Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizithandiza Alendo Kuti ‘Azitumikira Yehova Mokondwera’

Tizithandiza Alendo Kuti ‘Azitumikira Yehova Mokondwera’

“Yehova amayang’anira alendo okhala m’dziko la eni.”​—SAL. 146:9.

NYIMBO: 84, 73

1, 2. (a) Kodi abale ndi alongo athu ena akumana ndi mavuto otani? (b) Kodi tingadzifunse mafunso ati?

M’BALE wina dzina lake Lije ananena kuti: “Pamene nkhondo yapachiweniweni inkayambika ku Burundi, banja lathu linali kumsonkhano ndipo tinkaona anthu akuwombera anzawo komanso ena akuthawa. Ana tonse 11 limodzi ndi makolo athu tinathawa titangonyamula zinthu zochepa kwambiri. Anthu ena a m’banja lathu anathawira kumalo ena a anthu othawa kwawo ku Malawi, ndipo unali ulendo wa makilomita 1,600. Enafe tinathawira kumalo osiyanasiyana.”

2 Padziko lonse, chiwerengero cha anthu amene athawa kwawo chifukwa cha kuzunzidwa kapena nkhondo panopa ndi choposa 65,000,000. Chiwerengerochi n’chapamwamba kwambiri kuposa kale lonse. * M’gululi mulinso a Mboni za Yehova ambiri ndipo ena mwa iwo achibale awo anaphedwa komanso katundu wawo anawonongedwa kapena kulandidwa. Koma kodi ndi mavuto ena ati amene amakumana nawo? Nanga tingawathandize bwanji kuti ‘azitumikirabe Yehova mokondwera’? (Sal. 100:2) Kodi tingathandize bwanji anthu othawa kwawo omwe si Mboni kuti adziwe uthenga wabwino?

ZIMENE ANTHU OTHAWA KWAWO AMAKUMANA NAZO

3. Kodi Yesu komanso Akhristu ena anathawa kwawo chifukwa chiyani?

3 Mngelo wa Yehova atachenjeza Yosefe kuti Mfumu Herode inkafuna kupha Yesu, Yosefe anathawa ndi banja lake n’kupita ku Iguputo. Iwo anakhalabe komweko mpaka pamene Herode anamwalira. (Mat. 2:13, 14, 19-21) Pa nthawi ina, Akhristu oyambirira “anabalalikira m’zigawo za Yudeya ndi Samariya” chifukwa choti ankazunzidwa. (Mac. 8:1) Yesu anasonyezanso kuti otsatira ake ambiri adzathawa kwawo. Iye anati: “Akakuzunzani mumzinda wina, muthawire mumzinda wina.” (Mat. 10:23) Koma kodi anthu othawa kwawo amakumana ndi mavuto ati?

4, 5. Kodi anthu akhoza kukumana ndi mavuto ati (a) akamathawa kwawo? (b) akafika m’makampu?

4 Anthu akhoza kukumana ndi zinthu zoopsa akamathawa kwawo komanso akafika kumalo amene akuthawira. Mwachitsanzo, mng’ono wa Lije dzina lake Gad anati: “Tinayenda kwa milungu yambiri ndipo m’malo amene tinkadutsa tinkapeza mitembo ya anthu yambirimbiri. Pa nthawiyo n’kuti ndili ndi zaka 12 zokha. Mapazi anga anatupa kwambiri moti ndinauza makolo anga kuti kuli bwino angondisiya. Bambo anga anandinyamula chifukwa sanafune kuti ndigwidwe ndi zigawengazo. Tinkadalira kwambiri Yehova ndipo tinkangokhalira kupemphera. Nthawi zina tinkangodya mango a m’mbali mwa njira.”​—Afil. 4:12, 13.

