Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudzakambilana Kuti Muthetse Mkangano ndi Kulimbikitsa Mtendele?

Kodi Mudzakambilana Kuti Muthetse Mkangano ndi Kulimbikitsa Mtendele?

YEHOVA MULUNGU amalimbikitsa Akhristu kukhala amtendele. Iye amafuna kuti mtendele ukhale mbali ya umoyo wawo. Tikakhala amtendele, ndiye kuti pakati pa olambila oona padzakhalanso mtendele woculuka. Izi zidzacititsa anthu amene amafuna kukhala amtendele kubwela mumpingo wacikhristu.

Mwacitsanzo, ng’anga ina yochuka ku Madagascar, inaona kuti Mboni za Yehova ndi zamtendele. Mumtima mwake iye anati, ‘Ngati ningafune kuloŵa cipembedzo, ningayambe ku Mboni.’ Patapita nthawi analeka kucita zamizimu. Pambuyo pa miyezi ingapo, anakonza cikwati cake kuti cikhale cogwilizana ndi Malemba, ndipo anakhala wolambila Yehova, Mulungu wamtendele.

Mofanana ndi munthu ameneyu, caka ciliconse anthu masauzande ambili amabwela mumpingo wacikhristu, ndipo amapeza mtendele umene anali kusoŵa. Komabe, Baibo imafotokoza mosapita m’mbali kuti “nsanje yaikulu ndi kukonda mikangano,” zingawononge ubwenzi wathu na ena ndi kuyambitsa mavuto mumpingo. (Yak. 3:14-16) Koma n’zokondweletsa n’zakuti Baibo imatipatsa malangizo a mmene tingapewele mavuto amenewa ndi kulimbikitsa mtendele mumpingo. Kuti tidziŵe mmene tingacitile zimenezi, tiyeni tikambilane zitsanzo zina zimene zinacitikadi.

MAVUTO NA MMENE TINGAWATHETSELE

“Ine n’nali na vuto lokonda kukangana ndi m’bale amene nimaseŵenza naye. Tsiku lina pamene tinali kukangana, anthu aŵili anabwela kuti amvele zimene tinali kukangana.”—CHRIS.

“Mlongo wina amene kaŵili-kaŵili n’nali kugwila naye nchito yolalikila, mwadzidzidzi analeka kulalikila na ine. Analekanso kunikambitsa. Ine sin’nadziŵe cifukwa cimene anacitila zimenezo.”—JANET.

“Tsiku lina n’nalumikizana ndi anzanga aŵili n’kumaceza pafoni. Mmodzi wa iwo anakamba kuti bayi, kuonetsa kuti walaila. Ndipo ine n’naganiza kuti wadula foni. Conco, n’nayamba kukamba mau oipa okhudza mnzangayo, osadziŵa kuti iye sanadule foniyo.”—MICHAEL.

“Mumpingo mwathu, apaniya aŵili anayamba kukangana. Wina anali kukonda kukalipila mnzake. Kukangana kwawo kunali kukhumudwitsa ena mumpingo.”—GARY.

Mwina mungaganize kuti nkhani zimenezi n’zazing’ono. Ngakhale n’conco, ciliconse mwa zocitika zimenezi cikanayambitsa cidani ndi kusokoneza ubwenzi wawo na Mulungu. Komabe, mudzakondwela kudziŵa kuti nkhani zimenezi zinathetsedwa mwamtendele pakati pa abale na alongo amenewa. Iwo anagwilitsila nchito malangizo a m’Baibo. Kodi muganiza kuti anaseŵenzetsa malangizo ati a m’Baibo?

“Musakanganetu m’njila.” (Gen. 45:24) Aya ni malangizo amene Yosefe anapatsa abale ake pamene anali kubwelela kwa atate wawo. Malangizo amenewa anawathandiza kwambili. Ngati munthu amakwiya msanga, akhoza kukhumudwitsa ena. Chris anazindikila kuti anali na vuto la kunyada ndi kusafuna kuuzidwa zocita. Iye anaona kuti afunika kusintha khalidwe lake. Conco, anapepesa m’bale amene anali kukangana naye, ndipo anayesetsa kulamulila mkwiyo wake. Mnzakeyo ataona kuti Chris akuyesetsa kusintha khalidwe lake, nayenso anayamba kusintha. Lomba onse akusangalala kutumikila Yehova mogwilizana.

“Zolingalila sizikwanilitsidwa ngati anthu sakambilana moona mtima.” (Miy. 15:22) Janet anaona kuti afunika kugwilitsila nchito uphungu umenewu. Iye anaganiza kuti akakambilane ndi mlongo amene anamukwiyila. Pamene anali kukambilana, Janet mosamala anapempha mlongoyo kuti amasuke na kufotokoza cimene cinam’khumudwitsa. Poyamba zinali zovuta kuti iwo akambilane mwamtendele, koma zinthu zinasintha atayamba kukambilana nkhaniyo modekha. M’kukambilana kwawo, mlongoyo anazindikila kuti nkhani imene inam’khumudwitsa sanaimvetsetse, ndiponso siinali kukhudza Janet. Iye anam’pepesa Janet, ndipo lomba iwo atumikila Yehova mogwilizana.

“Conco ngati wabweletsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukila kuti m’bale wako ali nawe cifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako coyamba.” (Mat. 5:23, 24) Mwina mwakumbukila malangizo amenewa, amene Yesu anapeleka pa Ulaliki wake wa Paphili. Michael anadzimvela cisoni atazindikila kuti wakamba zinthu mosaganizila mnzake ndi mopanda cikondi. Iye anayesetsa kuti akhazikitse mtendele. Modzicepetsa anapita kukapepesa kwa m’bale amene anam’khumudwitsa. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Michael anati: “M’baleyo ananikhululukila ndi mtima wonse.” Mwa ici, ubwenzi wawo unakhalanso wolimba.

“Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake.” (Akol. 3:12-14) Pankhani ya apainiya aŵili amene atumikila kwa nthawi yaitali, mkulu wokoma mtima anawathandiza kuganizila mafunso aya: ‘Kodi m’poyenela kuti ise aŵili tizikhumudwitsa ena cifukwa ca kukangana kwathu? Kodi pali cifukwa colekela kukhululukilana ndi kupitiliza kutumikila Yehova mwamtendele?’ Iwo analandila uphungu wa mkuluyo na kuuseŵenzetsa. Tsopano amalalikila uthenga wabwino pamodzi mwamtendele.

Ngati wina wakukhumudwitsani, mungacite bwino coyamba kutsatila malangizo a m’Baibo a pa Akolose 3:12-14 . Ambili aona kuti kudzicepetsa kumawathandiza kukhululukila ena ndi kuiŵalako zimene awalakwila. Ngati izi sizinathandize, mwina mungafunike kutsatila malangizo a pa Mateyu 18:15. Palembali, Yesu anali kukamba zimene munthu afunika kucita ngati wina wamucitila colakwa cacikulu. Komabe, mfundo ya palembali mukhozanso kuiseŵenzetsa ngati mwasiyana maganizo na munthu wina. Mungapite kwa m’bale kapena mlongo wanu ndi kukambilana naye mokoma mtima ndi modzicepetsa kuti muthetse nkhaniyo.

M’Baibo mulinso malangizo ena othandiza. Koma kuti malangizowa akuthandizeni, inu mufunika kuonetsa “makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa . . . cikondi, cimwemwe, mtendele, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, cikhulupililo, kufatsa ndi kudziletsa.” (Agal. 5:22, 23) Monga mmene oilo imathandizila mashini kuseŵenza bwino, makhalidwe aumulungu amenewa amathandiza pokhazikitsa mtendele.

KUSIYANA KWA ZIBADWA KUMAKOMETSELA MPINGO

Ise anthu tili na zibadwa zosiyana-siyana. Zimenezi zimakometsa ubwenzi. Komabe, kusiyana zibadwa kungayambitse mikangano. Mwacitsanzo, mkulu wina amene watumikila paudindo kwa nthawi itali anati: “Munthu wamanyazi angamangike akakhala na munthu wansangala. Kusiyana kumeneku kungaoneke ngati nkhani yaing’ono, koma kungabweletse mavuto aakulu.” Koma kodi muganiza kuti anthu amene ni osiyana kwambili zibadwa sangacitile zinthu pamodzi mwamtendele? Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambilane za atumwi aŵili. Kodi Petulo anali munthu wotani? Mwina mungaganize kuti anali wokamba-kamba ndi wopupuluma. Nanga Yohane anali wotani? Mwinanso mungaganize kuti anali wacikondi, wodekha pokamba ndi pocita zinthu. Mwacionekele, pali zifukwa zimene mumawaonela conco atumwi amenewa. Zioneka kuti iwo analidi na zibadwa zosiyana. Ngakhale zinali conco, iwo anali kutumikila pamodzi mwamtendele. (Mac. 8:14; Agal. 2:9) Cotelo, n’zotheka Akhristu amene ni osiyana zibadwa kutumikila pamodzi masiku ano.

Mwina mumpingo mwanu muli m’bale amene kakambidwe kake na zocita zake zimakukhumudwitsani. Koma muyenela kukumbukila kuti Khristu anamufela munthuyo, ndipo inu mufunika kumukonda. (Yoh. 13:34, 35; Aroma 5:6-8) Conco, m’malo mothetsa ubwenzi kapena kumupewa, dzifunseni kuti: ‘Kodi zimene m’bale wanga amacita n’zosemphanadi ndi Malemba? Kodi iye amacitila dala kuti anikhumudwitse? Kapena tili cabe na zibadwa zosiyana?’ Funso lina lofunika kwambili n’lakuti: ‘Kodi m’baleyu ali na makhalidwe ati abwino amene ningatengeleko?’

Funso lotsilizali n’lothandiza ngako. Ngati munthuyo ni wokamba-kamba, ndipo imwe ndimwe wa zii, ganizilani mmene zimakhalila zosavuta kwa iye kuyambitsa makambilano muulaliki. Mungayende naye muulaliki ndi kuona zimene mungaphunzile kwa iye. Ngati ni woceleza, koma inu muona kuti muliko na vuto pa mbaliyi, ganizilani cimwemwe cimene iye amakhala naco kaamba kothandiza okalamba, odwala, na osauka. Apa mfundo ni yakuti, ngakhale kuti inu na m’bale muli na zibadwa zosiyana, n’zotheka ndithu kukhala ogwilizana ngati muyang’ana zabwino mwa iye. Si nthawi zonse pamene kucita zimenezi kungakupangitseni kukhala mabwenzi apamtima. Koma kungakuthandizeni kukhala ogwilizana ndi m’bale kapena mlongoyo. Komanso kungalimbikitse mtendele pakati panu ndi mumpingo.

Eodiya ndi Suntuke ayenela kuti anali osiyana zibadwa, kapena anali osiyana m’njila zina. Koma mtumwi Paulo anawalimbikitsa kuti “akhale amaganizo amodzi mwa Ambuye.” (Afil. 4:2) Kodi inunso mudzayesetsa kucita zimenezi kuti mulimbikitse mtendele?

MUSALOLE KUTI MKANGANO UPITILILE

Monga mmene udzu umakulila m’munda, mkwiyo ungakule mumtima ngati sitiyesetsa kuucotsa. Ngati mkwiyo wakula mphamvu ndipo munthu alephela kuulamulila, ukhoza kusokoneza mtendele wa mpingo. Ngati timakonda Yehova ndi abale athu, tidzacita zonse zimene tingathe kuti kusiyana zibadwa kusasokoneze mtendele pakati pa anthu a Mulungu.

Ngati mukhala odzicepetsa ndi kuyesetsa kukhazikitsa mtendele, mudzadalitsidwa ngako

Ngati tiyesetsa kuthetsa mikangano n’colinga cofuna kukhazikitsa mtendele, tidzapeza mapindu oculuka. Ganizilani zimene zinacitikila mlongo wina. Iye anati: “N’nali kuona kuti mlongo wina anali kucita nane zinthu ngati kamwana. Izi zinali kunikhumudwitsa kwambili. Mkwiyo utakula, n’nayamba kum’citila zinthu mwamwano. Mumtima n’nati: ‘Iye sanipatsa ulemu, na ine n’dzaleka kum’patsa ulemu.’”

Ndiyeno, mlongoyu anayamba kuganizila za khalidwe lake. Iye anati: “N’nazindikila kuti zimene n’nali kucita si zabwino, ndipo n’nayamba kudziimba mlandu. N’naona kuti nifunika kusintha. N’tapemphela kwa Yehova za nkhaniyi, n’nagulila mlongoyo kamphatso, kumulembela kakalata, na kupita kukam’pepesa. Tinakumbatilana ndi kugwilizana zoiŵalako nkhaniyo. Apa lomba, ndise ogwilizana.”

Anthu amafunitsitsa mtendele. Koma akaona kuti ena sakuwalemekeza, ambili amayamba kucita zinthu zosokoneza mtendele. Izi n’zimene anthu ambili osalambila Yehova amacita. Koma olambila Yehova ayenela kucita zonse zotheka kuti pakati pawo pakhalebe mtendele ndi mgwilizano. Paulo anauzilidwa kulemba kuti: “Ine, . . . ndikukucondelelani kuti muziyenda moyenela kuitana kumene munaitanidwa nako. Muziyenda modzicepetsa nthawi zonse, mofatsa, moleza mtima, ndiponso mololelana m’cikondi. Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo, ndi mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa.” (Aef. 4:1-3) Mtendele umene uli “monga comangila cotigwilizanitsa,” ndi wamtengo wapatali. Conco, tiyeni tizilimbikitsa mtendele mwa kuyesetsa kuthetsa mikangano imene ingabuke pakati pathu.