Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Mtendere wa Mulungu Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse’

‘Mtendere wa Mulungu Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse’

“Mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu.”​—AFIL. 4:7.

NYIMBO: 76, 141

1, 2. Kodi chinachitika n’chiyani kuti Paulo ndi Sila amangidwe ku Filipi? (Onani chithunzi choyambirira.)

PAULO ndi Sila ali ku Filipi, zinthu zinangosintha mwadzidzidzi. Gulu la anthu linawakokera kumsika kuti akaweruzidwe mwamsangamsanga m’bwalo la olamulira. Akuluakulu a boma anawavula zovala zawo mochita kuwang’ambira ndipo analamula kuti akwapulidwe ndi ndodo. (Mac. 16:16-22) Kenako anawatsekera m’chipinda cha m’kati mwenimweni mwa ndende. Mapazi awo anawamangirira m’matangadza ndipo ayenera kuti ankamva kupweteka kumsana chifukwa cha kumenyedwa kuja. (Mac. 16:23, 24) Zimene zinachitikazi sizinali zachilungamo chifukwa Paulo anali nzika ya Roma ndipo ankafunika kuweruzidwa bwinobwino. *

2 N’kutheka kuti cha pakati pa usiku, Paulo ankaganizira zonse zimene zinachitika masanawo. Mwina ankaganiziranso za anthu a ku Filipi. Mosiyana ndi mizinda yambiri imene Paulo analalikirako, mzinda wa Filipi unalibe sunagoge. Mwina zinali choncho chifukwa chakuti mumzindawo munalibe amuna achiyuda okwanira. Sunagoge ankamangidwa mumzinda ngati chiwerengero cha amuna achiyuda chakwana 10. Choncho Ayuda a kumeneko ankasonkhana m’mbali mwa mtsinje kunja kwa mzindawo. (Mac. 16:13, 14) Anthu a ku Filipi ankanyadira kwambiri kukhala nzika za Roma. (Mac. 16:21) N’kutheka kuti zimenezi n’zimene zinawachititsa kuganiza kuti Paulo ndi Sila, omwe anali Ayuda, sangakhale nzika za Roma. Kaya zoona zake n’ziti, anthu awiriwa anatsekeredwa m’ndende popanda kuweruzidwa mwachilungamo.

3. Kodi n’chifukwa chiyani mwina Paulo sankamvetsa chifukwa chake anamangidwa, koma anachita chiyani?

3 N’kutheka kuti Paulo ankaganiziranso zimene zinamuchitikira m’miyezi ingapo asanamangidwe. Iye ali tsidya lina la nyanja ya Aegean ku Asia Minor, mzimu woyera unkamuletsa kulalikira m’madera ena. Zinali ngati mzimuwo ukumuuza kuti apite kudera linalake. (Mac. 16:6, 7) Atafika ku Torowa anaona masomphenya amene anamuthandiza kuzindikira koyenera kupita. Paulo anauzidwa kuti: “Wolokerani ku Makedoniya.” Apa anadziwiratu kumene Yehova ankafuna kuti apite ndipo sanakane. (Werengani Machitidwe 16:8-10.) Koma atangofika ku Makedoniya, anatsekeredwa m’ndende. Mwina Paulo ankadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova walola kuti zimenezi zichitike? Kodi ndikhala m’ndende mpaka liti?’ Kaya Paulo ankadzifunsa mafunsowa kapena ayi, iye sanalole kuti amusokoneze maganizo mpaka kusiya kukhulupirira Yehova kapena kukhala wosangalala. Iye ndi Sila anayamba “kupemphera ndi kutamanda Mulungu poimba nyimbo.” (Mac. 16:25) Mtendere wa Mulungu unawathandiza kuti mitima yawo ndi maganizo awo zikhale m’malo.

4, 5. (a) Kodi zochitika pa moyo wathu zingafanane bwanji ndi za Paulo? (b) Kodi zinthu zinasintha bwanji mosayembekezereka pa moyo wa Paulo?

4 Mofanana ndi Paulo, mwina pa nthawi ina munaganiza kuti mukutsogoleredwa ndi mzimu woyera koma kenako zinthu sizinachitike mmene munkaganizira. N’kutheka kuti munakumana ndi mavuto, apo ayi zinthu zambiri zinasintha pa moyo wanu. (Mlal. 9:11) Ndiyeno mukaganizira zimene zinachitikazi mukhoza kudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti zimenezi zichitike?’ Ngati ndi choncho, kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mupirire komanso musasiye kukhulupirira Yehova? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tionenso nkhani ya Paulo ndi Sila ija.

5 Pa nthawi imene Paulo ndi Sila ankaimba nyimbo zotamanda Yehova, panachitika zinthu zina zimene sankayembekezera ngakhale pang’ono. Mwadzidzidzi panachitika chivomezi champhamvu ndipo zitseko za ndendeyo zinatseguka. Maunyolo onse a akaidi anamasuka. Woyang’anira ndendeyo ankafuna kudzipha koma Paulo anamuletsa. Munthuyo komanso banja lake lonse anabatizidwa. Kutacha, akuluakulu a boma anatuma asilikali kuti akamasule Paulo ndi Sila. Iwo anawapempha kuti atuluke mumzindawo mwamtendere. Kenako akuluakulu a bomawo anazindikira kuti alakwitsa pozunza nzika za Roma ndipo anabwera okha kuti awaperekeze. Koma Paulo ndi Sila ananena kuti akufuna atsanzikane kaye ndi Lidiya, yemwe anali atangobatizidwa kumene. Zimenezi zinawathandizanso kuti alimbikitse abale awo. (Mac. 16:26-40) Apatu zinthu zinali zitasinthanso mosayembekezereka.

MTENDERE WA MULUNGU “UMAPOSA KUGANIZA MOZAMA KULIKONSE”

6. Kodi tikambirana chiyani panopa?

6 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi? Tikakumana ndi mayesero tisamade nkhawa chifukwa Yehova akhoza kuchita zinthu zimene sitikuyembekezera. Paulo sanaiwale zimene zinachitikazi chifukwa patapita nthawi, analembera abale a ku Filipi mfundo zokhudza kuda nkhawa komanso mtendere wa Mulungu. Tiyeni tsopano tikambirane mawu a Paulo a pa Afilipi 4:6, 7. (Werengani.) Kenako tikambirana nkhani zina za m’Baibulo zosonyeza kuti Yehova amachita zimene anthu sakuyembekezera. Pomaliza, tikambirana mmene “mtendere wa Mulungu” ungatithandizire kuti tipirire komanso tizidalira Yehova.

7. Kodi Paulo analimbikitsa abale a ku Filipi kuchita chiyani, nanga tingaphunzire chiyani pa zimene analembazo?

7 N’zosachita kufunsa kuti abale a ku Filipi atawerenga kalata imene Paulo anawalembera anakumbukira zimene zinamuchitikira zija komanso zinthu zosayembekezereka zimene Yehova anachita. Kodi Paulo anawalimbikitsa kuchita chiyani? Mwachidule, anawauza kuti asamade nkhawa. M’malomwake azipemphera kuti alandire mtendere wa Mulungu. Koma Paulo ananena kuti mtendere wa Mulungu “umaposa kuganiza mozama kulikonse.” Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? Anthu ena anamasulira mawuwa kuti “umaposa chilichonse chimene tikulakalaka” kapena “umaposa mapulani onse amene anthu angakhale nawo.” Apa Paulo ankatanthauza kuti “mtendere wa Mulungu” umakhala wabwino kwambiri kuposa zimene tingaganizire. Choncho ngakhale titaona kuti palibiretu njira yothetsera vuto linalake, Yehova amadziwa njira yake ndipo angachite zimene sitikuyembekezera.​—Werengani 2 Petulo 2:9.

8, 9. (a) Kodi zinthu zopanda chilungamo zimene Paulo anakumana nazo ku Filipi zinali ndi zotsatira zabwino ziti? (b) Kodi abale a ku Filipi ankadziwa zotani zokhudza zimene Paulo analemba m’kalata yake?

8 Abale a ku Filipi akamaganizira zimene zinachitika pa zaka 10 kuchokera nthawi imene Paulo anaikidwa m’ndende ija, ayenera kuti ankalimbikitsidwa kwambiri. Zimene Paulo analemba m’kalata yake zinalidi zoona. Zinthu zopanda chilungamo zimene Yehova analola kuti zichitike zinathandiza “kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.” (Afil. 1:7) Zinathandiza kuti akuluakulu a boma aja aziganiza kawiri asanachitenso chilichonse kwa Akhristu atsopano amumzindawo. Mwina nkhani imeneyi inathandizanso kuti Luka, yemwe ankayenda ndi Paulo, atsale ku Filipi pambuyo poti Paulo ndi Sila achoka. Izi zinathandiza kuti Luka alimbikitse kwambiri Akhristu atsopano amumzindawu.

9 Pamene Abale a ku Filipi ankawerenga kalata ya Pauloyi ankadziwa kuti sankalemba zinthu zimene sanakumane nazo. Paulo anali atakumana ndi mavuto aakulu kwambiri koma anasonyeza kuti anali ndi “mtendere wa Mulungu.” Ngakhale pa nthawi imene Paulo ankalemba kalatayo n’kuti ali pa ukaidi wosachoka panyumba ku Roma. Komabe ankasonyeza kuti anali adakali ndi “mtendere wa Mulungu.”​—Afil. 1:12-14; 4:7, 11, 22.

“MUSAMADE NKHAWA NDI KANTHU KALIKONSE”

10, 11. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikapanikizika ndi nkhawa, nanga tingayembekezere chiyani?

10 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamade nkhawa ndi kanthu kalikonse koma tikhale ndi “mtendere wa Mulungu”? Zimene Paulo analembera Akhristu a ku Filipi zikusonyeza kuti pemphero ndi limene lingatithandize. Choncho tikakumana ndi mavuto, m’malo moda nkhawa, tiyenera kupemphera. (Werengani 1 Petulo 5:6, 7.) Muzipemphera ndi chikhulupiriro chonse podziwa kuti Yehova amakuderani nkhawa. Mawu oti tizipemphera “pamodzi ndi chiyamiko,” akutanthauza kuti tiziganiziranso madalitso amene tili nawo n’kumayamikira Mulungu. Tikamakumbukira mfundo yoti Mulungu “angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza,” timamukhulupirira kwambiri.​—Aef. 3:20.

11 Mofanana ndi Paulo ndi Sila ku Filipi, tikhoza kudabwa ndi zimene Yehova angatichitire. Mwina sizingakhale zochita kugometsa koma zingakhale zimene tikufunikira pa nthawiyo. (1 Akor. 10:13) Apanso sitikutanthauza kuti tizingokhala phee n’kumadikira Yehova kuti athetse vuto lathu. Tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athu. (Aroma 12:11) Zimene tingachitezo zingasonyeze kuti tikufunadi kuti Yehova atithandize ndipo iye angadalitse zimene tikuchitazo. Koma tisaiwalenso kuti Yehova samangochita zimene ifeyo tapempha kapena zimene tikuyembekezera. Nthawi zina tikhoza kudabwa atachita zinthu zimene ife sitinkayembekezera ngakhale pang’ono. Tiyeni tikambirane nkhani za m’Baibulo zotitsimikizira kuti Yehova akhoza kutithandiza m’njira imene sitinkayembekezera.

YEHOVA ANACHITA ZINTHU ZOMWE ANTHU SANKAYEMBEKEZERA

12. (a) Kodi Hezekiya anachita chiyani ataopsezedwa ndi Mfumu Senakeribu? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehova anachita pothetsa vutoli?

12 M’Baibulo muli nkhani zambiri zosonyeza kuti Yehova amachita zinthu zosayembekezereka. Mwachitsanzo, Hezekiya anali mfumu pa nthawi imene Senakeribu, yemwe anali mfumu ya Asuri, analanda mizinda yonse yokhala ndi mipanda ya ku Yuda, kupatulapo Yerusalemu. (2 Maf. 18:1-3, 13) Kenako Senakeribu ankafuna kuti alandenso Yerusalemu. Kodi Hezekiya anachita chiyani pa nthawi yovutayi? Iye anapemphera kwa Yehova komanso anafunsira nzeru kwa mneneri Yesaya. (2 Maf. 19:5, 15-20) Hezekiya anasonyezanso kuti si wamakani chifukwa anapereka ndalama zimene Senakeribu analamula. (2 Maf. 18:14, 15) Iye anachitanso zinthu zina pokonzera nthawi imene mzinda wa Yerusalemu udzazunguliridwe ndi Asuri. (2 Mbiri 32:2-4) Koma kodi nkhaniyi inatha bwanji? Yehova anatumiza mngelo yemwe anapha asilikali a Senakeribu okwana 185,000 usiku umodzi. Apatu Yehova anachita zinthu zimene ngakhale Hezekiya sankayembekezera.​—2 Maf. 19:35.

Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Yosefe?​—Gen. 41:42 (Onani ndime 13)

13. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Yosefe? (b) Kodi ndi zinthu zosayembekezereka ziti zimene zinachitikira Sara?

13 Chitsanzo china ndi zimene zinachitikira mwana wa Yakobo dzina lake Yosefe. Ali m’ndende ku Iguputo, Yosefe ayenera kuti sankaganiza n’komwe zoti adzakhala wachiwiri kwa mfumu ya Iguputo komanso kuti Yehova adzamugwiritsa ntchito kuti apulumutse achibale ake kuti asafe ndi njala. (Gen. 40:15; 41:39-43; 50:20) N’zosachita kufunsa kuti zimene Yehova anamuchitira zinali zosiyana kwambiri ndi zimene Yosefe ankayembekezera. Taganiziranso za Sara yemwe anali agogo a Yosefe. Kodi mukuganiza kuti iye ankayembekezera kuti Yehova angachititse kuti abereke mwana wakewake osati kungokhala ndi mwana wa wantchito wake? Mosakayikira kubadwa kwa Isaki kunaposa chilichonse chimene Sara ankaganizira.​—Gen. 21:1-3, 6, 7.