5 Anthu ambiri a m’banja la Lije anakhala zaka zambiri m’makampu a bungwe la United Nations. Koma sikuti anali otetezeka m’makampumo. Lije, yemwe panopa ndi woyang’anira dera, anati: “Anthu ambiri m’makampuwa sankagwira ntchito. Choncho ankangokhalira kulankhula miseche, kumwa mowa, kutchova juga, kuba komanso kuchita zachiwerewere.” Kuti a Mboni apewe zoipazi, ankayenera kukhala ndi zochita zambiri potumikira Yehova. (Aheb. 6:11, 12; 10:24, 25) Kuti akhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, anthu ambiri ankachita upainiya. A Mboniwa sankataya mtima chifukwa ankadziwa kuti tsiku lina adzachoka m’makampuwa ngati mmene zinalili ndi Aisiraeli m’chipululu.​—2 Akor. 4:18.

TIZISONYEZA CHIKONDI KWA ANTHU OTHAWA KWAWO

6, 7. (a) Kodi Akhristu amathandiza bwanji anzawo amene ali pa mavuto? (b) Perekani chitsanzo.

6 Chifukwa chokonda Mulungu, timasonyezana chikondi makamaka pa nthawi ya mavuto. (Werengani 1 Yohane 3:17, 18.) Mwachitsanzo, pamene Akhristu a ku Yuda ankavutika ndi njala, mpingo unakonza zoti alandire thandizo. (Mac. 11:28, 29) Mtumwi Paulo komanso Petulo analimbikitsanso Akhristu kuti azikhala ochereza. (Aroma 12:13; 1 Pet. 4:9) Ngati timafunika kulandira Akhristu anzathu amene angobwera kudzacheza, kuli bwanji amene athawa kwawo chifukwa choti moyo wawo unali pa ngozi kapena akuzunzidwa chifukwa chokhala a Mboni?​—Werengani Miyambo 3:27. *

7 Posachedwapa, a Mboni za Yehova ambirimbiri, kuphatikizapo ana, anathawa nkhondo imene inkachitika m’madera akum’mawa m’dziko la Ukraine. Mwatsoka, ena mwa iwo anaphedwa. Koma ambiri anatha kuthawa ndipo abale ndi alongo a m’madera ena a ku Ukraine ndiponso a m’dziko la Russia anawalandira m’nyumba zawo. A Mboni a m’mayiko onse awiriwa akupewabe kukhala “mbali ya dziko” ndipo akupitiriza mwakhama ‘kulengeza uthenga wabwino wa mawu opatulika.’​—Yoh. 15:19; Mac. 8:4.

TIZIWATHANDIZA KUTI AKHALE NDI CHIKHULUPIRIRO CHOLIMBA

8, 9. (a) Kodi anthu amene athawira m’dziko lina akhoza kukumana ndi mavuto ati? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuwathandiza moleza mtima?

8 Anthu ena amathawira m’madera ena a m’dziko lawo lomwelo pomwe ena amapita kudziko lina. Maboma akhoza kupereka chakudya, zovala ndiponso malo okhala komabe mwina zakudya zimene anthuwa anazolowera sazipeza. Anthu ochokera m’mayiko otentha amatha kuthawira m’mayiko ozizira kwambiri koma amakhala alibe zovala zoyenera. Komanso ngati anthu othawa kwawo akuchokera m’madera akumidzi ndipo afikira kumalo amene kuli zipangizo zamakono, mwina sangadziwe mmene angazigwiritsire ntchito.

9 Maboma ena amathandiza anthu othawa kwawo kuti azolowere moyo watsopano. Komabe nthawi zina pakangopita nthawi yochepa, amayembekezera kuti anthuwo ayambe kumapeza okha zofunika pa moyo. Zimenezi zingakhale zovuta kwambiri. Tangoganizirani zinthu zimene anthuwa mwina ayenera kusintha pa nthawi imodzi. Ayenera kuphunzira chinenero ndi chikhalidwe chatsopano. Ayeneranso kutsatira malamulo atsopano pa nkhani monga misonkho, njira zolipirira zinthu, kupita kusukulu komanso kulera ana. Choncho mungachite bwino kwambiri kukhala oleza mtima ndiponso aulemu pothandiza abale ndi alongo amene akukumana ndi zimenezi.​—Afil. 2:3, 4.

10. Kodi tingathandize bwanji anthu othawa kwawo kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba? (Onani chithunzi choyambirira.)

10 Nthawi zina zimene maboma amachita zimachititsa kuti abale azivutika kupeza a Mboni m’dziko limene athawira. Komanso abale akakana kugwira ntchito ina chifukwa chosafuna kujomba kumisonkhano, mabungwe ena amanena kuti saziwathandiza. Izi zachititsa kuti abale ena agonje chifukwa cha mantha. Choncho tiyenera kuyesetsa kukumana mwamsanga ndi abale ndi alongo amene athawira m’dziko lathu. Abalewa amafunikira kudziwa kuti timawakonda kwambiri. Tikamawathandiza ndiponso kuwachitira chifundo, akhoza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.​—Miy. 12:25; 17:17.

KODI TINGAWATHANDIZENSO M’NJIRA ZITI?

11. (a) Kodi anthu othawa kwawo amafunika zinthu ngati ziti? (b) Kodi iwo angasonyeze bwanji kuti ali ndi mtima woyamikira?

11 Poyamba, mwina tingafunikire kuthandiza abalewa kuti akhale ndi chakudya, zovala ndiponso zinthu zina zofunika pa moyo. * Ngakhale zinthu zing’onozing’ono ngati kupatsa munthu taye zingathandize kwambiri. Komanso abale amene athawa kwawo akamayamikira zimene ena akuwachitira ndiponso kupewa kupempha zinthu zambiri, abale amene akuwathandizawo amasangalala kwambiri. Koma si bwino kuti anthu othawa kwawo azingodalira kuthandizidwa ndi Akhristu anzawo. Zimenezi zingawachotsere ulemu komanso zingachititse kuti asiye kugwirizana ndi abale ena. (2 Ates. 3:7-10) Ngakhale zili choncho, timafunikabe kuwathandiza.

Kodi tingathandize bwanji abale ndi alongo athu amene athawa kwawo? (Onani ndime 11-13)

12, 13. (a) Kodi tingathandizenso anthu othawa kwawo m’njira ziti? (b) Perekani chitsanzo.

12 Sikuti pamafunika ndalama zambiri kuti tithandize anthu othawa kwawo. Chimene chimafunika ndi kupeza nthawi yowathandiza ndiponso kuwasonyeza chikondi. Nthawi zina tingafunike kuwathandiza kudziwa mmene angamayendere popita kumalo osiyanasiyana komanso mmene angagulire zakudya zabwino pamtengo wotsika. Mwinanso tingawathandize kupeza zipangizo zomwe angamagwiritse ntchito kuti azipeza kangachepe. Chofunika kwambiri n’kuwathandiza kuti asamachite chilendo mumpingo. Mwina tingawathandize pa nkhani ya kayendedwe popita kumisonkhano. Tingawatengenso polowa mu utumiki n’kumawafotokozera zimene anganene polalikira anthu m’gawolo.

13 Anyamata 4 atafika mumpingo wina, akulu anawaphunzitsa kuyendetsa galimoto, kutaipa komanso kulemba makalata ofunsira ntchito. Anawathandizanso kukonza ndandanda yowathandiza kuti azichita zambiri potumikira Yehova. (Agal. 6:10) Patangopita nthawi yochepa, anyamata onsewo anayamba upainiya. Malangizo a akuluwo komanso khama la anyamatawa zinawathandiza kuti azichita bwino mumpingo ndiponso kuti asatengeke ndi zinthu zoipa za m’dziko la Satanali.

14. (a) Kodi anthu othawa kwawo ayenera kusamala ndi chiyani? (b) Perekani chitsanzo.

