Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mulungu “Akwanilitse Zofuna Zanu”

Mulungu “Akwanilitse Zofuna Zanu”

“Sangalala mwa Yehova, ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.”—SAL. 37:4.

NYIMBO: 89, 140

1. Kodi acicepele afunika kusankha ciani cokhudza tsogolo lawo? Nanga n’cifukwa ciani safunika kucita mantha? (Onani pikica pamwambapa.)

IMWE acicepele mungavomeleze kuti ni cinthu canzelu kudziŵa kumene mufuna kupita mukalibe kuyamba ulendo. Moyo nawonso uli ngati ulendo, ndipo nthawi yabwino yosankha zimene mudzayamba kucita pa umoyo wanu, ndi pamene muli wacicepele. N’zoona kuti kupanga zosankha n’kovuta. Mtsikana wina dzina lake Heather anati: “Kupanga zosankha n’kovutadi. Munthu amafunika kusankha mmene adzagwilitsila nchito moyo wake.” Koma simuyenela kuopa kupanga zosankha. Yehova anauza anthu ake kuti: “Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”—Yes. 41:10.

2. Mudziŵa bwanji kuti Yehova amafuna kuti muzipanga zosankha mwanzelu n’colinga cakuti mudzakhale na tsogolo labwino?

2 Yehova amafuna kuti muzipanga zosankha mwanzelu zokhudza tsogolo lanu. (Mlal. 12:1; Mat. 6:20) Iye amafuna kuti muzisangalala. Zinthu zabwino za m’cilengedwe zimene timaona, kumva, ndi kudya, zimatipatsa umboni wakuti afuna tizisangalala. Umboni wina ni wakuti Mulungu amatisamalila ndi kutiphunzitsa mmene tingakhalile na umoyo wabwino. Kwa anthu okana malangizo ake, Yehova anati: “Munasankha zinthu zimene sindisangalala nazo. . . . Atumiki anga adzasangalala, koma inuyo mudzacita manyazi. Atumiki anga adzafuula mokondwa cifukwa cokhala ndi cimwemwe mumtima.” (Yes. 65:12-14) Yehova amalemekezedwa ngati anthu ake apanga zosankha mwanzelu pa umoyo wawo.—Miy. 27:11.

ZOLINGA ZIMENE ZIDZAKUTHANDIZANI KUKHALA NA UMOYO WACIMWEMWE

3. Kodi Yehova amakufunila zotani?

3 Kodi Yehova afuna kuti mukhale na zolinga zotani? Kuti tikhale acimwemwe, tifunika kudziŵa Mulungu ndi kum’tumikila mokhulupilika. Umu ni mmene iye anatilengela. (Sal. 128:1; Mat. 5:3) Anatilenga mosiyana ngako na zinyama, zimene zimangokhalila kudya, kumwa, ndi kubalana basi. Mulungu amafuna kuti mukhale na umoyo wacimwemwe mwa kucitanso zinthu zina zofunika kuposa zimene nyama zimacita. Mlengi wathu ndi “Mulungu wacikondi” ndi “wacimwemwe,” ndipo analenga anthu “m’cifanizilo cake.” (2 Akor. 13:11; 1 Tim. 1:11; Gen. 1:27) Ngati mutengela citsanzo ca Mulungu wathu, amene ni wacikondi, mudzakhala na umoyo wacimwemwe. Mwina inu mwadzionela nokha kuti, “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Mac. 20:35) Umu ni mmene zinthu zimakhalila paumoyo. Conco, Yehova amafuna kuti mukhale na zolinga zimene zidzakupatsani mwayi woonetsa kuti mumakonda iye ndi anthu anzanu.—Ŵelengani Mateyu 22:36-39.

4, 5. N’ciani cinathandiza Yesu kukhala wacimwemwe?

4 Yesu Khristu anapeleka citsanzo cabwino kwambili kwa inu acicepele. Ali mwana, mosakayikila anali kuseŵela ndi kucita zosangalatsa. Mau a Mulungu amati pali “nthawi yoseka . . . ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.” (Mlal. 3:4) Yesu analinso kuphunzila Malemba kuti alimbitse ubwenzi wake na Yehova. Pamene anali na zaka 12, aphunzitsi pa kacisi anadabwa kwambili na ‘mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa kwambili’ zinthu zauzimu.—Luka 2:42, 46, 47.

5 Yesu anakula ali na umoyo wacimwemwe. N’ciani cinamuthandiza kukhala wacimwemwe? Iye anadziŵa kuti Mulungu afuna kuti ‘alengeze uthenga wabwino kwa osauka’ ndi ‘kulalikila . . . zoti akhungu ayambe kuona.’ (Luka 4:18) Kucita zimene Mulungu afuna kunam’cititsa kukhala wacimwemwe. Salimo 40:8 imatiuza mmene iye anali kumvelela. Lembali limati: “Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga.” Yesu anali kukonda kuphunzitsa anthu za Atate wake wakumwamba. (Ŵelengani Luka 10:21.) Ataphunzitsa mayi wina zinthu zokhudza kulambila koona, Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Cakudya canga ndico kucita cifunilo ca amene anandituma ndi kutsiliza nchito yake.” (Yoh. 4:31-34) Kukonda Mulungu ndi anthu kunacititsa Yesu kukhala wacimwemwe. Inunso kungakuthandizeni kukhala wacimwemwe.

6. N’cifukwa ciani mufunika kukambilana zolinga zanu ndi Akhristu okhwima mwauzimu?

6 Akhristu ambili anali acimwemwe ngako pamene anali kucita upainiya ali acicepele. Bwanji osakambilana zolinga zanu ndi ena mwa iwo? Baibo imati: “Zolingalila sizikwanilitsidwa ngati anthu sakambilana moona mtima, koma aphungu akaculuka zimakwanilitsidwa.” (Miy. 15:22) Anthu okonda zinthu zauzimu amenewa angakuuzeni kuti ngati mucita utumiki wa nthawi zonse, mudzaphunzila zinthu zimene zidzakuthandizani pa umoyo wanu wonse. Yesu anaphunzitsidwa ndi Atate ŵake kumwamba, koma anaphunzila zowonjezeleka pamene anali kucita utumiki wake pano padziko lapansi. Mwacitsanzo, anaphunzila kulalikila uthenga wabwino mogwila mtima ndi kukhala wokhulupilika panthawi ya mayeselo. Zimenezi zinamuthandiza kukhala wacimwemwe. (Ŵelengani Yesaya 50:4; Aheb. 5:8; 12:2) Lomba tiyeni tikambilane mbali zina za utumiki wanthawi zonse zimene zingakuthandizeni kukhala wosangalala kwambili.

CIMENE CIMAPANGITSA ANTHU OPANGA OPHUNZILA KUKHALA ACIMWEMWE

7. N’cifukwa ciani acicepele ambili amasangalala na nchito yopanga ophunzila?

7 Yesu anati: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzila anga . . . ndi kuwaphunzitsa.” (Mat. 28:19, 20) Ngati colinga canu ni kupanga ophunzila, ndiye kuti mwasankha nchito yabwino kwambili imene idzakuthandizani kulemekeza Mulungu. Mofanana ndi nchito ina iliyonse, pafunika nthawi kuti mukhale na luso pa nchito imeneyi. Posacedwapa, m’bale wina dzina lake Timothy, amene anayamba upainiya ali wacicepele anati: “Nimakondwela kutumikila Yehova mu utumiki wanthawi zonse cifukwa ni njila imene nimaonetsela kuti nimam’konda. Poyamba n’nalibe phunzilo, koma pamene n’nasamukila m’gawo lina, n’napeza maphunzilo ambili m’mwezi umodzi cabe. Mmodzi wa ophunzilawo anayamba kupezeka pamisonkhano. N’tatsiliza maphunzilo a miyezi iŵili a Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Abale Osakwatila, * ananitumiza ku gawo lina kumene n’nayamba kutsogoza maphunzilo anayi a Baibo. Nchito yophunzitsa anthu nimaikonda cifukwa nimaona mmene mzimu woyela umathandizila anthu kusintha umoyo wawo.”—1 Ates. 2:19.

8. Kodi acicepele ena acikhristu acita zotani kuti acite zambili pa nchito yopanga ophunzila?

8 Akhristu ena acicepele aphunzilako citundu cina. Mwacitsanzo, Jacob wa ku North America, analemba kuti: “Pamene n’nali na zaka 7, anzanga ambili m’kilasi anali ocokela ku Vietnam. N’nali kufuna kuwauza za Yehova. Conco, patapita nthawi yocepa n’naganiza zoyamba kuphunzila citundu cawo. Cacikulu cimene cinanithandiza ni kulinganiza nkhani za m’magazini a Nsanja ya Mlonda yacizungu ndi ya Civietinamu. Cinanso, n’napeza anzanga mumpingo wa Civietinamu umene unali pafupi na kwathu. N’takwanitsa zaka 18, n’nayamba kucita upainiya. Pambuyo pake, n’naloŵa Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Abale Osakwatila. Zimene n’naphunzila m’sukuluyi zanithandiza kukwanilitsa maudindo anga monga mpainiya komanso mkulu. Tsopano nitumikila m’kagulu ka Civietinamu, ndipo ndine nekha amene nikutumikila monga mkulu. Anthu ambili ocokela ku Vietnam amadabwa kwambili kuti n’naphunzila citundu cawo. Iwo amanilandila ku nyumba zawo, ndipo ambili amavomela kuti niziphunzila nawo Baibo. Ena apita patsogolo mpaka kufika pa kubatizika.”—Yelekezelani na Machitidwe 2:7, 8.

9. Ni zinthu zabwino ziti zimene mungaphunzile ngati mugwila nchito yopanga ophunzila?

9 Kugwila nchito yopanga ophunzila kungakuphunzitseni kukhala akhama pa nchito, kukhala na luso lokamba bwino ndi anthu, kugwila nchito na mtima wonse, ndi kukhala wozindikila. (Miy. 21:5; 2 Tim. 2:24) Cina, nchito yopanga ophunzila imabweletsa cimwemwe coculuka cifukwa imakuthandizani kudziŵa bwino Malemba okhudza zimene mumakhulupilila. Mumaphunzilanso kugwila nchito pamodzi na Yehova.—1 Akor. 3:9.

10. Kodi mungakhale bwanji acimwemwe pa nchito yopanga ophunzila olo kuti mumalalikila m’gawo louma?

10 N’zotheka kukhala acimwemwe pa nchito yopanga ophunzila, ngakhale kuti ni anthu ocepa cabe amene amamvetsela uthenga wabwino m’gawo lanu. Kupanga ophunzila ni nchito ya gulu osati ya munthu mmodzi. Mpingo wonse umafufuza anthu oona mtima. Ngati m’bale kapena mlongo wapeza munthu amene m’kupita kwa nthawi wakhala wophunzila, tonse timakondwela cifukwa timagwilila pamodzi nchito yofufuza anthu oona mtima. Mwacitsanzo, m’bale Brandon anacita upainiya kwa zaka 9 m’gawo limene anthu analibe cidwi na uthenga wabwino. Iye anati: “Nimakonda kulalikila uthenga wabwino cifukwa n’zimene Yehova afuna kuti tizicita. N’nayamba kucita upainiya n’tangotsiliza sukulu. Nimakonda kulimbikitsa abale acicepele mumpingo mwathu ndipo nimasangalala kuona mmene akupitila patsogolo mwauzimu. N’tatsiliza maphunzilo a Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Abale Osakwatila, ananitumiza ku gawo lina latsopano kumene n’napitiliza kucita upainiya. N’zoona kuti pa anthu amene n’nali kuphunzila nawo Baibo m’gawolo, palibe amene anapita patsogolo kufika pobatizika. Koma pali abale na alongo ena amene akwanitsa kuthandiza anthu mpaka kubatizika. Ndine wokondwela ngako kuti n’nasankha kucita zambili pa nchito yopanga ophunzila.”—Mlal. 11:6.

