Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuthandiza Ana a Alendo Ocokela m’Dziko Lina

Kuthandiza Ana a Alendo Ocokela m’Dziko Lina

“Palibe cimene cimandisangalatsa kwambili kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’coonadi.”—3 YOH. 4.

NYIMBO: 88, 41

1, 2. (a) Ni vuto liti limene makolo ambili osamukila m’dziko lina amakumana nalo? (b) Tidzakambilana mafunso ati m’nkhani ino?

“INE ndi makolo anga tinasamukila m’dziko lina, ndipo pamene n’nali mwana n’nali kukamba citundu cawo kunyumba na kumisonkhano,” anatelo Joshua. Iye anapitiliza kuti: “Koma n’tayamba kupita kusukulu, n’nayamba kukonda citundu ca m’dziko limene tinasamukila. Patapita zaka zocepa cabe, zinthu zinasinthilatu. Sin’nali kumvetsetsa zimene zinali kukambidwa pa misonkhano, ndipo sin’nali kudziŵa bwino cikhalidwe ca makolo anga.” Vuto limene Joshua anakumana nalo n’lofala masiku ano.

2 Masiku ano, anthu oposa 240,000,000 amakhala m’dziko lina osati limene anabadwila. Ngati ndinu kholo ndipo munasamukila m’dziko lina, kodi mungawaphunzitse bwanji ana anu kukonda zinthu zauzimu ndi kupitiliza “kuyenda m’coonadi”? (3 Yoh. 4) Nanga ena angakuthandizeni bwanji kucita zimenezi?

MAKOLO, KHALANI CITSANZO CABWINO

3, 4. (a) Kodi makolo angapeleke bwanji citsanzo cabwino kwa ana awo? (b) Kodi makolo sayenela kuyembekezela ciani kwa ana awo?

3 Makolo, citsanzo canu n’cofunika kwambili kuti muthandize ana anu kuyamba kuyenda m’njila ya ku moyo wosatha. Ana anu akaona kuti ‘mukufuna-funa ufumu coyamba,’ amaphunzila kudalila Yehova kuti adzawapatsa zofunika pa umoyo. (Mat. 6:33, 34) Conco, muzikhala na umoyo wosalila zambili. Muziika zinthu zauzimu patsogolo osati zakuthupi. Muziyesetsa kupewa nkhongole. Muzifuna-funa ‘cuma cakumwamba,’ kapena kuti ciyanjo ca Yehova, osati “ulemelelo wa anthu.”—Ŵelengani Maliko 10:21, 22; Yoh. 12:43.

4 Musamakhale bize kwambili mpaka kusoŵa nthawi yoceza ndi ana anu. Auzeni kuti mumawanyadila ngati asankha kuika cifunilo ca Yehova patsogolo osati cuma kapena kuchuka. Pewani maganizo amene anthu ambili a m’dzikoli ali nawo, akuti ana afunika kupezela makolo awo zinthu zambili kuti akhale na umoyo wawofu-wofu. Kumbukilani kuti “ana sayenela kusunga cuma kuti cidzathandize makolo awo mtsogolo, koma makolo ndiye ayenela kusungila ana awo.”—2 Akor. 12:14.

MAKOLO, CEPETSANI VUTO LA KUSIYANA KWA ZITUNDU

5. N’cifukwa ciani makolo afunika kumakamba ndi ana awo za Yehova?

5 Monga mmene Baibo inakambila, anthu “ocokela m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu” akubwela m’gulu la Yehova. (Zek. 8:23) Koma kusiyana kwa zitundu kungapangitse kuti cikhale covuta kwa makolo kuphunzitsa ana awo coonadi. Ana anu ndiwo maphunzilo anu a Baibo ofunika kwambili, ndipo afunika ‘kuphunzila ndi kudziwa’ za Yehova kuti akapeze moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Kuti ana anu aphunzile mfundo za Yehova, mufunika ‘kumalankhula nawo’ za mau ake pa mpata uliwonse woyenelela.—Ŵelengani Deuteronomo 6:6, 7.

