Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuthandiza Alendo Ocokela ku Mayiko Ena “Kutumikila Yehova Mokondwela”

Kuthandiza Alendo Ocokela ku Mayiko Ena “Kutumikila Yehova Mokondwela”

“Yehova amayang’anila alendo okhala m’dziko la eni.”—SAL. 146:9.

NYIMBO: 84, 73

1, 2. (a) Ni mavuto ati amene abale na alongo athu ena akumana nawo? (b) Nanga pakubuka mafunso ati?

M’BALE Lije anati: “Pamene nkhondo yapaciweni-weni inayamba m’dziko la Burundi, banja lathu linali pa msonkhano wadela. Tinaona anthu akuthaŵa, ndipo ena anali kuombela mfuti anzawo. Makolo anga na ise ana 11 tinathaŵa kuti tipulumutse miyoyo yathu, ndipo tinangothaŵa na zovala za m’thupi. Patapita nthawi yaitali, ena a m’banja lathu anafika ku kampu ya anthu othaŵa kwawo m’dziko la Malawi, imene inali pamtunda wa makilomita 1,600. Ife ena tinathaŵila kumadela osiyana-siyana.”

2 Padziko lonse, ciŵelengelo ca anthu othaŵa kwawo cifukwa ca nkhondo kapena cizunzo, tsopano cipitilila 65,000,000. Ciŵelengelo cimeneci cimaposa ziŵelengelo zonse za m’mbuyomu. * Pakati pa anthu amenewa, pali Mboni za Yehova masauzande oculuka. Ambili mwa iwo, okondedwa awo anafa ndipo katundu wawo unawonongeka. Kodi ni mavuto ena ati amene abale na alongo othaŵa kwawo amakumana nawo? Kodi tingawathandize bwanji ‘kutumikila Yehova mokondwela’ ngakhale kuti akumana ndi mavuto? (Sal. 100:2) Nanga tingalalikile bwanji uthenga wabwino mogwila mtima kwa anthu othaŵa kwawo amene sadziŵa Yehova?

UMOYO WA ANTHU OTHAŴA KWAWO

3. N’cifukwa ciani Yesu ndi ophunzila ake ambili anathaŵa kwawo?

3 Pamene mngelo wa Yehova anacenjeza Yosefe kuti Mfumu Herode ifuna kupha Yesu, Yesu na makolo ake anathaŵa n’kukhala ku Iguputo. Iwo anakhala m’dzikolo mpaka pamene Herode anamwalila. (Mat. 2:13, 14, 19-21) Patapita zaka zambili, ophunzila a Yesu oyambilila “anabalalikila m’zigawo za Yudeya ndi Samariya” cifukwa ca cizunzo. (Mac. 8:1) Yesu anadziŵa kuti otsatila ake ambili adzakakamizika kusiya nyumba zawo. Iye anati: “Akakuzunzani mumzinda wina, muthaŵile mumzinda wina.” (Mat. 10:23) Munthu akathaŵa kwawo, amakumana ndi mavuto mosasamala kanthu za cifukwa cimene wathaŵila.

4, 5. Ni mavuto ati amene anthu othaŵa kwawo amakumana nawo (a)  pothaŵa? (b) pamene akhala m’kampu?

4 Anthu othaŵa kwawo angakumane ndi mavuto pamene athaŵa kapena pamene akhala m’kampu ya anthu othawa kwawo. Gad, mng’ono wake wa Lije anati: “Tinayenda kwa mawiki angapo ndipo tinali kuona mitembo yambili-mbili. Panthawiyo n’nali na zaka 12. Mendo yanga yanatupa ngako cakuti n’nauza abale anga kuti anisiye cabe. Koma atate ananinyamula. Sanafune kuti asilikali oukilawo anipeze n’kunipha. Tsiku lililonse tinali kupemphela ndi kudalila Yehova. Nthawi zina, tinali kudya cabe mango za m’mitengo imene tinali kupeza m’njila.”—Afil. 4:12, 13.

