Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mungapambane Bwanji Nkhondo Yoteteza Maganizo Anu?

Mungapambane Bwanji Nkhondo Yoteteza Maganizo Anu?

DZIŴANI kuti muli pankhondo. Ndipo mdani wanu wamkulu, Satana, akuseŵenzetsa cida coopsa kwambili polimbana nanu. Kodi cida cimeneci n’citi? Ni mauthenga osoceletsa. Colinga cake poseŵenzetsa cida cimeneci ni kusokoneza maganizo anu, osati kukuwonongani mwakuthupi.

Mtumwi Paulo anali kudziŵa bwino kuopsa kwa mauthenga osoceletsa a Satana. Koma si Akhristu onse panthawiyo amene anali kudziŵa zimenezi. Mwacitsanzo, Akhristu ena a ku Korinto anali kudzidalila. Anali kudziona monga olimba kwambili m’coonadi cakuti sangagwe mwauzimu. (1 Akor. 10:12) N’cifukwa cake Paulo anapeleka cenjezo lakuti: “Nkhawa yanga ndi yakuti mwina, monga mmene njoka inanamizila Hava ndi cinyengo cake, maganizo anunso angapotozedwe kuti musakhalenso oona mtima ndi oyela ngati mmene muyenela kucitila kwa Khristu.”—2 Akor. 11:3.

Nkhawa imene Paulo anali nayo polemba mau amenewa ionetsa kuti sitifunika kudzidalila tekha. Kuti tipambane pa nkhondo yoteteza maganizo athu, tifunika kuzindikila kuopsa kwa mauthenga osoceletsa a Satana ndi kupeza njila zodzitetezela.

KODI MAUTHENGA OSOCELETSA NI OOPSA BWANJI?

Anthu amaseŵenzetsa mauthenga osoceletsa pofuna kupusitsa anzawo kapena kulamulila maganizo awo ndi zocita zawo. Malinga n’zimene buku lina linakamba, mauthenga aconco “ndi oipa, owononga, ndi osayenela.” Mau ena amene anthu amakamba amene amatanthauza mauthenga osoceletsa ndi monga akuti ‘mabodza, cinyengo, ndi kupusitsa.’—Propaganda and Persuasion.

Kodi mauthenga osoceletsa ndi oopsa bwanji? Ndi oopsa cifukwa amasoceletsa munthu pang’ono-pang’ono, koma iye osadziŵa. Mauthenga osoceletsa ali monga mpweya wakupha, koma wopanda fungo. Popeza nthawi zina mauthenga amenewa sitingawazindikile, katswili wina wa cikhalidwe ca anthu, dzina lake Vance Packard, anati: “Ambili a ise timasoceletsedwa kwambili, koma osadziŵa.” Katswili winanso anakamba kuti cifukwa cotsatila mauthenga osoceletsa, amuna ndi akazi ambili “asoceletsedwa mosavuta mpaka kufika pocita zinthu zoipitsitsa,” monga ‘kupulula mtundu wathunthu wa anthu, nkhondo, kudana cifukwa cosiyana mitundu ndi zipembedzo, ndiponso makhalidwe ena oipitsitsa.’—Easily Led—A History of Propaganda.

Ndiye ngati anthu amakwanitsa kutisoceletsa na mauthenga awo abodza, kuli bwanji Satana? Iye wakhala akuphunzila zocita za anthu kucokela pamene munthu woyamba analengedwa. Pali pano, “dziko lonse” lili m’manja mwake. Iye angaseŵenzetse ciliconse m’dzikoli pofalitsa mabodza ake. (1 Yoh. 5:19; Yoh. 8:44) Tsopano, Satana wakhala katswili ‘wocititsa khungu maganizo a anthu’ cakuti “akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (2 Akor. 4:4; Chiv. 12:9) Kodi mungacite ciani kuti musasoceletsedwe na mauthenga ake abodza?

KHWIMITSANI CITETEZO CANU

Yesu anakamba mfundo yosavuta imene ingatiteteze ku mabodza a Satana. Anati: “Mudzadziŵa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Koma Satana safuna kuti tidziŵe coonadi. Zili ngati kunkhondo. Adani amafalitsa mabodza pofuna kupusitsa asilikali, ndipo asilikali amafunika kudziŵa kumene angapeze cidziŵitso colongosoka. Ifenso tifunika kukhala na gwelo la mfundo zodalilika za coonadi zimene zingatiteteze kwa mdani wathu amene amafuna kutisoceletsa. Yehova watipatsa gwelo la coonadi. M’Baibo, tingapezemo zonse zofunikila zimene zingatiteteze ku mabodza a Satana.—2 Tim. 3:16, 17.

Satana, amene ni katswili wofalitsa mabodza, amadziŵa zimenezi. Conco, iye amaseŵenzetsa dziko lakeli kugwetsa anthu mphwayi kuti asamaŵelenge ndi kuphunzila Baibo. Koma imwe musasoceletsedwe na njila yake yacinyengo imeneyi. (Aef. 6:11) Yesetsani “kudziŵa bwino” coonadi conse. (Aef. 3:18) Kucita zimenezi kumafuna khama. Kumbukilani mfundo yosatsutsika imene munthu wina, dzina lake Noam Chomsky, analemba. Iye anati: “Palibe munthu adzacita kuika coonadi m’maganizo mwanu. Mufunika kucitapo kanthu kuti mucipeze.” Conco, ‘citamponi kanthu kuti mucipeze’ mwa “kufufuza Malemba mosamala” ndi mwakhama tsiku ndi tsiku.—Mac. 17:11.

Kuti mupambane pa nkhondo yoteteza maganizo anu, mufunika kuzindikila kuopsa kwa mauthenga osoceletsa a Satana ndi kupeza njila zodzitetezela

Kumbukilani kuti Satana safuna kuti inu muziganiza bwino. Cifukwa ciani? Mogwilizana ndi zimene buku lina linakamba, mauthenga osoceletsa “amagwila bwino nchito yake ngati anthu . . . sakwanitsa kuganiza bwino.” (Media and Society in the Twentieth Century). Conco, musamakhulupilile zilizonse kapena kuvomeleza zinthu m’cimbuli-mbuli. (Miy. 14:15) Gwilitsilani nchito luso la kuganiza limene Mulungu anakupatsani kuti mutenge coonadi kukhala canu-canu.—Miy. 2:10-15; Aroma 12:1, 2.

SAMALANI NA MACENJELA AKE OFUNA KUTIGAWANITSA NA KUTIGONJETSA

Akatswili pa zankhondo amafalitsa mauthenga abodza kuti afooketse adani awo. Iwo angafalitse mabodza amene angacititse asilikaliwo kumenyana okha-okha kapena amene angawacititse kudzipatula kwa asilikali anzawo. Mkulu wina wa asilikali a ku Germany anakamba kuti cimodzi cimene cinacititsa dziko lawo kugonja pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse n’cakuti, anthu “anapusitsidwa ndi mauthenga abodza ocokela kwa adani awo ngati mmene njoka imapusitsila kalulu.” Satana amafalitsa mabodza pofuna kutigaŵanitsa ndi kutigonjetsa. Mwacitsanzo, angalimbikitse mikangano pakati pa abale na alongo kapena kuwacititsa kucoka m’gulu la Yehova cifukwa coona ngati kuti zinthu zina sizicitika mwacilungamo.

Koma inu musasoceletsedwe. Lolani Mau a Mulungu kukutsogolelani. Mwacitsanzo, pankhani yolimbikitsa mgwilizano pakati pa abale ndi alongo athu, Baibo imatilimbikitsa kupitiliza “kukhululukilana ndi mtima wonse” ndi kuthetsa mikangano mwamsanga. (Akol. 3:13, 14; Mat. 5:23, 24) Imaticenjeza mwamphamvu kuti sitifunika kuleka kugwilizana ndi mpingo. (Miy. 18:1) Conco, dzipendeni kuti muone ngati ndimwe otetezeka ku mauthenga osoceletsa a Satana. Dzifunseni kuti: ‘Ni mfundo za ndani zimene n’natsatila panthawi imene n’nasiyana maganizo na Mkhristu mnzanga? Kodi n’natsatila mfundo za dziko kapena za Mulungu?’—Agal. 5:16-26; Aef. 2:2, 3.

KHALANIBE OKHULUPILIKA

Adani amadziŵa kuti ngati msilikali ni wosakhulupilika kwa mtsogoleli wake, sangamenye bwino nkhondo. Conco, amafalitsa mabodza kuti acititse asilikali kuyamba kukayikila atsogoleli awo. Angakambe mabodza monga akuti: “Musawamvele atsogoleli anu, angokunamizani,” kapena kuti “Samalani, adzakuphetsani.” Kuwonjezela apo, angatengelepo mwayi pa zophophonya za atsogoleliwo kuti afooketse asilikaliwo. N’zimenenso Satana amacita. Nthawi zonse, iye amayesa kukupangitsani kukayikila anthu amene Yehova wawaika kuti azikutsogolelani.

Kodi mungadziteteze bwanji? Tsimikizani mtima kumamatila ku gulu la Yehova ndi kucilikiza mokhulupilika anthu amene waika kuti azititsogolela, ngakhale kuti angalakwitse zinthu zina. (1 Ates. 5:12, 13) “Musafulumile kugwedezeka pa maganizo anu” ngati mwamvela zinthu zina zofooketsa zokambiwa na anthu ampatuko kapena anthu ena abodza, ngakhale zitamveka ngati zoona. (2 Ates. 2:2; Tito 1:10) Tsatilani malangizo amene anapelekedwa kwa Timoteyo. Gwilitsitsani coonadi cimene munaphunzila, ndipo muzikumbukila kumene munaciphunzilila. (2 Tim. 3:14, 15) Ndithudi, pali umboni wokwanila wotsimikizila kuti njila imene Yehova wakhala akugwilitsila nchito kwa zaka pafupi-fupi 100 potiphunzitsa coonadi, ni yodalilika.—Mat. 24:45-47; Aheb. 13:7, 17.

MUSAFOOKE CIFUKWA COOPSEZEDWA

Kumbukilani kuti nthawi zina macenjela a Satana amakhala oonekelatu. Iye angatiyese mwa kutiwopseza, ndipo imeneyi ni “imodzi mwa njila zakale kwambili zosoceletsela anthu.” (Easily Led—A History of Propaganda) Mwacitsanzo, pulofesa wina wa ku Britain, dzina lake Philip M. Taylor analemba kuti Asuri anali kugonjetsa adani awo mwa “kuwaopseza ndi kufalitsa mauthenga abodza.” Satana angaticititse kukhala na mzimu woopa anthu, cizunzo, imfa, ndi zinthu zina kuti atifooketse ndi kuticititsa kuleka kutumikila Yehova.—Yes. 8:12; Yer. 42:11; Aheb. 2:15.

Musalole kuti Satana akulefuleni kapena kukulepheletsani kukhala wokhulupilika kwa Mulungu mwa kukuwopsezani. Yesu anati: “Musamaope amene amapha thupi lokha, amene sangathe kucita zoposa pamenepa.” (Luka 12:4) Musakayikile ngakhale pang’ono kuti Yehova adzakuyang’anilani monga mmene analonjezela, ndi kukupatsani “mphamvu yoposa yacibadwa,” ndiponso adzakuthandizani kuti musagonje pamene muopsezedwa.—2 Akor. 4:7-9; 1 Pet. 3:14.

N’zoona kuti nthawi zina mungakumane na mavuto aakulu ndi ofooketsa. Koma kumbukilani mau olimbikitsa amene Yehova anauza Yoswa. Anamuuza kuti: “Ukhale wolimba mtima ndipo ucite zinthu mwamphamvu. Usacite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.” (Yos. 1:9) Mukakhala na nkhawa, muzipemphela kwa Yehova ndi kumuuza nkhawa zanu zonse. Mukacita zimenezi, “mtendele wa Mulungu . . . udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu” ndipo mudzatha kukaniza mabodza onse a Satana.—Afil. 4:6, 7, 13.

Kodi mukumbukila mabodza amene nthumwi ya Asuri, Rabisake, anaseŵenzetsa polimbana ndi anthu a Mulungu? M’mau ena, tinganene kuti iye anati: ‘Palibe cimene cingakutetezeni kwa Asuri. Olo Mulungu wanu, Yehova, sangakupulumutseni.’ Anakambanso kuti: ‘Yehovayo ndiye watiuza kuti tiwononge dziko lanu.’ Poyankha, kodi Yehova anawauza ciani? Iye anati: “Usacite mantha cifukwa ca mau amene wamva, amene atumiki a mfumu ya Asuri andilankhulila monyoza.” (2 Maf. 18:22-25; 19:6) Ndiyeno, iye anatumiza mngelo amene anapha asilikali Aasuri 185,000 pa usiku umodzi cabe.—2 Maf. 19:35.

KHALANI WANZELU MWA KUMVELA YEHOVA NTHAWI ZONSE

Kodi munatambako filimu imene kwa inu, zinali zocita kuonekelatu kuti munthu wina akumunyengelela mpaka kumusoceletsa? Mwina munali kudzikambila mumtima kuti: ‘Usakhulupilile! Angokunamiza cabe!’ Lomba yelekezelani kuti mukuona angelo amene akukuuzani mofuula kuti: “Usasoceletsedwe na mabodza a Satana!”

Conco, musamamvetsele mauthenga osoceletsa a Satana. (Miy. 26:24, 25) Muzimvetsela kwa Yehova na kum’dalila m’zocita zanu zonse. (Miy. 3:5-7) Labadilani pempho lake lacikondi lakuti: “Mwana wanga, khala wanzelu ndi kukondweletsa mtima wanga.” (Miy. 27:11) Mukacita zimenezi, mudzapambana nkhondo yoteteza maganizo anu.