Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ikani Mtima Wanu pa Cuma Cauzimu

Ikani Mtima Wanu pa Cuma Cauzimu

“Kumene kuli cuma canu, mitima yanunso idzakhala komweko.”—LUKA 12:34.

NYIMBO: 153, 104

1, 2. (a) Kodi Yehova watipatsa zinthu zitatu ziti zimene ndi cuma cauzimu? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

YEHOVA ali na cuma cambili kuposa wina aliyense m’cilengedwe conse. (1 Mbiri 29:11, 12) Monga Tate woolowa manja, iye amagaŵila cuma cake cauzimu kwa anthu amene amaciona kukhala cofunika. Ndise oyamikila kwambili kuti Yehova watipatsa cuma cauzimu. Cuma cimeneci ciphatikizapo, (1) Ufumu wa Mulungu, (2) utumiki wathu wopulumutsa moyo, ndi (3) coonadi camtengo wapatali copezeka m’Mau ake. Komabe, ngati sitisamala, tingaleke kuyamikila cuma cimeneci, mpaka kufika pocitaya, titelo kunena kwake. Conco, kuti ticisunge, tifunika kuciseŵenzetsa bwino na kupitiliza kucita zinthu zotithandiza kucikonda kwambili. Paja Yesu anati: “Kumene kuli cuma canu, mitima yanunso idzakhala komweko.”—Luka 12:34.

2 Lomba tiyeni tikambilane zimene tingacite kuti tipitilize kukonda Ufumu wa Mulungu, ulaliki, ndi coonadi. Tidzaonanso zimene tingacite kuti tipitilize kuona zinthu zimenezi kukhala zofunika. Pamene tikambilana, ganizilani zimene inu pamwekha mungacite kuti muzikonda kwambili cuma cauzimu cimeneci.

UFUMU WA MULUNGU ULI NGATI NGALE YAMTENGO WAPATALI

3. Kodi wamalonda wa m’fanizo la Yesu anali wofunitsitsa kucita ciani kuti agule ngale yamtengo wapatali? (Onani pikica kuciyambi.)

3 Ŵelengani Mateyu 13:45, 46. Yesu anafotokoza fanizo la munthu wamalonda amene anali kufuna-funa ngale. Kwa zaka zoculuka, wamalondayu ayenela kuti anagula na kugulitsa ngale zambili-mbili. Koma panthawiyi, anapeza ngale yamtengo wapatali kwambili cakuti atangoiwona, anakondwela ngako. Kuti aigule, anafunika kugulitsa zonse zimene anali nazo. Mosakayikila, ngaleyo inalidi yamtengo wapatali kwa iye.

4. Ngati tikonda Ufumu wa Mulungu monga mmene wamalonda anakondela ngale, kodi tidzacita ciani?

4 Kodi tiphunzilapo ciani pa fanizo limeneli? Coonadi conena za Ufumu wa Mulungu cili ngati ngale yamtengo wapatali. Ngati timakonda coonadi monga mmene wamalonda anakondela ngale ija, tidzakhala okonzeka kusiya zilizonse n’colinga cakuti tikhale nzika za Ufumu wa Mulungu, ndi kupitiliza kucita zinthu monga nzika. (Ŵelengani Maliko 10:28-30.) Tiyeni tikambilane za anthu aŵili amene anacita zimenezi.

5. Kodi Zakeyu anacita ciani kuti akhale woyenelela kuloŵa Ufumu wa Mulungu?

5 Zakeyu anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo analemela kwambili cifukwa cobela anthu ndalama. (Luka 19:1-9) Koma pamene munthu wosalungama ameneyu anamvela Yesu akuphunzitsa za Ufumu, anazindikila kuti zinthu zimene anali kumvazo zinali zofunika, ndipo sanazengeleze kucitapo kanthu. Zakeyu anati: “Ambuye, ine ndipeleka ndithu hafu ya cuma canga kwa osauka. Ndipo ciliconse cimene ndinalanda munthu aliyense pomunamizila mlandu ndibweza kuwilikiza kanayi.” Iye anabwezela cuma conse cimene anapeza mwacinyengo, ndipo analeka kukhala na mtima wadyela.

6. N’zinthu ziti zimene Rose anasintha pa umoyo wake kuti akhale nzika ya Ufumu wa Mulungu? Nanga n’cifukwa ciani anasintha?

6 Zaka zapitazo, mzimayi wina amene tam’patsa dzina lakuti Rose anamvela uthenga wa Ufumu. Panthawiyo, iye anali ndi khalidwe logonana ndi akazi anzake. Analinso pulezidenti wa bungwe lomenyela ufulu wa amuna kapena akazi ogonana okha-okha. Koma Rose ataphunzila Baibo, anadziŵa kuti coonadi conena za Ufumu wa Mulungu n’camtengo wapatali. Iye anaona kuti afunika kusintha kwambili khalidwe lake. (1 Akor. 6:9, 10) Cifukwa cokonda Mulungu, anatula pansi udindo wake ndi kuleka khalidwe logonana ndi akazi anzake. Rose anabatizika mu 2009, ndipo m’caka cotsatila, anayamba upainiya wanthawi zonse. Cikondi cake pa Yehova ndi Ufumu wake cinali camphamvu kwambili kuposa zilakolako zathupi.—Maliko 12:29, 30.

7. Tingacite ciani kuti tipitilize kukonda Ufumu wa Mulungu na mtima wathu wonse?

7 Ambili a ise tasintha zinthu zambili pa umoyo wathu kuti tikhale nzika za Ufumu wa Mulungu. (Aroma 12:2) Ngakhale n’conco, pakali zina zofunika kucita. Tifunika kukhalabe chelu na zinthu zimene zingacititse kuti tileke kukonda Ufumu. Zina mwa zinthu zimenezi ndi kukonda zinthu zakuthupi ndi cilakolako coipa ca kugonana. (Miy. 4:23; Mat. 5:27-29) Pofuna kutithandiza kuti tipitilize kukonda Ufumu wa Mulungu na mtima wathu wonse, Yehova watipatsa cinthu cina cimenenso ni cuma camtengo wapatali.

UTUMIKI WATHU WOPULUMUTSA MOYO

8. (a) N’cifukwa ciani mtumwi Paulo anakamba kuti utumiki wathu ni “cuma m’zonyamulila zoumbidwa ndi dothi?” (b) Kodi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali kuona ulaliki kukhala wofunika?

8 Yesu anatipatsa nchito yolalikila ndi kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mat. 28:19, 20) Mtumwi Paulo anazindikila kuti nchito yolalikila ni yofunika ngako. Iye anafotokoza kuti utumiki wa pangano latsopano ni “cuma m’zonyamulila zoumbidwa ndi dothi.” (2 Akor. 4:7; 1 Tim. 1:12.) Cifukwa copanda ungwilo, tili monga zonyamulila zoumbidwa na dothi. Ngakhale n’conco, uthenga umene timalalikila udzatithandiza kuti tidzapeze moyo wosatha pamodzi ndi anthu amene amamvetsela uthengawo. Ndiye cifukwa cake Paulo anati: “Ndikucita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino, kuti ndiugaŵilenso kwa ena.” (1 Akor. 9:23) Kukonda nchito yolalikila, kunalimbikitsa Paulo kucita khama pa nchito yopanga ophunzila. (Ŵelengani Aroma 1:14, 15; 2 Timoteyo 4:2.) Izi zinam’thandiza kupilila citsutso coopsa. (1 Ates. 2:2) Kodi ise tingaonetse bwanji kuti timakonda ulaliki?

9. Ni njila zina ziti zimene tingaonetsele kuti timayamikila nchito yolalikila?

9 Imodzi mwa njila zimene Paulo anaonetsela kuti anali kuyamikila nchito yolalikila, ndi kulalikila anthu pa mpata uliwonse umene wapezeka. Mofanana ndi atumwi ndi Akhristu oyambilila, ifenso masiku ano timacita ulaliki wamwayi, wapoyela, ndi wa kunyumba ndi nyumba. (Mac. 5:42; 20:20) Malinga ni mmene zinthu zilili pa umoyo wathu, tingacite bwino kuona njila za mmene tingawonjezele utumiki wathu. Mwina tingaciteko upainiya wothandiza kapena wanthawi zonse. Tingaphunzilekonso citundu cina, ndi kupita kumene kuli alengezi a Ufumu ocepa m’dziko lathu kapena m’dziko lina.—Mac. 16:9, 10.

10. Kodi Irene anadalitsidwa bwanji cifukwa cofunitsitsa kuuzako ena uthenga wabwino?

10 Ganizilani citsanzo ca mlongo Irene wa ku United States, amene sali pabanja. Iye anali kufunitsitsa kulalikila anthu okamba Cirasha amene anasamukila m’dzikolo. Pamene anayamba kucita zimenezo mu 1993, mumzinda wa New York munali kagulu ka ofalitsa 20 cabe okamba Cirasha. Kwa zaka 20, Irene wakhala akulalikila mwakhama anthu okamba citundu cimeneci. Iye anakamba kuti: “Mpaka lomba sinikamba bwino-bwino citundu ca Cirasha.” Komabe, Yehova wadalitsa khama lake ndi la ena odzipeleka ngati iye. Pali pano, mumzinda wa New York muli mipingo 6 ya citundu ca Cirasha. Anthu 15 mwa anthu amene Irene anaphunzila nawo Baibo, anabatizika. Ena mwa iwo ni atumiki a pa Beteli, ena ni apainiya, ndipo ena ni akulu. Irene anati: “Niona kuti palibe colinga cina cimene cikananibweletsela cimwemwe coculuka kuposa zimene n’nasankha kucita.” Ndithudi, iye amaona utumiki wake kukhala cuma camtengo wapatali.

Kodi inu mumaona nchito yolalikila kukhala yofunika pa umoyo wanu mwa kupatula nthawi yopita mu ulaliki wiki iliyonse? (Onani palagilafu 11, 12)

11. Kodi pamakhala zotulukapo zotani ngati tipitiliza kulalikila ngakhale kuti ena akutizunza?

11 Ngati timaona utumiki wathu monga cuma, tidzatsatila citsanzo ca mtumwi Paulo mwa kupitilizabe kulalikila olo tikumane na cizunzo. (Mac. 14:19-22) Mwacitsanzo, m’zaka za m’ma 1930 mpaka kuciyambi kwa zaka za m’ma 1940, abale athu ku United States anakumana ndi citsutso coopsa. Koma mofanana ndi Paulo, iwo anakhalabe olimba ndipo sanaleke kulalikila. Pofuna kuti akhale na ufulu wolalikila, iwo anakamba ndi kupambana milandu yambili ku makhoti. Mu 1943, M’bale Nathan H. Knorr anakambako zokhudza mlandu umene abale anapambana mu Khoti Lalikulu kwambili ku United States. Iye anati: “Tapambana milandu kukhoti cifukwa ca kulimba mtima kwanu. Ofalitsa akanaleka kulalikila, sembe ku Khoti Lalikulu kulibe milandu. Koma popeza inu ofalitsa, abale padziko lonse simunaleke kulalikila, n’cifukwa cake tagonjetsa anthu amene akutizunza. Kulimba mtima kwa anthu a Ambuye n’kumene kwacititsa kuti tipambane milandu.” Kulimba mtima kwa abale athu m’mayiko ena kwacititsanso kuti tipambane milandu ina ngati imeneyi m’mayikowo. Zoonadi, kukonda utumiki kumatithandiza kuti tisagonje kwa anthu amene amatizunza.

12. Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kucita ciani panchito yolalikila?

12 Ngati timaona utumiki monga cuma camtengo wapatali cocokela kwa Yehova, sitidzakhutila na kupanga cabe maola tikapita mu ulaliki. Koma tidzacita zilizonse zimene tingathe kuti ‘ticitile umboni mokwanila za uthenga wabwino.’ (Mac. 20:24; 2 Tim. 4:5) Kodi n’ciani cimene tidzalalikila kwa anthu? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambilane za cinthu cina cimene Mulungu watipatsa, cimenenso ni cuma.

NKHOKWE YATHU YOSUNGILAMO COONADI CA MTENGO WAPATALI

13, 14. Kodi “mosungilamo cuma,” kapena kuti nkhokwe, imene Yesu anachula pa Mateyu 13:52 n’ciani? Nanga timaikamo bwanji cumaco?

13 Cinthu cinanso cimene ndi mbali ya cuma cathu cauzimu ni coonadi cimene tinaphunzila. Yehova, ni Mulungu wa coonadi. (2 Sam. 7:28; Sal. 31:5) Monga Tate woolowa manja, amaphunzitsa coonadi anthu amene amamuopa. Kucokela pamene tinayamba kuphunzila coonadi, taphunzila mfundo zambili za coonadi m’Mau a Mulungu, Baibo, m’zofalitsa zathu, pamisonkhano yacigawo, yadela, ndi yampingo. M’kupita kwa nthawi, tinakhala na cimene Yesu anacicha “mosungilamo cuma,” cimene ndi mfundo za coonadi, zakale ndi zatsopano. (Ŵelengani Mateyu 13:52.) Tikamayesetsa kufuna-funa coonadi ngati cuma cobisika, Yehova adzatithandiza kupeza mfundo zatsopano za coonadi zimene tingaike “mosungilamo cuma” cathu. (Welengani Miyambo 2:4-7.) Kodi tingacite bwanji zimenezi?

14 Tifunika kukhala na cizoloŵezi cabwino cocita phunzilo laumwini, ndipo tizifufuza mokwanila mfundo za m’Mau a Mulungu ndi m’zofalitsa zathu. Kucita izi kudzatithandiza kupeza mfundo za coonadi zimene zingakhale zatsopano kwa ife. (Yos. 1:8, 9; Sal. 1:2, 3) Magazini yoyamba ya Nsanja, imene inafalitsidwa mu July 1879, inati: “Coonadi cili ngati duŵa laling’ono m’sanga, limene lili pakati pa viudzu vimene vatsala pang’ono kuliphimba. Kuti mulipeze, mufunika kusakila mwakhama. . . . Kuti mukhale nalo, mufunika kuŵelama ndi kulitenga. Musakhutile ndi duŵa limodzi cabe la coonadi. . . . Pitilizani kusakila ena ambili, musaleke.” Inde, tifunika kukhala na mtima wofuna kuphunzila mfundo zambili za coonadi.

15. Kodi tingakambe kuti mfundo zina za coonadi ndi “zakale” m’lingalilo lotani? Nanga ni mfundo ziti za coonadi zimene imwe mumakonda ngako?

15 Pali mfundo zina za coonadi zofunika kwambili zimene tinadziŵa pamene tinayamba kugwilizana ndi anthu a Mulungu. Zimenezi zili ngati coonadi “cakale” m’lingalilo lakuti tinazidziŵa ndi kuzimvetsetsa titangokhala Mkhristu. Kodi mfundo za coonadi zamtengo wapatali zimenezi n’ziti? Tinaphunzila kuti Yehova ndiye Mlengi wathu ndi Wotipatsa Moyo, ndipo ali nafe na colinga. Tinaphunzilanso kuti cifukwa ca cikondi, Mulungu anapeleka nsembe ya dipo la Mwana wake kuti atimasule ku ucimo na imfa. Cinanso, tinaphunzila kuti Ufumu wake udzathetsa mavuto onse, ndi kuti tili na ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha, mwamtendele ndi mosangalala mu Ufumuwo.—Yoh. 3:16; Chiv. 4:11; 21:3, 4.

16. Kodi tifunika kucita ciani pakakhala kusintha kwa kamvedwe ka mfundo zina za coonadi?

16 Nthawi na nthawi, kamvedwe kathu ka maulosi a m’Baibo kapena Malemba ena kamasintha. Pakakhala kusintha kwa conco, tifunika kupatula nthawi yophunzila nkhaniyo mosamala na kuisinkhasinkha. (Mac. 17:11; 1 Tim. 4:15) Sitifunika cabe kumvetsetsa mfundo zikulu-zikulu zimene zasintha, koma tifunikanso kumvetsetsa mfundo zonse, ngakhale zimene zingaoneke ngati zazing’ono. Tikatelo, ndiye kuti mfundo zatsopano za coonadi zidzakhazikika mumtima mwathu. N’cifukwa ciani tifunika kucita khama mwanjila imeneyi?

17, 18. Kodi mzimu woyela ungatithandize bwanji?

17 Yesu anakamba kuti mzimu wa Mulungu ungatikumbutse zinthu zimene tinaphunzila. (Yoh. 14:25, 26) Kodi zimenezi zingatithandize bwanji monga aphunzitsi a uthenga wabwino? Ganizilani zimene zinacitikila m’bale wina, dzina lake Peter. Mu 1970, anali na zaka 19 ndipo anali atayamba kumene kutumikila pa Beteli ya ku Britain. Tsiku lina pamene anali kulalikila nyumba na nyumba, anakumana ndi mwamuna wina wavindevu. Peter anafunsa munthuyo ngati anali kufuna kumvetsetsa Baibo. Modabwa, munthuyo anauza Peter kuti, pano wafika ni panyumba ya arabi aciyuda. M’rabiyo pofuna kuyesa Peter anamufunsa kuti: “Mnyamata iwe, buku la Danieli linalembedwa m’citundu canji?” Peter anayankha kuti: “Mbali ina inalembedwa m’Ciaramu.” Pofotokoza zimene zinacitika, Peter anati: “M’rabiyo anadabwa kuti n’nali kuidziŵa yankho, koma ine sin’naone ngati ni funso lovuta. Kodi n’nadziŵa bwanji yankho? Pamene n’nabwelela kunyumba ndi kufufuza m’magazini a Nsanja ndi Galamukani! a miyezi yapambuyo, n’napeza nkhani imene inafotokoza kuti buku la Danieli linalembedwa m’Ciaramu.” (Dan. 2:4) Izi zionetsa kuti mzimu woyela ungathe kutikumbutsa mfundo zimene tinaŵelenga ndi kuzisunga bwino mosungilamo cuma cathu.—Luka 12:11, 12; 21:13-15.

18 Ngati tiona kuti nzelu zocokela kwa Yehova n’zofunika kwambili, tidzakhala wofunitsitsa kudzaza mosungila cuma cathu mfundo zatsopano ndi zakale za coonadi. Pamene tipitiliza kukonda na kuyamikila nzelu zocokela kwa Yehova, tidzakhala okonzeka kugwila nchito yathu yophunzitsa ena mau a Mulungu.

TETEZANI CUMA CANU CAUZIMU

19. N’cifukwa ciani tifunika kuteteza cuma cathu cauzimu?

19 Satana ndi dziko lake akuyesetsa kutifooketsa ndi kuticititsa kuti tisamaone cuma cauzimu cimene taphunzila m’nkhani ino kukhala cofunika. Iye amatiyesa na misampha yake. Ndipo ngati sitisamala, tikhoza kucenjenekewa na zinthu monga kufuna kuloŵa nchito yapamwamba yokhala na malipilo ambili, kukhala na umoyo wofewa, kapena kudzionetsela na zimene tili nazo pa umoyo. Mtumwi Paulo anaticenjeza kuti dzikoli likupita pamodzi ndi cilakolako cake. (1 Yoh. 2:15-17) Conco, tifunika kuyesetsa kuteteza cuma cathu cauzimu ndi kumaciona kuti ni cofunika kwambili.

20. Kodi imwe pacanu, mwatsimikiza mtima kucita ciani kuti muteteze cuma canu cauzimu?

20 Khalani ofunitsitsa kuleka kucita zinthu zimene zingakulepheletseni kukonda Ufumu wa Mulungu ndi mtima wanu wonse. Pitilizani kulalikila mokangalika, ndipo musaleke kuona kuti nchito yopulumutsa moyo imeneyi ni yofunika ngako. Pitilizani kufufuza mwakhama coonadi ca m’Baibo. Pamene mucita zimenezi, mudzaunjika “cuma cosatha kumwamba, kumene mbala singafikeko, ndipo njenjete singawononge. Pakuti kumene kuli cuma canu, mitima yanunso idzakhala komweko.”—Luka 12:33, 34.