Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mmene Timavulila Umunthu Wakale ndi Kusauvalanso

Mmene Timavulila Umunthu Wakale ndi Kusauvalanso

“Vulani umunthu wakale pamodzi ndi nchito zake.”—AKOL. 3:9.

NYIMBO: 83, 129

1, 2. Kodi anthu ena akamba ciani ponena za Mboni za Yehova?

ANTHU ambili amakamba za makhalidwe ocititsa cidwi amene anthu a Yehova ali nawo. Mwacitsanzo, ponena za abale na alongo athu m’nthawi ya ulamulilo wa Nazi ku Germany, munthu wina dzina lake Anton Gill analemba kuti: “Mboni za Yehova zinali kudedwa kwambili ndi cipani ca Nazi. . . . Podzafika mu 1939, [m’ndende zozunzilako anthu] za Nazi munali Mboni za Yehova zokwana 6,000.” Iye anakambanso kuti ngakhale kuti a Mboni anazunzidwa kwambili, anakhalabe “odalilika ndi odekha,” ndiponso anaonetsa kuti anali “okhulupilika ndi ogwilizana.”

2 Komanso, posacedwapa anthu ena ku South Africa aona makhalidwe abwino amene anthu a Mulungu ali nawo. Mwacitsanzo, m’zaka za m’mbuyomu, Mboni zacikuda ndi zacizungu m’dzikolo sizinali kucitila zinthu pamodzi momasuka cifukwa cosiyana mitundu. Koma pa Sondo, pa December 18, 2011, zinali zokondweletsa kwambili kuona abale athu oposa 78,000 a mitundu yosiyana-siyana ocokela ku South Africa ndi maiko ena apafupi, atasonkhana pamodzi. Iwo anasonkhana m’sitediyamu yaikulu mumzinda wa Johannesburg, kuti asangalale ndi pulogilamu yauzimu. Ponena za abale amene anasonkhanawo, mmodzi wa oyang’anila sitediyamuyo anati: “Ili ni gulu la anthu a khalidwe labwino kwambili limene sin’nalionepo n’kale lonse m’sitediyamu ino. Onse avala bwino. Ndiponso anthu inu mwayeletsa bwino kwambili sitediyamuyi. Koma koposa zonse, ndinudi gulu locokela m’mitundu yosiyana-siyana.”

3. N’ciani cimacititsa gulu lathu la abale padziko lonse kukhala locititsa cidwi?

3 Mau ngati amenewa, okambidwa ndi anthu amene si Mboni amaonetsa kuti gulu lathu la abale padziko lonse n’lapadeladi. (1 Pet. 5:9) Koma kodi n’ciani cimatipangitsa kukhala osiyana kwambili ndi gulu lina lililonse la anthu? Mothandizidwa ndi Mau a Mulungu ndiponso mzimu wake woyela, timayesetsa ‘kuvula umunthu wakale’ na ‘kuvala umunthu watsopano.’—Akol. 3:9, 10.

4. Kodi tidzaphunzila ciani m’nkhani ino? Nanga n’cifukwa ciani?

4 Tikavula umunthu wakale, tifunika kupitiliza kupewa makhalidwe oipa amene tinali nawo poyamba. M’nkhani ino, tidzakambilana mmene tingavulile umunthu wakale ndi cifukwa cake tifunika kucita zimenezi mwamsanga. Tidzakambilananso cifukwa cake n’zotheka munthu kusintha ngakhale kuti analoŵelela kwambili m’makhalidwe oipa. Komanso, tidzakambilana zimene aciyambakale m’coonadi angacite kuti apewe kuvalanso umunthu wawo wakale. N’cifukwa ciani kukambilana zimenezi n’kofunika? Cifukwa cakuti ena amene poyamba anali kutumikila Yehova, afooka mwauzimu ndi kubwelelanso ku makhalidwe awo akale. Conco, tonse tifunika kukumbukila cenjezo lakuti: “Amene akuyesa kuti ali cilili asamale kuti asagwe.”—1 Akor. 10:12.