5 Abale ake ambili a Lije anakhala zaka zambili m’makampu a United Nations a anthu othaŵa kwawo. Koma kumeneko, anali osatetezeka. Lije, amene lomba ni woyang’anila dela, anati: “Anthu ambili kumeneko anali malova. Anali kungokhalila kujeda anzawo, kuledzela, kuchova njuga, kuba, ndipo anali kucita ciwelewele.” Kuti abale na alongo apewe makhalidwe oipa amenewa, anali kugwilizana kwambili ndi mpingo. (Aheb. 6:11, 12; 10:24, 25) Komanso, kuti akhale olimba mwauzimu, anali kugwilitsila nchito nthawi yawo mwanzelu. Ambili anali kucita upainiya. Cimene cinali kuwalimbikitsa ndi kukumbukila za umoyo wa Aisiraeli pa ulendo wawo m’cipululu. Anadziŵa kuti, mofanana ndi Aisiraeli, iwonso tsiku lina adzaleka kukhala m’kampu.—2 Akor. 4:18.

KUONETSA CIKONDI KWA ANTHU OTHAŴA KWAWO

6, 7. (a) Kodi ‘kukonda Mulungu’ kumalimbikitsa bwanji Akhristu kuthandiza abale awo ovutika? (b) Fotokozani citsanzo.

6 ‘Kukonda Mulungu’ kumatilimbikitsa kukonda anzathu, maka-maka panthawi ya mavuto. (Ŵelengani 1 Yohane 3:17, 18.) Pamene Akhristu a m’zaka 100 zoyambilila ku Yudeya anakhudzidwa na njala, Akhristu anzawo anawathandiza. (Mac. 11:28, 29) Mtumwi Paulo ndi Petulo analimbikitsa Akhristu kuti azicelezana. (Aroma 12:13; 1 Pet. 4:9) Popeza Akhristu amaceleza abale na alongo amene abwela kudzaceza, ndiye kuti afunikanso kuceleza Akhritsu anzawo amene miyoyo yawo ili paciopsezo, kapena amene akuzunzidwa cifukwa ca cikhulupililo cawo.—Ŵelengani Miyambo 3:27. *

7 Caposacedwa, abale na alongo masauzande ambili, kuphatikizapo ana, anathaŵa nkhondo ndi cizunzo m’cigawo ca kum’mawa kwa dziko la Ukraine. N’zomvetsa cisoni kuti ena anaphedwa. Koma ena ambili anatengedwa n’kuyamba kusamalidwa ndi abale awo auzimu a m’dzikolo, ndiponso a ku Russia. M’maiko aŵili onsewa, iwo satengako mbali m’ndale cifukwa ‘sali mbali ya dzikoli,’ ndipo akupitiliza kulalikila mwacangu ‘uthenga wabwino wa mau opatulika.’—Yoh. 15:19; Mac. 8:4.

KUTHANDIZA ANTHU OTHAŴA KWAWO KULIMBITSA CIKHULUPILILO

8, 9. (a) Ni mavuto ati amene othaŵa kwawo amakumana nawo m’dziko lina? (b) N’cifukwa ciani tifunika kuwathandiza moleza mtima?

8 Anthu ena akathaŵa kwawo, amakakhala m’dela lina m’dziko lawo lomwelo. Koma ambili amathaŵila kudziko lina, kumene umoyo umakhala wosiyana ngako na umene anajaila. Maboma angapeleke cakudya, zovala, ndi malo okhala, koma cakudya cimene angawapatse cingakhale cosiyana kwambili na cimene anajaila. Anthu a ku maiko otentha akathaŵila ku maiko ozizila, angavutike na nyengo yozizila, ndipo sangadziŵe zovala zamphepo zoyenela kuvala. Ngati anacokela kumadela a kumidzi, sangadziŵe moseŵenzetsela zipangizo zamakono zam’nyumba.

9 Maboma ena amakonza pulogilamu yothandiza anthu othaŵa kwawo kuti ajaile umoyo watsopano. Komabe, pakangopita miyezi ingapo, iwo angafunike kumadzisamalila okha. Cingakhale covuta kwa iwo kujaila umoyo watsopano. Ganizilani cabe: Iwo angafunike kuphuzila citundu cina, malamulo ndi cikhalidwe catsopano. Angafunikenso kujaila zinthu monga kupeleka misonkho, kulipila mabilu, kupita kusukulu yatsopano, kucita zinthu panthawi yake, ndi kulangiza ana. Tiyenela kuwathandiza mwaulemu ndi moleza mtima abale na alongo amene akukumana ndi mavuto ngati amenewa.—Afil. 2:3, 4.

10. Kodi tingalimbitse bwanji cikhulupililo ca abale othaŵa kwawo akangofika m’dela lathu? (Onani pikica kuciyambi.)

10 Kuwonjezela apo, nthawi zina olamulila amacititsa kuti abale na alongo avutike kugwilizana na mpingo. Mwacitsanzo, mabungwe ena amaopseza abale kuti adzawacotsa m’dzikolo kapena adzaleka kuwathandiza ngati akana kugwila nchito imene imacititsa kuti aziphonya misonkhano. Cifukwa ca mantha, abale ena aleka kugwilizana na mpingo. Conco, tifunika kuonana ndi abale othaŵa kwawo mwamsanga akangofika m’dela lathu. Iwo afunika kuona kuti timawakonda. Ngati tiwaonetsa cikondi ndi kuwathandiza, cikhulupililo cawo cidzalimba.—Miy. 12:25; 17:17.

KUPELEKA THANDIZO LAKUTHUPI KWA OTHAŴA KWAWO

11. (a) Kodi anthu othaŵa kwawo amafunika zinthu ziti? (b) Nanga angaonetse bwanji kuyamikila?

11 Coyamba, tingathandize abale athu mwa kuwapatsako cakudya, zovala, ndi zinthu zina zofunika. * Ngakhale kuwapatsa kamphatso kakang’ono monga tayi, kungakhale kothandiza ngako. Ndipo abale othaŵa kwawo angaonetse mtima woyamikila ngati apewa kupempha-pempha. Izi zingacititse abale a m’dziko limene athaŵilako kuti aziwathandiza mokondwela. N’zoona kuti umoyo wodalila thandizo la ena ungacotsele ulemu abale othaŵa kwawo, ndi kusokoneza ubale wawo ndi Akhristu ena. (2 Ates. 3:7-10) Komabe, tifunika kuwathandiza ndithu.

Kodi tingawathandize bwanji abale na alongo athu othaŵa kwawo? (Onani mapalagilafu 11-13))

12, 13. (a) Kodi tingawathandize bwanji abale othaŵa kwawo? (b) Fotokozani citsanzo.

12 Cofunika kwambili popeleka thandizo kwa anthu othaŵa kwawo si ndalama, koma kupeza nthawi yoceza nawo ndi kucita zinthu zoonetsa kuti timawaganizila. Tingawathandize pa zinthu zing’ono-zing’ono monga kuwadziŵitsa za mayendedwe, kumene angagule zakudya zopatsa thanzi koma zochipa, ndiponso mmene angapezele zipangizo zogwilila nchito monga mashini osokela kapena okhwapila udzu, kuti azipezako ndalama. Koma cacikulu n’cakuti tifunika kuwathandiza kuti azigwilizana ngako na mpingo wawo watsopano. Ngati zingatheke, mukhoza kumawanyamulako pa motoka yanu popita kumisonkhano. Komanso, mungawathandize kudziŵa mmene angafikile anthu polalikila uthenga wa Ufumu m’gawo lanu. Popita mu ulaliki, muziwatengako abale ndi alongo amenewa.

13 Acicepele anayi othaŵa kwawo atafika mumpingo wina, akulu osiyana-siyana anawaphunzitsa kuyendetsa motoka, kutaipa, kulemba makalata ofunsila nchito, ndi kugaŵa bwino nthawi kuti azitumikila Yehova mokwanila. (Agal. 6:10) Patangopita nthawi yocepa, onse anayi anayamba upainiya. Thandizo limene anawapatsa, kuphatikizapo khama lawo lofuna kukwanilitsa zolinga zauzimu, zinawathandiza kupita patsogolo. Zinawathandizanso kuti asasoceletsedwe na dziko loipa la Satanali.

14. (a) Ni ciyeso citi cimene othaŵa kwawo afunika kupewa? (b) Fotokozani citsanzo.

14 Mofanana ndi Akhristu ena onse, othaŵa kwawo amafunika kupewa mzimu wokonda zinthu zakuthupi kuti asawononge ubale wawo na Yehova. * Lije, amene tamuchula kuciyambi, ndi abale ake, amakumbukila mfundo zolimbitsa cikhulupililo zimene atate awo anawaphunzitsa pamene anali kuthaŵa. Iye anati: “Atate anayamba kutaya katundu wosafunika umene tinanyamula m’cola. Ndiyeno, ananyamula cola copanda katundu cija n’kukamba kuti: ‘Mwaona ka? Zonse zimene zinali m’colamu sizofunika kweni-kweni pa moyo!’”—Ŵelengani 1 Timoteyo 6:8.

KUPELEKA THANDIZO LOFUNIKA KWAMBILI KWA OTHAŴA KWAWO

15, 16. Kodi anthu othaŵa kwawo (a) tingawathandize bwanji mwauzimu? (b) tingawalimbikitse bwanji?

15 Timafunika kupeleka thandizo lakuthupi kwa anthu othaŵa kwawo, koma cofunika kwambili n’kuwathandiza mwauzimu ndi kuwalimbikitsa. (Mat. 4:4) Akulu angawathandize mwa kuwapezela mabuku a m’citundu cawo ndi kupeza abale amene amakamba citundu cawo. Anthu ambili othaŵa kwawo amasiya acibale, mabwenzi, ndi mipingo yawo. Conco, akafika m’dela lathu afunika kuona kuti Yehova na ise Akhristu anzawo timawakonda. Apo ayi, angayambe kugwilizana kwambili ndi acibale awo osakhulupilila, kapena anthu ocokela m’dziko lawo amene ali na cikhalidwe colingana na cawo. (1 Akor. 15:33) Tikawalandila bwino mumpingo, ndiye kuti tikugwila nchito na Yehova yoyang’anila kapena kuti kuteteza alendo ocokela m’dziko lina.—Sal. 146:9.

16 Monga mmene zinalili kwa Yesu ndi makolo ake, anthu othaŵa kwawo sangafune kubwelela kudziko lawo ngati amene anali kuwazunza akali kulamulila. Komanso, mogwilizana ndi zimene Lije anakamba, “makolo ambili amene anaona acibale awo akugwililidwa ndi kuphedwa, sangalole kuti iwo ndi ana awo abwelele kumalo kumene zoipazi zinacitikila.” Abale amene alandila anthu othaŵa kwawo afunika kukhala “acifundo cacikulu, ndiponso amaganizo odzicepetsa,” kuti akwanitse kuthandiza anthu amene anacitilidwa zinthu zankhanza zimenezi. (1 Pet. 3:8) Cifukwa ca zimene zinawacitikila, anthu ena othaŵa kwawo amakhala omangika, ndipo angacite manyazi kuuzako ena mavuto awo, maka-maka pakakhala ana awo. Conco, dzifunseni kuti, ‘Kodi izi zikanakhala kuti zacitikila ine, sembe nifuna kuti ena azicita nane zinthu motani?’—Mat. 7:12.

KULALIKILA ANTHU OTHAŴA KWAWO

17. Kodi anthu othaŵa kwawo amapindula bwanji tikawalalikila?

17 Masiku ano, anthu ambili othaŵa kwawo amacokela m’mayiko amene nchito yolalikila si yovomelezeka mwalamulo. Cifukwa ca khama la Mboni zokhala m’madela amene kumafikila othaŵa kwawo, anthu ambili othaŵa kwawo amvela “mau a ufumu” kwa nthawi yoyamba. (Mat. 13: 19, 23) Ambili amene ndi “olemedwa” amatsitsimulidwa mwauzimu pa misonkhano yathu, ndipo mwamsanga amazindikila kuti ‘zoonadi Mulungu ali pakati pathu.’—Mat. 11:28-30; 1 Akor. 14:25.

18, 19. Tingaonetse bwanji kuti ndise anzelu tikamalalikila kwa anthu othaŵa kwawo?

18 Ngati mulalikila anthu othaŵa kwawo, mufunika kukhala “ocenjela.” (Mat. 10: 16; Miy. 22: 3) Muziwamvetsela moleza mtima akamafotokoza mavuto awo, koma muzipewa kukambilana nawo nkhani zandale. Muzitsatila malangizo ocokela ku ofesi ya nthambi ndi kwa akulu-akulu a boma, kuti musaike moyo wanu kapena wa ena paciopsezo. Dziŵani cipembedzo ndi cikhalidwe cawo, ndipo muzipewa kucita zinthu zimene zingawakhumudwitse. Mwacitsanzo, anthu ocokela kumayiko ena amakhumudwa na mavalidwe ena a azimayi kulingana ndi cikhalidwe cakwawo. Conco, mukamalalikila kwa anthu othaŵa kwawo, muzivala zovala zoyenela kuti musawakhumudwitse.

19 Molingana ndi Msamaliya wacifundo wa m’fanizo la Yesu, timafuna kuthandiza anthu ovutika, kuphatikizapo amene si Mboni. (Luka 10: 33-37) Njila yabwino kwambili imene tingawathandizile ndi kuwauzako uthenga wabwino. Mkulu wina amene wathandiza anthu ambili othaŵa kwawo anati: “Tikangofikila anthu othaŵa kwawo, tifunika kuwauzilatu kuti ndise Mboni za Yehova ndi kuti colinga cathu cacikulu ndi kuwathandiza mwauzimu osati mwakuthupi. Ngati sitingawauze, ena angayambe kugwilizana nafe cifukwa cofuna cabe thandizo lakuthupi.”

ZOTULUKAPO ZABWINO

20, 21. (a) N’zotulukapo zabwino ziti zimene zimakhalapo ngati tionetsa cikondi cacikhristu kwa anthu othaŵa kwawo? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

20 Kuonetsa cikondi cacikhristu kwa alendo ocokela m’dziko lina, kumakhala na zotulukapo zabwino. Mwacitsanzo, pamene mwamuna wa mlongo Alganesh anamwalila, iye ndi ana ake 6 aang’ono, anathaŵa m’dziko la Eritrea cifukwa ca cizunzo. Atayenda ulendo wolemetsa wa masiku 8 kudutsa m’cipululu, anafika m’dziko la Sudan. Mlongoyu anati: “Abale kumeneko anatilandila monga acibale awo. Anatipatsa zakudya, zovala, pogona ndi ndalama zoyendela. Ndaninso ena amene angalandile alendo m’nyumba zawo, cabe cifukwa cakuti amalambila Mulungu m’modzi? Ni Mboni za Yehova zokha!”—Ŵelengani Yohane 13:35.

21 Nanga bwanji za ana ambili amene anathaŵa kwawo kapena kusamukila ku mayiko ena pamodzi na makolo awo? M’nkhani yotsatila tidzakambilana mmene ife tonse tingawathandizile kutumikila Yehova mokondwela.

^ par. 2 M’nkhani ino, mau akuti “anthu othaŵa kwawo” amene taseŵenzetsa akutanthauza anthu amene akakamizika kuthaŵa n’kukakhala m’dziko lina kapena m’dela lina m’dziko lawo lomwelo cifukwa ca nkhondo, kuzunzidwa, kapena masoka. Bungwe la UNHCR (United Nations High Commissioner for Refugees) linati masiku ano, “munthu mmodzi pa anthu 113” padziko lonse “ni wothaŵa kwawo.”

^ par. 6 Onani nkhani yakuti “Musaiŵale Kuceleza Alendo” mu Nsanja ya Mlonda ya October 2016, mapeji 8-12.

^ par. 11 Abale othaŵa kwawo akangofika, akulu ayenela kutsatila malangizo a m’buku la Gulu Lochita Chifunilo ca Yehova mutu 8, palagilafu 30. Akulu angakambilane ndi mipingo ya m’dziko limene kunacokela abalewo mwa kulemba kalata ndi kuitumiza ku ofesi ya nthambi ya m’dziko lawo kupitila pa jw.org. Poyembekezela, iwo mosamala angafunse abale othaŵa kwawo za mipingo imene anali kusonkhanako, ndi zokhudza utumiki kuti adziŵe umoyo wawo wauzimu.

^ par. 14 Onani nkhani yakuti “Palibe Munthu Angatumikile Ambuye Aŵili” ndi yakuti “Limbani Mtima Yehova ndi Mthandizi Wanu” mu Nsanja ya Mlonda ya April 1, 2014, mapeji 17-26.