Kodi Mukhoza Kuyembekezera Moleza Mtima?

Kodi Mukhoza Kuyembekezera Moleza Mtima?

“Nanunso khalani oleza mtima.”​—YAK. 5:8.

NYIMBO: 78, 139

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chingatichititse kufunsa kuti, “Mpaka liti”? (b) Kodi zimene atumiki okhulupirika akale anachita zingatilimbikitse bwanji?

 MNENERI YESAYA anafunsa kuti, “Mpaka liti?” ndipo mneneri Habakuku anafunsa kuti, “Kufikira liti?” (Yes. 6:11; Hab. 1:2) Nayenso Mfumu Davide, yemwe analemba Salimo 13, anafunsa maulendo 5 kuti: “Kufikira liti?” (Sal. 13:1, 2) Ngakhale Yesu Khristu Ambuye wathu anafunsa funso lomweli ataona anthu opanda chikhulupiriro. (Mat. 17:17) Choncho tisamadabwe ngati nthawi zina nafenso timadzifunsa funso limeneli.

2 Koma kodi n’chiyani chingatichititse kufunsa kuti, “Mpaka liti”? Mwina anthu akhala akutichitira zinthu zopanda chilungamo. Apo ayi tikuvutika ndi ukalamba, matenda kapena mavuto ena a ‘munthawi yovutayi.’ (2 Tim. 3:1) Mwinanso tatopa ndi maganizo olakwika amene anthu ambiri ali nawo. Kaya vuto limene latitopetsa ndi lotani, n’zolimbikitsa kudziwa kuti atumiki a Yehova akale, omwe analinso okhulupirika, sanadzudzulidwe atafunsa funso lomweli.

3. Kodi n’chiyani chingatithandize tikakumana ndi mavuto?

3 Kodi n’chiyani chingatithandize pa nthawi imene takumana ndi mavuto ngati amenewa? Yakobo, yemwe anali m’bale wake wa Yesu, analemba kuti: “Lezani mtima abale, kufikira kukhalapo kwa Ambuye.” (Yak. 5:7) Choncho tikakumana ndi mavuto tiyenera kukhala oleza mtima. Koma kodi munthu woleza mtima amatani?

KODI MUNTHU WOLEZA MTIMA AMATANI?

4, 5. (a) Kodi munthu woleza mtima amatani? (b) Kodi Yakobo anagwiritsa ntchito fanizo liti posonyeza zimene munthu woleza mtima amachita? (Onani chithunzi choyambirira.)

4 Baibulo limasonyeza kuti kuleza mtima ndi khalidwe limene mzimu woyera umatulutsa. Choncho popanda kuthandizidwa ndi Mulungu, munthu yemwe si wangwiro sangakhale woleza mtima bwinobwino. Mulungu ndi amene amathandiza munthu kukhala woleza mtima ndipo munthu akamaleza mtima amasonyeza kuti amakonda Mulungu komanso anthu ena. Munthu akamaleza mtima, chikondi chake chimalimba koma akamalephera kuchita zimenezi chikondi chake chimachepa ndipo anthu ena samukondanso. (1 Akor. 13:4; Agal. 5:22) Kuti munthu akhale woleza mtima ayenera kukhalanso ndi makhalidwe ena abwino. Mwachitsanzo, ayenera kukhala wopirira chifukwa khalidweli limamuthandiza kukhalabe ndi maganizo abwino akakumana ndi mavuto. (Akol. 1:11; Yak. 1:3, 4) Munthu woleza mtima amapewa kubwezera akalakwiridwa komanso amakhalabe wokhulupirika zivute zitani. Baibulo limanena kuti tiyenera kukhala ndi mtima wotha kudikira ndipo lemba la Yakobo 5:7, 8 limatsindika mfundo imeneyi. (Werengani.)

5 N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi mtima woyembekezera kuti Yehova atithandize? Yakobo anayerekezera zimene tiyenera kuchita ndi zimene mlimi amachita. Mlimi amagwira ntchito mwakhama kuti abzale mbewu, koma sangachititse kuti mvula izigwa kapena kuti mbewuzo zizikula. Iye sangachititsenso kuti zinthu zichitike mwamsanga. Amadziwa kuti ayenera kudikira moleza mtima kuti mbewuzo zibereke. Ifenso pali zinthu zambiri zimene sitingasinthe tikamadikira kuti Yehova akwaniritse malonjezo ake. (Maliko 13:32, 33; Mac. 1:7) Choncho tiyenera kuyembekezera moleza mtima ngati mmene mlimi amachitira.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha mneneri Mika?

6 Zimene tikukumana nazo masiku ano zikufanana ndi zimene zinkachitika munthawi ya mneneri Mika. Iye anakhala pa nthawi imene Ahazi anali mfumu ndipo zinthu zambiri zopanda chilungamo zinkachitika. Baibulo limanena kuti anthu ‘ankachita zoipa ndipo ankazichita bwino kwambiri.’ (Werengani Mika 7:1-3.) Mika anazindikira kuti palibe zimene iyeyo angachite kuti athetse mavutowa. Ndiye kodi anatani? Iye ananena kuti: “Ine ndidzadikirira Yehova. Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa. Mulungu wanga adzandimvera.” (Mika 7:7) Mofanana ndi Mika, ifenso tiyenera ‘kuyembekezera moleza mtima.’

7. Kodi tiyenera kukhala ndi mtima wotani poyembekezera Yehova?

7 Ngati tili ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha Mika nafenso tidzakhala ndi mtima wofuna kuyembekezera Yehova. Sitili ngati mkaidi yemwe akudikira nthawi yoti aphedwe. Zinthu zimene akudikirazo sazifuna koma amangodikirabe chifukwa choti sangachitire mwina. Koma ifeyo timayembekezera Yehova chifukwa chodziwa kuti iye adzakwaniritsa lonjezo lake loti adzatipatsa moyo wosatha pa nthawi yoyenera. Choncho ‘timapirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.’ (Akol. 1:11, 12) Koma tikamayembekezera kwinaku tikudandaula kuti Yehova akuchedwa kukwaniritsa malonjezo ake, iye sangasangalale nafe.​—Akol. 3:12.

ANTHU OKHULUPIRIKA AMENE ANALI OLEZA MTIMA

8. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikamaganizira zitsanzo za amuna ndi akazi okhulupirika akale?

8 Kuganizira amuna ndi akazi okhulupirika akale amene anadikira moleza mtima kuti Yehova akwaniritse malonjezo ake kungatithandize kukhalanso ndi mtima wofuna kuyembekezera. (Aroma 15:4) Tikamaganizira zitsanzo zawo, tiyenera kukumbukira zinthu zitatu. Tizikumbukira nthawi imene anayembekezera, chifukwa chimene anayembekezera ndiponso madalitso amene analandira chifukwa chokhala oleza mtima.

Abulahamu anadikira zaka zambiri kuti adzukulu ake Esau ndi Yakobo abadwe (Onani ndime 9 ndi 10)

9, 10. Kodi Abulahamu ndi Sara anayembekezera Yehova kwa nthawi yaitali bwanji?

9 Taganizirani chitsanzo cha Abulahamu ndi Sara. Iwo ali m’gulu la anthu ‘olandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo chifukwa cha chikhulupiriro ndi kuleza mtima kwawo.’ Malemba amanena kuti “Abulahamu ataonetsa kuleza mtima, analandira lonjezo” lakuti Yehova adzamudalitsa ndiponso kuchulukitsa ana ake. (Aheb. 6:12, 15) Koma kodi n’chifukwa chiyani Abulahamu anayenera kukhala woleza mtima? Mwachidule, anafunika kuchita zimenezi chifukwa zinatenga nthawi yaitali kuti lonjezo la Mulungulo likwaniritsidwe. Pangano limene Yehova anachita ndi Abulahamu linayamba kugwira ntchito pa Nisani 14, 1943 B.C.E. Pa nthawiyo m’pamene Abulahamu ndi Sara limodzi ndi a m’nyumba yawo anawoloka mtsinje wa Firate n’kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Koma kuchokera nthawi imeneyo, Abulahamu anadikira zaka 25 kuti mwana wake Isaki abadwe mu 1918 B.C.E. Kenako anadikiranso zaka zina 60 kuti adzukulu ake Esau ndi Yakobo abadwe mu 1858 B.C.E.​—Aheb. 11:9.

10 Kodi Abulahamu analandira dera lalikulu bwanji monga cholowa? Baibulo limanena kuti: “Komatu [Yehova] sanam’patse cholowa chilichonse mmenemu ayi, ngakhale kadera kochepetsetsa. Koma anamulonjeza kuti adzamupatsa dzikoli monga cholowa chake, ndi cha mbewu yake, ngakhale kuti pa nthawiyo n’kuti alibe mwana.” (Mac. 7:5) Panadutsa zaka 430 kuchokera nthawi imene Abulahamu anawoloka mtsinje wa Firate kufika nthawi imene ana ake anakhala mtundu waukulu n’kulandira dziko lolonjezedwalo.​—Eks. 12:40-42; Agal. 3:17.

11. Kodi n’chifukwa chiyani Abulahamu anatha kuyembekezera Yehova, nanga adzalandira madalitso otani?

11 Abulahamu anatha kudikira moleza mtima chifukwa choti ankakhulupirira Yehova. (Werengani Aheberi 11:8-12.) Iye anadikira moyo wake wonse koma sanaone lonjezo lonse litakwaniritsidwa. Ngakhale zinali choncho, sanadandaule. Koma tangoganizirani mmene adzamvere akadzaukitsidwa padzikoli. Iye adzadabwa kuona kuti m’Baibulo muli mavesi ambiri ofotokoza za iye ndi ana ake. a Adzasangalalanso kudziwa kuti zimene anachita zinali zofunika kwambiri kuti cholinga cha Yehova chokhudza mbewu yolonjezedwa chikwaniritsidwe. Mosakayikira, adzaona kuti anachita bwino kwambiri kudikira moleza mtima.

12, 13. Kodi n’chifukwa chiyani Yosefe anayenera kukhala woleza mtima, nanga anasonyeza khalidwe labwino liti?

12 Yosefe, yemwe anali chidzukulu cha Abulahamu, anasonyezanso kuti anali ndi mtima wotha kuyembekezera. Anthu ambiri anamuchitira zopanda chilungamo. Choyamba, iye ali ndi zaka pafupifupi 17, azichimwene ake anamugulitsa kuti akhale kapolo. Kenako ananamiziridwa kuti ankafuna kugwirira mkazi wa abwana ake ndipo anatsekeredwa m’ndende. (Gen. 39:11-20; Sal. 105:17, 18) Iye ankachita chilungamo koma m’malo modalitsidwa zinkaoneka kuti akungolangidwa. Koma patapita zaka 13, zinthu zinasintha mwamsanga. Yosefe anamasulidwa m’ndende muja n’kupatsidwa udindo wokhala wachiwiri kwa mfumu ya ku Iguputo.​—Gen. 41:14, 37-43; Mac. 7:9, 10.

13 Koma kodi Yosefe anakwiya chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene zinamuchitikirazo? Kodi anasiya kukhulupirira Yehova Mulungu? Ayi. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti adikire moleza mtima? Iye ankakhulupirira kwambiri Yehova ndipo anazindikira kuti Yehova ali ndi mphamvu yokonza zinthu. Umboni wake ndi zimene anauza azichimwene ake. Iye anawauza kuti: “Musaope ayi. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu? Inu munali ndi cholinga chondichitira zoipa. Koma Mulungu anali ndi cholinga chabwino, kuti apulumutse miyoyo ya anthu ambiri ngati mmene akuchitira panomu.” (Gen. 50:19, 20) Yosefe anazindikira kuti anachita bwino kwambiri podikira moleza mtima.

14, 15. (a) Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Davide ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya kuleza mtima? (b) N’chiyani chinathandiza Davide kuti adikire moleza mtima?

14 Nayenso Davide anachitiridwa zinthu zambiri zopanda chilungamo. Ngakhale kuti Yehova anamudzoza ali wamng’ono kuti adzakhale mfumu, iye anadikira kwa zaka 15 kuti ayambe kulamulira fuko lake. (2 Sam. 2:3, 4) Pa nthawi yodikirayi, Sauli, yemwe anali mfumu yosakhulupirika, ankamusakasaka kuti amuphe. b Izi zinachititsa kuti Davide azingothawathawa, kubisala m’mapanga a m’chipululu ndiponso nthawi zina ankakhala kudziko lina. Sauliyo ataphedwa kunkhondo, Davide anadikiranso zaka zina pafupifupi 7 kuti ayambe kulamulira mtundu wonse wa Isiraeli.​—2 Sam. 5:4, 5.

