Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Mulungu Akwaniritse Zofuna Zanu’

‘Mulungu Akwaniritse Zofuna Zanu’

“Sangalala mwa Yehova, ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.”​—SAL. 37:4.

NYIMBO: 89, 140

1. Kodi achinyamata amayenera kusankha chiyani, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi siziyenera kuwachititsa mantha? (Onani chithunzi choyambirira.)

ACHINYAMATA akhoza kuvomereza kuti munthu asanayambe ulendo amafunika kudziwiratu kumene akupita. Moyo wathuwu uli ngati ulendo ndipo ndi bwino kuti munthu azidziwiratu zimene adzachite pa moyo wake adakali wachinyamata. N’zoona kuti kusankha zochita pa moyo n’kovuta. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Heather anati: “Zimandiopsa ndikaganizira zoti ndiyenera kusankha zimene ndingadzachite kwa moyo wanga wonse.” Ngati nanunso mumaona choncho, musataye mtima. Paja Yehova analonjeza anthu ake kuti: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”​—Yes. 41:10.

2. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizisankha zinthu zimene zingatithandize kukhala ndi tsogolo labwino?

2 Yehova amatilimbikitsa kuti tizisankha zinthu mwanzeru. (Mlal. 12:1; Mat. 6:20) Iye amafuna kuti tizikhala osangalala. Umboni wa zimenezi ndi zinthu zosangalatsa zimene timadya, kumva kapena kuona m’chilengedwechi. Yehova amatisamaliranso ndipo amatiphunzitsa zimene tingachite kuti tikhale osangalala. Anthu amene amakana malangizo ake, iye amawauza kuti: “Munasankha zinthu zimene sindisangalala nazo. . . . Atumiki anga adzasangalala, koma inuyo mudzachita manyazi. Atumiki anga adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.” (Yes. 65:12-14) Yehova amalemekezeka anthu ake akamasankha zochita mwanzeru.​—Miy. 27:11.

ZOLINGA ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI KUKHALA NDI TSOGOLO LABWINO

3. Kodi Yehova amafuna kuti zolinga zathu zizikhala zotani?

3 Kodi Yehova amafuna kuti zolinga zanu zikhale zotani? Iye analenga anthu m’njira yoti azisangalala akamamudziwa bwino komanso kumutumikira mokhulupirika. (Sal. 128:1; Mat. 5:3) Anthufe ndi osiyana kwambiri ndi nyama. Tikutero chifukwa chakuti pa moyo wa nyama, chofunika ndi kudya, kumwa ndi kuswana basi. Koma Mulungu amafuna kuti anthufe tizikhala ndi zolinga zinanso zomwe zingatithandize kukhala osangalala. Mlengi wathu ndi “Mulungu wachikondi” komanso “Mulungu wachimwemwe” ndipo anatilenga “m’chifaniziro chake.” (2 Akor. 13:11; 1 Tim. 1:11; Gen. 1:27) Tikamatsanzira Mulungu wathu wachikondi timasangalala. Paja Baibulo limati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Mfundo imeneyi ndi yoona ndipo mwina inuyo mwatsimikizapo zimenezi. Choncho Yehova amafuna kuti zolinga zathu zizisonyeza kuti timakonda Mulungu komanso anthu ena.​—Werengani Mateyu 22:36-39.

4, 5. N’chiyani chinkathandiza Yesu kuti azisangalala?

4 Yesu Khristu anapereka chitsanzo chabwino kwa achinyamata. N’zosachita kufunsa kuti ali mwana ankasewera ndiponso kusangalala. Paja Mawu a Mulungu amanena kuti pali “nthawi yoseka” ndi “nthawi yodumphadumpha mosangalala.” (Mlal. 3:4) Koma Yesu ankakondanso kuphunzira Malemba n’cholinga choti alimbitse ubwenzi wake ndi Yehova. Iye ali ndi zaka 12 zokha, aphunzitsi akukachisi anadabwa kwambiri ndi ‘mayankho ake komanso poona kuti ankamvetsa kwambiri zinthu’ zokhudza Yehova.​—Luka 2:42, 46, 47.

5 Yesu atakula ankakhalanso wosangalala chifukwa chakuti ankakonda kuchita zimene Mulungu amafuna. Mwachitsanzo, Mulungu ankafuna kuti iye azilengeza ‘uthenga wabwino kwa osauka komanso kuthandiza akhungu kuti ayambe kuona.’ (Luka 4:18) Lemba la Salimo 40:8 limafotokoza mmene Yesu ankamvera akamachita zimene Mulungu amafuna. Limanena kuti: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.” Yesu ankakonda kwambiri kuphunzitsa anthu zokhudza Atate wake wakumwamba. (Werengani Luka 10:21.) Iye ataphunzitsa mayi wina anauza ophunzira ake kuti: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yoh. 4:31-34) Yesu ankasonyeza kuti amakonda Mulungu komanso anthu ndipo izi zinkachititsa kuti azisangalala. Inunso mukhoza kukhala osangalala mukamachita zimenezi.

6. Kodi kukambirana zolinga zanu ndi Akhristu ena kungakuthandizeni bwanji?

6 Pali Akhristu ambiri amene anayamba upainiya ali achinyamata ndipo zimenezi zinawathandiza kuti akhale osangalala. Choncho ndi bwino kukambirana nawo zolinga zanu. Malemba amati: “Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima, koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.” (Miy. 15:22) Anthu amene achita utumiki wa nthawi zonse akhoza kukuuzani kuti utumikiwo unawaphunzitsa zinthu zimene zidzawathandize kwa moyo wawo wonse. Yesu anaphunzitsidwa ndi Atate wake kumwamba koma atabwera padzikoli anapitiriza kuphunzira zinthu. Mwachitsanzo, iye anaona kuti zimasangalatsa kwambiri ukamufika munthu pamtima ndi uthenga wabwino komanso ukamakhalabe wokhulupirika pokumana ndi mavuto. (Werengani Yesaya 50:4; Aheb. 5:8; 12:2) Tiyeni tsopano tikambirane za utumiki umene ungakuthandizeni kukhala osangalala.

NTCHITO YOPHUNZITSA ANTHU IMATITHANDIZA KUKHALA OSANGALALA

7. N’chifukwa chiyani achinyamata ambiri amakonda ntchito yophunzitsa anthu?

7 Yesu ananena kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga.” (Mat. 28:19, 20) Mukasankha kugwira ntchito yophunzitsa anthu ndiye kuti mwasankha ntchito yosangalatsa ndipo mudzalemekeza kwambiri Mulungu. Koma mofanana ndi ntchito zina zonse, pamafunika nthawi kuti mukhale ndi luso. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Timothy. M’baleyu anayamba upainiya ali wachinyamata ndipo anati: “Ndimakonda kwambiri utumiki wa nthawi zonse chifukwa chakuti ndi njira imene ndingasonyezere kuti ndimakonda Yehova. Poyamba, ndinalibe phunziro lililonse koma nditasamukira kudera lina ndinakhala ndi maphunziro angapo mwezi usanathe. Munthu wina amene ndinkamuphunzitsa anayamba kufika ku Nyumba ya Ufumu. Nditapita ku Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira * ananditumizanso kudera lina ndipo ndinayambitsa maphunziro 4. Ndimakonda kwambiri kuphunzitsa anthu chifukwa choti ndimatha kuona mzimu woyera ukuwathandiza kusintha.”​—1 Ates. 2:19.

8. Kodi achinyamata ena achita zotani kuti aphunzitse anthu ambiri?

8 Achinyamata ena amayesetsa kuphunzira chinenero china. Mwachitsanzo, m’bale wina wa ku North America dzina lake Jacob anati: “Ndili ndi zaka 7 ndinazindikira kuti anthu ambiri m’kalasi mwanga anali ochokera ku Vietnam. Ndinkafunitsitsa kuwaphunzitsa za Yehova choncho ndinayamba kuphunzira chilankhulo chawo. Kuti ndiphunzire, nthawi zambiri ndinkangotenga Nsanja ya Olonda yachingelezi ndi yachilankhulo chawo n’kumayerekezera. Ndinapezanso anzanga mumpingo wachilankhulocho wapafupi ndi kwathu. Nditakwanitsa zaka 18 ndinayamba upainiya. Kenako ndinapita ku Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira. Zimene ndinaphunzira kusukuluyi zikundithandiza kwambiri pamene ndikutumikira kukagulu kachivetinamu. Ndikuchita upainiya kukagulu kameneka ndipo mkulu ndiliko ndekha. Anthu ambiri a ku Vietnam amadabwa kuona kuti ndinaphunzira chilankhulo chawo. Iwo amandipempha kuti ndilowe m’nyumba zawo ndipo ambiri amavomera kuphunzira Baibulo. Ena mpaka afika pobatizidwa.”​—Yerekezerani ndi Machitidwe 2:7, 8.

9. Kodi timaphunzira chiyani tikamagwira ntchito yophunzitsa anthu Baibulo?

9 Ntchito yophunzitsa anthu Baibulo imatithandiza kuti tikhale akhama, tisamadzikayikire komanso tizitha kulankhula bwinobwino ndi anthu popanda kuwakhumudwitsa. (Miy. 21:5; 2 Tim. 2:24) Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti ntchitoyi imatithandizanso kudziwa bwino Malemba amene amatsimikizira kuti mfundo zimene timakhulupirira ndi zoona. Timaphunziranso kugwira ntchito limodzi ndi Yehova.​—1 Akor. 3:9.

10. N’chifukwa chiyani simuyenera kudandaula ngakhale kuti mumalalikira m’gawo lovuta?

10 Ntchito yolalikira imasangalatsabe ngakhale m’gawo limene anthu ambiri sakonda kumvetsera. Paja ntchitoyi ndi ya mpingo wonse osati munthu aliyense payekha. Ngakhale kuti m’bale kapena mlongo mmodzi ndi amene amapeza munthu yemwe amayamba kusonkhana, zoona zake n’zakuti mpingo wonse unkafufuza, choncho aliyense amasangalala. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Brandon amene analalikira m’gawo lovuta kwa zaka 9. Iye anati: “Ndimakonda kwambiri kulalikira uthenga wabwino chifukwa chakuti n’zimene Yehova amafuna kuti tizichita. Ndinayamba upainiya nditangomaliza sukulu. Ndimakonda kwambiri kulimbikitsa achinyamata mumpingo wathu ndipo ndimasangalala ndikaona kuti ayamba kuchita zambiri m’gulu. Nditalowa Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira, ananditumiza kugawo lina. Chifikireni kugawoli sindinakhalepo ndi mwayi wothandiza munthu kufika pobatizidwa koma ena akwanitsa kuchita zimenezi. Ndimasangalala kwambiri kuti ndinasankhiratu kuti ndizichita zambiri pa ntchito yolalikira.”​—Mlal. 11:6.

ZOLINGA ZABWINO ZINGAKUTHANDIZENI KUCHITANSO ZINTHU ZINA ZAMBIRI

11. Kodi achinyamata ambiri achita utumiki wotani?

11 Pali zinthu zambiri zimene mungachite potumikira Yehova. Mwachitsanzo, achinyamata ambiri amadzipereka kuti azithandiza pa ntchito zomangamanga. Panopa pakufunika Nyumba za Ufumu zambirimbiri. Munthu akamathandiza pomanga nyumbazi amakhala akuchita utumiki wopatulika umene umalemekeza Mulungu komanso umamuthandiza kukhala wosangalala. Mofanana ndi utumiki wina uliwonse, kugwira ntchito limodzi ndi Akhristu ena kumasangalatsa. Mukamagwira ntchitoyi mumaphunziranso zambiri. Mwachitsanzo, mumaphunzira kupewa ngozi, kugwira ntchito mwakhama komanso kugwirizana ndi anthu amene akuyang’anira ntchitoyo.

Anthu amene amachita utumiki wa nthawi zonse amadalitsidwa kwambiri (Onani ndime 11-13)

12. Kodi kuchita upainiya kungakuthandizeni bwanji kuchitanso zinthu zina?

12 M’bale wina dzina lake Kevin anati: “Kuyambira ndili wamng’ono ndakhala ndikufuna kuchita utumiki wa nthawi zonse. Ndinayamba upainiya ndili ndi zaka 19. Ndinkapeza zofunika pa moyo wanga pogwira ntchito ndi m’bale wina amene ankamanga nyumba. Ndinaphunzira kukhoma malata komanso kuika mawindo ndi zitseko. Kenako kwa zaka ziwiri ndinakagwira ntchito ndi gulu lothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi mphepo yamkuntho. Tinkamanganso Nyumba za Ufumu ndiponso nyumba za abale. Koma nditamva kuti ku South Africa kukufunika anthu ambiri ogwira ntchito zomangamanga, ndinafunsira utumikiwu ndipo anandiitana. Ku Africa kuno, ndimathandiza pomanga Nyumba ya Ufumu imodzi kwa milungu ingapo ndipo kenako ndimapita kukathandiza kumanga Nyumba ya Ufumu ina. Panopa anthu amene timagwira ntchito yomangayi timangokhala ngati anthu a m’banja limodzi. Zili choncho chifukwa timakhala limodzi, kuphunzira Baibulo limodzi komanso kugwira ntchito limodzi. Ndimasangalalanso polalikira ndi abale amumpingo mlungu uliwonse. Zolinga zimene ndinasankha ndili mnyamata zandithandiza kukhala wosangalala kwambiri kuposa mmene ndinkaganizira.”

13. Kodi kutumikira pa Beteli kumathandiza bwanji achinyamata kuti azisangalala?

13 Anthu ena amene anali ndi zolinga zoti azichita utumiki wa nthawi zonse, panopa akutumikira ku Beteli. Kutumikira ku Beteli kumasangalatsa kwambiri chifukwa zonse zimene mumachita mumachitira Yehova. Anthu ogwira ntchito pa Beteli amathandiza popereka chakudya chauzimu. M’bale wina amene amatumikira ku Beteli dzina lake Dustin ananena kuti: “Ndili ndi zaka 9 ndinali ndi cholinga choti ndidzachite utumiki wa nthawi zonse. Choncho nditangomaliza sukulu, ndinayamba upainiya. Nditachita upainiyawo kwa chaka chimodzi ndi hafu, ndinaitanidwa ku Beteli. Ndinaphunzira kugwiritsa ntchito mashini osindikizira mabuku ndipo kenako kulemba mapulogalamu apakompyuta. Ku Beteli kuno ndimasangalalanso kumva mwamsanga malipoti a mmene ntchito yolalikira ikuyendera padziko lonse. Ndimakonda kwambiri kutumikira kuno chifukwa chakuti zimene timachita zimathandiza anthu kuti azilimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova.”

KODI INUYO MUKUFUNA KUTI MUDZACHITE CHIYANI M’TSOGOLO?

14. Kodi inuyo mungakonzekere bwanji kuti mudzachite utumiki wa nthawi zonse?

14 Kodi inuyo mungakonzekere bwanji kuti mudzachite utumiki wa nthawi zonse? Chofunika kwambiri ndi kukhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Yehova. Choncho muyenera kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama, kusinkhasinkha tanthauzo lake komanso kufotokoza zimene mumakhulupirira pa misonkhano. Pa nthawi imene muli pa sukulu mukhoza kuphunzira njira zolalikirira mwaluso. Muziyesetsa kuchita chidwi ndi anthu powafunsa maganizo awo komanso kuwamvetsera akamayankha. Muzidziperekanso kugwira nawo ntchito zina mumpingo monga kuyeretsa ndi kukonza zinthu pa Nyumba ya Ufumu. Yehova amagwiritsa ntchito anthu odzichepetsa komanso odzipereka. (Werengani Salimo 110:3; Mac. 6:1-3) Kumbukirani kuti mtumwi Paulo anatenga Timoteyo kuti azichita naye umishonale chifukwa choti abale “anamuchitira umboni wabwino.”​—Mac. 16:1-5.

15. Kodi mungakonzekere bwanji kuti muzipeza zofunika pa moyo?

15 Atumiki a nthawi zonse ambiri amafunikanso kupeza zofunika pa moyo wawo. (Mac. 18:2, 3) Choncho kupanga kosi inayake ya nthawi yochepa kungakuthandizeni kuti muzipeza timaganyu. Mukamakonzekera utumikiwo ndi bwino kukambirana ndi woyang’anira dera komanso apainiya a m’dera lanu. Muziwafunsa ntchito imene ingakuthandizeni kuti muzipeza kangachepe uku mukuchita upainiya. Kenako mungatsatire mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Pereka ntchito zako kwa Yehova, ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.”​—Miy. 16:3; 20:18.

16. Kodi kutumikira Yehova mwakhama muli wachinyamata kungadzakuthandizeni bwanji m’tsogolo?

16 Dziwani kuti Yehova amafuna kuti ‘mugwire mwamphamvu’ tsogolo labwino. (Werengani 1 Timoteyo 6:18, 19.) Mukamachita utumiki, mumagwira ntchito ndi atumiki a nthawi zonse ena ndipo izi zimakuthandizani kuti mukhale Mkhristu wolimba mwauzimu. Ambiri azindikira kuti kutumikira Yehova mwakhama ali achinyamata kwawathandiza kukhala ndi mabanja abwino. Ndipo anthu ambiri amene amachita upainiya asanalowe m’banja amadzapitiriza utumikiwu limodzi ndi mwamuna kapena mkazi wawo.​—Aroma 16:3, 4.

17, 18. Popeza zolinga za munthu zimayambira mumtima, kodi muyenera kuchita chiyani?

17 Lemba la Salimo 20:4 limanena kuti Yehova “akupatseni zokhumba za mtima wanu, ndipo akwaniritse zofuna zanu.” Zolinga za munthu zimayambira mumtima. Choncho muyenera kuganizira kwambiri zimene mudzachite pa moyo wanu. Muziganizira zimene Yehova akuchita masiku ano komanso mmene mungathandizire pa ntchito yake. Ndiyeno muzikhala ndi zolinga zimene zingamusangalatse.

18 Mukamatumikira Yehova mwakhama mudzamulemekeza kwambiri ndipo mudzakhala wosangalala. Choncho yesetsani kuti mukhale ‘osangalala mwa Yehova, ndipo iye adzakupatsani zokhumba za mtima wanu.’​—Sal. 37:4.

^ ndime 7 Panopa sukuluyi inalowedwa m’malo ndi Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu.