Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Udalitsike Cifukwa ca Kulingalila Bwino Kwako”

“Udalitsike Cifukwa ca Kulingalila Bwino Kwako”

DAVIDE wa ku Isiraeli wakale ndi amene anakamba mau amenewa poyamikila mkazi amene anakumana naye. Mkaziyo anali Abigayeli. N’ciani cinacititsa Davide kuyamikila mkaziyu? Nanga citsanzo ca mkazi ameneyu citiphunzitsa ciani?

Davide anakumana ndi mkazi ameneyu panthawi imene anali kuthaŵa Mfumu Sauli. Abigayeli anali mkazi wa Nabala, munthu wolemela amene anali na nkhosa zambili. Nkhosazo anali kuziŵetela m’dela la mapili, kum’mwela kwa Yuda. Davide ndi anyamata ake anali “ngati khoma” kwa abusa a Nabala ndi nkhosa zake. Patapita nthawi, Davide anatumiza anyamata ake kwa Nabala kuti akapempheko cakudya ‘ciliconse cimene dzanja lake [la Nabala] linapeza.’ (1 Sam. 25:8, 15, 16) Panali pomveka Davide kupempha thandizo kwa Nabala cifukwa iye ndi anyamata ake anateteza cuma ca Nabalayo.

Koma Nabala, amene dzina lake limatanthauza “Wopanda nzelu,” kapena “Wopusa,” anacita zinthu mogwilizana ndi dzina lake. Iye anakana kuthandiza Davide, ndipo anayankha anyamatawo mwamwano ndi monyoza. Conco Davide anakonzekela kuti akalange Nabala cifukwa comuyankha mwamwano ndi kucita zinthu mosam’ganizila. Nabala ndi onse a m’nyumba yake anali kudzalangidwa cifukwa ca kupanda nzelu kwake.—1 Sam. 25:2-13, 21, 22.

Pozindikila mavuto amene adzatsatilapo cifukwa ca zocita za mwamuna wake, molimba mtima Abigayeli anacitapo kanthu mwamsanga. Iye mwaulemu anacondelela Davide kuti asabwezele coipa ndi kuwononga ubwenzi wake na Yehova. Conco anatenga cakudya coculuka n’kupatsa Davide ndi anyamata ake. Davideyo ndiye anali kudzakhala mfumu yotsatila ya Isiraeli. Davide anazindikila kuti Yehova anaseŵenzetsa mkaziyo, pofuna kum’teteza kuti asacite zinthu zimene zikanam’pangitsa kukhala na mlandu wamagazi pamaso pa Mulungu. Davide anauza Abigayeli kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene wakutumiza kudzakumana nane lelo! Iwenso udalitsike cifukwa ca kulingalila bwino kwako. Udalitsike cifukwa ca kundigwila lelo kuti ndisapalamule mlandu wamagazi ndi kudzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.”—1 Sam. 25:18, 19, 23-35.

N’zoonekelatu kuti sitingafune kukhala na mtima ngati wa Nabala, amene sanayamikile zabwino zimene anacitilidwa. Kuwonjezela apo, ngati taona kuti pali cinacake coipa cimene cingacitike, tiyenela kucitapo kanthu mmene tingathele kuti cisacitike. Inde, mofanana ndi wamasalimo, naise tingapemphe Mulungu kuti: “Ndiphunzitseni kucita zabwino, kulingalila bwino ndi kudziŵa zinthu.”—Sal. 119:66.

Zocita zathu zidzathandiza anthu ena kuzindikila kuti ndise anzelu ndi oganiza bwino. Kaya acite kukamba zimenezi kapena ayi, iwo angamvele ngati Davide amene anati: “Udalitsike cifukwa ca kulingalila bwino kwako.”