Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Kupilila Ziyeso Kumabweletsa Madalitso

Kupilila Ziyeso Kumabweletsa Madalitso

MWAUKALI, wapolisi wina ananiuza kuti: “Iwe ndiwe tate woipa kwambili. Unasiya mkazi wako ali na pakati ndiponso mwana wako wamng’ono. N’ndani adzawapezela zakudya na kuwasamalila? Leka cabe zimene umacita kuti utulutsidwe.” N’nayankha kuti: “Sin’nawasiyile dala. Koma imwe munanimanga. Nanga munanimangilanji?” Wapolisiyo anakalipa, amvekele: “Kukhala wa Mboni ni mlandu waukulu kwambili kuposa wina uliwonse.”

Zimenezi zinanicitikila mu 1959, nili m’ndende ina mumzinda wa Irkutsk, ku Russia. Lekani nifotokoze cifukwa cake ine na mkazi wanga Maria, tinali okonzeka ‘kuvutika cifukwa ca cilungamo,’ ndi mmene tinadalitsidwila cifukwa cokhalabe wokhulupilika.—1 Pet. 3:13, 14.

N’nabadwila ku Ukraine mu 1933, m’mudzi wa Zolotniki. Mu 1937, ang’ono awo a amayi ndi amuna awo amene anali a Mboni, anabwela kudzaticezela kucokela ku France ndipo anatisiyila mabuku ochedwa Government ndi Deliverance, ofalitsidwa ndi Watch Tower Society. Pamene atate anaŵelenga mabukuwo, cikhulupililo cawo mwa Mulungu cinalimba. N’zacisoni kuti mu 1939 anadwala kwambili, koma akalibe kumwalila anauza amayi kuti: “Ici ndiye coonadi. Uŵaphunzitse ana.”

SIBERIA—GAWO LATSOPANO LOLALIKILAKO

Mu April 1951, olamulila anayamba kutenga mwacikakamizo Mboni za kum’madzulo kwa dziko la USSR n’kukaziika ku Siberia. Ine, amayi anga, na mng’ono wanga Grigory, anaticotsa ku Ukraine. Tinayenda pa sitima kwa makilomita 6,000, n’kukafika mumzinda wa Tulun, ku Siberia. Patapita mawiki aŵili, mkulu wanga Bogdan, anafika kundende ina mumzinda wa Angarsk, pafupi ndi Tulun. Iye anali ataweluzidwa kuti apike ndende kwa zaka 25.

Ine, amayi, na Grigory, tinali kulalikila m’midzi ya pafupi ndi mzinda wa Tulun, koma tinali kucita izi mosamala. Mwacitsanzo, tikafika tinali kufunsa kuti, “Kodi pali aliyense amene agulitsako ng’ombe?” Tikapeza munthu amene agulitsa ng’ombe, tinali kukamba naye za mmene ng’ombezo zinapangidwila modabwitsa. Ndiyeno, tinali kuyamba kukambilana naye za Mlengi. Panthawiyo, m’nyuzipepa ina analemba kuti a Mboni amakamba kuti afuna ng’ombe zogula, koma m’ceni-ceni amafuna nkhosa. Ndipo tinawapezadi anthu amene anali ngati nkhosa. Tinali kusangalala kwambili kuphunzitsa Baibo anthu odzicepetsa ndiponso okonda kuceleza a m’gawo losagaŵilidwa limenelo. Tsopano ku Tulun kuli mpingo umene uli na ofalitsa oposa 100.

MMENE CIKHULUPILILO CA MARIA CINAYESEDWELA

Mkazi wanga Maria anaphunzila coonadi ku Ukraine mkati mwa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Pamene anali na zaka 18, wapolisi wina anayamba kumunyengelela kuti acite naye ciwelewele, koma iye anakanitsitsa. Tsiku lina atafika m’nyumba, anapeza kuti wapolisiyo wagona pabedi yake. Maria anathaŵa. Wapolisiyo anakwiya ndipo anamuwopseza kuti adzam’mangitsa cifukwa cokhala wa Mboni. Ndipo zimenezo zinacitikadi. Mu 1952, Maria anaweluzidwa kuti akhale m’ndende kwa zaka 10. Iye anamvela monga mmene Yosefe anamvelela pamene anaikidwa m’ndende cifukwa cokhala wokhulupilika. (Gen. 39:12, 20) Pocoka ku khoti, dilaiva amene ananyamula Maria kupita naye ku ndende anamuuza kuti: “Usacite mantha. Anthu ambili amene amaikidwa m’ndende amatulukamo bwino-bwino popanda kuwacotsela ulemu.” Mau amenewa anamulimbikitsa ngako.

Kucoka mu 1952 kufika mu 1956, Maria anali kugwila nchito yakalavula gaga m’ndende ya pafupi na mzinda wa Gorkiy, (umene lomba umachedwa kuti Nizhniy Novgorod) ku Russia. Iye analamulidwa kuti azigobola mitengo ngakhale m’nyengo yozizila. Maria anayamba kudwala-dwala, koma mu 1956 anatulutsidwa m’ndende ndipo anauyamba ulendo wopita ku Tulun.

N’NAKAKHALA KUTALI NA MKAZI WANGA NDI ANA ANGA

Pamene m’bale wina ku Tulun ananiuza kuti kukubwela mlongo, n’napita ku sitesheni na njinga yanga kuti nikam’landile. N’tangomuona Maria, n’namukonda kwambili. Panafunika khama kuti anivomele, ndipo zinatheka. Tinakwatilana mu 1957. Patapita caka cimodzi, mwana wathu wamkazi, Irina, anabadwa. N’nakondwela ngako, koma cimwemwe canga sicinakhalitse. Mu 1959, ananimanga cifukwa copulinta mabuku ophunzitsa Baibo. Ananiika m’cipinda canekha kwa miyezi 6. Kuti nipitilize kukhala na mtendele wa m’maganizo, nthawi zonse n’nali kupemphela, kuimba nyimbo za Ufumu ndi kuganizila mmene nidzalalikilila nikadzamasulidwa.

Nili m’ndende mu 1962

Pamene wapolisi anali kunifunsa mafunso m’ndende, ananizazila, amvekele: “Posacedwapa tidzakuphwanyani monga nsabwe!” N’nayankha kuti: “Yesu anati uthenga wabwino wa Ufumu UDZALALIKIDWA ku mitundu yonse, ndipo palibe aliyense angalepheletse zimenezi.” Ndiyeno, monga mmene nakambila kuciyambi, wapolisiyo anayamba kuninyengelela kuti nisiye cikhulupililo canga. Ataona kuti sin’nagonje ngakhale pambuyo poniwopseza ndi kuninyengelela, ananiweluza kuti nikagwile nchito yakalavula gaga kwa zaka 7 m’ndende ina pafupi na mzinda wa Saransk. Nili paulendo wopita kundendeko, n’namvela kuti mwana wathu waciŵili wamkazi Olga, wabadwa. Olo kuti n’nali kukhala kutali na mkazi wanga ndi ana anga, n’nalimbikitsidwa kudziŵa kuti ine na Maria takhalabe wokhulupilika kwa Yehova.

Maria ali ndi ana athu, Olga ndi Irina, mu 1965

Kamodzi pacaka, Maria anali kubwela ku Saransk kudzaniona ngakhale kuti ulendo wa pa sitima kucoka ku Tulun ndi kubwelela, unali kutenga masiku 12. Caka ciliconse anali kunibweletsela nsapato zanyowani zoseŵenzela. M’nsapatomo anali kubisamo makope atsopano a Nsanja ya Mlonda. Caka cina, ulendo wa Maria wodzaniona unali wapadela kwambili cifukwa anabwela ndi ana athu aŵili. Ganizilani cabe mmene n’namvelela n’tawaona ndi kukhalako nawo pamodzi!

UMOYO WOKUKA-KUKA NA MAVUTO ENA

Mu 1966 n’natulutsidwa m’ndende ndipo tonse anayi tinakukila kumzinda wa Armavir, pafupi na Nyanja Yakuda. Tili kumeneko, ana athu aamuna, Yaroslav ndi Pavel, anabadwa.

Pasanapite nthawi yaitali, apolisi anayamba kubwela kunyumba kwathu kudzafuna-funa mabuku ophunzilila Baibo. Iwo anali kufuna-funa paliponse, ngakhale m’zakudya zang’ombe. Ulendo wina apolisiwo atabwela, anali kucoka ciŵe, cifukwa tsikulo kunapsa kwambili, ndipo zovala zawo zinafipa ngako. Maria anawamvela cifundo podziŵa kuti anali kucita izi cabe cifukwa comvela malamulo. Anawapatsa zakumwa, bulasho yakuti apukutile zovala, madzi, na thaulo. Pamene mkulu wa apolisi anabwela, apolisiwo anamuuza zinthu zabwino zimene tinawacitila. Pocoka, mkulu wa apolisiyo anamwetulila ndi kutibayibitsa. Tinasangalala kuona zabwino zimene zimatulukapo ngati ‘tipitiliza kugonjetsa coipa mwa kucita cabwino.’—Aroma 12:21.

Ngakhale kuti tinali kukumana na mavuto amenewa, tinapitiliza kugwila nchito yolalikila ku Armavir. Tinathandizanso kulimbitsa kagulu kocepa ka ofalitsa a m’tauni ya Kurganinsk, imene inali pafupi na mzinda wa Armavir. Nimakondwela ngako kudziŵa kuti lomba ku Armavir kuli mipingo 6, ndipo ku Kurganinsk kuli mipingo inayi.

M’zaka zimenezo, nthawi zina tinali kufooka mwauzimu. Timayamikila kwambili kuti Yehova kupitila mwa abale okhulupilika, anatithandiza ndi kutilimbikitsa mwauzimu. (Sal. 130:3) Tinakumananso na ciyeso cacikulu cotumikila pamodzi ndi akazitape a boma, amene anayamba kugwilizana ndi mpingo mwaciphamaso. Iwo anali kuoneka kuti ni ocita bwino mwauzimu, ndipo anali akhama mu ulaliki. Ena anafika polandila maudindo m’gulu. Koma m’kupita kwa nthawi tinawadziŵa.

Mu 1978, Maria anakhalanso ndi pathupi ali na zaka 45. Cifukwa cakuti anali na vuto la mtima, madokota anadela nkhawa kuti adzafa, ndipo anamunyengelela kuti acotse mimbayo. Koma Maria anakana. Conco, madokota ena anayamba kumulondola kulikonse kumene wapita m’cipatalaco ali na nyeleti n’colinga cakuti amulase mankhwala otaitsa mimba. Pofuna kuteteza mwana wosabadwayo, Maria anathaŵa m’cipatalaco.

Apolisi anatilamula kuti ticoke mumzindawo. Conco, tinakukila m’mudzi wina pafupi ndi mzinda wa Tallinn, ku Estonia, dziko limene linali mbali ya USSR. Pamene tinali ku Tallinn, Maria anabeleka mwana wathanzi wamwamuna dzina lake Vitaly. Izi zinasiyana ndi zimene madokota anatiuza pamene tinali ku Armavir.

Patapita nthawi, tinakuka ku Estonia n’kukakhala ku Nezlobnaya, kum’mwela kwa dziko la Russia. Kumeneko, tinali kulalikila mosamala m’matauni apafupi, kumene anthu ocokela kumadela osiyana-siyana a dzikolo anali kubwela kudzasangalala. Iwo anali kubwela kudzacita zinthu zowathandiza kukhala na moyo wathanzi, koma anali kubwelela kwawo ali na ciyembekezo ca moyo wosatha.

KUPHUNZITSA ANA ATHU KUKONDA YEHOVA

Tinayesetsa kuphunzitsa ana athu kuti azikonda Yehova na kum’tumikila. Nthawi zambili, tinali kuitana abale a citsanzo cabwino kunyumba kwathu, amene anali kulimbikitsa ana athu mwauzimu. Mmodzi mwa abale amene anali kubwela kaŵili-kaŵili ndi mng’ono wanga Grigory, amene anatumikila monga woyang’anila woyendela kuyambila mu 1970 mpaka 1995. Banja lonse linali kusangalala kuceza naye cifukwa anali wansangala ndi wanthabwala. Tikalandila alendo, nthawi zambili tinali kucita maseŵela a nkhani za m’Baibo, ndipo pamene ana athu anali kukula, anali kukonda kwambili nkhani za m’Baibo.

Ana anga ndi azikazi awo.