14. Kodi timadziwa kuti Yehova akhoza kuchita chiyani?

14 N’zoona kuti sitingayembekezere kuti Yehova adzathetsa mavuto athu onse dziko latsopano lisanafike ndipo sitipempha kuti atichitire zinthu zodabwitsa. Koma timadziwa kuti Mulungu wathuyu ndi amenenso anathandiza atumiki ake modabwitsa m’mbuyomo. (Werengani Yesaya 43:10-13.) Kudziwa mfundo imeneyi kumatithandiza kuti tizimukhulupirira kwambiri. Timadziwanso kuti iye akhoza kuchita chilichonse chimene chingafunike potithandiza kuti tizichita zimene amafuna. (2 Akor. 4:7-9) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani za m’Baibulo zimene takambiranazi? Nkhani ya Hezekiya, Yosefe ndi Sara zikusonyeza kuti tikakhala okhulupirika kwa Yehova, iye angatithandize kuchita zinthu zimene zingaoneke kuti n’zosatheka.

Tikakhala okhulupirika kwa Yehova, iye angatithandize kuchita zinthu zimene zingaoneke kuti n’zosatheka

15. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe ndi “mtendere wa Mulungu,” nanga zimenezi zimatheka bwanji?

15 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe ndi “mtendere wa Mulungu” tikamakumana ndi mavuto? Kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu wathu Yehova n’kumene kungatithandize. Koma zimenezi zingatheke kudzera “mwa Khristu Yesu” yemwe anapereka moyo wake monga nsembe ya dipo. Kupereka nsembeyi ndi chinthu china chodabwitsa chimene Atate wathu anatichitira. Iye amagwiritsa ntchito dipoli kuti atikhululukire machimo athu ndipo timatha kukhala ndi chikumbumtima chabwino komanso kukhala naye pa ubwenzi wolimba.​—Yoh. 14:6; Yak. 4:8; 1 Pet. 3:21.

MTENDERE WA MULUNGU UDZATETEZA MITIMA YATHU NDI MAGANIZO ATHU

16. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akalandira “mtendere wa Mulungu”? Perekani chitsanzo.

16 Kodi chimachitika n’chiyani tikalandira “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse”? Baibulo limanena kuti mtenderewo ‘udzateteza mitima yathu ndi maganizo athu mwa Khristu Yesu.’ (Afil. 4:7) Mawu amene anawamasulira kuti “udzateteza” ankagwiritsidwa ntchito ponena za asilikali. Ankanena za gulu la asilikali lomwe limalondera mzinda wokhala ndi mpanda. Zoterezi n’zimene zinkachitika mumzinda wa Filipi. Anthu amumzindawu ankagona mosaopa chilichonse chifukwa chakuti panali asilikali amene ankalondera pageti lake. Ifenso tikakhala ndi “mtendere wa Mulungu” mitima yathu ndi maganizo athu zimakhala m’malo. Timadziwa kuti Yehova amatikonda ndipo amatifunira zabwino. (1 Pet. 5:10) Kudziwa zimenezi kumatiteteza kuti tisamapanikizike ndi nkhawa komanso tisamakhumudwe kwambiri.

17. N’chiyani chingatithandize kuti tisamade nkhawa tikaganizira za m’tsogolo?

17 Posachedwapa, padzikoli pachitika chisautso chachikulu kuposa chilichonse chimene chinachitikapo. (Mat. 24:21, 22) Panopa sitikudziwa zimene aliyense wa ife angakumane nazo pa nthawiyo. Koma palibe chifukwa choti tizidera nkhawa kwambiri. Ngakhale kuti sitidziwa zonse zimene Yehova adzachite, Yehovayo timamudziwa bwino. Zimene wakhala akuchita m’mbuyomu zimasonyeza kuti pa vuto lililonse, iye amatha kukwaniritsa cholinga chake ndipo nthawi zina amakwaniritsa m’njira imene anthu sankayembekezera. Nthawi iliyonse imene Yehova amatichitira zimenezi, tikhoza kuona njira yatsopano imene ‘mtendere wa Mulungu umaposera kuganiza mozama kulikonse.’

^ ndime 1 Zikuoneka kuti nayenso Sila anali nzika ya Roma.​—Mac. 16:37.