi opanda ungwilo. Conco, kulibe cikwati cangwilo. N’cifukwa cake Baibo imakamba kuti anthu oloŵa m’banja nthawi zina “adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akor. 7:28) N’zomvetsa cisoni kuti anthu ambili m’dzikoli amaona cikwati mopepuka. Iwo akayambana ndi mnzawo wa m’cikwati, amangomuthaŵa. Koma Mkhristu safunika kucita zimenezi. Kuphwanya lonjezo la cikwati n’kunamiza Mulungu, ndipo Mulungu amadana ndi anthu abodza. (Lev. 19:12; Miy. 6:16-19) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kodi ndiwe womangika kwa mkazi? Leka kufunafuna njila yomasukila.” (1 Akor. 7:27) Paulo anakamba izi cifukwa anali kudziŵa kuti Yehova amadana ndi anthu amene amathetsa cikwati mwacinyengo.—Mal. 2:13-16.

16. Kodi Baibo imakamba zotani pa pankhani yothetsa cikwati ndi kupatukana?

16 Yesu anaphunzitsa kuti maziko okha a m’Malemba othetsela cikwati ndi pamene wina wacita cigololo, ndipo mnzake wosalakwa wasankha kuti asam’khululukile. (Mat. 19:9; Aheb. 13:4) Nanga bwanji za kupatukana ndi mnzako wa m’cikwati, osati kusudzulana? Baibo imapeleka malangizo osapita mbali pankhani imeneyi. (Ŵelengani 1 Akorinto 7:10, 11.) Koma siifotokoza mwacindunji zifukwa zimene zingacititse anthu kupatukana. Ngakhale n’conco, Akhristu ena amene ali pabanja asankha kupatukana ndi mnzawo pa zifukwa zina. Mwacitsanzo, ena asankha kupatukana poona kuti moyo wawo wauzimu kapena wakuthupi uli pa ciopsezo cacikulu cifukwa mnzawo wa m’cikwati ndi wankhanza kapena wampatuko. *

17. Kodi mabanja acikhristu angacite ciani kuti cikwati cawo cikhale colimba?

17 Ngati anthu afikila akulu kuti awathandize pa mavuto a m’banja, akuluwo angacite bwino kuwafunsa ngati posacedwapa anaonelelako monga banja vidiyo yakuti Chikondi Chenicheni. Angawafunsenso ngati anaphunzilako pamodzi kabuku kakuti N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe. N’cifukwa ciani afunika kucita conco? Cifukwa zida zimenezi zifotokoza mfundo za m’Baibo zimene zathandiza anthu ambili kulimbitsa vikwati vawo. Banja lina linati: “Kucokela pamene tinayamba kuphunzila kabuku kameneka, banja lathu lakhala lacimwemwe ngako.” Mkazi wina amene wakhala m’cikwati kwa zaka 22, amene cikwati cawo cinatsala pang’ono kutha, anakamba kuti: “Tonse ndise obatizika, koma tinakhumudwitsana kwambili ndipo sitinali kugwilizana. Vidiyo yakuti Cikondi Ceniceni inabwela panthawi yake. Lomba banja lathu likuyenda bwino.” Kodi inu muli pabanja? Ngati n’conco, muziyesetsa kuseŵenzetsa mfundo za Yehova m’cikwati canu. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kusunga malumbilo anu acikwati, ndipo mudzakhala acimwemwe.

LONJEZO LA ATUMIKI ANTHAWI ZONSE APADELA

18, 19. (a) Kodi makolo ambili Acikhristu acita ciani? (b) Fotokozani zokhudza atumiki a nthawi zonse apadela.

18 Kodi cinthu cina cimene Yefita ndi Hana anali kufanana n’citi? Zimene iwo analonjeza zinacititsa kuti ana awo ayambe utumiki wapadela pacihema. Mu utumiki umenewo, anawo anakhala na umoyo wabwino koposa. Masiku anonso, makolo ambili acikhristu alimbikitsa ana awo kuyamba utumiki wanthawi zonse ndi kutumikila Mulungu na mtima wawo wonse. Makolo ndi acicepele amene acita zimenezi timawayamikila kwambili.—Ower. 11:40; Sal. 110:3.

Lonjezo la utumiki wanthawi zonse wapadela (Onani palagilafu 19)

19 Palipano, pali abale na alongo pafupi-fupi 67,000 amene ali m’Gulu la Padziko Lonse la Atumiki Apadela a Mboni za Yehova. Ena amatumikila pa Beteli, ena amagwila nchito yomanga kapena yadela. Enanso amatumikila monga apainiya apadela, amishonale, alangizi a masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu, kapena atumiki a pa Bwalo la Msonkhano kapena pamalo ocitila sukulu yophunzitsa Baibo. Atumiki onsewa anacita Lumbilo la Kumvela ndi Umoyo Wosalila Zambili. Mwa kupanga lumbilo limeneli, amaonetsa kuti avomeleza kugwila nchito iliyonse imene angapatsidwe kuti apititse patsogolo nchito ya Ufumu. Amavomelezanso kuti adzakhala na umoyo wosalila zambili, ndi kuti sadzaloŵa nchito kwina kulikonse popanda cilolezo. Sikuti anthu amene amacita utumikiwu ni apadela, koma utumiki wawo ndiwo wapadela. Iwo amadziŵa kuti afunika kuyesetsa kusunga lonjezo lawo pamene ali mu utumiki wanthawi zonse wapadela.

20. Kodi tifunika kucita ciani “tsiku ndi tsiku”? Nanga n’cifukwa ciani?

20 Pa malonjezo amene takambilana, kodi inu munapangapo malonjezo angati kwa Mulungu? Limodzi, aŵili, kapena onse atatu? Lomba tadziŵa kuti malonjezo athu sitiyenela kuyaona mopepuka. (Miy. 20:25) Kulephela kusunga lonjezo lathu kwa Yehova kungatibweletsele mavuto aakulu. (Mlal. 5:6) Conco, tiyeni ‘tiziyimba mokondwela nyimbo zotamanda dzina la Yehova mpaka muyaya, pamene tikukwanilitsa malonjezo athu tsiku ndi tsiku.’—Sal. 61:8.

^ par. 7 Hana analonjeza kuti akadzabeleka mwana, mwanayo adzakhala Mnazili kwa moyo wake wonse, kutanthauza kuti adzapatulidwa ndi kupelekedwa kwa Yehova kuti nchito yake ikhale kutumikila iye basi.—Num. 6:2, 5, 8.

^ par. 13 Popeza pali zambili zimene akulu amapenda pofuna kutsimikizila kuti munthu ni woyenelela kubatizika, sizicitika-citika kuti ubatizo wa munthu ukhale wosayenelela.

^ par. 16 Onani buku lakuti Khalanibe M’cikondi ca Mulungu,mapeji. 219-221.