MAUTUMIKI ENA AMENE MUNGACITE MUKAKHALA MPAINIYA

11. Ni utumiki wopatulika uti umene acicepele ambili amasangalala kuucita?

11 Pali mipata yambili yotumikila Yehova. Mwacitsanzo, acicepele ambili amadzipeleka kugwila nchito yomanga. Nyumba za Ufumu zambili zatsopano zifunika kumagidwa. Kugwila nawo nchito yomanga imeneyi ni mbali ya utumiki wopatulika umene umalemekeza Mulungu, ndipo kungakuthandizeni kukhala wacimwemwe. Mofanana ndi mautumiki ena opatulika, kutumikila pamodzi ndi abale pa nchito yomanga kumabweletsa cimwemwe. Kugwila nchito yomanga kungakuphunzitseni mmene mungapewele ngozi, kukhala wakhama pa nchito, na kugwilizana ndi okutsogolelani.

Amene amacita utumiki wanthawi zonse amapeza madalitso ambili (Onani palagilafu 11-13)

12. Kodi kucita upainiya kungakupatseni bwanji mwayi wocitako mautumiki ena?

12 M’bale wina dzina lake Kevin anati: “Kuyambila nili mwana, n’nali na colinga cakuti nikadzakula nidzatumikile Yehova mu utumiki wanthawi zonse. N’takwanitsa zaka 19, n’nayamba kucita upainiya. Kuti nizipeza zofunika pa umoyo, n’nali kuseŵenza kwa maola ocepa kwa m’bale amene anali kugwila nchito yomanga. N’naphunzila kukhoma mtenje, kuika mawindo ndi zitseko. Pambuyo pake, kwa zaka ziŵili n’natumikila m’gulu la abale amene anali kupeleka thandizo kwa okhudzidwa ndi cimphepo coopsa ca mkuntho. Tinali kukonza Nyumba za Ufumu ndi nyumba za abale zowonongeka. N’tamvela kuti ku South Africa kufunikila anchito omanga, n’nafunsila utumiki umenewu ndipo ananiitana. Kuno ku Africa, timamanga Nyumba ya Ufumu kwa mawiki angapo cabe, ndipo tikatsiliza timapita pa ina. Gulu limene nimagwila nalo nchito yomanga lili ngati banja langa. Timakhala pamodzi, kuphunzila Baibo pamodzi, na kuseŵenzela pamodzi. Nimasangalalanso kugwila nchito yolalikila wiki iliyonse pamodzi na abale a pampingo umene tili. Zolinga zimene n’napanga nili mwana zanicititsa kukhala na cimwemwe coculuka kuposa cimene n’nali kuyembekezela.”

13. Kodi utumiki wa pa Beteli umathandiza bwanji acicepele kukhala osangalala?

13 Abale ndi alongo ena amene anakwanilitsa colinga cawo cotumikila Yehova mu utumiki wanthawi zonse, pali pano akutumikila pa Beteli. Kucita utumiki wa pa Beteli kumabweletsa cimwemwe cifukwa zilizonse zimene munthu ungacite, umacitila Yehova. Banja la Beteli limathandiza kupeleka cakudya cauzimu. Dustin amene akutumikila pa Beteli anati: “N’nakhala na colinga cocita utumiki wanthawi zonse nili na zaka 9, ndipo n’nayamba upainiya n’tatsiliza sukulu. Patapita caka cimodzi na hafu ananiitana ku Beteli. Kumeneko, n’naphunzila kuseŵenzetsa mashini opulintila, ndipo pambuyo pake n’naphunzila kukonza mapulogilamu a pa kompyuta. Kuno ku Beteli, nimadzionela nekha mmene nchito yopanga ophunzila ikupitila patsogolo padziko lonse. Nimakondwela kutumikila kuno cifukwa zimene timacita zimathandiza anthu kukhala pa ubwenzi na Yehova.”

KODI MUDZAPANGA ZOLINGA ZANJI ZOKHUDZA TSOGOLO LANU?

14. Mungakonzekele bwanji kuti mukakhale mtumiki wanthawi zonse?

14 Kodi mungakonzekele bwanji kuti mudzakhale mtumiki wanthawi zonse? Cofunika kwambili ndi kukhala na makhalidwe abwino acikhristu amene adzakuthandizani kucita zambili potumikila Yehova. Conco, muziphunzila Mau a Mulungu mwakhama ndi kusinkha-sinkha tanthauzo lake. Muziyesetsa kuonetsa cikhulupililo canu mwa kutengako mbali pa misonkhano ya mpingo. Mukali pasukulu, yesetsani kukulitsa luso lolalikila uthenga wabwino. Phunzilani kuonetsa anthu cidwi mwa kuwafunsa mafunso mosamala kuti afotokoze maganizo awo, ndipo muziwamvetsela. Komanso, mungadzipeleke kugwila nchito zina za pampingo, monga kuyeletsa ndi kukonza zowonongeka pa Nyumba ya Ufumu. Yehova amasangalala kugwilitsila nchito anthu odzicepetsa ndi odzipeleka. (Ŵelengani Salimo 110:3; Mac. 6:1-3) Mtumwi Paulo anatenga Timoteyo pa ulendo wa umishonale cifukwa “abale . . . anamucitila umboni wabwino.”—Mac. 16:1-5.

15. Mungakonzekele bwanji kuti muzikapeza zofunikila pa umoyo pocita upainiya?

15 Atumiki a nthawi zonse amafunika kugwila nchito kuti azipeza zofunikila paumoyo. (Mac. 18:2, 3) Mwina mungafunike kucitako kosi yaifupi kuti mudzathe kupeza nchito ya maola ocepa m’dela lanu. Kuti mudziŵe mtundu wa kosi imene mungacite, funsani woyang’anila dela ndi apainiya m’dela lanu. Afunseni kuti ni nchito iti imene apainiya angacite. Komanso, monga mmene Baibo imakambila, ‘pelekani nchito zanu kwa Yehova, ndipo zolinga zanu ndithu zidzakhazikika.’—Miy. 16:3; 20:18.

16. Kodi kucita zambili potumikila Yehova mukali wacicepele, kungakuthandizeni bwanji kukonzekela maudindo ena am’tsogolo?

16 Yehova amafuna kuti ‘mugwile mwamphamvu’ tsogolo lacimwemwe. (Ŵelengani 1 Timoteyo 6:18, 19) Kucita utumiki wanthawi zonse kungakupatseni mwayi wodziŵana ndi atumiki anzanu anthawi zonse, ndipo kungakuthandizeni kukhala Mkhristu wofikapo kuuzimu. Ambili aona kuti kucita zambili potumikila Yehova akali acicepele, kwawathandiza kukhala na banja lacimwemwe. Nthawi zambili, amene anayamba upainiya asanaloŵe m’banja, amapitiliza kucita utumikiwu akaloŵa m’banja.—Aroma 16:3, 4.

17, 18. Kodi zolinga zimene munthu amakhala nazo zimagwilizana bwanji na zimene zili mumtima mwake?

17 Munthu amapanga mapulani kapena zolinga mogwilizana ndi zimene zili mumtima mwake. Salimo 20:4 imati: “[Yehova] akupatseni zokhumba za mtima wanu, ndipo akwanilitse zofuna zanu.” Conco, dzifunseni kuti, ‘Kodi moyo wanga nidzaugwilitsila nchito bwanji?’ Ganizilani zimene Yehova akucita masiku ano na zimene imwe mungacite mu utumiki wake. Ndiyeno, dziikileni zolinga zimene zingam’kondweletse.

18 Kucita zambili mu utumiki wa Yehova kudzakuthandizani kukhala na umoyo wokhutilitsa cifukwa mudzakhala na mwayi wolemekeza Mulungu nthawi zonse. Conco, ‘sangalalani mwa Yehova, ndipo adzakupatsani zokhumba za mtima wanu.’—Sal. 37:4.

^ par. 7 Tsopano imachedwa kuti Sukulu ya Alengezi a Ufumu.