14 Mofanana ndi Akhristu ena onse, anthu othawa kwawo ayenera kusamala kuti asamachite zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wawo ndi Yehova pongofuna kupeza ndalama. * Lije, yemwe tamutchula kale uja, limodzi ndi abale ake amakumbukirabe zimene bambo awo anawaphunzitsa ngakhale pa nthawi imene ankathawa. Iye ananena kuti bambo “anayamba kutaya katundu amene tinatenga chifukwa anali wosafunika kwenikweni. Pomaliza anatisonyeza chikwama chopanda kanthu n’kutiuza uku akumwetulira kuti: ‘Mwaona? Zonse zinali zosafunika kwenikweni.’”​—Werengani 1 Timoteyo 6:8.

TIZIWATHANDIZA KUTI APEZE ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI

15, 16. Kodi tingathandize bwanji anthu othawa kwawo kuti (a) alimbitse ubwenzi wawo ndi Yehova? (b) maganizo awo akhazikike?

15 Anthu othawa kwawo amafunika kuwathandiza kuti alimbitse ubwenzi wawo ndi Yehova komanso kuti maganizo awo akhazikike. (Mat. 4:4) Mwachitsanzo, akulu angawathandize powapezera mabuku achilankhulo chawo komanso abale ndi alongo amene amadziwa chilankhulocho. Anthu ambiri akathawa amasiyana ndi achibale awo, anzawo komanso mipingo yawo. Choncho amafunika kuwaganizira kuti azidziwa kuti Yehova ndiponso Akhristu anzawo amawakonda. Kupanda kutero, angayambe kugwirizana kwambiri ndi achibale kapena anthu ena akwawo omwe si Mboni. (1 Akor. 15:33) Tikamawathandiza kuti azimasuka mumpingo ndiye kuti tikugwira ntchito limodzi ndi Yehova ‘yoyang’anira alendo okhala m’dziko la eni.’​—Sal. 146:9.

16 Mofanana ndi banja la Yesu, anthu ena sangabwerere kwawo pa nthawi imene anthu owazunzawo akulamulirabe. Lije anatchulanso chifukwa china chimene anthu sabwerera kwawo. Iye anati: “Makolo ambiri anaona anthu a m’banja lawo akugwiriridwa kapena kuphedwa, choncho sangafune kubwerera ndi ana awo kudziko limene kunachitika zimenezo.” Kuti tilimbikitse anthu amene anakumana ndi zimenezi, tiyenera kukhala “omverana chisoni, okonda abale, achifundo chachikulu, ndiponso amaganizo odzichepetsa.” (1 Pet. 3:8) Mavuto amene anthu othawa kwawo amakumana nawo akhoza kuwachititsa kuti asamamasuke ndipo mwina angamachite manyazi kufotokoza zimene zinawachitikira, makamaka ngati ana awo alipo. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikanakumana ndi vuto lawoli ndikanafuna kuti anthu andichitire chiyani?’​—Mat. 7:12.

MMENE TINGATHANDIZIRE ANTHU OMWE SI MBONI

17. Kodi chimachitika n’chiyani tikamalalikira anthu amene athawa kwawo?

17 Anthu ambiri amene amathawa kwawo amachokera m’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Koma chosangalatsa n’chakuti abale ndi alongo a m’mayiko amene amathawirawo amachita khama powathandiza kuti ayambe kumva “mawu a Ufumu.” (Mat. 13:19, 23) Anthu ambiri “olemedwa” amatsitsimulidwa pamisonkhano ndipo sachedwa kuvomereza kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.”​—Mat. 11:28-30; 1 Akor. 14:25.

18, 19. Kodi tingachite bwanji zinthu mwanzeru polalikira kwa anthu othawa kwawo?

18 Koma tikamalalikira kwa anthu othawa kwawo tiyenera kukhala “ochenjera” komanso osamala. (Mat. 10:16; Miy. 22:3) Tiyenera kuwamvetsera moleza mtima koma si bwino kukambirana nawo za ndale. Ndi bwino kutsatira malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi komanso kwa akuluakulu a boma ndipo tizipewa kuika moyo wathu kapena wa anthu ena pa ngozi. Tiziyesetsa kulemekeza zimene anthuwo amakhulupirira komanso chikhalidwe chawo. Mwachitsanzo, anthu ochokera m’mayiko ena amakhala ndi maganizo amphamvu pa nkhani ya zovala za akazi. Choncho polalikira kwa anthu oterowo ndi bwino kuvala zovala zimene sizingawakhumudwitse.

19 Mofanana ndi Msamariya wachifundo wa mufanizo la Yesu, tiyenera kuthandiza anthu ovutika ngakhale omwe si Mboni. (Luka 10:33-37) Njira yabwino yowathandizira ndi yowauza uthenga wabwino. Mkulu wina amene anathandiza anthu ambiri othawa kwawo anati: “Tiyenera kuyamba n’kuwadziwitsa kuti ndife a Mboni za Yehova ndipo cholinga chathu chachikulu n’kuwathandiza kuti aphunzire za Yehova osati kuwapezera zinthu. Kupanda kutero angayambe kucheza nafe n’cholinga choti angopeza kenakake.”

UBWINO WOTHANDIZA ANTHUWA

20, 21. (a) Kodi tikamasonyeza chikondi kwa anthu othawa kwawo, zotsatira zake zimakhala zotani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

20 Tikamasonyeza chikondi kwa alendo, zotsatira zake zimakhala zabwino kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku Eritrea dzina lake Alganesh. Mwamuna wake anamwalira ndipo iye ataona kuti anthu akuzunzidwa kwambiri anathawa m’dzikoli ndi ana ake 6. Anayenda ulendo wodutsa m’chipululu kwa masiku 8 kenako anakafika ku Sudan. Iye anati: “Abale a m’dzikoli anatilandira ngati kuti ndife achibale awo enieni. Anatipatsa chakudya, zovala, malo ogona komanso ankatithandiza pa nkhani ya mayendedwe. A Mboni za Yehova okha ndi amene amalandira anthu achilendo kunyumba zawo chifukwa choti amalambira Mulungu mmodzi.”​—Werengani Yohane 13:35.

21 Nanga tingathandize bwanji ana amene amachoka limodzi ndi makolo awo n’kufika m’dziko lathu? Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene tingachite kuti azitumikira Yehova mosangalala.

^ ndime 2 Munkhaniyi, mawu oti “anthu othawa kwawo” akunena za anthu amene athawa m’dziko lawo kapena m’dera lawo chifukwa cha nkhondo, kuzunzidwa kapena ngozi inayake. Nthambi ya bungwe la United Nations yoona za anthu othawa kwawo (UNHCR) inanena kuti masiku ano “munthu mmodzi pa anthu 113 alionse amathawa kwawo.”

^ ndime 6 Onani nkhani yakuti “Musaiwale Kuchereza Alendo” mu Nsanja ya Olonda ya October 2016, tsamba 8-12.

^ ndime 11 Anthu othawa kwawo akafika, akulu ayenera kutsatira mwamsanga malangizo opezeka pamutu 8, ndime 30 m’buku lakuti Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova. Akulu angapemphe ofesi ya nthambi ya m’dziko lawo kuti iwathandize kuti azilumikizana ndi mipingo ya m’dziko lina. Akhoza kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org. Angachite bwinonso kufufuza mwanzeru kuti adziwe mpingo umene anthuwo akuchokera komanso moyo wawo wauzimu.

^ ndime 14 Onani nkhani yakuti “Simungatumikire Ambuye Awiri” komanso yakuti “Limbani Mtima, Yehova Akuthandizani” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2014, tsamba 17-26.