“CITITSANI” ZILAKO-LAKO ZANU “KUKHALA ZAKUFA KU DAMA”

5. (a) Fotokozani citsanzo coonetsa kuti tifunika kuvula mwamsanga umunthu wakale. (Onani pikica kuciyambi.) (b) Malinga ndi Akolose 3:5-9, ni makhalidwe ati amene ali mbali ya umunthu wakale?

5 Mungacite ciani ngati covala canu cada ndipo cayamba kununkha? Mungacivule mwamsanga, si conco? Mofananamo, tifunika kucitapo kanthu mwamsanga kuti tileke makhalidwe amene Mulungu amadana nawo. Tifunika kutsatila malangizo omveka bwino amene mtumwi Paulo anapeleka kwa Akhristu a m’nthawi yake. Ponena za makhalidwe oipa, iye anawauza kuti: ‘Muwataye kutali ndi inu.’ Tsopano, tiyeni tikambilane aŵili mwa makhalidwe oipa amene mtumwi Paulo anachula. Makhalidwewa ni dama komanso zinthu zodetsa.—Ŵelengani Akolose 3:5-9.

6, 7. (a) Kodi mau a Paulo amaonetsa bwanji kuti tifunika kucita khama kuti tivule umunthu wakale? (b) Kodi Sakura anali na khalidwe lanji poyamba? Nanga n’ciani cinamuthandiza kusintha?

6 Dama. Liu la cinenelo coyambilila ca Baibo limene analimasulila kuti “dama,” limaphatikizapo kugonana kwa anthu amene si okwatilana mwalamulo, ndiponso kugonana kwa amuna okha-okha kapena akazi okha-okha. Paulo anauza Akhristu anzake kuti ‘acititse ziwalo za thupi lawo . . . kukhala zakufa,’ kutanthauza kuthetselatu zilako-lako zonse zoipa zokhudzana ndi “dama.” Mau amphamvu ndi omveka bwino amenewa a Paulo, aonetsa kuti pamafunika khama kuti munthu akwanitse kuthetsa zilako-lako zoipa. Ndipo n’zotheka ndithu kupambana pa nkhondo yolimbana ndi zilako-lako zoipazi.

7 Ganizilani zimene zinacitikila Sakura * wa ku Japan. Kuyambila ali mwana, anali kusungulumwa kwambili ndi kudziona ngati wosafunika. Atafika zaka 15, anayamba kucita ciwelewele ndi amuna osiyana-siyana pofuna kuthetsa vuto lake la kusungulumwa. Pofotokoza zotulukapo zake, iye anati: “N’nacotsa mimba katatu.” Anakambanso kuti: “Poyamba, kucita zaciwelewele kunali kunipangitsa kudziona kuti ndine wofunika, ndi kuona kuti anthu ena amanikonda. Koma pamene n’napitiliza kucita zaciwelewele, vuto langa lodziona kuti ndine wosafunika linakulila-kulila.” Sakura anapitiliza khalidwe loipali mpaka pamene anakwanitsa zaka 23. Kenako, anayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Zimene anaphunzila anazikonda kwambili, ndipo mothandizidwa na Yehova analeka kucita zaciwelewele. Anakwanitsanso kuthetsa maganizo odziimba mlandu amene anali nawo. Sakura lomba ni mpainiya wanthawi zonse, ndipo salinso wosungulumwa. M’malomwake, iye anati, “Ndine wokondwa kwambili cifukwa ca cikondi cimene Yehova amanionetsa tsiku lililonse.”

MMENE TINGATHETSELE ZIZOLOŴEZI ZOIPA

8. N’zinthu ziti zimene zingalengetse munthu kukhala wodetsedwa pamaso pa Mulungu?

8 Zinthu zodetsa. Liu la cinenelo coyambilila ca Baibo limene linamasulidwa kuti “zinthu zodetsa” limaphatikizapo zinthu zambili, osati cabe macimo okhudzana ndi zaciwelewele. Zinthu zodetsa zingaphatikizepo zizoloŵezi zoipa monga kukoka fodya kapena kukamba nthabwala zotukwana. (2 Akor. 7:1; Aef. 5:3, 4) Komanso, zimaphatikizapo makhalidwe oipa amene munthu angacite mseli, monga kuŵelenga nkhani zoutsa cilako-lako ca kugonana kapena kutamba zamalisece. Zimenezi zingalengetse munthu kuyamba cizoloŵezi coipa ca kudzipukusa umalisece.—Akol. 3:5. *

9. Kodi kukhala na “cilakolako ca kugonana” cosaletseka kumabweletsa mavuto anji?

9 Anthu amene ali na cizoloŵezi cotamba zamalisece, amakhala ndi “cilakolako ca kugonana” cosaletseka, moti nthawi zonse amalaka-laka kucita ciwelewele. Ofufuza apeza kuti anthu amene amakondetsetsa kutamba zamalisece, amalephela kudziletsa mofanana ndi anthu amene amamwa mowa mwaucidakwa ndi amene amaseŵenzetsa mankhwala osokoneza ubongo. Conco, n’zosadabwitsa kuti kutamba zamalisece kumakhala na zotulukapo zoipa. Mwacitsanzo, kumacititsa munthu kudziimba mlandu, kusagwila nchito mwakhama, kukhala ndi maganizo ofuna kudzipha, kusoŵa mtendele m’banja, ngakhalenso kutha kwa banja. Munthu wina pokondwelela kuti watha caka osatambako zamalisece, analemba kuti: “Poyamba n’nali kudziona ngati wacabe-cabe, koma tsopano nimadziona kuti ndine munthu.”

10. N’ciani cinathandiza Ribeiro kuleka cizoloŵezi cake cotamba zamalisece?

10 Anthu ambili zimawavuta kuthetsa cizoloŵezi cotamba zamalisece. Koma zimene zinacitikila Ribeiro wa ku Brazil, zionetsa kuti n’zotheka kuthetsa cizoloŵezi cimeneci. Ribeiro anacoka panyumba ali na zaka pakati pa 13 ndi 19, ndipo m’kupita kwa nthawi anakaloŵa nchito pa fakitale ina yopanga mapepa kucokela ku mabuku amene amataidwa. Kumeneko, anaona zithunzi zamalisece. Iye anati: “Pang’ono ndi pang’ono, n’nakhala na cizoloŵezi cotamba zamalisece. Zinthu zinafika poipa kwambili cakuti n’nali kucita kulaka-laka kuti mkazi wanga acoke panyumba kuti nitambe bwino mavidiyo a zamalisece.” Ndiyeno, tsiku lina pamene iye anali kuseŵenza, anayang’ana pa mulu wa mabuku akale oti apangile mapepa, ndipo anaona buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Iye analitenga ndi kuliŵelenga. Zimene anaŵelengazo zinamulimbikitsa kuti ayambe kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Koma zinam’tengela nthawi yaitali kuti athetse cizoloŵezi cake coipa. Kodi n’ciani cinamuthandiza? Iye anati: “Pemphelo, kuphunzila Baibo, ndi kusinkhasinkha zimene n’naphunzila, zinanithandiza kudziŵa bwino makhalidwe a Mulungu cakuti n’nayamba kukonda kwambili Yehova kuposa kutamba zamalisece.” Mothandizidwa ndi Mau a Mulungu ndi mzimu wake woyela, Ribeiro anakwanitsa kuvula umunthu wake wakale. Iye anabatizika, ndipo pano tikamba ni mkulu mumpingo.

11. N’ciani cimene munthu afunika kucita kuti athetse vuto la kutamba zamalisece?

11 Onani kuti Ribeiro sanangoŵelenga Baibo cabe kuti aleke cizoloŵezi cotamba zamalisece. Iye analola zimene anaphunzila m’Baibo kumufika pamtima. Inde, kupemphela ndi kusinkha-sinkha kunacititsa kuti cikondi cake pa Mulungu cikhale camphamvu kwambili kuposa cilako-lako cake cofuna kutamba zamalisece. Conco, kukulitsa cikondi pa Yehova komanso kudana ndi zoipa ndiye cisinsi cothetsela vuto la kutamba zamalisece.—Ŵelengani Salimo 97:10.

MUTAYE KUPSA MTIMA, MAU ACIPONGWE, NDI KUNAMA

12. N’ciani cinathandiza Stephen kuleka kupsa mtima ndi kukamba mau acipongwe?

12 Anthu a mtima wapacala, amakonda kukamba mau acipongwe akapsa mtima. Munthu amene amakwiya msanga sangakhale na banja lacimwemwe. Stephen wa ku Australia, amene ni kholo anakamba kuti: “N’nali kukonda kukamba mau onyoza ndiponso n’nali kukwiya kaŵili-kaŵili pa nkhani zing’ono-zing’ono. Katatu konse, ine na mkazi wanga tinapatukana ndipo cikwati cathu cinatsala pang’ono kutha.” Kenako, onse aŵili anayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Kodi n’ciani cinacitika Stephen atayamba kutsatila malangizo a m’Baibo? Iye anati: “Zinthu zinayamba kuyenda bwino m’banja lathu. Mothandizidwa ndi Yehova, tsopano nili na mtendele wa m’maganizo ndipo ndine wodekha, koma kale n’nali monga bomba yoteya-teya. N’nali wamkali ndipo n’nali kukwiya kwambili na zinthu zocepa.” Pali pano, Stephen ni mtumiki wothandiza, ndipo mkazi wake wakhala akucita upainiya wa nthawi zonse kwa zaka zambili. Akulu mumpingo wa Stephen anati: “Stephen ni m’bale wodekha, wakhama pa nchito, ndiponso wodzicepetsa.” Iwo anakambanso kuti sanamuonepo atakwiya. Kodi Stephen amaona kuti anakwanitsa yekha kusintha? Iye anati: “Nikanapanda kulola Yehova kunithandiza kuvula umunthu wakale ndi kuvala watsopano, sembe sin’nakwanitse kukhala na makhalidwe abwino amenewa.”

13. Kodi kupsa mtima kungabweletse mavuto ati? Nanga Baibo imapeleka cenjezo lanji?

13 M’pomveka kuti Baibo imaticenjeza kuti tifunika kupewa kupsa mtima, kukamba mau acipongwe, ndi kulalata. (Aef. 4:31) Makhalidwe amenewa amapangitsa munthu kukhala waciwawa. Anthu m’dzikoli amaona kuti kupsa mtima kuli cabe bwino, koma vuto n’lakuti kumanyozetsa Mlengi wathu. Abale na alongo athu ambili aleka makhalidwe oipa amenewa ndipo avala umunthu watsopano.—Ŵelengani Salimo 37:8-11.

14. Kodi n’zotheka munthu waciwawa kusintha n’kukhala wofatsa?

14 Mwacitsanzo, ganizilani za Hans, amene ni mkulu mumpingo wina ku Austria. Mgwilizanitsi wa bungwe la akulu mumpingo wawo anati: “Iye ni mmodzi mwa abale ofatsa kwambili.” Koma kale Hans sanali wofatsa. Pamene anali wacinyamata, anayamba kumwa moŵa mwaucidakwa, ndipo zotulukapo zake anakhala munthu waciwawa. Tsiku lina atakolewa, anapha cisumbali cake ndipo anaweluzidwa kuti akakhale m’ndende kwa zaka 20. Poyamba, umoyo wa m’ndende sunamuthandize Hans kusintha khalidwe lake laciwawa. Conco, m’kupita kwa nthawi, amayi ake anapempha mkulu wina mumpingo kuti akaonane naye m’ndendemo. Zotulukapo zake, Hans anayamba kuphunzila Baibo. Iye anakamba kuti: “Zinali zovuta kuvula umunthu wanga wakale. Koma malemba amene ananilimbikitsa kusintha ndi Yesaya 55:7, imene imati: ‘Munthu woipa asiye njila yake,’ ndi 1 Akorinto 6:11, imene imakamba za anthu amene analeka makhalidwe oipa. Lembali limati: ‘Ndipo ena mwa inu munali otelo.’ Kwa zaka zambili, Yehova ananithandiza moleza mtima pogwilitsila nchito mzimu wake woyela kuti nivale umunthu watsopano.” Hans atapika ndende zaka 17 na hafu, anatulutsidwa ndipo panthawiyo anali atabatizika monga Mboni. Iye anati: “Nimayamikila ngako kuti Yehova ananionetsa cifundo cacikulu na kunikhululukila.”

15. Ni khalidwe lanji limene ni lofala masiku ano? Nanga Baibo imakamba ciani za khalidweli?

15 Kunama nakonso ni mbali ya umunthu wakale. Mwacitsanzo, anthu ambili amakonda kunama pa nkhani za msonkho. Ena amanama kuti apewe kulandila cilango cifukwa ca macimo amene acita. Koma Yehova ni “Mulungu wacoonadi.” (Sal. 31:5) Mwa ici, iye amafuna kuti “aliyense wa” olambila ake ‘azilankhula zoona kwa mnzake’ ndi kupewa ‘kunama.’ (Aef. 4:25; Akol. 3:9) Conco, tifunika kumakamba zoona ngakhale kuti kucita zimenezo nthawi zina kungakhale kocititsa manyazi.—Miy. 6:16-19.

ZIMENE ZINAWATHANDIZA KUVULA UMUNTHU WAKALE

16. N’ciani cingathandize munthu kuvula umunthu wakale?

16 Munthu sangakwanitse kuvula umunthu wakale mwa mphamvu zake cabe. Anthu amene tawachula m’nkhani ino, Sakura, Ribeiro, Stephen, ndi Hans, anacita khama kuti aleke makhalidwe oipa. Iwo anakwanitsa kuleka makhalidwe oipawa cifukwa analola mphamvu ya Mau a Mulungu ndi mzimu wake woyela kutsogolela maganizo ndi mitima yawo. (Luka 11:13; Aheb. 4:12) Kuti nafenso tipindule na mphamvu imeneyi, tifunika kumaŵelenga Baibo tsiku lililonse, ndi kusinkhasinkha zimene taŵelenga. Tifunikanso kupempha Mulungu kuti atipatse nzelu ndi mphamvu n’colinga cakuti tikwanitse kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo. (Yos. 1:8; Sal. 119:97; 1 Ates. 5:17) Timapindulanso ndi Mau a Mulungu ndi mzimu wake woyela ngati timakonzekela ndi kupezeka pa misonkhano. (Aheb. 10:24, 25) Cinanso, tifunika kuseŵenzetsa ziwiya zonse zimene Mulungu amagwilitsila nchito pogaŵila cakudya cauzimu kwa anthu ake padziko lonse.—Luka 12:42.

N’ciani cingatithandize kuvula umunthu wakale? (Onani palagilafu 16)

17. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

17 Takambilana makhalidwe angapo oipa amene Akhristu afunika kuleka kapena kuwapewa. Koma kodi kucita zimenezi n’kokwanila kuti munthu akhale pa ubwenzi wabwino na Mulungu? Iyai. Timafunikanso kuvala umunthu watsopano. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana makhalidwe ena abwino amene afunika kukhala mbali ya umunthu wathu watsopano.

^ par. 7 M’nkhani ino, maina ena asinthidwa.

^ par. 8 Onani mutu 25 m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba.