Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumathetsa Kusamvana N’kukhazikitsa Mtendere?

Kodi Mumathetsa Kusamvana N’kukhazikitsa Mtendere?

YEHOVA MULUNGU amalimbikitsa Akhristu kuti aziyesetsa kwambiri kuti azikhala mwamtendere. Tikamachita zimenezi timakhala ndi mtendere wochuluka. Izi zimachititsa kuti anthu ena amene amafuna kukhala mwamtendere azichita chidwi ndi gulu la Yehova.

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi munthu wina wa ku Madagascar yemwe anali sing’anga. Iye ataona kuti a Mboni za Yehova amakhala mwamtendere kwambiri, ananena kuti: ‘Ngati nditafuna kulowa chipembedzo chinachake ndikhoza kulowa cha Mboni za Yehova.’ Patapita nthawi, iye anasiya kuchita zamatsenga ndipo anakonza zinthu kuti ukwati wake ukhale wovomerezeka ngakhale kuti zinamutengera miyezi yambiri. Kenako anakhala wa Mboni za Yehova n’kumalambira Mulungu yemwe ndi wamtendere.

Mofanana ndi munthuyu, chaka chilichonse anthu masauzande ambiri amalowa mumpingo wachikhristu ndipo amapeza mtendere umene akhala akuufunafuna. Koma Baibulo limasonyeza kuti “nsanje yaikulu ndi kukonda mikangano” zikhoza kusokoneza mgwirizano mumpingo. (Yak. 3:14-16) Koma n’zosangalatsa kuti m’Baibulo muli malangizo amene angathandize anthu kupewa kusamvana komanso kukhazikitsa mtendere. Koma tisanakambirane za malangizowo, tiyeni tione kaye mavuto amene anthu ena akumana nawo.

MAVUTO AMENE TINGAKUMANE NAWO KOMANSO NJIRA YOWATHETSERA

“Ndinkavutika kuti ndizigwirizana ndi m’bale wina amene ndinkagwira naye ntchito. Tsiku lina anthu awiri anatipeza tikukangana kwambiri.”—CHRIS.

“Tsiku lina mlongo wina amene ndinkalowa naye mu utumiki, anangosiya mwadzidzidzi kuyenda nane. Kenako anasiyanso kundilankhula. Sindinkadziwa chimene chinachitika.”—JANET.

“Tsiku lina ndinkalankhula pa foni ndi anthu awiri nthawi imodzi. Kenako wina anatsanzika ndipo ndinaganiza kuti wadula foniyo moti ndinayamba kunena zinthu zoipa zokhudza munthuyo kwa wina amene anatsalayo. Koma sindinkadziwa kuti amene ndinkaganiza kuti wadula foniyo anali asanadule.”—MICHAEL.

“Mumpingo wathu, apainiya awiri anayamba kusagwirizana. Tsiku lina, wina anayamba kukalipira mnzakeyo ndipo kukangana kwawo kunakhumudwitsa anthu ena.”—GARY.

Mwina mungaone kuti mavuto amene tawatchulawa ndi aang’ono. Komabe vuto lililonse limene tatchulali likanasokoneza kwambiri anthuwo komanso ubwenzi wawo ndi Yehova. Chosangalatsa n’chakuti abale ndi alongowa anakhazikitsa mtendere chifukwa chotsatira malangizo a m’Baibulo. Kodi mukuganiza kuti anatsatira malangizo ati a m’Baibulo?

“Musakanganetu m’njira.” (Gen. 45:24) Yosefe anapereka malangizowa kwa abale ake pamene ankanyamuka kubwerera kwawo. Malangizowa anali anzeru kwambiri. Munthu akapanda kuugwira mtima n’kukwiya akhoza kukwiyitsanso anthu ena. Chris anazindikira kuti anali ndi vuto lonyada komanso sankafuna kuuzidwa zochita. Iye anaona kuti akufunika kusintha ndipo anapepesa m’bale amene ankakangana naye uja. Ankayesetsanso kwambiri kuti asamapse mtima msanga. M’bale uja ataona kuti Chris akuyesetsa kusintha nayenso anayamba kusintha. Panopa amatumikira limodzi Yehova mosangalala.

“Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima.” (Miy. 15:22) Janet anazindikira kuti ankayenera kuyesetsa kutsatira malangizowa. Iye anasankha zokakambirana ndi mlongo uja. Janet anamufunsa mwaulemu kuti afotokoze mmene ankamvera. Poyamba sizinali zophweka kuti akambirane zimenezi. Koma atapitiriza kukambirana modekha anayamba kumvetsetsana. Mlongoyo anazindikira kuti sanamvetse nkhani inayake imene sinkamukhudza n’komwe Janet. Mlongoyo anapepesa ndipo iye ndi Janet anayambanso kutumikira Yehova mogwirizana.

“Ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba.” (Mat. 5:23, 24) Mwina mungakumbukire kuti malangizowa ndi amene Yesu anapereka pa ulaliki wake wa paphiri. Michael anadzimvera chisoni atazindikira kuti zimene anachita zija zinali zoipa kwambiri. Choncho ankafunitsitsa kuti akhazikitse mtendere ndi m’baleyo. Anapita kukakumana naye ndipo anamupepesa modzichepetsa. Kodi zimenezi zinathandiza bwanji? Michael anati: “M’bale wangayo anandikhululukira kuchokera pansi pa mtima.” Kenako anayambanso kugwirizana.

“Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.” (Akol. 3:12-14) Mkulu wina anakambirana ndi apainiya awiri amene sankagwirizana aja. Mkuluyo anawauza kuti aganizire mafunso awa: ‘Kodi ndi bwino kuti tizikhumudwitsa anthu ena chifukwa cha kusamvana kwathu? Kodi tilidi ndi chifukwa chomveka chotichititsa kuti tisakhululukirane komanso kuti tisamatumikire Yehova mwamtendere?’ Iwo anamvera malangizo a mkuluyo moti panopa amagwirizana ndiponso amalalikira limodzi.

Ngati munthu wina wakukhumudwitsani, mungachite bwino kutsatira malangizo a pa Akolose 3:12-14 amene tatchulawa. Anthu ambiri aona kuti kudzichepetsa kumawathandiza kukhululukira ena n’kuiwala zimene anawalakwira. Koma ngati mukuona kuti zimenezi sizingatheke, mukhoza kutsatira mfundo ya pa Mateyu 18:15. N’zoona kuti malangizo a Yesu palembali ndi opita kwa anthu amene alakwira anzawo pa nkhani yaikulu. Komabe mfundo yake ikhoza kukuthandizani ngakhale pa nkhani zing’onozing’ono. Mukhoza kupita kwa m’bale kapena mlongo wanuyo kuti mukakambirane naye mwachikondi ndiponso modzichepetsa n’cholinga choti muthetse vutolo.

M’Baibulo muli malangizo ambiri othandiza pa nkhaniyi. Kuti mutsatire malangizowa mumafunika kusonyeza makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa omwe ndi “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.” (Agal. 5:22, 23) Makhalidwewa amathandiza kuti tizikhala ndi anthu mwamtendere ngati mmene oilo amathandizira kuti mashini azigwira bwino ntchito.

MPINGO UMASANGALATSA UKAKHALA NDI ANTHU OSIYANASIYANA

Anthu osiyana kwambiri akhoza kugwirizana ndiponso kuthandizana. Koma nthawi zina, kusiyanaku kungachititse kuti anthu asamamvane. Mkulu wina anapereka chitsanzo ichi: “Munthu wamanyazi angamavutike kuti azigwirizana ndi munthu womasuka kwambiri. Mwina tingaone kuti kusiyana kwa anthuwo si nkhani yaikulu koma zikhoza kubweretsa mavuto.” Koma kodi mumaona kuti n’zosatheka kuti anthu osiyana kwambiri azigwirizana? Ngati ndi choncho, taganizirani za mtumwi Petulo ndi mtumwi Yohane. Mwina mumaona kuti Petulo ankakonda kunena maganizo ake komanso anali wopupuluma. Pomwe Yohane anali wachikondi kwambiri ndipo ankasamala polankhula komanso pochita zinthu. Pali zifukwa zomveka zoganizira kuti anthuwa anali ndi makhalidwe osiyana chonchi. Komabe ankagwira ntchito limodzi mogwirizana. (Mac. 8:14; Agal. 2:9) Masiku anonso, Akhristu osiyana kwambiri akhoza kuchitira zinthu limodzi bwinobwino.

