Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”

“Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”

“Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?”—YOH. 21:15.

NYIMBO: 128, 45

1, 2. N’ciani cinacitikila Petulo atacezela usiku wonse kuti aphe nsomba?

OPHUNZILA a Yesu 7 anacezela usiku wonse pa Nyanja ya Galileya kuti aphe nsomba, koma sanaphe kanthu. Panthawiyo, Yesu anali atangoukitsidwa kumene. Iye anaimilila m’mbali mwa nyanjayo n’kumayang’ana ophunzilawo. Ndiyeno, anati: “‘Ponyani ukonde kumbali ya kudzanja lamanja kwa ngalawayo ndipo mupeza kenakake.’ Pamenepo anaponyadi ukondewo, koma sanathenso kuukoka cifukwa ca kuculuka kwa nsomba.”—Yoh. 21:1-6.

2 Atawapatsa cakudya ca m’maŵa, Yesu anafunsa Simoni Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?” Kodi pamenepa Yesu anali kukamba zinthu ziti? Petulo anali kukonda nchito yausodzi. Conco, Yesu ayenela kuti anali kufuna kudziŵa cimene Petulo anali kukonda kwambili. Kodi anali kukonda kwambili nsomba ndi bizinesi ya nsomba kuposa mmene anali kukondela Yesu ndi zinthu zimene anam’phunzitsa? Poyankha, Petulo anati: “Inde Ambuye, inunso mukudziŵa kuti ndimakukondani kwambili.” (Yoh. 21:15) Pa moyo wake wonse, Petulo anacitadi zinthu mogwilizana ndi mau ake. Kuyambila nthawiyo, iye anaonetsa cikondi cake pa Khristu mwa kugwila mwakhama nchito yopanga ophunzila, ndipo anakhala mzati mumpingo wacikhristu wa m’zaka 100 zoyambilila.

3. Kodi Akhristu afunika kusamala na ciani?

3 Kodi tingaphunzilepo ciani pa funso limene Yesu anafunsa Petulo? Tifunika kusamala kuti cikondi cathu pa Khristu cisazilale ndiponso kuti tisalole zinthu zina kutilepheletsa kuika zinthu za Ufumu patsogolo. Yesu anali kudziŵa bwino kuti m’dongosolo loipali, padzakhala zinthu zambili zotangwanitsa ndi zodetsa nkhawa. M’fanizo la wofesa mbeu, Yesu anakamba kuti ena adzavomeleza “mau a ufumu,” ndipo adzapita patsogolo kwakanthawi, koma ‘nkhawa za m’nthawi ino ndi cinyengo camphamvu ca cuma cidzalepheletsa mauwo kukula.’ (Mat. 13:19-22; Maliko 4:19) Kukamba zoona, ngati sitisamala, nkhawa za moyo zingatisoceletse ndi kutifooketsa mwauzimu. N’cifukwa cake Yesu anacenjeza ophunzila ake kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambili, kumwa kwambili, ndi nkhawa za moyo.”—Luka 21:34.

4. N’ciani cingatithandize kudziŵa ngati timakonda kwambili Khristu? (Onani pikica kuciyambi.)

4 Mofanana ndi zimene Petulo anacita pambuyo pokumana ndi Yesu, nafenso tifunika kuonetsa kuti timakondadi Khristu mwa kuika patsogolo nchito imene watipatsa. Kodi tingacite ciani kuti tipitilize kucita zimenezi? Nthawi na nthawi, tifunika kudzifunsa kuti: ‘N’ciani cimene nimakonda maka-maka? Kodi nimakondwela kwambili nikamacita zinthu ziti, zauzimu kapena zakuthupi?’ Tsopano tiyeni tikambilane mbali zitatu za umoyo wathu zimene tifunika kusamala nazo kuti tipitilize kukonda kwambili Khristu ndi zinthu zauzimu. Mbali zimenezi ndi nchito yakuthupi, zosangulutsa, na cuma.

KUONA NCHITO YAKUTHUPI MOYENELELA

5. Kodi mitu ya mabanja ili na udindo uti wa m’Malemba?

5 Petulo anali kucita usodzi, osati monga cosangulutsa, koma monga njila yopezela zinthu zofunika paumoyo. Masiku ano, Akhristu amene ndi mitu ya mabanja amadziŵa kuti ali na udindo wa m’Malemba wopezela mabanja awo zinthu zofunika pa umoyo. (1 Tim. 5:8) Iwo afunika kugwila nchito mwakhama kuti akwanilitse udindo umenewu. Komabe, masiku otsiliza ano, nchito ingapangitse anthu kukhala na nkhawa kwambili.

6. Ni mavuto ati amene anthu amakumana nawo kunchito masiku ano?

6 Popeza kuti nchito n’zosoŵa ndipo pali anthu ambili amene afuna nchito, anthu amene ali panchito amakakamizika kuseŵenza kwa maola ambili, mwinanso n’kumalandila malipilo ocepa. Komanso, makampani ambili amafuna kupanga zinthu zambili olo kuti ali na anchito ocepa. Zimenezi zapangitsa kuti anchito ambili azikhala na nkhawa ndiponso azikhala olema. Anchito amakakamizika kucita zilizonse zimene abwana awo awalamula cifukwa coopa kuti angawacotse nchito.

7, 8. (a) Kodi cofunika kwambili kwa ife ndi kukhala wokhulupilika kwa ndani? (b) Ni mfundo yofunika kwambili iti imene m’bale wina ku Thailand anaphunzila pankhani yokhudza nchito?

7 Monga Akhristu, timakhala okhulupilika kwa anthu amene anatilemba nchito, koma timaona kuti cinthu cofunika ngako ndi kukhala wokhulupilika kwa Yehova Mulungu. (Luka 10:27) Nchito ni njila cabe yotithandiza kukwanilitsa udindo wathu. Timaseŵenza kuti tipeze zofunika pa umoyo ndi kuti tizicita bwino utumiki wathu. Koma ngati sitisamala, nchito ingasokoneze kulambila kwathu. Mwacitsanzo, m’bale wina ku Thailand anati: “Nchito yanga yokonza makompyuta n’nali kuikonda ngako, koma n’nali kufunika kuseŵenza maola ambili. Zimenezi zinapangitsa kuti nizisoŵa nthawi yocita zinthu zauzimu. Patapita nthawi, n’nazindikila kuti nifunika kupeza nchito ina kuti nizikwanitsa kuika zinthu za Ufumu patsogolo.” Kodi m’baleyu anacita ciani?

8 M’baleyu anati: “N’takonzekela pafupi-fupi kwa caka cathunthu, n’naleka kugwila nchitoyo n’kuyamba kugulitsa aisikilimu m’misewu. Poyamba, n’nali kusoŵa ndalama, ndipo n’nanganiza zongoleka. Nikakumana na anzanga amene n’nali kugwila nawo nchito yokonza makompyuta, anali kuniseka ndi kunifunsa cifukwa cake n’naleka nchito yokonza makompyuta pa malo abwino n’kuyamba kugulitsa aisikilimu. N’napemphela kwa Yehova kuti anithandize kupilila ndi kukwanilitsa colinga canga cofuna kukhala na nthawi yokwanila yocita zinthu zauzimu. Pasanapite nthawi yaitali, zinthu zinayamba kusintha. N’nafika podziŵa bwino zimene makasitomala anga anali kukonda, ndipo n’naidziŵa bwino nchito yopanga aisikilimu. N’nayamba kugulitsa aisikilimu yonse imene napanga patsiku. Kunena zoona, n’nali kupeza ndalama zambili kusiyana ndi pamene n’nali kugwila ntchito yokonza makompyuta. Ndine wosangalala kwambili cifukwa nilibenso nkhawa ngati imene n’nali nayo pa nchito yakale ija. Ndipo cokondweletsa ngako n’cakuti lomba nili pa ubale wolimba na Yehova.”—Ŵelengani Mateyu 5:3, 6.