Kucoka kumanzele kupita kulamanja. Kumbuyo: Yaroslav, Pavel, Jr., na Vitaly

Kutsogolo: Alyona, Raya, na Svetlana

Mu 1987, mwana wathu wamwamuna Yaroslav, anakukila ku Riga, m’dziko la Latvia. Kumeneko anali kulalikila momasuka. Koma pamene anakana kuloŵa usilikali, anaweluzidwa kuti akhale m’ndende kwa caka cimodzi na hafu, ndipo anakhala m’ndende zokwana 9 zosiyana-siyana. Zimene zinamuthandiza kupilila ni zimene n’namuuza zokhudza zomwe n’nakumana nazo m’ndende. Atatuluka m’ndende, anayamba kucita upainiya. Mu 1990, mwana wathu wina wamwamuna Pavel, amene anali na zaka 19 panthawiyo, anatiuza kuti afuna kukacita upainiya ku cisumbu cochedwa Sakhalin, kumpoto kwa dziko la Japan. Poyamba, sitinamulole. Pa cisumbuco panali ofalitsa 20 cabe, ndipo cinali pa mtunda wa makilomita 9,000 kucokela kumene tinali kukhala. Koma m’kupita kwa nthawi, tinamulola kupita ndipo tinacita bwino kwambili. Anthu kumeneko anali kumvetsela uthenga wa Ufumu. M’zaka zocepa cabe, kunakhazikitsidwa mipingo 8. Pavel anatumikila ku Sakhalin mpaka mu 1995. Panthawiyo, pakhomo tinatsala cabe na mwana wathu wamwamuna wothela, Vitaly. Kucokela ali mwana, iye anali kukonda kuŵelenga Baibo. Atafika zaka 14, anayamba kucita upainiya, ndipo tinacitako pamodzi upainiya kwa zaka ziŵili. Inali nthawi yokondweletsa ngako. Atafika zaka 19, Vitaly, anapita kukacita upainiya wapadela.

Mu 1952, wapolisi anauza Maria kuti: “Siya cikhulupililo cako, apo ayi ukapika ndende kwa zaka 10. Pamene udzatuluka, udzakhala utakalamba ndiponso udzakhala wekha-wekha.” Koma umu si mmene zinthu zinakhalila. Tinaona cikondi ca Yehova, Mulungu wathu wokhulupilika, ca ana athu, ndi ca anthu ambili amene tinawathandiza kuphunzila coonadi. Ine na Maria, tinali kukondwela tikapita kukaceza kumalo kumene ana athu anali kutumikila. Kumeneko, anthu amene ana athu anawathandiza kuphunzila za Yehova, anali kuyamikila kwambili.

KUYAMIKILA UBWINO WA YEHOVA

Mu 1991, nchito ya Mboni za Yehova inakhazikitsidwa mwalamulo. Izi zinathandiza kuti nchito yolalikila ipite patsogolo. Mpingo wathu unafika pogula basi kuti tizikwanitsa kukalalikila ku matauni ndi ku midzi ina yoyandikana ndi tauni yathu kumapeto kwa wiki iliyonse.

Nili na mkazi wanga mu 2011

Ndine wokondwa kuti Yaroslav na mkazi wake Alyona, ndiponso Pavel na mkazi wake Raya, akutumikila pa Beteli. Nayenso Vitaly na mkazi wake Svetlana akutumikila m’dela. Mwana wathu woyamba wamkazi Irina, ndi banja lake, amakhala ku Germany. Mwamuna wake Vladimir, ndi ana awo atatu aamuna, onse ni akulu mumpingo. Mwana wathu wamkazi Olga amakhala ku Estonia, ndipo kaŵili-kaŵili amanitumila foni. N’zacisoni kuti mkazi wanga wokondedwa Maria, anamwalila mu 2014. Nilakalaka kudzamuonanso panthawi ya ciukililo. Pali pano, nikhala mumzinda wa Belgorod, ndipo abale kuno amanithandiza kwambili.

Pa zaka zonse zimene natumikila Yehova, naphunzila kuti kukhala okhulupilika kumafuna kupilila, ndipo mtendele umene Yehova amapeleka ni cuma cimene sitingaciyelekezele na cina ciliconse. Madalitso amene tapeza ine na Maria cifukwa cokhala okhulupilika ni oculuka kuposa amene tinali kuganizila. Ulamulilo wa Soviet Union usanathe mu 1991, panali ofalitsa oposa 40,000 cabe. Tsopano m’maiko amene anali mbali ya Soviet Union muli ofalitsa oposa 400,000! Lomba nili na zaka 83, ndipo nikali kutumikila monga mkulu. Yehova nthawi zonse amanipatsa mphamvu, kuti nikwanitse kupilila mavuto. Zoonadi, Yehova wanidalitsa ngako.—Sal. 13:5, 6.