15 Kodi n’chifukwa chiyani Davide anayembekezera moleza mtima? Yankho la funsoli tingalipeze pa zimene iye ananena mu Salimo lomwe lija limene anafunsa maulendo 5 kuti: “Kufikira liti?” Davide ananena kuti: “Koma ine ndakhulupirira kukoma mtima kwanu kosatha. Mtima wanga ukondwere chifukwa cha chipulumutso chanu. Ndidzaimbira Yehova chifukwa wandifupa ndi zinthu zabwino.” (Sal. 13:5, 6) Davide ankakhulupirira kuti Yehova ndi wokoma mtima kwambiri. Choncho sanakhumudwe koma ankayembekezera kuti Yehova adzamupulumutsa ndipo ankaganizira zinthu zabwino zimene Yehovayo anamuchitira. Davide ankadziwa ubwino wodikira moleza mtima.

Sikuti Yehova amangotiuza kuti tiziyembekezera moleza mtima koma nayenso amaleza mtima

16, 17. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi Yesu ndi zitsanzo zabwino pa nkhani yoyembekezera moleza mtima?

16 Sikuti Yehova amangotiuza kuti tiziyembekezera moleza mtima koma nayenso amaleza mtima. Iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. (Werengani 2 Petulo 3:9.) Mwachitsanzo, zaka masauzande m’mbuyomo, Satana ananena kuti Yehova salamulira bwino. Komabe Yehova wakhala akuyembekezera moleza mtima nthawi yoti athetse nkhaniyi n’kuyeretsa dzina lake. Zimenezi zidzathandiza kuti anthu amene “amamuyembekezera” adzalandire madalitso osaneneka.​—Yes. 30:18.

17 Nayenso Yesu amatha kudikira moleza mtima. Pamene anali padzikoli anasonyeza kuti ndi wokhulupirika ndipo anapereka nsembe ya dipo mu 33 C.E., koma anadikira mpaka mu 1914 kuti ayambe kulamulira. (Mac. 2:33-35; Aheb. 10:12, 13) Ndipo adzadikirabe mpaka pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 kuti adani ake onse atheretu. (1 Akor. 15:25) N’zoona kuti adikira kwa nthawi yaitali koma kudikira kwakeko sikudzapita pachabe.

N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE KUKHALA OLEZA MTIMA?

18, 19. N’chiyani chingatithandize kuti tiziyembekezera moleza mtima?

18 Apa zikuonekeratu kuti tonsefe tiyenera kukhala oleza mtima n’kumayembekezera Yehova. Koma kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi? Tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake. Tizikumbukira kuti kuleza mtima ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. (Aef. 3:16; 6:18; 1 Ates. 5:17-19) Choncho tiyenera kuchonderera Yehova kuti atithandize kupirira moleza mtima.

19 Tizikumbukiranso zimene zinathandiza Abulahamu, Yosefe komanso Davide kuti aziyembekezera malonjezo a Yehova moleza mtima. Iwo ankakhulupirira kwambiri Yehova ndiponso kukumbukira zimene anawachitira. Sankangoganizira zimene ankafuna pa moyo wawo. Kuganizira madalitso amene anthu amenewa anapeza chifukwa choleza mtima kungatithandize kuti nafenso tiziyembekezera moleza mtima.

20. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

20 Choncho ngakhale kuti timakumana ndi mavuto, tiyenera kuyesetsa kuti tikhale ndi “mtima wodikira.” N’zoona kuti nthawi zina tingafunse kuti, “Mpaka liti, Yehova?” (Yes. 6:11) Koma mzimu woyera wa Mulungu ungatipatse mphamvu ndipo tingafune kunena mawu amene Yeremiya ananena akuti: “Yehova ndiye cholowa changa. Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima womudikira.”​—Maliro 3:21, 24.

a Nkhani ya Abulahamu imapezeka m’machaputala okwana 15 a buku la Genesis. Komanso olemba mabuku a m’Malemba Achigiriki anatchula Abulahamu maulendo oposa 70.

b Ngakhale kuti Yehova anakana Sauli atalamulira zaka ziwiri zokha, anamulola kulamulira zaka zina 38 mpaka pamene anafa.​—1 Sam. 13:1; Mac. 13:21.