9. Tingacite ciani kuti tiziona nchito yakuthupi moyenela?

9 Yehova amayamikila ngati tigwila nchito mwakhama. Komanso, kulimbikila nchito kumabweletsa madalitso. (Miy. 12:14) Komabe, mogwilizana ndi zimene m’bale wa ku Thailand ameneyu anaona, nchito yakuthupi tifunika kuiona moyenela. Yesu anati: “Cotelo pitilizani kufunafuna ufumu coyamba ndi cilungamo cake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mat. 6:33) Kuti tidziŵe ngati timaona zinthu zakuthupi ndi zauzimu moyenela, tifunika kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimakondwela na nchito yanga yakuthupi koma zinthu zauzimu nimaziona monga zosafunika kweni-kweni kapena zotopetsa?’ Kuyelekezela mmene timaonela nchito yathu yakuthupi ndi mmene timaonela zinthu zauzimu kungatithandize kudziŵa zimene timakonda kwambili.

10. Ni mfundo yofunika iti imene Yesu anaphunzitsa pankhani yosankha zinthu zoyenela kuika patsogolo?

10 Yesu anafotokoza mfundo imene ingatithandize kuika zinthu zakuthupi ndi zauzimu pamalo ake. Nthawi ina, iye anapita kukaceza kunyumba kwa Marita ndi Mariya. Pamene Marita anatangwanika na kukonza cakudya, Mariya anakhala pafupi na Yesu n’kumamvetsela zokamba zake. Marita atadandaula kuti Mariya sakum’thandiza, Yesu anamuuza kuti: “Mariya wasankha cinthu cabwino kwambili, ndipo sadzalandidwa cinthu cimeneci.” (Luka 10:38-42) Pamenepa, Yesu anali kuphunzitsa Marita mfundo yofunika ngako. Kuti tipewe kucenjenekewa na zinthu zakuthupi ndi kuonetsa kuti timakondadi Khristu, tifunika kupitiliza kuika zinthu zauzimu patsogolo. Tikatelo, ndiye kuti tasankha “cinthu cabwino kwambili.”

MMENE TIYENELA KUONELA ZOSANGULUTSA

11. Kodi Malemba amakamba ciani pankhani yopumula na kusanguluka?

11 Popeza timakhala na zocita zambili, timafunika nthawi yopumulako ndi kucitako zosangulutsa. Mau a Mulungu amati: “Kwa munthu, palibe cabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake cifukwa coti wagwila nchito mwakhama.” (Mlal. 2:24) Yesu anali kudziŵa kuti kupumula n’kofunika. Mwacitsanzo, pambuyo polalikila kwa nthawi yaitali ndi ophunzila ake, iye anawauza kuti: “Inuyo bwelani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.”—Maliko 6:31, 32.

12. Ni cenjezo lotani limene lilipo pankhani ya zosangulutsa? Fotokozani citsanzo.

12 Ndithudi, zosangulutsa n’zofunika pa umoyo wa munthu. Koma tifunika kusamala kuti tisamaone zosangulutsa monga zinthu zofunika kwambili pa umoyo. M’zaka 100 zoyambilila, anthu ambili anali kukonda zosangulutsa. Iwo anali kukamba kuti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.” (1 Akor. 15:32) Mzimu umenewu ni wofala m’madela ambili padzikoli. Mwacitsanzo, zaka zapitazo, mnyamata wina ku Europe anayamba kupezeka pa misonkhano yacikhristu. Koma anali kukonda kwambili zosangulutsa cakuti analeka kugwilizana ndi anthu a Yehova. M’kupita kwa nthawi, anaona kuti kukonda zosangulutsa kunam’bweletsela mavuto ambili. Conco, anayambanso kuphunzila Baibo, ndipo m’kupita kwa nthawi anayenelela kukhala wofalitsa uthenga wabwino. Atabatizika, anati: “Nimaona kuti n’nachedwa kuyamba kutumikila Mulungu. Kutumikila Yehova kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kucita zosangulutsa za m’dzikoli.”

13. (a) Fotokozani citsanzo coonetsa ngozi imene ingakhalepo ngati timakonda kwambili zosangulutsa. (b) N’ciani cingatithandize kuti tiziona zosangulutsa moyenela?

13 Zosangulutsa zimatitsitsimula ndi kutithandiza kupezanso mphamvu. Koma kodi tifunika kuthela nthawi yoculuka bwanji pa zosangulutsa kuti zikhaledi zothandiza? Tiyelekezele tele: Ambili a ife timasangalala kudya zakudya zonzuna nthawi na nthawi. Koma timadziŵa kuti kudya kaŵili-kaŵili zakudya zonzuna monga makeke, cokoleti, mabisiketi, ndi zina zaconco kungawononge thanzi lathu. Ndiye cifukwa cake timakonda kudya zakudya zopatsa thanzi. Mofanana ndi zimenezi, kukonda zosangulutsa kungatifooketse mwauzimu. Kuti tipewe vuto limeneli, tifunika kumacita zinthu zocilikiza Ufumu nthawi zonse. Kodi tingadziŵe bwanji kuti timaona zosangulutsa moyenelela? Wiki ina, tingalembe ciŵelengelo ca maola amene tathela pocita zinthu zauzimu, monga kusonkhana, kulalikila, na kucita phunzilo laumwini ndi la pabanja. Ndiyeno, tingalembe ciŵelengelo ca maola amene tathela wiki imodzi-modziyo pocita zosangulutsa monga zamaseŵela, kuonelela TV, kucita maseŵela a pakompyuta, ndi zosangulutsa zina zimene timakonda. Pambuyo poyelekezela, kodi muona kuti mumathela nthawi yaitali pa zinthu ziti? Kodi mungafunike kucepetsa nthawi imene mumathela pocita zosangulutsa?—Ŵelengani Aefeso 5:15, 16.

14. N’ciani cingatithandize kusankha zosangulutsa zoyenela?

14 Mkhristu aliyense ali na ufulu wosankha zosangulutsa zimene wakonda, ndipo mitu ya mabanja nayonso ingasankhile banja lawo zosangulutsa. Komabe, zosankhazo zifunika kukhala zogwilizana ndi mfundo za Yehova zopezeka m’Baibo. * Zosangulutsa zoyenela ni “mphatso yocokela kwa Mulungu.” (Mlal. 3:12, 13) N’zoona kuti anthufe timakonda zosangulutsa zosiyana-siyana. (Agal. 6:4, 5) Komabe, kaya tasankha zosangulutsa zotani, tifunika kuziika pamalo ake oyenelela. Yesu anati: “Kumene kuli cuma cako, mtima wako umakhalanso komweko.” (Mat. 6:21) Conco, kukonda Yesu na mtima wonse, kudzatilimbikitsa kuganiza, kukamba, na kucita zinthu zoonetsa kuti timaika zinthu za Ufumu patsogolo osati zakuthupi.—Afil. 1:9, 10.

KUPEWA MZIMU WOKONDA ZINTHU ZAKUTHUPI

15, 16. (a) Kodi kukonda cuma kungakhale msampha kwa Mkhristu m’njila yanji? (b) Kodi Yesu anapeleka malangizo anzelu ati pankhani yokonda cuma?