6. Kodi ana anu angapindule bwanji ngati aphunzila citundu canu? (Onani pikica kuciyambi.)

6 Ana anu amaphunzila citundu ca m’dziko limene munasamukilako akakhala ku sukulu komanso akakhala ndi anthu ena. Koma amaphunzila citundu canu maka-maka ngati mukamba nawo kaŵili-kaŵili m’citundu canuco. Iwo akaphunzila citundu canu, zimathandiza kuti muzikamba nawo momasuka. Koma palinso mapindu ena. Akadziŵa zitundu zonse ziŵili, canu na ca m’dzikolo, zimawathandiza kukulitsa luso la kuganiza, ndiponso amaphunzila kukhala bwino na anthu ena. Zimawapatsanso mwayi wowonjezela utumiki wawo. Carolina, amene anasamukila m’dziko lina pamodzi na makolo ake, anati: “Nimakondwela ngako kutumikila mumpingo wa citundu ca m’dziko limene tinacokela. Ndipo n’zosangalatsa kuthandiza mpingo umene muli olengeza ufumu ocepa.”

7. Mungacite ciani ngati m’banja lanu muli vuto la kusiyana zitundu?

7 Komabe, ana ena amene anasamukila m’dziko lina akaphunzila cikhalidwe na citundu ca m’dzikolo, amalephela kukamba citundu ca makolo awo kapena safuna kucikamba. Inu makolo, ngati ana anu ali na vuto laconco, mungacite bwino kuphunzilako citundu cimene iwo amamvetsetsa. Mukacita zimenezi, mudzakwanitsa kuphunzitsa ana anu coonadi mosavuta. Tikutelo cifukwa mudzatha kudziŵa zimene anawo amakamba, zosangulutsa zimene amakonda, ndi zimene amaphunzila kusukulu. Mudzathanso kukambilana mosavuta ndi matica awo. N’zoona kuti kuphunzila citundu cina kumatenga nthawi, ndiponso kumafuna khama ndi kudzicepetsa. Koma yelekezelani kuti mwana wanu amene anali kumva na kukamba bwino-bwino, wakhala wogontha. Kodi mungacite ciani? Kodi simungaphunzile cinenelo camanja kuti muzikwanitsa kukamba naye? Mofananamo, mufunika kucita khama kuphunzila citundu cimene mwana wanu amamvetsetsa. *

8. Kodi mungawathandize bwanji ana anu ngati simudziŵa bwino citundu cawo?

8 Makolo ena amene anasamukila m’dziko lina angaphunzile citundu catsopano ca ana awo, koma osafika pocikamba bwino-bwino. Zimenezi zingapangitse kuti cikhale covuta kwa makolowo kuphunzitsa ana awo mfundo zozama za ‘m’malemba oyela.’ (2 Tim. 3:15) Ngati m’banja lanu muli vuto laconco, n’zotheka ndithu kuthandiza ana anu kudziŵa Yehova ndi kum’konda. Shan, amene ndi mkulu mumpingo, anati: “Amayi sanali kumvetsetsa citundu cimene ife tinali kudziŵa, ndipo ine na azilongosi anga tinali kulephela kukamba bwino citundu cawo. Koma tinali kuwaona akucita phunzilo laumwini, kupemphela, ndi kucititsa kulambila kwa pabanja wiki iliyonse. Zimenezi zinatithandiza kuona kuti kudziŵa Yehova n’kofunika ngako.”

9. N’cifukwa ciani ana ena amafunika kuphunzila za Yehova m’zitundu ziŵili?

9 Ana ena angafunike kuphunzila za Yehova m’zitundu ziŵili—ca kusukulu kwawo ndi cimene amakamba panyumba. Pa cifukwa cimeneci, makolo ena amaseŵenzetsa mabuku, zomvetsela, na mavidiyo a zitundu zonse ziŵili. Inde, makolo amene akhala m’dziko lina, afunika kupeza nthawi yokwanila yothandiza anawo kukhala pa ubale wolimba na Yehova. Afunikanso kupeza njila zosiyana-siyana zowathandizila.

KODI MUYENELA KUSONKHANA MUMPINGO WA CITUNDU CANJI?

10. (a) N’ndani afunika kusankha mpingo umene banja lizisonkhanako? (b) Nanga angacite ciani kuti asankhe mwanzelu?

10 Ngati alendo ocokela m’dziko lina ali kutali na kumene kuli Mboni zokamba citundu cawo, afunika kusonkhana na mpingo wa cinenelo ca m’delalo. (Sal. 146:9) Koma ngati pafupi pali mpingo wa cinenelo canu, mufunika kusankha kaya kukhala mumpingo wa cinenelo canu olo wa cinenelo ca m’delalo. Mutu wa banja afunika kuiganizila mosamala nkhaniyi, kuipemphelela, ndi kufunsako mkazi ndi ana ake. Akacita zimenezi, ayenela kupanga cosankha. (1 Akor. 11:3) Koma kodi n’zinthu ziti zimene mutu wa banja ayenela kuganizila asanapange cosankhaci? Nanga ni mfundo za m’Malemba ziti zimene afunika kuganizila? Tiyeni tikambilane zina mwa zimenezi.

11, 12. (a) Kodi citundu cingakhudze bwanji mmene mwana amapindulila na misonkhano? (b) N’cifukwa ciani ana ena safuna kuphunzila citundu ca makolo awo?

11 Makolo afunika kudziŵa bwino zimene ana awo amafunikila. Kuti ana amvetsetse coonadi, pali zambili zimene zimafunikila. Kupezeka pa misonkhano wiki iliyonse pakokha si kokwanila, olo misonkhanoyo itakhala kuti imacitika m’citundu codziŵika. Komabe, zingakhale bwino kuti ana azipezeka pa misonkhano ya citundu cimene amamvetsetsa cifukwa amaphunzila zambili, mwinanso kuposa mmene makolo angaganizile. Koma ngati citundu sacimvetsetsa, sangapindule mokwanila. (Ŵelengani 1 Akorinto 14:9, 11.) Komanso, nthawi zina zinthu zokambidwa m’cinenelo ca makolo sizingamufike pamtima mwana. Mwacitsanzo, ana ena amaphunzila kupeleka ndemanga, kucita zitsanzo, ndi kukamba nkhani m’citundu ca makolo awo, koma zimene amakamba sizikhala zocokela pansi pamtima.

12 Kuwonjezela apo, pali zinthu zina zimene zimakhudza mtima wa mwana kupatulapo citundu. N’zimene zinacitikila Joshua, amene tamuchula kuciyambi kwa nkhani ino. Mlongosi wake, Esther, anati: “Ngati ana amakamba citundu ca makolo, amayambanso kukonda cikhalidwe ndi cipembedzo ca makolowo.” Conco, ngati ana sadziŵa cikhalidwe ca makolo, sangafunenso kuphunzila cinenelo cawo ndi zikhulupililo zawo. Kodi makolo afunika kucita ciani zikakhala conco?

13, 14. (a) N’cifukwa ciani banja lina limene linasamukila m’dziko lina linasankha kusamukila mumpingo wa cinenelo ca m’dzikolo? (b) N’ciani cimene makolo anali kucita kuti akhalebe olimba mwauzimu?

13 Makolo acikhristu amaona moyo wauzimu wa ana awo kukhala wofunika ngako kuposa zofuna zawo. (1 Akor. 10:24) A Samuel, amene ndi atate ake Joshua ndi Esther, anati: “Ine na mkazi wanga tinali kuona mmene ana athu anali kucitila mwauzimu kuti tidziŵe citundu cimene cingawathandize kupita patsogolo. Tinalinso kupempha nzelu kwa Mulungu. Zimene tinapeza sizinali zotikomela. Koma titaona kuti anawo sapindula mokwanila na misonkhano ya m’citundu cathu, tinaganiza zosamukila mumpingo wa citundu ca m’dzikolo. Nthawi zonse, tinali kusonkhana ndi kuyenda muulaliki pamodzi. Tinalinso kuitana abale na alongo a kumaloko, kuti tidzadye nawo cakudya kapena kupita nawo kokaona malo. Zimenezi zinathandiza ana athu kudziŵana ndi abale. Zinawathandizanso kudziŵa Yehova Mulungu ndi kuyamba kumuona monga Tate ndi Bwenzi lawo. Tinaona kuti zimenezi ndizo zinali zofunika ngako kwa anawo kupambana kuti aphunzile citundu cathu.”

14 M’bale Samuel anakambanso kuti: “Pofuna kuti tikhalebe olimba mwauzimu, ine na mkazi wanga tinali kusonkhananso na mpingo wa citundu cathu. Umoyo unali wa bize kwambili, ndipo tinali kukhala otopa. Koma Yehova anatidalitsa cifukwa ca khama lathu ndi kudzipeleka kwathu, ndipo timamuyamikila kwambili. Tsopano, ana athu onse atatu akutumikila Yehova mu utumiki wanthawi zonse.”

ZIMENE ACICEPELE ANGACITE

15. N’cifukwa ciani mlongo Kristina anaona kuti afunika kusamukila mumpingo wacitundu ca m’dziko limene akhala?

15 Nthawi zina, ana akulu-akulu angazindikile kuti afunika kusamukila mumpingo wa citundu cimene amamvetsetsa kuti akwanitse kutumikila bwino Yehova. Zikakhala conco, makolo awo safunika kuona ngati kuti anawo akuwakana. Kristina anati: “N’nali kudziŵako ndithu citundu ca makolo anga, koma zimene zinali kukambidwa kumisonkhano sin’nali kuzimvetsetsa. Pamene n’nafika zaka 12, n’napezeka pa msonkhano wacigawo wa m’citundu cimene n’naphunzila kusukulu. Kwa nthawi yoyamba, n’nadziŵa kuti zimene n’nali kumva ni coonadi. Zinthu zinasinthanso kwambili n’tayamba kupemphela m’citundu cimene n’naphunzila kusukulu. N’nayamba kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima.” (Mac. 2:11, 41) Atakula, Kristina anakambilana nkhaniyi ndi makolo ake, ndipo anaganiza zosamukila mumpingo wa citundu ca kumaloko. Iye anakamba kuti: “Kuphunzila za Yehova m’citundu cimene n’naphunzila kusukulu kunanithandiza kupita patsogolo.” Patangopita nthawi yocepa, Kristina anayamba kucita upainiya ndipo akusangalala.

16. N’cifukwa ciani Nadia amakondwela kuti sanacoke mumpingo wa citundu ca m’dziko limene anacokela?

16 Inu acicepele, kodi muona kuti mufunika kusamukila mumpingo wa citundu ca m’dela limene mukhala? Ngati n’conco, dzifunseni kuti, ‘Kodi kusamukila mumpingo umenewu kudzanithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova?’ (Yak. 4:8) ‘Kapena nifuna kusamuka n’colinga cakuti makolo anga asamaone zimene nimacita kapenanso kuti nisamakhale na zocita zambili?’ Nadia, amene lomba atumikila pa Beteli, anati: “Pamene ine na abale anga tinafika zaka za pakati pa 13 ndi 19, tinafuna kusamukila mumpingo wacinenelo ca m’dela limene tikhala.” Koma makolo awo anaona kuti kusamuka sikukanawathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino na Yehova. Nadia anati: “Tsopano timayamikila kuti makolo athu anayesetsa kutiphunzitsa citundu cawo, ndipo tinapitiliza kukhala mumpingo wa citundu ca m’dziko limene tinacokela. Zimenezi zatithandiza kukhala na umoyo watanthauzo, ndiponso zatipatsa mwayi waukulu wothandiza anthu kudziŵa Yehova.”

MMENE ENA ANGATHANDIZILE

17. (a) Kodi Yehova anapatsa ndani udindo wolela ana? (b) Nanga makolo angapeze kuti thandizo pophunzitsa ana awo coonadi?

17 Yehova anapatsa makolo udindo wophunzitsa ana awo coonadi, osati ambuye awo kapena munthu wina aliyense. (Ŵelengani Miyambo 1:8; 31:10, 27, 28.) Komabe, makolo amene sadziŵa bwino cinenelo ca ana awo, afunika thandizo kuti aphunzitse ana awo mowafika pamtima. Ngati makolo apempha thandizo kwa Akhristu ena, sindiye kuti akupatsa ena udindo wawo wophunzitsa ana. Koma kucita zimenezi kungakhale mbali yolelela ana awo “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Mwacitsanzo, makolo angapemphe akulu kuti awauzeko zimene angacite pa kulambila kwa pabanja, ndi mmene angapezele mabwenzi abwino a ana awo.

Ana ndi makolo awo, onse amapindula akamagwilizana ndi mpingo (Onani mapalagilafu 18 ndi 19)

18, 19. (a) Kodi abale na alongo ofikapo kuuzimu angathandize bwanji acicepele? (b) Kodi makolo afunika kupitiliza kucita ciani?

18 Nthawi na nthawi, makolo angamapemphe mabanja ena acikhristu kuti akhale nawo pa kulambila kwawo kwa pabanja. Komanso, acicepele ambili amapita patsogolo ngati akhala na anzawo okhwima mwauzimu, amene angamapite nawo mu ulaliki kapena kucita nawo zosangulutsa zina zoyenela. (Miy. 27:17) Shan, amene tam’chula kale, anati: “Nikumbukila kuti abale anali kunithandiza. Akanithandiza kukonzekela nkhani za m’sukulu, n’nali kuphunzilapo zambili. Komanso n’nali kukondwela na zosangulutsa zimene tinali kucita.”

19 Akhristu amene makolo asankha kuti athandize ana awo mwauzimu, afunika kukamba zinthu zimene zingalimbikitse anawo kulemekeza makolo awo. Afunika kukamba zabwino ponena za makolowo, osati kucita ngati afuna kuwalanda udindo. Cinanso, othandizawo afunika kupewa khalidwe limene lingapangitse anthu ena mumpingo kapena kunja kwa mpingo kuwakayikila. (1 Pet. 2:12) Makolo akapempha Akhristu ena kuti athandize ana awo, afunika kudziŵa mmene Akhristuwo akuthandizila anawo. Komabe, safunika kusiyila ena nchito yophunzitsa anawo cifukwa ni udindo wawo.

20. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kukhala atumiki a Yehova ocita bwino kuuzimu?

20 Makolo, muzipemphela kwa Yehova kuti akuthandizeni, ndipo muzicita zimene mungathe kuti muphunzitse ana anu. (Ŵelengani 2 Mbiri 15:7.) Muziona ubwenzi wa anawo ndi Yehova kuti ni wofunika kwambili kuposa zofuna zanu. Muzicita zimene mungathe kuti muphunzitse ana anu Mau a Mulungu mowafika pamtima. Musamakayikile kuti mwana wanu angathe kukhala mtumiki wa Yehova. Ngati ana anu amvela Mau a Mulungu ndi kutengela citsanzo canu cabwino, mudzamvela monga mmene Yohane anamvelela atamva za ana ake auzimu. Iye anati: “Palibe cimene cimandisangalatsa kwambili kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’coonadi.”—3 Yoh. 4.

^ par. 7 Onani nkhani yakuti “Mungathe Kuphunzira Chinenero China!” imene ili mu Galamukani! ya March 2007, mapeji 10-12.