Mwina mumpingo wanu muli m’bale amene zochita kapena zolankhula zake sizimakusangalatsani. Komabe mumadziwa kuti Khristu anamufera ndipo mumafunika kumusonyeza chikondi. (Yoh. 13:34, 35; Aroma 5:6-8) Choncho m’malo momupewa n’kumaona kuti n’zosatheka kugwirizana naye, ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zimene m’bale wangayu amachita ndi zosemphanadi ndi Malemba? Kodi iye amachitira dala zinthuzi kuti tiyambane? Kapena kodi timangosiyana zochita?’ Koma funso lofunika kwambiri limene tingadzifunse n’lakuti: ‘Kodi ali ndi makhalidwe abwino ati amene ndikhoza kutengera?’

Funso lomalizali ndi lofunika kwambiri. Ngati munthuyo amakonda kulankhula pamene inu mumakonda kungokhala phee, mwina mukhoza kuphunzira kwa iye mmene amayambira kulankhula ndi anthu mu utumiki. Mungamupemphe kuti mulowe naye mu utumiki kuti muone makhalidwe ake abwino amene mungatengere. Kapena ngati munthuyo ali ndi mtima wopatsa, pomwe inu zimakuvutani, mukhoza kuona mmene amakhalira wosangalala chifukwa chothandiza anthu okalamba, odwala kapena osauka. Mfundo yaikulu ndi yakuti ngakhale kuti ndinu osiyana, mukamaganizira makhalidwe abwino a m’bale kapena mlongo wanuyo, mukhoza kumagwirizana naye. Mwina sizingatheke kuti akhale mnzanu wa ponda apa m’pondepo koma kutsatira malangizowa kungakuthandizeni kuti muzigwirizana, mukhale ndi mtendere wamumtima komanso kuti mumpingo musakhale chisokonezo.

N’kutheka kuti Eodiya ndi Suntuke anali anthu osiyana kwambiri. Koma mtumwi Paulo anawalimbikitsa kuti “akhale amaganizo amodzi mwa Ambuye.” (Afil. 4:2) Inunso mungachite bwino kutsatira malangizowa kuti muzikhala mwamtendere ndi anthu ena.

TIZITHETSA MSANGA KUSAMVANA

Mofanana ndi udzu umene umamera m’dimba, maganizo olakwika okhudza anthu ena akhoza kukula tikapanda kuwachotsa. Munthu akalola kuti maganizowo akule mumtima mwake, zingasokonezenso mgwirizano wa mpingo. Ngati timakonda Yehova komanso abale athu, tidzachita zonse zimene tingathe kuti tizipewa kusemphana maganizo ndi abale athu komanso kusokoneza mtendere mumpingo.

Mukamakhala odzichepetsa ndiponso kuyesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu ena zotsatira zingakhale zabwino kwambiri

Tikamayesetsa kuthetsa kusamvana n’cholinga choti tikhazikitse mtendere, zotsatira zake zingakhale zabwino kwambiri. Mwachitsanzo, mlongo wina anati: “Ndinkaona kuti mlongo winawake ankanditenga ngati mwana. Zimenezi zinkandikhumudwitsa kwambiri. Kenako ndinasiya kumupatsa ulemu. Ndinkaona kuti ngati sakundipatsa ulemu nanenso ndingosiya kumupatsa ulemu.”

Ndiyeno mlongoyu anayamba kuganizira zimene ankachitazi. Iye anati: “Ndinazindikira zinthu zimene ndimalakwitsa ndipo ndinakhumudwa kwambiri. Ndinaonanso kuti ndiyenera kusintha mmene ndimaonera zinthu. Nditaipempherera nkhaniyi, ndinaganiza zogulira mlongo uja kamphatso komanso ndinamulembera kalata yopepesa. Tinakumbatirana ndipo tinagwirizana kuti tingoiwala nkhaniyo. Kuchokera nthawi imeneyo takhala tikugwirizana.”

Anthu amalakalaka kukhala mwamtendere. Koma akaona kuti anthu ena sakuwalemekeza kapena kulemekeza udindo wawo, amayamba kuchita zinthu zosokoneza mtendere. Izi n’zimene anthu a m’dzikoli amachita koma anthu a Yehova ayenera kuyesetsa kuti azikhala mwamtendere. Paulo analemba kuti: “Ndikukuchondererani kuti muziyenda moyenera kuitana kumene munaitanidwa nako. Muziyenda modzichepetsa nthawi zonse, mofatsa, moleza mtima, ndiponso mololerana m’chikondi. Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa.” (Aef. 4:1-3) Mgwirizano ndiponso mtendere umenewu ndi wamtengo wapatali kwambiri. Choncho tiyeni tiziyesetsa kukhala mwamtendere ndiponso kuthetsa kusamvana kulikonse kumene kungachitike.