15 Masiku ano, anthu ambili amafunitsitsa kukhala na zinthu zimene zili m’fashoni, kaya ni zovala, mafoni, makompyuta, kapena zinthu zina. Conco, Mkhristu aliyense afunika kudzifufuza nthawi na nthawi kuti adziŵe ngati amaona zinthu zimenezi moyenela. Angacite zimenezi mwa kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimaona zinthu zakuthupi kukhala zofunika kwambili, cakuti nimathela nthawi yaitali kufufuza na kuganizila za mamotoka amakono, kuposa nthawi imene nimathela pokonzekela misonkhano yampingo? Kodi nimakhala wotangwanika ngako na zocita za tsiku na tsiku cakuti nimakhala na nthawi yocepa yopemphela kapena kuŵelenga Baibo?’ Tikaona kuti kukonda zinthu zakuthupi kukucititsa cikondi cathu pa Khristu kuzilala, tifunika kukumbukila mau a Yesu akuti: “Cenjelani ndi kusilila kwa nsanje kwamtundu uliwonse.” (Luka 12:15) N’cifukwa ninji Yesu anapeleka cenjezo lamphamvu limeneli?

16 Yesu anakamba kuti “kapolo sangatumikile ambuye aŵili.” Anakambanso kuti: “Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” Zili conco cifukwa kutumikila Mulungu ndiponso kutumikila cuma, zonse zimafuna nthawi ndi kudzipeleka na mtima wonse. Yesu anati ‘tidzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo,’ kapena ‘tidzakhulupilika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo.’ (Mat. 6:24) Popeza ndise opanda ungwilo, tonse tifunika kupitiliza kulimbana ndi “zilakolako za thupi lathu,” kuphatikizapo mzimu wokonda cuma.—Aef. 2:3.

17. (a) N’cifukwa ciani anthu okonda zinthu zakuthupi amalephela kuona cuma moyenelela? (b) N’ciani cimatithandiza kupewa mzimu wokonda cuma?

17 Anthu okonda zinthu zakuthupi cimawavuta kuika zinthu zauzimu patsogolo. Cifukwa? Ni wogontha mwauzimu. (Ŵelengani 1 Akorinto 2:14.) Popeza kuti alibe mphamvu zokwanila za kuzindikila, zimawavuta kusiyanitsa coyenela na cosayenela. (Aheb. 5:11-14) Zotulukapo zake n’zakuti ena akhala na mtima wofunitsitsa kulemela, ndipo sakhutila na zimene ali nazo. (Mlal. 5:10) Koma pali njila imene tingapewele vuto la kukonda cuma. Tifunika kumaphunzila Mau a Mulungu, Baibo, tsiku lililonse. (1 Pet. 2:2) Mwacitsanzo, kusinkha-sinkha coonadi ca Mau a Mulungu kunathandiza Yesu kuti asagonje atakumana ndi ciyeso. Nafenso ngati titsatila mfundo za m’Baibo, tidzatha kupewa mzimu wokonda cuma. (Mat. 4:8-10) Tikacita zimenezi, tidzaonetsa kuti timakonda Yesu kuposa zinthu zakuthupi.

N’ciani cimene mumaika patsogolo mu umoyo wanu? (Onani palagilafu 18)

18. Kodi inu mwatsimikiza mtima kucita ciani?

18 Pamene Yesu anafunsa Petulo kuti: “Kodi umandikonda ine kuposa izi?” anali kum’kumbutsa za kufunika koika zinthu zauzimu patsogolo mu umoyo wake. Dzina lakuti Petulo limatanthauza “cidutswa ca mwala,” ndipo pa moyo wake wonse, iye anacitadi zinthu mogwilizana ndi tanthauzo la dzinali. Anacita zinthu zoonetsa kuti anali ndi cikhulupililo colimba ngati thanthwe. (Mac. 4:5-20) Naise masiku ano, tatsimikiza mtima kupitilizabe kukonda Khristu, kuona moyenela nchito yakuthupi, zosangulutsa, na cuma. Zosankha zathu pa umoyo zifunika kuonetsa kuti tili na maganizo monga a Petulo, amene anauza Yesu kuti: “Ambuye, inunso mukudziŵa kuti ndimakukondani kwambili.”

^ par. 14 Onani nkhani yakuti “Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2011, mapeji 9-12, mapalagilafu 6-15.